Kodi Kalirole Amasonyezanji?
YANG’ANANI m’kalirole. Kodi mukuonanji? Nthaŵi zina, kupenya m’kalirole kumasonyeza kanthu kena kochititsa manyazi pa kaonekedwe kanu kamene mumakhala wokondwera kukakonza ena asanakaone.
Baibulo limafanana kwambiri ndi kalirole. Lingatithandize kukhala oona mtima ponena za ife eni, zimene zingatiletse kudzikweza kwambiri—kapena kudzitsitsa kwambiri—ponena za kufunika kwathu pamaso pa Mulungu. (Mateyu 10:29-31; Aroma 12:3) Ndiponso, Baibulo lingasonyeze zolakwa m’mawu athu, zochita, kapena mzimu zimene tiyenera kuwongolera. Zitachitika zimenezi, kodi mudzangonyalanyaza zimene kalirole asonyeza?
Yakobo mlembi wa Baibulo akuti: “Ngati munthu ali wakumva mawu wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang’anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m’kalirole; pakuti wadziyang’anira yekha, nachoka, naiŵala pompaja nali wotani.”—Yakobo 1:23, 24.
Mosiyana ndi ameneyo, Yakobo akufotokoza munthu wina, amene “akupenyerera m’lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere.” (Yakobo 1:25) Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa kuti “akupenyerera” limatanthauza kuŵeramira pambali kapena kupendekera kuti uone. “Nkhani ili pano siyakungopenya kwakanthaŵi,” ikutero Theological Dictionary of the New Testament. Liwulo limatanthauza kufunafuna mosamala kanthu kobisika. “Pali kanthu kena kofunika kamene wopenyayo akufuna kuona, ngakhale kuti kangakhale kovuta kwa iye kukaona ndi kuzindikira tanthauzo lake kamodzinkamodzi,” akulemba motero R. V. G. Tasker wothirira ndemanga pa Baibulo.
Chotero kodi mudzadziyang’anitsitsa m’kalirole wa Mawu a Mulungu ndiyeno kutsatira zimene akufuna? Yakobo akupitiriza kuti: “Ameneyo, posakhala wakumva wakuiŵala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m’kuchita kwake.”—Yakobo 1:25.