Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 12/1 tsamba 13-18
  • Kutchinjiriza Chikhulupiriro Chathu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutchinjiriza Chikhulupiriro Chathu
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Kufatsa Kwanu Kuzindikirike ndi Anthu Onse”
  • Pamene Tingatonthole, Pamene Tingalankhule
  • Bwanji za Nkhani Zabodza Zofalitsidwa?
  • Kutchinjiriza Uthenga Wabwino Mwalamulo
  • Mmene Akristu Amachitira ndi CHitonzo Chofalitsidwa
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Anadedwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chawo
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Mboni za Yehova
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sayankha Nkhani Zina Zomwe Anthu Amawanena?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 12/1 tsamba 13-18

Kutchinjiriza Chikhulupiriro Chathu

“Mumpatulikitse Ambuye Kristu m’mitima yanu; okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu.”​—1 PETRO 3:15.

1, 2. Kodi nchifukwa chiyani chitsutso sichidabwitsa Mboni za Yehova, koma kodi zimafuna chiyani?

M’MAIKO ochuluka, Mboni za Yehova kaŵirikaŵiri zimadziŵika monga anthu oona mtima ndi a makhalidwe abwino. Ambiri amaziona kuti ndi anansi abwino amene sayambitsa mavuto. Komatu, modabwitsa Akristu okonda mtendere amenewa azunzidwa mwankhanza​—m’nthaŵi za nkhondo ngakhalenso za mtendere. Iwo sadabwa ndi kutsutsidwa koteroko. Ndithudi, amakuyembekezera. Ndiponsotu, amadziŵa kuti Akristu okhulupirika m’zaka za zana loyamba C.E. anali ‘kudedwa,’ ndiye kodi pali chifukwa chilichonse choti aja amene akuyesa kukhala otsatira oona a Kristu lerolino ayembekeze zosiyana ndi zimenezo? (Mateyu 10:22) Komanso Baibulo limati: “Onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.”​—2 Timoteo 3:12.

2 Mboni za Yehova sizifunafuna chizunzo, kapenanso kusangalala ndi mavuto amene chingabweretse monga kulipira fayindi, kuikidwa m’ndende, kapena kusautsidwa. Zimafuna kukhala ndi ‘moyo wodikha mtima ndi wachete’ kotero kuti zizilalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu popanda choletsa. (1 Timoteo 2:1, 2) Zimayamikira ufulu wachipembedzo umene zili nawo m’maiko ambiri kuti zizitha kulambira, ndipo mosamalitsa zimachita zonse zimene zingathe kuti ‘zikhale ndi mtendere ndi anthu onse,’ kuphatikizapo olamulira a maboma a anthu. (Aroma 12:18; 13:1-7) Nangano, nchifukwa chiyani ‘zimadedwa’?

3. Kodi Mboni za Yehova zakhala zikudedwa pachifukwa chimodzi chiti?

3 Kwenikweni, Mboni za Yehova zakhala zikudedwa pazifukwa zofanana ndi zomwe Akristu oyambirira anazunzidwira. Choyamba, Mboni za Yehova zimasonyeza zikhulupiriro zawo zachipembedzo m’njira imene ena amanyasidwa nayo. Mwachitsanzo, zimalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu mwachangu, koma anthu kaŵirikaŵiri samvetsetsa, amaona ngati kuti changu chawo pa kulalikira ndiko “kutembenuza anthu mokakamiza.” (Yerekezerani ndi Machitidwe 4:19, 20.) Sizichita nawonso ndale kapena nkhondo za mitundu, ndipo nthaŵi zina zimenezi molakwa zatengedwa ngati kuti Mboni ndi nzika zosakhulupirika.​—Mika 4:3, 4.

4, 5. (a) Kodi ndi motani mmene Mboni za Yehova zakhala zikunenezedwa mabodza? (b) Kodi ndani amene kaŵirikaŵiri akhala akusonkhezera kwambiri kuzunza atumiki a Yehova?

4 Chachiŵiri, Mboni za Yehova zakhala zikunenezedwa mabodza​—mabodza a mkunkhuniza ndiponso kupotozedwa kwa zikhulupiriro zawo. Chifukwa cha zimenezo, m’maiko ena zaukiridwa popanda chifukwa. Ndiponso, chifukwa chakuti amafuna kupatsidwa mankhwala opanda msanganizo za magazi mogwirizana ndi chifuno chawo cha kumvera lamulo la Baibulo la ‘kusala mwazi,’ molakwa atchedwa kuti “akupha ana” ndiponso “gulu lodzipha.” (Machitidwe 15:29) Koma choonadi nchakuti Mboni za Yehova zimaona moyo kukhala wamtengo wapatali, ndipo zimafuna kupeza chithandizo chamankhwala chabwino kwambiri chimene chingapezeke kwa iwo ndiponso kwa ana awo. Zakuti ana ochuluka a Mboni za Yehova amafa chaka chilichonse chifukwa chokana kuikidwa magazi ndi zonama. Ndponso popeza kuti choonadi cha Baibulo sichingakhudze anthu a banja limodzi mofanana, Mboni zakhalanso zikunenezedwa kuti zimapasula mabanja. Komatu, amene azoloŵerana ndi Mboni za Yehova amadziŵa kuti zimalemekeza moyo wabanja kwambiri ndipo zimayesetsa kutsatira malamulo a Baibulo akuti mwamuna ndi mkazi azikondana ndi kulemekezana ndi kuti ana ayenera kumvera makolo awo mosasamala kanthu kuti iwo ndi okhulupirira kapena ayi.​—Aefeso 5:21–6:3.

5 Mu zochitika zambiri, otsutsa achipembedzo ndiwo amene akhala akusonkhezera kwambiri kuzunza atumiki a Yehova; iwo akhala okhoza kusonkhezera anthu andale ndi ofalitsa nkhani kuti apondereze ntchito ya Mboni. Kodi ifeyo, Mboni za Yehova, tiyenera kuchitanji pamene tatsutsidwa chonchi​—kaya ndi chifukwa cha zikhulupiriro ndi zochita zathu kapena chifukwa cha zinenezo zabodza?

“Kufatsa Kwanu Kuzindikirike ndi Anthu Onse”

6. Kodi nchifukwa chiyani kuli kofunika kukhala ndi kaonedwe koyenera ka anthu amene saali mumpingo wachikristu?

6 Choyambirira, tifunikira kukhala ndi kaonedwe koyenera​—kaonedwe ka Yehova​—ka anthu amene sitifanana nawo zikhulupiriro zachipembedzo. Apo phuluzi, tingachititse anthu ena kudana nafe kapena kutinyoza. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse.” (Afilipi 4:5) Motero Baibulo limatilimbikitsa kukhala ndi kaonedwe koyenera ka anthu amene saali mumpingo wachikristu.

7. Kodi ‘kusachitidwa maŵanga ndi dziko lapansi’ kumatanthauzanji?

7 Kumbali ina, Malemba momveka bwino amatichenjeza kuti ‘tisachitidwe maŵanga ndi dziko lapansi.’ (Yakobo 1:27; 4:4) Pano mawu akuti “dziko,” monganso m’malo ena ochuluka m’Baibulo, akunena za anthu onse kupatulapo Akristu oona. Tikukhala ndi anthu oterowo; timakumana nawo kuntchito, kusukulu, m’mudzi mwathu. (Yohane 17:11, 15; 1 Akorinto 5:9, 10) Komabe, sitichitidwa maŵanga ndi dzikoli mwa kupeŵa malingaliro, kalankhulidwe, ndi khalidwe limene likutsutsana ndi njira zolungama za Mulungu. Kulinso kofunika kwambiri kuzindikira kuopsa kwa kukhala ndi ubwenzi wathithithi ndi dzikoli, makamaka ndi aja amene amanyalanyaziratu miyezo ya Yehova.​—Miyambo 13:20.

8. Kodi nchifukwa chiyani uphungu wa kusachitidwa maŵanga ndi dziko lapansi sutipatsa chifukwa chilichonse chonyozera anthu ena?

8 Komabe, uphungu wa kusachitidwa maŵanga ndi dziko sutipatsa chifukwa chilichonse chonyozera anthu amene si Mboni za Yehova. (Miyambo 8:13) Kumbukirani chitsanzo cha atsogoleri achipembedzo achiyuda, amene afotokozedwa m’nkhani yoyambayo. Chipembedzo chimene anapanga sichinali ndi chiyanjo cha Yehova; ndiponso sichinabweretse unansi wabwino ndi anthu osakhala Ayuda. (Mateyu 21:43, 45) Pokhala odzilungamitsa ndi odzikuza, anthu otengeka maganizo amenewa anali kunyoza Akunja. Ife tilibe malingaliro obwerera oterowo, sitinyoza anthu amene saali Mboni. Mofanana ndi mtumwi Paulo, chikhumbo chathu nchakuti onse amene amamva uthenga wa choonadi cha Baibulo apeze chiyanjo cha Mulungu.​—Machitidwe 26:9; 1 Timoteo 2:3, 4.

9. Kodi malingaliro oyenera ndi a m’Malemba ayenera kukhudza motani mmene timalankhulira za anthu amene ali ndi zikhulupiriro zosiyana ndi zathu?

9 Malingaliro oyenera ndi a m’Malemba ayenera kukhudza mmene timalankhulira ponena za anthu amene saali Mboni. Paulo analangiza Tito kukumbutsa Akristu a pachilumba cha Krete kuti “asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andewu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.” (Tito 3:2) Onani kuti Akristu sanafunike kuchitira mwano “munthu aliyense”​—ngakhale amene sanali Akristu pa Krete, ena a iwo omwe anali odziŵika ndi mabodza, umbombo, ndi ulesi. (Tito 1:12) Choncho kukakhala kosagwirizana ndi Malemba ngati ife tigwiritsa ntchito mawu onyoza polankhula za anthu amene ali ndi zikhulupiriro zosiyana ndi zathu. Kudzikweza sikungakope ena kuti azilambira Yehova. Koma pamene tiona ena ndi kuchita nawo mogwirizana ndi malamulo abwino a Mawu a Yehova, ‘timakometsera chiphunzitso’ cha Mulungu.​—Tito 2:10.

Pamene Tingatonthole, Pamene Tingalankhule

10, 11. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anadziŵa pamene inali (a) “mphindi yakutonthola”? (b) “mphindi yakulankhula”?

10 Mlaliki 3:7 amati pali “mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula.” Pamenepa ndipo pali vuto: kudziŵa pamene tifunikira kunyalanyaza zonena za otsutsa ndi pamene tifunikira kulankhulapo kuti titchinjirize chikhulupiriro chathu. Tingaphunzire zochuluka m’chitsanzo cha munthu wina amene nthaŵi zonse sanali kuphonya pakuzindikira kwake​—Yesu. (1 Petro 2:21) Iye anadziŵa pamene inali “mphindi yakutonthola.” Mwachitsanzo, pamene ansembe aakulu ndi akulu anamneneza kwa Pilato, Yesu “sanayankha kanthu.” (Mateyu 27:11-14) Sanafune kunena chilichonse chimene chikanalepheretsa chifuno cha Mulungu pa iye. M’malo mwake, iye anasankha kuti zimene anachita zimchitire umboni. Anadziŵa kuti ngakhale choonadi sichikanasintha malingaliro ndi mitima yawo yodzikonda. Motero ananyalanyaza chinenezo chawo, mwadala nakhalabe du.​—Yesaya 53:7.

11 Komabe, Yesu anadziŵanso pamene inali “mphindi yakulankhula.” Nthaŵi zina anatsutsana zolimba ndiponso poyera ndi omunyoza, akumatsutsa zinenezo zawo zonama. Mwachitsanzo, pamene alembi ndi Afarisi anayesa kumnyazitsa pagulu mwa kumnena kuti anali kutulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Beelzibule, Yesu anasankha kusalekerera bodzalo. Ndi mfundo zosatsutsika ndi fanizo lomveka, iye anatsutsa bodzalo. (Marko 3:20-30; onaninso Mateyu 15:1-11; 22:17-21; Yohane 18:37) Komanso pamene Yesu, ataperekedwa ndi kumangidwa, anatengeredwa kubwalo la Sanhedrin, Mkulu wa Ansembe Kayafa mochenjera anamlamula kuti: “Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Kristu, Mwana wa Mulungu.” Iyinso inali “mphindi yakulankhula,” chifukwa akanati asalankhule zikanatanthauza kuti akukana kuti saali Kristu. Tero Yesu anayankha kuti: “Ndine amene.”​—Mateyu 26:63, 64; Marko 14:61, 62.

12. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene inapangitsa Paulo ndi Barnaba kulankhula molimba mtima ku Ikoniyo?

12 Lingaliraninso chitsanzo cha Paulo ndi Barnaba. Machitidwe 14:1, 2 amati: “Kunali pa Ikoniyo kuti analoŵa pamodzi m’sunagoge wa Ayuda, nalankhula kotero, kuti khamu lalikulu la Ayuda ndi Ahelene anakhulupira. Koma Ayuda osamvera anautsa mitima ya Ahelene kuti aipse abale athu.” The New English Bible limati: “Koma Ayuda osatembenuka anautsa mitima ya Akunja ndi kuipitsa maganizo awo pa Akristu.” Posakhutira ndi kuti iwo akana uthengawo, Ayuda otsutsa anayamba kufalitsa mphekesera zoipa, akumayesa kupangitsa anthu Akunja kuti akhale ndi maganizo oipa ponena za Akristu.a Iwo anadadi Chikristu! (Yerekezerani ndi Machitidwe 10:28.) Apa Paulo ndi Barnaba anaona kuti inali “mphindi yakulankhula,” apo ayi ophunzira atsopanowo ataya mtima ponyozedwa ndi anthu. “Chifukwa chake [Paulo ndi Barnaba] anakhala nthaŵi yaikulu nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye,” amene anasonyeza kuwavomereza kwake mwa kuwapatsa mphamvu yochita zizindikiro zozizwitsa. Zimenezi zinagaŵanitsa anthu, ena “anali ndi Ayuda, koma ena anali ndi atumwi.”​—Machitidwe 14:3, 4.

13. Pamene tanyozedwa, kodi ndi liti pamene kaŵirikaŵiri imakhala “mphindi yakutonthola”?

13 Pamenepa, kodi tiyenera kuchita motani titanyozedwa? Zimenezo zimadalira pa mikhalidwe. Mikhalidwe ina imafuna kuti tigwiritse ntchito pulinsipulo lakuti pali “mphindi yakutonthola.” Makamaka izi zimakhala choncho pamene anthu otsimikiza mtima kutitsutsa ayesa kutiloŵetsa m’mikangano yopanda pake. Tisaiwale kuti anthu ena safuna chabe kudziŵa choonadi. (2 Atesalonika 2:9-12) Nzosapindulitsa kuyesa kukambirana ndi anthu amene mitima yawo yazikidwa monyada pa kusakhulupirira. Komanso, ngati titati tizitsutsana ndi munthu aliyense amene watineneza, tingasiye ntchito imene ili yofunika ndi yopindulitsa kwambiri​—ija yothandiza anthu oona mtima amene akufunadi kuphunzira choonadi cha Baibulo. Chotero pamene tikumana ndi otsutsa amene ali ndi malingaliro ofalitsa bodza ponena za ife, malangizo ouziridwa amati: “Potolokani pa iwo.”​—Aroma 16:17, 18; Mateyu 7:6.

14. Kodi tingatchinjirize chikhulupiriro chathu kwa ena m’njira ziti?

14 Komatu izi sizitanthauza kuti sititchinjiriza chikhulupiriro chathu. Ndi iko komwe, palinso “mphindi yakulankhula.” Moyenera timakhudzidwa ndi anthu amaganizo abwino amene amva nkhani zotsutsana nafe. Timafuna kulongosola momveka bwino zikhulupiriro zathu zapamtima kwa ena; inde, timayamikira mwayi wakutero. Petro analemba kuti: “Mumpatulikitse Ambuye Kristu m’mitima yanu; okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.” (1 Petro 3:15) Pamene anthu ofunadi kudziŵa atifunsa kupereka umboni wa zikhulupiriro zathu zapamtima, pamene afunsa za mabodza amene akambidwa ndi otsutsa, ife tiyenera kutchinjiriza chikhulupiriro chathu ndi kuwapatsa mayankho omveka a m’Baibulo. Ndiponso, khalidwe lathu labwino linganene zambiri. Pamene anthu osakondera ationa kuti timayesetsa kukhala mogwirizana ndi miyezo yolungama ya Mulungu, angadziŵe mosavuta kuti nkhani zimene ena akutinenera ndi zabodza.​—1 Petro 2:12-15.

Bwanji za Nkhani Zabodza Zofalitsidwa?

15. Kodi nchitsanzo chiti chimene chikusonyeza kuti nkhani zonama zokhudza Mboni za Yehova zakhala zikufalitsidwa?

15 Nthaŵi zina, nkhani zonama zokhudza Mboni za Yehova zakhala zikufalitsidwa. Mwachitsanzo, pa August 1, 1997, nyuzipepala ya ku Russia inafalitsa nkhani yabodza imene, mwa zina, inati, Mboni zimafuna kuti mamembala ake ‘asiyane ndi akazi awo, amuna awo, ndi makolo awo ngati anthuwo samvetsetsa ndiponso sakhala ndi zikhulupiriro zonga ngati zawo.’ Aliyense amene wazoloŵeranadi ndi Mboni za Yehova akudziŵa kuti limeneli ndi bodza. Baibulo limati Akristu ayenera kukhala mwachikondi ndi mwaulemu ndi a pabanja lawo osakhulupirira, ndipo Mboni zimayesetsa kutsatira malangizo amenewo. (1 Akorinto 7:12-16; 1 Petro 3:1-4) Ngakhale zili choncho, nkhaniyo inasindikizidwa ndipo oŵerenga ambiri ananamizidwa. Kodi chikhulupiriro chathu tingachitchinjirize bwanji pamene tanenezedwa?

16, 17, ndi bokosi patsamba 16. (a) Kodi Nsanja ya Olonda inati chiyani nthaŵi ina ponena za kuyankha nkhani zonama zofalitsidwa? (b) Kodi Mboni za Yehova zingayankhe nkhani zonama zomwe zafalitsidwa pamene kuli mikhalidwe yotani?

16 Apanso pali “mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula.” Nsanja ya Olonda nthaŵi ina inati: “Kaya tiyenera kunyalanyaza nkhani zonama zofalitsidwa kapena kutchinjiriza choonadi mwa kutsatira njira yoyenera zimadalira pa mikhalidwe, pa wosonkhezera kunyozako, ndi pa cholinga chake.” M’zochitika zina kungakhale bwino kunyalanyaza nkhani zonama, kotero kuti nkhanizo sizingapitirire kufalitsidwa.

17 M’zochitika zina ingakhale “mphindi yakulankhula.” Mtolankhani wokhulupirika angakhale kuti ananamizidwa za Mboni za Yehova ndipo angasangalale kumva choonadi chonena za ife. (Onani bokosi lakuti “Kutsutsa Bodza.”) Ngati nkhani zonama zomwe zafalitsidwa zikupangitsa anthu kukhala ndi maganizo oipa amene akulepheretsa ntchito yathu yolalikira, oimira ofesi yanthambi ya Watch Tower Society angachitepo kanthu kuti atchinjirize choonadi mwa njira zoyenerera.b Mwachitsanzo, akulu oyeneretsedwa angafunsidwe kukalongosola choonadi, monga ngati papologalamu ya pa TV, pamene ngati angalephere kutero zingatanthauze kuti Mboni za Yehova zilibepo mawu. Pankhani zoterezi, Mboni iliyonse mwanzeru imagwirizana ndi malangizo operekedwa ndi Watch Tower Society ndi oimira Sosaiteyo.​—Ahebri 13:17.

Kutchinjiriza Uthenga Wabwino Mwalamulo

18. (a) Kodi nchifukwa chiyani sitifunika chilolezo cha maboma a anthu kuti tizilalikira? (b) Kodi timatsatira njira yotani pamene sitinapatsidwe chilolezo cha kulalikira?

18 Tikuvomerezedwa kuchokera kumwamba kuti tizilalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Yesu, amene anatituma kuchita ntchito imeneyi, wapatsidwa ‘mphamvu zonse Kumwamba ndi padziko lapansi.’ (Mateyu 28:18-20; Afilipi 2:9-11) Choncho, sitifunika chilolezo cha maboma a anthu kuti tizilalikira. Ngakhale ndi choncho, timazindikira kuti kukhala ndi ufulu wachipembedzo nkwabwino pa kufalitsa uthenga wa Ufumu. M’maiko amene tili ndi ufulu wa kulambira, tidzauteteza ndi malamulo. Kumene takanizidwa ufulu umenewo, monga mmene malamulo angatilolere, tidzayesetsa kuti tiupeze. Cholinga chathu si kusintha chikhalidwe cha anthu, koma ‘kuteteza ndi kutsimikiza [mwalamulo] Uthenga Wabwino.’c​—Afilipi 1:7, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono.

19. (a) Kodi nchiyani chimene chingatsatire pamene ‘tipatsa Mulungu zake za Mulungu’? (b) Kodi tili otsimikiza mtima kuchitanji?

19 Monga Mboni za Yehova, timazindikira kuti Yehova ndiye Mfumu ya Chilengedwe Chonse. Lamulo lake ndilo lalikulu kuposa onse. Chikumbumtima chathu chimatisonkhezera kumvera maboma a anthu, motero ‘timapatsa Kaisara zake za Kaisara.’ Koma sitidzalola chilichonse kutisokoneza kukwaniritsa udindo wathu wofunika koposa​—‘kupatsa Mulungu zake za Mulungu.’ (Mateyu 22:21) Tikuzindikira bwino lomwe kuti kuchita zimenezi kudzatipangitsa kukhala ‘odedwa’ ndi mitundu, koma zimenezi tikuziona monga mbali ya mtengo wa kukhala ophunzira. Zimene zakhala zikuchitikira Mboni za Yehova m’makhoti m’zaka za zana la 20 zino ndi umboni wakuti tili otsimikiza mtima kutchinjiriza chikhulupiriro chathu. Nchithandizo ndi chichirikizo cha Yehova, ‘sitidzaleka kuphunzitsa ndi kulalikira [“uthenga wabwino,” NW].’​—Machitidwe 5:42.

[Mawu a M’munsi]

a Matthew Henry’s Commentary on the Whole Bible limati Ayuda otsutsa “anaipanga kukhala ntchito yawo yopita mwadala kwa anthu [Akunja] amene anali atazoloŵerana nawo, ndi kukawauza zonse zimene apeka, kuti awapatse malingaliro osati kokha olakwika komanso oipa onena za Chikristu.”

b Nkhani yabodza itafalitsidwa m’nyuzipepala ya ku Russia (yotchulidwa m’ndime 15), Mboni za Yehova zinatula nkhaniyo ku Russian Federation Presidential Judicial Chamber for Media Disputes (Nyumba ya Pulezidenti ya Chiweruzo ya Chitaganya cha Russia Yoona za Mikangano pa Nkhani Zofalitsidwa). Zinapempha kuti nkhani zabodza zolembedwa m’nkhaniyo zifufuzidwe. Posachedwapa, khoti linapereka chigamulo chimene chinadzudzula nyuzipepalayo chifukwa chosindikiza nkhani yonyazitsayo.​—Onani Galamukani! yachingelezi ya November 22, 1998, masamba 26-7.

c Onani nkhani yakuti “Kuteteza Uthenga Wabwino Mwalamulo,” pamasamba 19-22.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi nchifukwa chiyani Mboni za Yehova ‘zimadedwa’?

◻ Kodi anthu amene tikusiyana nawo zikhulupiriro zachipembedzo tiyenera kuwaona motani?

◻ Pochita ndi otsutsa, kodi Yesu anatipatsa chitsanzo choyenera chotani?

◻ Pamene tanyozedwa, kodi tingagwiritse ntchito motani pulinsipulo lakuti pali “mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula”?

[Bokosi patsamba 16]

Kutsutsa Bodza

“Gulu lina lolalikira ku Yacuiba, Bolivia, linagwirizana ndi nyumba ya wailesi yakanema kuti lionetse filimu imene mwachionekere inali itatulutsidwa ndi anthu ampatuko. Polingalira za zotulukapo zoipa za pologalamu imeneyo, akulu anaganiza zokafikira nyumba ziŵiri za wailesi yakanema ndi kupempha kuti alipire kuti aonetse anthu mavidio akuti Jehovah’s Witnesses​—The Organization Behind the Name ndi The Bible​—A Book of Fact and Prophecy. Ataonerera mavidio a Sosaitewo, mwini wake wa nyumba ya wailesi ina anakalipa chifukwa cha mabodza osonyezedwa m’pologalamu ya ampatukoyo ndipo anati adzalengeza kwaulere pawailesi yake msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova umene unali kudzachitika. Anthu ochuluka kusiyana ndi nthaŵi zonse anafika pamsonkhanopo, ndipo anthu oona mtima ambiri anayamba kufunsa mafunso ogwira mtima pamene Mboni zinawachezera pa utumiki wawo.”​—1997 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 61-2.

[Chithunzi patsamba 17]

Nthaŵi zina Yesu anatsutsa poyera zinenezo zonama za omtsutsa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena