Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2001 | October 1
    • Mtumwi Paulo anawalembera Akristu achihebri a zaka za zana loyamba kuti: “Utsalira mpumulo wa Sabata wa kwa anthu a Mulungu. Pakuti iye amene adaloŵa mpumulo wake, adapumulanso mwini wake ku ntchito zake, monganso Mulungu ku zake za Iye. Chifukwa chake tichite changu cha kuloŵa mpumulowo.”​—Ahebri 4:9-11.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2001 | October 1
    • Tikabwerera ku zimene Paulo anawauza Ahebri, tikuona kuti ananena kuti “utsalira mpumulo wa Sabata wa kwa anthu a Mulungu,” ndipo analimbikitsa Akristu anzake kuti achite changu “cha kuloŵa mpumulowo.” Zimenezi zikusonyeza kuti nthaŵi imene Paulo analemba mawu ameneŵa, “tsiku lachisanu ndi chiŵiri” la kupumula kwa Mulungu, limene linayamba zaka pafupifupi 4,000 m’mbuyo mwakemo, linalipobe. Silidzatha mpaka cholinga cha Mulungu kwa anthu ndi dziko lapansi atachikwaniritsa bwinobwino pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu Kristu, yemwe ndi “mwini tsiku la Sabata.”​—Mateyu 12:8; Chivumbulutso 20:1-6; 21:1-4.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2001 | October 1
    • Kufotokoza kwa Paulo za mpumulo wa Mulungu ndi mmene munthu angauloŵere kunalidi kolimbikitsa kwa Akristu achihebri a ku Yerusalemu, amene anapirira kwambiri pamene anthu anawazunza ndi kuwanyoza chifukwa cha zimene anali kukhulupirira. (Machitidwe 8:1; 12:1-5) Mofananamo, zimene Paulo ananena zingalimbikitse Akristu lerolino. Ifenso, podziŵa kuti zimene Mulungu analonjeza kuti adzabweretsa dziko lapansi la paradaiso mu Ufumu wake wolungama watsala pang’ono kuzikwaniritsa, tiyenera kupumula ku ntchito zathu ndi kuchita changu kuloŵa mpumulowo.​—Mateyu 6:10, 33; 2 Petro 3: 13.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena