Lingaliro la Baibulo
Kodi Baibulo Limaletsa Ufulu wa Kulingalira?
MALAŴI ali lapilapi pamene chimoto chikupsereza mabuku amtengo wapatali amene aponyedwapo ndi akuluakulu Achijeremani. Kodi ndicho chochitika cha ku Nazi Germany? Inde, koma chingakhalenso chochitika cha m’chaka cha 1199, pamene akibishopu wa Roma Katolika analamula kuti Mabaibulo onse achinenero cha Chijeremani atenthedwe.
Kwenikweni, kutenthedwa kwa mabuku—chizindikiro cha padziko lonse cha kutsenderezedwa kwa ufulu wa kulingalira ndi kulankhula—kwachitika m’maiko ambiri ndiponso m’zaka mazana zambiri. Kaŵirikaŵiri, kwasonkhezeredwa ndi atsogoleri achipembedzo amene anawopa chiyambukiro chimene ufulu wa kulingalira ukakhala nacho pa anthu wamba.
Mposadabwitsa kuti lerolino ambiri amalingalira kuti Baibulo lili ndi malamulo amphamvu oletsa kufufuza kwanzeru kwapoyera. Koma kodi ilo lili nawodi? Kodi Baibulo limalimbikitsa ziletso za ufulu wa kulingalira?
‘Kondani Mulungu ndi Nzeru Zanu Zonse’
Baibulo silimaletsa kugwiritsiridwa ntchito kwa maganizo. Kwenikweni, Yesu analimbikitsa aliyense wa ife ‘kukonda Mulungu ndi nzeru zathu zonse.’ (Marko 12:30) Utumiki wake umasonyeza kuti iye anali ndi chikondwerero chachikulu m’zochitika zapanthaŵiyo (Luka 13:1-5), zamoyo (Mateyu 6:26, 28; Marko 7:18, 19), zamalimidwe (Mateyu 13:31, 32), ndi chikhalidwe cha munthu (Mateyu 5:28; 6:22-24). Mafanizo ake amasonyeza kuti anazindikira bwino kwambiri malamulo a mkhalidwe a m’Mawu a Mulungu ndi mkhalidwe ndi maganizo a omvetsera ake ndi kuti analingalira mosamala ponena za mmene angagwirizanitsire ziŵirizo pamodzi.
Paulo anadandaulira Akristu onse kupereka utumiki wawo kwa Mulungu ndi “mphamvu [yawo] ya kuganiza.” (Aroma 12:1, NW) Iye analimbikitsa Atesalonika kusasokeretsedwa ndi ‘kusagwedezeka mtima ndi kutaya maganizo awo.’ (2 Atesalonika 2:2) Iye anadziŵa pang’ono ndakatulo za Agiriki ndi za Akrete (Machitidwe 17:28; Tito 1:12) ndi zida zankhondo ndi njira zake zogwiritsira ntchito (Aefeso 6:14-17; 2 Akorinto 2:14-16). Ndipo anadziŵa miyambo ya anthu akumaloko.—Machitidwe 17:22, 23.
Ngakhale kuti Yesu ndi Paulo anali ndi ufulu wambiri wa kulingalira wotero, sanadzione kukhala ndi ulamuliro wonse pa chabwino ndi choipa. Mmalo mwa kukana Baibulo chifukwa cha kukonda kuganiza kwake, Yesu anagwira mawu m’Malemba mobwerezabwereza. Yankho lake lofulumira ndi lodzudzula kwambirilo pamene Petro anamsonkhezera kutenga njira ina yosiyana ndi ya imfa yansembe imene inali chifuniro cha Mulungu kwa iye limasonyeza kuti iye sanalingalirepo konse motero. (Mateyu 16:22, 23) Mofananamo, Paulo anauza Akorinto kuti: “Pamene ndinadza kwa inu, sindinadze ndi chisonyezero chilichonse cha kudziŵa kulankhula kapena cha nthanthi, koma kudzangokuuzani zimene Mulungu watsimikiza kuchita.” (1 Akorinto 2:1, The Jerusalem Bible) Mofanana ndi Yesu, kuganiza kwake kunazikidwa mwamphamvu pa Malemba.—Machitidwe 17:2.
Baibulo limalimbikitsa munthu kugwiritsira ntchito kwambiri maganizo ake komatu osati mosadziletsa. Komabe, thayo lalikulu la kusunga kuganiza kwathu kuli kogwirizana ndi kwa Yehova laikidwa pa Mkristu aliyense payekha, osati pa mpingo. Chotero, pamene Aefeso ambiri anakana poyera machitachita awo a kulambira mizimu ndi kukhala Akristu, Paulo sanawatenthere mabuku awo, koma “ambiri a iwo amene anachita matsenga anasonkhanitsa mabuku awo nawatentha m’chimoto poyera.” (Machitidwe 19:19, JB) Kodi nchifukwa ninji Akristu ameneŵa anakuona kukhala koyenera kutentha mabuku awo?
Njira Yoyamba Yotetezera
Talingalirani za chitsanzo ichi. Luso lankhondo la kudzitetezera lachipambano kaŵirikaŵiri limaloŵetsamo njira zingapo za kudzitetezera. Palibe mkulu wankhondo amene angaganize kuti imodzi ya njira zimenezi n’njosafunika ndi kuileka popanda kuyesayesa. M’kulimbana ndi uchimo kwa Mkristu, mulinso njira zingapo za kudzitetezera.
Yakobo 1:14, 15 amafotokoza kuti “munthu ali yense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo.” Sitepe loyamba lomkera kuuchimo ndilo kukulitsidwa kwa chilakolako choipa m’maganizo. Motero, njira yoyamba ya kudzitetezera ndiyo ya kuleka kukulitsa chilakolako—kulamulira maganizo a munthuwe.
Chili chifukwa cha kugwirizana kumeneku kumene kuli pakati pa malingaliro ndi zochita kumene timachenjezedwa nako ndi Baibulo kuti: “Lingalirani zakumwamba osati za padziko ayi.” (Akolose 3:2) Pamene Akristu akana kuika malingaliro pa makhalidwe oipa, kulambira mizimu, kapena pa mpatuko, amapanga chosankha chimenechi, osati chifukwa chakuti amawopa kuti malingaliro ameneŵa angakhale oposa choonadi cha Baibulo, koma chifukwa chakuti amafuna kupeŵa kanthu kalikonse kamene kangawakokere ku njira yauchimo.
‘Zonse Zili Zovundukuka’
Chifukwa china chofunika chimene tiyenera kulamulilira kuganiza kwathu ndicho chikondi chathu pa Yehova ndi kulemekeza kukhoza kwake kudziŵa malingaliro athu. Tayerekezerani kuti inu munali ndi bwenzi limene mumakonda kwambiri kapena wachibale amene amadana ndi fumbi kotheratu. Kodi mungaleke kuitanira bwenzi lanulo kwanu, chifukwa cha kusafuna kupukuta bwinobwino fumbilo kumene kungafunike m’nyumba mwanu? Kodi chikondi sichikakusonkhezerani kuchita zoyesayesa zina zofunika kuti mkatimo mukhale moyera? Kuyambukiridwa kwa Yehova ndi malingaliro athu amkatikati kwasonyezedwa pa Salmo 44:21 kuti: “Adziŵa zinsinsi za mtima.” Paulo anati tili ndi mangawa a malingaliro amenewo: “Palibe cholengedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.”—Ahebri 4:13; Salmo 10:4; Miyambo 6:16, 18.
Yobu anasonyeza thayo la munthu kwa Mulungu la malingaliro ake. “Yobu . . . nafukiza nsembe zopsereza, . . . ; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m’mtima mwawo.” (Yobu 1:5) Kulingalira njira yolakwa modzifunira mwa iko kokha kungaonedwe ndi Yehova kukhala tchimo.—Yerekezerani ndi Eksodo 20:17.
Ufulu Woona wa Kulingalira
Baibulo limalimbikitsa Mkristu aliyense kuika monga chonulirapo “kugonjetsa ganizo lonse ku kumvera kwa Kristu.” (2 Akorinto 10:5) Zimenezi zimachitidwa, osati kupyolera mwa ziletso zoikidwa ndi atsogoleri achipembedzo, koma kupyolera mwa kusonyeza kudziletsa kwa munthu aliyense ndi kupyolera m’chikondi chake ndi kuzindikira kwake Yehova ndi malamulo Ake amkhalidwe. Pamodzi ndi kufikira chonulirapo chimenechi pamadza ufulu woona wa kulingalira, wolamuliridwa kokha ndi miyezo yaumulungu ndi kukulitsidwa ndi chisangalalo cha kudziŵa kuti, ngakhale m’malingaliro mwathu, tikukondweretsa Yehova.
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
Kuchokera m’buku lakuti Bildersaal deutscher Geschichte