Kodi Chimatanthauzanji Kukhala Wowona Mtima?
KUKHALA wowona mtima kumatanthauza kukhala wokhulupiririka ndi womasuka ku chinyengo. Kuwona mtima kumafunikira kuti mukhale womvera chisoni m’kuchita kwanu ndi ena—wolunjika, wolemekezeka, osati wonyenga kapena kusokeretsa. Munthu wowona mtima ali munthu waumphumphu. Kukhala wodalirika nthaŵi zonse, iye sadzanyenga munthu mnzake. Tonsefe tingakonde kuchitiridwa mwanjira imeneyo, kodi sitingatero? Chotero kodi kuwona mtima kungakhale kwachikale?
Mkristu mwamsanga amawona m’kalongosoledwe kapamwambaka chifukwa chimene aliyense wodzinenera kukhala mlambiri wowona ayenera kukhala munthu wowona mtima. (Yohane 4:24) Iye amalambira “Yehova Mulungu wa chowonadi.” (Masalmo 31:5; Tito 1:2) Moyenerera, kokha “anthu a chowonadi” amayenerera kumuimira iye.—Eksodo 18:21, New World Translation Reference Bible, mawu a m’munsi.
Kuwona mtima kumayambukira mbali zambiri za miyoyo yathu, chotero chiri chomvekera kuti mtumwi Paulo ananena kuti: “Pofuna kukhala nawo makhalidwe abwino.” Chimenecho chimaphatikizapo m’kulankhula, pa ntchito, m’nkhani za banja, ndi machitachita a bizinesi, ndiponso m’kuyankha ku zifuno zirizonse za lamulo za boma zoikidwa pa ife.—Ahebri 13:18.
M’zimene Timanena
Pali njira zambiri—ngakhale kuti kaŵirikaŵiri zimawonedwa kukhala zopanda liwongo ndiponso zolandirika—mu zimene anthu salankhula chowonadi. Iwo amanamizira maripoti a maora a ntchito, kuwauza ana kukamba bodza kwa okufunani, kupereka malingaliro osalongosoka kwa nthumwi za ndalama zosungidwa kaamba ka chitetezero, ndi kunama ponena za kudwala kuti asapite ku ntchito, kungotchula zochepa zokha.
Nthaŵi zina zimene timanena kwa wina zikafunikira kulembedwa. Kaamba ka chifukwa china, anthu amene sakonda kunama mwakulankhula adzimva kuti iri nkhani yosiyana pamene asimba ndalama za msonkho kapena kuwonetsa chinthu kwa nthumwi za kasitomu pa malire a dziko. Kunama kumeneku kumataikira anthu onse olipira msonkho. Kodi chimenecho chiri chikondi chenicheni kaamba ka mnansi? Pa mbali pa icho, kodi Akristu sali ndi thayo la “kupereka zinthu za Kaisara kwa Kaisara”?—Luka 20:25; 10:27; onaninso Aroma 13:1, 2, 7, 8.
M’zimene tilankhula, ife ndithudi timafuna kutsanzira “Mulungu wa chowonadi,” osati “atate wa bodza.” (Masalmo 31:5; Yohane 8:44) Anthu opanda lamulo amakhoterera ku kulankhula paŵiri kuti apereke nkhani ya bodza ndi kunyenga. Koma kunama kwa mnansi wathu sikuli kumkonda iye. Pambali pa icho, abodza alibe mtsogolo mwenimweni.—Aefeso 4:25; Chivumbulutso 21:27; 22:15.
Pa Ntchito
Kugwira ntchito ya tsiku mowona mtima kaamba ka malipiro olandiridwa kuli koyenera ndipo chifuno cha Malemba. (Akolose 3:22-24) Komabe, pali zikwi zochulukira za mbala za nthaŵi zomwe zimataya nthaŵi ya kampani mwa kupuma mopitilira malire, kubwera ku ntchito mochedwa ndi kuchoka msanga, kuwononga nthaŵi yambiri kudzikonza iwo eni pambuyo pa kufika pa ntchito, kugwiritsira ntchito foni ya kampani kaamba ka malamya aumwini a atali osavomerezedwa, kuchita bizinesi yawoyawo panthaŵi ya kampani, ndipo ngakhale kuwodzera. Kuba kwawo kumachulukitsa zowonongedwa za aliyense.
Mitundu ina ya kuba pa ntchito imaphatikizapo kutenga zinthu ndi ziwiya kaamba ka kugwiritsira ntchito kwaumwini. Ena amadzinenera kuti ‘ichi sichiri kanthu kalikonse kowonjezereka kuposa kukwaniritsira kokha malipiro osakwanira, monga ngati akukwaniritsa zinthu ndi olemba ntchito owuma khosi! Koma ngati kutenga zinthuzo kuli kopanda chidziŵitso ndi chilolezo cha mwini wake kapena wolemba ntchito, iko ndithudi kuli mtundu wa kuba.
M’mikhalidwe yonseyi, Akristu owona adzagwiritsira ntchito uphungu wouziridwa: “Wakubayo asabenso, . . . nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho cha kuchereza osowa.”—Aefeso 4:28; Machitidwe 20:35.
Komabe, bwanji ngati wokulembani ntchito akufunsani inu kuchita kachitidwe kena kosawona mtima kapena kachitidwe kosakhala ka lamulo, ndipo akumawopsyeza kuti adzakuchotsani ntchito ngati simugwirizana naye? Zitsanzo zina: Kulipiritsa kasitomala wanu kaamba ka kubwezeretsa mbali za galimoto zomwe sizinaikidwe pa galimotoyo; kuikapo za mtengo wotsika, zinthu zopanda pake m’bokosi kotero kuti makasitomala angalipiritsidwe mtengo wapamwamba; kulemba kuti chatsopano, “chatsitsidwa mtengo” pa zinthu zakale, pamene mitengo yoyambirira inali imodzimodziyo kapena yotsitsidwako. Olemba ntchito ambiri angawone ichi monga thayo la wowalemba ntchito, osati la ogwira ntchito. Nchiyani chimene Mboni za Yehova zachita pamene zayang’anizana ndi mkhalidwe woterewu? Daryl J , akulongosola kuti:
“Pamene ndinali kugwira ntchito monga manijala wotulutsa zinthu mu golosale ya sitolo, ndinafikiridwa ndi oyang’anira zinthu ndi kufunsidwa kuwonjezera phindu popanda kuwonjezera mitengo iriyonse. Malingaliro akukwaniritsira ichi anali akuti: Ndinene monyenga kulemera kwa zinthu zina, ndi kupereka makardi a ngongole ‘onyenga’ kwa opereka zinthuwo. Machitachita ofala koma osawona mtima.”
Daryl anakana kuimira monyenga ndi kunama. (Miyambo 20:23) Milungu yochepa pambuyo pake iye anachotsedwa ntchito. Kodi iye anali wopanda nzeru kugonjetsera banja lake ku zotulukapo za kupanda kwake ntchito? Kodi iye anadandaula chifukwa cha kukhala wowona mtima? Ayi, popeza pamene Mboni inzake inamva zimene zinachitika, inamupatsa ntchito. Daryl akunena kuti: “Mu milungu itatu kufika ku inayi, ndinabwerera pa kudzichirikiza inemwini ndi banja langa mwa njira za kuwona mtima. Ndimachiwona icho monga mwaŵi wa kudalitsidwa ndi Yehova kaamba ka kusunga umphumphu wanga kwa iye.”
Pambali ina, mungapeze ntchito chifukwa NDINU wowona mtima. Nthumwi ya kampani yosunga ndalama za chitetezero cha dziko lonse yodziŵika koposa inalangiza mwiniwake wa sitolo ya chipambano kunsi kwa mzinda wa Toronto, Canada, kuthetsa vuto lake la kuba kochitidwa ndi anthu antchito mwa kulemba ntchito Mboni za Yehova. Mwiniwake analongosola kuti: ‘Pamene ndinali mu mzinda wina kulandira maphunziro anga a kusunga ndalama za chitetezero, ndinapeza kuti pakati pa anthu awo owagwirira ntchito panali msika waukulu kwambiri womwe unalemba ntchito kokha Mboni kubwezeretsanso zinthu pa mashelefu usiku. Iwo anali atakumana ndi zokumana nazo zina zoipa ndi antchito ena koma sanatayepo chinthu chirichonse kuyambira pamene mfungulo zinaperekedwa kwa Mboni kubwera pambuyo pa maora ogwira ntchito kaamba ka kubwezeretsanso zinthu.’
Njira Zina za Kukhalira Owona Mtima
Pa nthaŵi yobwereka ndalama, wobwerekayo kaŵirikaŵiri amasonyeza kudzichepetsa ndi ulemu, ndipo amalongosola mawu otsimikizira ponena za kubwezera ndi chiyamikiro kaamba ka thandizolo. Koma pamene nthaŵi ya kubwezera ndalamazo ifika, kusintha kwa mkhalidwe kodabwitsa kwa mbali ziŵiri ina yabwino ndi ina yoipa kumabwera pa ena obwerekawo. Chotero chiri chofala kuwona mkwiyo, ukali, kudandaula kwa kuvutitsidwa kaamba ka kubwezera, ndi kudzinenera kwakuti wobwerekayo alibe chifundo. M’maso mwa wobwerekayo, wobwereketsa woolowa manjayo amasinthidwa kukhala chowopsya! Baibulo, ngakhale kuli tero, limanena kuti ‘woipa akongola wosabweza.’ (Masalmo 37:21; Aroma 13:8) Ichi mwapadera chingakhale tero kumene wobwerekayo sakupanga kuyesayesa kulikonse kwa kubwezeretsa ngakhale ndalama zochepera kuchitira chitsanzo chikhulupiriro chabwino, mwinamwake osapanga ngakhale kuyesayesa kulikonse kwa kuyesera kulankhula ndi wobwereketsayo.
M’moyo wa banja, kuwona mtima kumaitanira ku nkhani zambiri: Mutu wa banja ufunikira kukhala wowona kwa mkazi wake ponena za ndalama zake zomwe amalandira ndi nkhani za chuma; mkazi ayenera kukhala wowona mtima kwa iye mwa mmene amawonongera ndalama za banja; onse afunikira kukhala anthu aumphumphu, kuphatikizapo kuika malire ku zikondwerero zawo za kugonana kwa wina ndi mnzake; ana amachita bwino kukhala owona ndi omvera ponena za mayanjano awo ndi mtundu wa zosangulutsa, mogwirizana ndi zikhumbo zokhazikitsidwa ndi makolo awo.—Aefeso 5:33; 6:1-3.
Kuchokera ku zonse zomwe zanenedwa, chifunikira kukhala chowonekera bwino kuti Mkristu weniweni ayenera “kudzipatula ku chosalungama”—ntchito zoipa ndi zipatso zoipa zomwe zimatsagana ndi kusawona mtima, kunama, kunyenga, kuba, ndi kuipa kwa makhalidwe abwino.—2 Timoteo 2:19; Aroma 2:21-24.
Mphoto ndi Mapindu
Kulingalira ndi kulunjika, kuchita ndi ena mowona, kumapititsa patsogolo mtendere. Mkhalidwe wa kukhulupirira ndi kudalira umakula, ndi kutsogolera ku mkhalidwe wabwino ndi maunansi abwino. Kuwona mtima kumaperekanso mkhalidwe wa kukhala kotsimikizirika, aufulu ku nthaŵi ndi kuchinjiriza kumene kumatha mphamvu komwe kumayambitsidwa ndi kulingalira, kukaikira, ndi kuwopa ena.—Yerekezani ndi Yesaya 35:8-10.
Kuwona mtima kumagawirako ku kukhala kwathu ndi chikumbumtima chabwino, chomwe chiri chofunikira ngati tikafunikira kupereka “utumiki wopatulika kwa Mulungu wa moyo.” (Ahebri 9:14; 1 Timoteo 1:19) Chimapereka mtendere wa maganizo, ndi kutsogolera, ku tulo tabwino usiku. Mungayang’anizane ndi ena popanda kumvetsedwa manyazi. Kukhala wowona mtima kumachotsapo mantha akuwopa kugwidwa m’kuchita cholakwa. Mwa njira imeneyi tingasunge ulemerero waumunthu ndi kudzilemekeza kwaumwini. Ndimotani mmene iko kungakhalire kwachikale kapena kosagwira ntchito?
Chotero, pali mphoto zambiri za pa nthaŵi ino ndi mapindu omwe adzabwera kwa ife ndi ena ngati tikhala anthu owona mtima. Komabe, koposa china chirichonse, tiyenera kufuna kukhala owona mtima osati kokha chifukwa chakuti uli mkhalidwe wabwino koposa kapena chifukwa chakuti tikulamuliridwa kukhala owona mtima koma chifukwa chakuti timakonda Atate wathu Yehova. Tikufuna kusunga unansi wathu wapadera ndi iye ndi kukhala ndi chivomerezo chake. Tifunikiranso kukhala owona mtima chifukwa mwakutero timasonyeza chikondi kaamba ka mnansi. Chotero, titachiika mofupikitsa, kukhala Mkristu wowona kumatanthauza kukhala wowona mtima.—Mateyu 22:36-39.
Wamasalmo ananena kuti: “Yehova, ndani adzagonera m’chihema mwanu? Adzagonera ndani m’phiri lanu lopatulika? Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo. Nanena zowonadi mu mtima mwake . . . Ndipo satola mseke pa mnansi wake.” (Masalmo 15:1-3) Ngati titsogoza miyoyo yowona mtima monga alambiri a Yehova, chotero pamene iye molungama adzatha dongosolo lopanda chilungamo liripoli ndi pamene “hema wa Mulungu adzakhala ndi anthu,” tidzakhala pakati pa awo omwe adzasangalala ndi madalitso osatha monga “mlendo” wake. Kenaka IFE sitidzakhalanso achikale!—Chivumbulutso 21:1-5.
[Bokosi patsamba 5]
Kodi Mungachite ndi Chitokoso cha Kuwona Mtima Kwanu?
Dziko limene tikukhalamo liri ndi chitokoso cha zitsimikiziro zathu ndi zigamulo zathu za kuchita chomwe chiri cholungama. Ilo lapangidwa kugogomezera kuika ife eni choyamba, ngakhale pa chivulazo cha ena.
Kodi chiri kawonedwe kanu kosungiliridwa kakuti kuwona mtima kudakali mkhalidwe wabwino koposa? Kodi zitsimikiziro zanu ziri zamphamvu mokwanira KUSUNGA kuwona mtima kwanu pamene zitsenderezo zibweretsa pa inu chiyeso? Mwachitsanzo, nchiyani chimene mungachite ngati:
◻ Pambuyo pa kukhala wosalembedwa ntchito kwa miyezi ingapo, mupeza ndalama zambiri zimene zingakwaniritse zinthu zanu zoyenera kulipira ndi kukupatsani ndalama zapadera?
◻ Ngati kunyenga pa mayeso ofunika kwambiri mu sukulu kunali njira yokha ya kupezera gredi imene ikagamulapo mtsogolo mwanu mwa ndalama?
◻ Kuti muzindikirike monga wasayansi kukakufunikirani “kusintha” ndandanda ya zopeza zanu kotero kuti ripoti lanu lifalitsidwe?
◻ Pa tchuthi chanu ku dziko lina, mugula chinthu cha mtengo wapamwamba pa mtengo wabwino koma kuti muchisonyeze icho pa malire chikatanthauza kulipira ndalama zochuluka?
[Bokosi patsamba 6]
Zochita za Kuwona Mtima Siziri Zachikale
Kodi anthu amasamalirabe ponena za anthu anzawo? Inde, ngakhale kuti manyuzipepala amasimba zochita za kuwona mtima ngati kuti izo zinali zapadera ndipo chotero zoyenera kufalitsidwa.
Apolisi mu Fort Wayne, Indiana, U.S.A., anayesera kunyengeza mbala mwa kuika TV ya mtengo wapamwamba m’galimoto yosatsekedwa. Iwo anaiyang’ana iyo kwa milungu ingapo kuti awone chimene chidzachitika. “Chomwe tinapeza chinali chakuti anthu anali kuyenda ku mbali kwa galimotoyo, kuyang’ana mkati ndi kuwona TV, kutsegula chitseko, kusindikiza pansi batani lokhomera, kutseka chitsekocho ndi kuchokapo.” Mwa kuchita tero anasonyeza kuwona mtima.
Mutu wa nyuzipepala ya ku Canada inanena ponena za kubwezeretsedwa kwa ndalama zotaika chifukwa cha chiyambukiro chopindulitsa cha chiphunzitso cha Baibulo:
“M’samariya Wabwino apulumutsa tchuthi.”—The Windsor Star
“Pat wowona mtima abweza $421.”—The Spectator
“Kubwezeretsedwa kwa $983 yosowa kubwezeretsa chikhulupiriro cha wa malonda.”—The Toronto Star
M’nkhani zimenezi, awo amene anabwezeretsa ndalama zotaikazo anali Mboni za Yehova. Mu yoyambirirayo, Mboni ziŵiri zachichepere zikumatengamo mbali mu utumiki wa ku khomo ndi khomo zinapeza ndi kubwezeretsa chola cha ndalama kwa mkazi. Iye ananena kuti: “Ndikuganiza kuti anyamata amenewo ali mmodzi mwa miliyoni. . . . Mukudziŵa, iwo ndithudi amabwezeretsa chikhulupiriro cha wina mwa mtundu wa anthu.” Popeza kuti iye anali kunja kwa tauni, chikanakhala chapafupi kwa anyamatawo kuzisunga ndalamazo, koma iwo ananena kuti: “Sizinali chinthu chirichonse. Tinali kungoyesera kuchita chinachake chabwino kwa winawake.”
Ripoti lachiŵirilo linayeneranso kuchita ndi woyenda. “Koma chiyeso sichinasiye funso m’maganizo mwa [wopezayo],” pepalalo linasimba tero. Wopezayo analongosola kuti iye anali mmodzi wa Mboni za Yehova, “ndipo timakhulupirira mwamphamvu m’kuwona mtima.”
M’nkhani yachitatu, munthu yemwe anataya ndalamayo “ananena kuti anali atatairatu chikhulupiriro mwa munthu.” Mwamuna wa Mboni yomwe inapeza chola cha pepala chodera pang’ono cha ndalama anauza mtola nkhani kuti kutsogozedwa ndi Baibulo inali mfungulo: “Icho chinachipanga icho kukhala chopepuka kwa mkazi wanga” kubweza izo.
M’nkhani ina, Mboni ziŵiri zikumagwira ntchito ya ku nyumba ndi nyumba zinapeza enivulupu ya malipiro a ku ntchito yotaika. Pamene anaitenga iyo ku polisi ya kumaloko, nduna yaikulu yomwe inali pa ntchito inanena kuti panalibe ripoti lonena za ndalama zotaika. Mbonizo zinalingalira za kulengeza chopezedwacho pa nyumba ya wailesi ya kumaloko. Wapolisiyo anawoneka wodabwitsidwa. Iye ananena kuti: “Mukupanga kuyesayesa kokulira kwa kubwezeretsa ndalamazo. Kodi ndinu a chipembedzo chiti?” Pamene Mbonizo zinayankha, ndunayo inayankha kuti: “Ndinalingalira choncho, popeza ndinu nokha amene muli owona mtima mokwanira kupanga kuyesayesa koteroko.”
Akupanga maulendo a ku nyumba ndi nyumba mmodzi wa Mboni za Yehova W. K , anakumanizidwa ndi pempho lachilendo koposa. Mwamuna ndi mkazi wanyumbayo onse anali odwala kwenikweni koma anayenera kukasungitsa ndalama ku banki pa tsiku limenelo. Iwo anafunsa Mboniyo ngati ingachite tero. Pamene anavomereza, iye anapatsidwa $2,000 kutenga ku banki. Akubwerera kuchoka ku bankiko, iye sanaleke kufunsa kuti: “Nchifukwa ninji munandikhulupirira ine popanda kundidziŵa?” Yankho: “Tikudziŵa, ndipo aliyense amadziŵa, kuti Mboni za Yehova ziri okha amene ungakhulupirire.”
Ngakhale kuti mowonadi pali anthu owona mtima omwe angapezeke m’maiko onse, m’kuwonjezera ku Mboni za Yehova, chikuwoneka kuti iwo moyenerera ali ochepera kuti afikire pa kudziŵika kwapadera. Tiri oyamikira chotani nanga kuti chiphunzitso cha Baibulo pa kuwona mtima chikutulutsa zotulukapo zopindulutsa ndi zokhoza kugwirirapo ntchito!