Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Zimene Tingachite Kuti Tizisangalalabe Tikakumana ndi Mayesero
    Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2021 | February
    • 2 Anthu ambiri amaona kuti kuzunzidwa si chifukwa chimene chingawapangitse kukhala osangalala. Komatu izi ndi zimene mawu a Mulungu amanena. Mwachitsanzo, mtumwi Yakobo analemba kuti m’malo moti tizida nkhawa tikakumana ndi mayesero, tizisangalala. (Yak. 1:2, 12) Komanso Yesu ananena kuti tizisangalala pamene tikuzunzidwa. (Werengani Mateyu 5:11.) Ndiye kodi tingatani kuti tizisangalala pamene tikukumana ndi mayesero? Tingaphunzire zambiri tikaganizira mfundo zina zimene zili m’kalata imene Yakobo analembera Akhristu oyambirira. Choyamba, tiyeni tione mavuto ena omwe Akhristuwa ankakumana nawo.

      KODI AKHRISTU OYAMBIRIRA ANKAKUMANA NDI MAYESERO OTANI?

      3. Kodi chinachitika n’chiyani Yakobo atangokhala wophunzira wa Yesu?

      3 Patangopita kanthawi kochepa kuchokera pamene Yakobo, mchimwene wake wa Yesu anakhala wophunzira, Akhristu ku Yerusalemu anayamba kuzunzidwa. (Mac. 1:14; 5:17, 18) Ndipo wophunzira Sitefano ataphedwa, Akhristu ambiri anathawa mumzindawo ndipo “anabalalikira m’zigawo za Yudeya ndi Samariya,” ndipo ena anakafika mpaka kumadera akutali ngati ku Kupuro ndi ku Antiokeya. (Mac. 7:58–8:1; 11:19) Kunena zoona, ophunzirawo anakumana ndi mavuto ambiri. Komabe kulikonse kumene iwo ankapita, ankalalikira uthenga wabwino mofunitsitsa ndipo anakhazikitsa mipingo m’madera ambiri omwe anali pansi pa ufumu wa Roma. (1 Pet. 1:1) Koma pambuyo pa zimenezi Akhristuwo anakumananso ndi mavuto ena ambiri.

      4. Kodi ndi mavuto enanso ati omwe Akhristu oyambirira anakumana nawo?

      4 Akhristu oyambirira anakumana ndi mayesero osiyanasiyana. Mwachitsanzo, cha m’ma 50 C.E., mfumu Kalaudiyo analamula kuti Ayuda achoke ku Roma. Choncho Ayuda omwe anakhala Akhristu anakakamizika kusiya nyumba zawo n’kusamukira kumadera ena. (Mac. 18:1-3) Cha m’ma 61 C.E., mtumwi Paulo analemba kuti Akhristu anzake ankatonzedwa poyera poikidwa m’ndende komanso kulandidwa katundu. (Aheb. 10:32-34) Mofanana ndi anthu onse, Akhristu nawonso ankapirira mavuto osiyanasiyana ngati umphawi komanso matenda.​—Aroma 15:26; Afil. 2:25-27.

  • Zimene Tingachite Kuti Tizisangalalabe Tikakumana ndi Mayesero
    Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2021 | February
    • Chithunzi: 1. Lawi la nyale likuyakabe ngakhale kuti kuli mphepo komanso kukugwa mvula. 2. M’bale wachikulire wanyamula Baibulo lotsegula m’manja mwake.

      Mofanana ndi lawi la nyale yagalasi lomwe limakhala lotetezeka, chimwemwe chimene Yehova amapereka chimayakabe mumtima mwa Mkhristu (Onani ndime 6)

      6. Mogwirizana ndi Luka 6:22, 23, n’chifukwa chiyani Mkhristu angakhalebe wosangalala akamakumana ndi mayesero?

      6 Anthu ambiri amaganiza kuti angakhale osangalala ngati ali ndi thanzi labwino, ndalama zambiri komanso banja losangalala. Komatu chimwemwe chimene Yakobo ankanena ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umatulutsa ndipo sichidalira mmene zinthu zilili pa moyo wa munthu. (Agal. 5:22) Mkhristu angakhale ndi chimwemwe kapena kuti wosangalala, akadziwa kuti akusangalatsa Yehova komanso kutsatira chitsanzo cha Yesu. (Werengani Luka 6:22, 23; Akol. 1:10, 11) Chimwemwe chimene chimakhala mumtima mwa Mkhristu chili ngati lawi la nyale yagalasi lomwe limakhala lotetezeka. Lawilo limayakabe ngakhale kukuomba mphepo kapena kukugwa mvula. Chimwemwe chimenechi chimakhalapobe ngakhale tidwale kapena tikhale ndi ndalama zochepa. Ndipo sichitha ngakhale pamene anthu ena kapena a m’banja lathu akutinyoza kapena kutitsutsa. M’malo mokhala okhumudwa, chimwemwe chathu chimawonjezereka nthawi iliyonse imene anthu ena akufuna kutilanda chimwemwecho. Mayesero amene timakumana nawo chifukwa cha chikhulupiriro chathu ndi amene amatsimikizira kuti ndifedi ophunzira a Khristu. (Mat. 10:22; 24:9; Yoh. 15:20) N’chifukwa chake Yakobo analemba kuti: “Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana.”​—Yak. 1:2.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena