Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Pitirizanibe Kukhala M’gulu la Yehova
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
    • 8 Yakobo anafotokoza m’kalata yake kufunika kophunzira kupirira, kuti: “Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana, monga mukudziwira kuti chikhulupiriro chanu chikayesedwa, chimabala kupirira. Koma mulole kuti kupirira kumalize kugwira ntchito yake, kuti mukhale okwanira ndi opanda chilema m’mbali zonse, osaperewera kalikonse.” (Yak. 1:2-4) Yakobo ananena kuti Akhristu ayenera kumasangalala akakumana ndi mayesero chifukwa mayeserowo amawaphunzitsa kupirira. Kodi ndi mmene inuyo mumaonera? Kenako Yakobo anasonyeza kuti kupirira kumagwira ntchito yake, yotithandiza kukhala ndi makhalidwe achikhristu ndiponso kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Timakhala anthu opirira kwambiri tikamagonjetsa mayesero amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku. Ndiyeno kupirirako kumatithandiza kukhala ndi makhalidwe enanso abwino amene timafunikira kukhala nawo.

  • Pitirizanibe Kukhala M’gulu la Yehova
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
    • 10 Monga Akhristu, kuti tipitirize kupirira m’masiku ovuta ano, tiyenera kumaona moyenera mavuto amene timakumana nawo. Kumbukirani kuti Yakobo analemba kuti: “Sangalalani.” Komatu kuchita zimenezi si kophweka makamaka ngati mavutowo akuchititsa kuti munthu azimva ululu kapena kuvutika maganizo. Koma kumbukirani kuti chofunika ndi moyo wam’tsogolo. Zimene zinachitikira atumwi zingatithandize kuona mmene tingakhalire osangalala tikakumana ndi mavuto. Nkhaniyi imapezeka m’buku la Machitidwe ndipo imati: “Anaitanitsa atumwiwo. Ndiyeno [anawakwapula] ndi kuwalamula kuti asiye kulankhula m’dzina la Yesu, kenako anawamasula. Choncho atumwiwo anachoka pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda, ali osangalala chifukwa chakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu.” (Mac. 5:40, 41) Atumwiwo anadziwa kuti kuvutika kwawoko unali umboni woti anamvera lamulo la Yesu ndiponso anasangalatsa Yehova. Kenako patadutsa zaka, pa nthawi imene Petulo ankalemba kalata yake yoyamba, anafotokoza kufunika kovutika chifukwa cha chilungamo.​—1 Pet. 4:12-16.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena