Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Kunama Kuli Koipa Chotero?
Michelle anadziŵa kuti anzake akakhoza kukalipitsidwa atadziŵa kuti iye anaphwanya chidoli chokondeka. Iye sanali m’mkhalidwewo, ngakhale ndi tero, wa kupatsidwa chilango kapena kukhaulitsidwa. Chotero iye akupeza kachitidwe kopepuka ka kuchinjiriza ukali wa makolo ake: iye apatsa mlandu wa kuphwanyaku kwa mbale wake wachichepere.
KUNAMA—achichepere ambiri amadzimva kuti kuli kwabwino pansi pa mikhalidwe ina yake. Ena amanena kuti akakhoza kunama m’malo mofuna kuletsa kachitidwe kena kake ka upandu, kuchinjiriza wopanda mlandu, kapena kupulumutsa moyo. Mikhalidwe yoteroyo, ngakhale kuli tero, iri ya kamodzikamodzi m’moyo weniweni. Kaŵirikaŵiri kwambiri, achichepere amakhoterera ku kunama kaamba ka chifukwa chofananacho chimene Michelle anachita: kupewa chilango kapena kuchoka mumkhalidwe wosakhala bwino.
Donald anauza amayi ake kuti anali anayeretsa chipinda chake pamene, m’chenicheni, iye anali ataponya zinthu zonse pansi pa kama. M’kachitidwe kofananako, Richard anauza makolo ake kuti analephera ku sukulu, osati chifukwa chakuti sanaphunzire, koma chifukwa chakuti ‘sanali kumvana ndi aphunzitsi ake.’ Chimene chiri chosakhutiritsa kwenikweni.
Chikhalirechobe, inu mungadzimve kuti chifukwa chakuti uku sikunali kunama kokulira, palibe kuvulaza kulikonse kumene kunachitika. ‘Kodi ndi kuvulaza kotani kumene kuliko m’kunama kochepa’? inu mungafunse tero. Ndipo popeza kuti mabukhu otembenuza amatembenuza kunama kochepa kukhala “kunama kwa ulemu kapena kosavulaza,” kunena bodza laling’ono sikungawoneke kukhala koipa.
M’bukhu lakuti The Importance of Lying, H. L. Mencken akugwidwa mawu kukhala akupereka chifukwa chinachake chimene ena amakhoterera ku kunama: “Chomwe chimaipitsa chowona chiri chakuti iko kwakukulukulu kuli kosayenera, ndipo kaŵirikaŵiri kuli kupusa. Malingaliro a munthu amafunafuna chinachake chomwe chiri chosangalatsa koposa ndi chosamalira.” Chotero, nchosadabwitsa, kuti anthu kaŵirikaŵiri samafuna kumvera chowona kwenikweni, akumasankha m’malo mwake “kuyabwa makutu awo.” (2 Timoteo 4:3) Mphunzitsi wamkulu yemwe anakhalapo ndi moyo kuposa aliyense, Yesu Kristu, anachipeza icho kukhala chowona. “Ngati ndilankhula chowonadi,” iye ananena tero kwa anthu a m’tsiku lake, “chifukwa ninji simundikhulupirira ine?” (Yohane 8:46) Chiri chiyeso chotani nanga panthaŵi zina kulankhula bodza losangalatsa m’malo mwa chowonadi chofala!
Koma kodi nsonga yakuti kunama kungakhale kokoka kapena kanthu kakang’ono kapena kotanthauzidwa bwino kungatanthauze kuti kuli kwabwino?
Kawonedwe ka Mulungu ka Kunama
Chikhoterero cha anthu cha kunama chinadziŵika kumbuyoko mu nthaŵi za Baibulo. Anatero wamasalmo kuti: “Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wotyasika, ndi mitima iŵiri.” Chikondwerero chaumwini chinasonkhezera kumbuyo kwa kunama kwawo. Iwo ananena kuti: “Milomo yathu [yonama] nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?” Dziŵani, ngakhale kuli tero, mmene Mulungu amadzimverera ponena za njira ya kunama kwawo: “Yehova adzadula milomo yonse yotyasika, lilime lakudzitamandira.”—Masalmo 12:2-4.
Inde, “lilime lonama” linali ndipo liri limodzi la zinthu zimene “Yehova amada.” (Miyambo 6:16, 17) Ndiko nkomwe, ali Satana Mdyerekezi iyemwini amene ali “atate wa bodza.” (Yohane 8:44) Mosangalatsa, ngakhale kuli tero, Baibulo silimapanga kusiyana pakati pa kunama ndi ‘kunama kochepa.’ Ilo limangonena kuti, “kulibe bodza lochokera kwa chowonadi.” (1 Yohane 2:21) Icho ndicho chifukwa chake “wamphulupulu anyansa Yehova, koma chinsinsi chake chiri ndi owongoka.” (Miyambo 3:32) Inde, Yehova mwachidule sadzakhala ndi unansi wathithithi ndi winawake yemwe ali wosawona mtima.
Chotero wachichepere wowopa Mulungu sangawone mtundu uliwonse wa kunama kukhala wolandirika. Monga mmene wachichepere wotchedwa Tyrone achiikira icho kuti: “Chiri monga mayeso owona kapena abodza. Chinachake chimakhala kaya cholondola kapena cholakwika.”
Kunama—Chifukwa Chimene Kuliri Kovulaza
Nchifukwa ninji, ngakhale kuli tero, chimene kunama kuliri kolakwika? Kodi kunama sikungakhoze kukupulumutsani inu kukupatsidwa chilango? Mwinamwake. Koma nchiyani chimene chimachitika ngati bodza lavumbulutsidwa? Chotero ilo langochedwetsa kokha chilango. André wachichepere anawonanso kuti: “Chimakupangitsa kukhala wopenga pamene winawake akuuza iwe chinachake ndipo uchipeza pambuyo pake kuti chinali kunama.” Inde kunama kumadzutsa mkwiyo ndi kukalipitsidwa. Ndipo ngati amene mwawanamiza ali makolo anu—mankhwala owopsya achilango angatulukepo.
Nchosadabwitsa kuti Baibulo limanena kuti: “Kupata chuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda.” (Miyambo 21:6) M’mawu ena, mwaŵi uliwonse umene kunama kungabweretse umakhala wosakhalitsa monga nkhungu.
Kunama ndi Chikumbumtima Chanu
Kunama kumavulazanso wonama iyemwini. Michelle (yemwe wangotchulidwa poyambirirapo) anakhoza kukhutiritsa makolo ake kuti anali mbale wake yemwe anaphwanya chidolicho. Komabe, iye pambuyo pake anadzimva kukhala wokakamizidwa kuwulula cholakwa chake kwa iwo. Michelle akulongosola kuti: “Ndithudi ndinadzimva woipidwa kwambiri nthaŵi zambiri. Makolo anga anaika chikhulupiriro mwa ine, ndipo ndinawakhumudwitsa.”
Chikumbumtima choipa cha Michelle chimachitira chitsanzo bwino lomwe lamulo lolongosoledwa ndi mtumwi Paulo. Pa Aroma 2:14, 15 iye akusonyeza kuti Mulungu waika mkati mwa mtundu wa anthu kuzindikira kwa chikumbumtima. Paulo akulongosola mmene ichi chimagwirira ntchito, mwakunena kuti: “Chikumbumtima chawo chichitiranso umboni pamodzi nawo, ndipo maganizo awo wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana.” M’nkhani ya Michelle chikumbumtima chake ‘chinachitira umboni’ ku chenicheni chakuti kunama kunali kolakwa ndipo ‘chinamuneneza iye’—kumusautsa iye ndi malingaliro a kukhala wa liwongo.
Nzowona kuti, munthu anganyalanyaze chikumbumtima chake, akumachilimbitsa icho. Nkhani mu magazini yakuti Adolescence inasonyeza, mwachitsanzo, kuti achichepere amakhoterera ku kuwona kunama kukhala kolakwika. Koma pamene akula, kawonedwe kawo ka kunama kamaipirako. “A zaka zakubadwa khumi ndi zisanu,” inatero nkhaniyo, “amawona kunama nthaŵi zina monga chinthu chinachake chosalakwika ndi kubwereza kokulira kuposa mmene amachitira a zaka zakubadwa khumi ndi ziŵiri.” Mwachiwonekere, kuchulukira kumene munthu amachita ndi kunama, kumakhalanso kuchulukira kumene iye amakhalira mu ngozi ya kukhala ‘wolochedwa m’chikumbumtima mwake monga ndi chitsulo cha moto.’—1 Timoteo 4:2.
Kukulitsa “Chikumbumtima Chokoma”
Mwa njira ya kusiyanitsa, mtumwi Paulo anakhoza kunena ponena za iyemwini ndi atsamwali ake kuti: “Takopeka mtima kuti tiri nacho chikumbumtima chokoma.” (Ahebri 13:18) Chikumbumtima cha Paulo sichinamulole iye kugonjera ku kunama kapena chowonadi chochepa. Kodi chikumbumtima chanu chiri chozindikira ku chomwe chiri chosawona? Ngati sitero, chiphunzitseni icho mwa kuphunzira Baibulo ndi mabukhu ozikidwa pa Baibulo, onga ngati magazini ino ndi inzake, Nsanja ya Olonda.
Wachichepere wotchedwa Bobby wachita choterocho, ndi zotulukapo zabwino. Pa nthaŵi imodzi zofalitsidwa zimenezi zachita ndi mavuto omwe iye anakhala nawo. M’malo mwa kuphimba vutolo ndi chokuta chonama, iye wavutitsidwa ndi chikumbumtima chake kufikira makolo ake ndi kukambitsirana mowona mtima za nkhaniyo. Pa nthaŵi zina ichi chatulukapo m’kulandira kwake chilango. Iye ngakhale kuli tero amavomereza kuti ‘amadzimva bwino mu mtima” kaamba ka kukhala wowona mtima.
Chitayerekezedwa, monga mmene wachichepere mmodzi anachiikira: “Ngati mulankhula chowona, chidzakalipitsa makolo anu,” komabe, iwo adzalemekeza kuwauza kwanu chowonadi. Icho chidzasonyeza kwa iwo kuti inu mukukula ndi kuzindikira kuti mudzadziŵerengera kaamba ka zochita zanu.
Chithandizo china m’kukulitsa chikumbumtima chokoma chiri kukhala wosamala m’kusankha mabwenzi. “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru, koma m’nzawo wa opusa adzapwetekedwa,” yatero Miyambo 13:20. Anawona tero Bobby: “Bwenzi amene umanama naye adzakuika m’mavuto. Iye sali bwenzi yemwe ungakhulupirire.” Chotero wamasalmo ananena mwanzeru kuti: “Sindinakhala pansi ndi anthu achabe.” (Masalmo 26:4) Yesani kupeza mabwenzi amene amalemekeza malamulo aumulungu.
Potsirizira pake, mutayesedwa kuti muname, kumbukirani malamulo amene Yehova Mulungu wawaika kaamba ka mabwenzi a iyemwini. “Yehova, ndani adzagonera m’chihema mwanu?” anafunsa tero wamasalmo. “Iye amene . . . amanena zowonadi mumtima mwake.” (Masalmo 15:1, 2) Kuwunikira pa mmene chiriri cha mwaŵi kukhala ndi unansi ndi Yehova kudzasonkhezera wina kukhala wowona mtima!
Kulankhula chowona sichiri nthaŵi zonse chopepuka. Inu mungakhoze ngakhale kukhala mumkhalidwe umene “gulu la anthu limanena bodza, ndipo inu mukufunikira kulankhula chowona,” monga mmene wachichepere wotchedwa Mark akuchiikira icho. Koma uyo amene amapanga chigamulo cha kulankhula chowonadi adzasungilira chikumbumtima chabwino, unansi wabwino ndi mabwenzi ake enieni, ndipo chabwino koposa, unansi wabwino ndi Mlengi wake. Chotero wachichepere wotchedwa Steven anafupikitsa nkhaniyo bwino lomwe pamene ananena kuti: “Chenicheni chakuti ena amanena bodza sichimatanthuza kuti inu mufunikiranso!”
[Mawu Otsindika patsamba 20]
Kunama kaŵirikaŵiri kumakhala kosakhutiritsa ndipo kungangochedwetsa chilango kufikira zitavumbulutsidwa
[Chithunzi patsamba 21]
Kuwulula cholakwa sichiri chopepuka, koma makolo anu adzalemekeza kuwona mtima kwanu