-
Zipembedzo Zonyenga Zimaphunzitsa Zabodza Zokhudza MulunguMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
Zipembedzo zonyenga zakhala ‘zikusinthanitsa choonadi cha Mulungu ndi bodza.’ (Aroma 1:25) Mwachitsanzo, zipembedzo zambiri sizimaphunzitsa anthu dzina la Mulungu. Komatu Baibulo limaphunzitsa kuti tiyenera kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu. (Aroma 10:13, 14) Atsogoleri ena azipembedzo amanena kuti chinachake choipa chikachitika, chimakhala kuti ndi cholinga cha Mulungu. Koma limeneli ndi bodza. Mulungu si amene amachititsa zinthu zoipa. (Werengani Yakobo 1:13.) N’zomvetsa chisoni kuti mabodza amene zipembedzozi zimaphunzitsa amachititsa kuti anthu asamakonde Mulungu.
-
-
N’chifukwa Chiyani Anthu Amavutika?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
4. Ndi ndani amene amachititsa kuti tizivutika?
Anthu ambiri amakhulupilira kuti Mulungu ndi amene akulamulira dzikoli. Kodi zimenezi ndi zoona? Onerani VIDIYO.
Werengani Yakobo 1:13 ndi 1 Yohane 5:19, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Mulungu ndi amene amachititsa kuti tizivutika?
-