Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi a Mboni za Yehova Ndi Akhristu Enieni?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 3. Kodi a Mboni za Yehova amatsanzira bwanji Yesu pa nkhani yosonyeza chikondi?

      Yesu ankakonda kwambiri ophunzira ake moti ankawaona ngati abale ake enieni. (Werengani Maliko 3:35.) Choncho a Mboni za Yehova nawonso ndi banja limodzi logwirizana la padziko lonse. N’chifukwa chake timati ndife abale ndi alongo. (Filimoni 1, 2) Timamveranso lamulo lakuti: “Muzikonda gulu lonse la abale.” (1 Petulo 2:17) A Mboni za Yehova amasonyeza kuti amakonda abale awo m’njira zambiri. Mwachitsanzo, Akhristu anzawo padziko lonse lapansi akakumana ndi mavuto amawathandiza.

  • Ubatizo Ungakuthandizeni Kuti Mukhale Ndi Tsogolo Labwino
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 6. Tikabatizidwa timakhala m’banja la Yehova

      Tikabatizidwa, timakhala m’banja logwirizana lapadziko lonse. Ngakhale kuti timachokera madera osiyanasiyana komanso tili ndi zikhalidwe zosiyanasiyana, timakhulupirira zinthu zofanana ndiponso timayendera mfundo zamakhalidwe abwino zofanana pa moyo wathu. Werengani Salimo 25:14 ndi 1 Petulo 2:17, kenako mukambirane funso ili:

      • Mogwirizana ndi mavesiwa, kodi ubatizo umathandiza bwanji munthu?

      Zithunzi: Mlongo wobatizidwa akuganizira madalitso amene akusangalala nawo chifukwa chokhala pa ubwenzi wabwino Akhristu anzake mumpingo. Akufotokozera mlongo wina nkhawa zake. 2. Akuthandiza mlongo wachikulire kuyenda. 3. Waitanira chakudya anzake amisinkhu yosiyanasiyana. 4. Akulalikira bambo wina limodzi ndi mlongo wina. 5. Ali kumsonkhano ndi anzake ndipo akudzijambula.
  • Pitirizani Kuchita Zinthu Mogwirizana Mumpingo
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • Tikakhala ndi Akhristu anzathu timamva ngati Mfumu Davide yemwe anati: “Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana!” (Salimo 133:1) Komatu mgwirizanowu sumangobwera wokha. Tonsefe tiyenera kumachita khama kuti tithandizire kuti mgwirizano umenewu upitirire.

      1. Kodi anthu a Yehova amachita zinthu ziti zomwe zimakuchititsani chidwi?

      Mukapita kudziko lina n’kupezeka pamisonkhano abale ndi alongo amakulandirani ndi manja awiri, amakusonyezani chikondi komanso mumakhala omasuka ngakhale kuti simumva chinenero chawo. Zili choncho chifukwa chakuti zinthu zomwe timagwiritsa ntchito pophunzira Baibulo n’zofanana kulikonse. Kuwonjezera pamenepa, timayesetsa kusonyezana chikondi. Kaya timakhala kuti, tonsefe ‘timaitanira pa dzina la Yehova n’kumamutumikira mogwirizana.’​—Zefaniya 3:9.

      2. Kodi mungathandize bwanji kuti mumpingo mupitirize kukhala mgwirizano?

      Baibulo limati: “Muzikondana kwambiri kuchokera mumtima.” (1 Petulo 1:22) Kodi inuyo mungagwiritse ntchito bwanji malangizo amenewa? M’malo momangoona zimene anthu ena amalakwitsa, muziganizira kwambiri makhalidwe awo abwino. Musamangocheza ndi anthu okhawo amene amakonda zimene inuyo mumakonda. M’malomwake muziyesetsa kudziwana ndi abale ndi alongo osiyanasiyana. Ngati tili ndi kamtima ka tsankho tiyenera kuyesetsa kukathetsa.​—Werengani 1 Petulo 2:17.a

      3. Kodi muyenera kuchita chiyani mukasemphana maganizo ndi Mkhristu mnzanu?

      Ngakhale kuti ndife anthu ogwirizana, timasemphana maganizo kapena kukhumudwitsana chifukwa chakuti ndife anthu ochimwa. Choncho, Mawu a Mulungu amatiuza kuti: “Pitirizani . . . kukhululukirana . . . Mofanana ndi Yehova amene anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso muzichita chimodzimodzi.” (Werengani Akolose 3:13.) Anthufe timakhumudwitsa Yehova kambirimbiri komabe iye amatikhululukira. Choncho iye amafuna kuti nafenso tizikhululukira abale ndi alongo athu. Mukazindikira kuti mwakhumudwitsa winawake, inuyo muziyesetsa kukambirana ndi mnzanuyo n’cholinga choti muthetse kusamvana.​—Werengani Mateyu 5:23, 24b

      FUFUZANI MOZAMA

      Ganizirani zimene mungachite pothandiza kuti mumpingo mupitirize kukhala mgwirizano ndi mtendere.

      Zithunzi: M’bale akuyesetsa kukhazikitsa mtendere. 1. M’bale wina akumulankhula mwaukali. 2. Akuganizira zimene m’bale winayo wamulankhula. 3. Akuganizira malangizo a m’Baibulo okhudza kuthetsa kusamvana. 4. Akumwa khofi limodzi ndi m’baleyo kwinaku akukambirana n’cholinga choti akhazikitse mtendere.

      Kodi mungachite zotani kuti mukhazikitse mtendere?

      4. Yesetsani kuthetsa mtima watsankho

      Tonsefe timafuna kumakonda abale ndi alongo athu onse. Komabe tingavutike kugwirizana ndi munthu amene akuoneka wosiyana ndi ife. Ndiye n’chiyani chimene chingatithandize? Werengani Machitidwe 10:34, 35, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Yehova amalandira anthu amitundu yonse kuti akhale Mboni zake. Ndiye kodi mungatengere bwanji chitsanzo cha Yehova pa nkhani ya mmene mumaonera anthu amene ndi osiyana ndi inu?

      • Kodi inuyo mukufuna kupewa zinthu ziti zimene anthu ambiri m’dera lanu amachita posonyeza tsankho?

      Werengani 2 Akorinto 6:11-13, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi mukuganiza kuti muyenera kuchita chiyani kuti muzikonda kwambiri abale ndi alongo amene mumasiyana nawo zinthu zina?

      5. Muzikhululuka ndi mtima wonse komanso muziyesetsa kukhazikitsa mtendere

      Yehova amatikhululukira ndi mtima wonse ngakhale kuti iyeyo satilakwira. Werengani Salimo 86:​5, kenako mukambirane mafunso awa:

      • Kodi vesili likutiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova pa nkhani yokhululuka?

      • Kodi mumathokoza Yehova chifukwa chakuti amatikhululukira? N’chifukwa chiyani mukutero?

      • Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatilepheretse kukhala mwamtendere ndi anzathu?

      Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhani yokhululuka n’kumachitabe zinthu mogwirizana ndi abale ndi alongo athu? Werengani Miyambo 19:​11, kenako mukambirane funso ili:

      • Munthu wina akakukhumudwitsani kapena kukuchitirani zinthu zoipa, kodi mungatani kuti mukhalebe naye pamtendere?

      Nthawi zina ifenso timakhumudwitsa ena. Ndiye tizitani zimenezi zikachitika? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.

      VIDIYO: Kukhazikitsa Mtendere Kumabweretsa Madalitso (6:01)

      • Kodi mlongo wa muvidiyoyi anachita zotani kuti akhazikitse mtendere?

      6. Muziona zabwino mwa abale ndi alongo anu

      Tikayamba kudziwana bwino ndi abale ndi alongo athu m’pamene timayamba kuona makhalidwe awo abwino komanso zimene amalakwitsa. Ndiye tingatani kuti tiziganizira kwambiri makhalidwe awo abwino? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.

      VIDIYO: Muziona Zinthu Moyenera! (5:10)

      • Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muziona zabwino mwa abale ndi alongo anu?

      Yehova amaona kwambiri makhalidwe athu abwino. Werengani 2 Mbiri 16:9a, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi mukumva bwanji podziwa kuti Yehova amaona kwambiri makhalidwe abwino amene muli nawo?

      Mphete yodula.

      Ngakhale mphete yodula itakandika, imakhalabe yamtengo wapatali. N’chimodzimodzinso ndi abale ndi alongo athu, ngakhale kuti si angwiro, Yehova amawaonabe kuti ndi amtengo wapatali

      ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Sindimukhululukira pokhapokha andipepese kaye.”

      • N’chifukwa chiyani tiyenera kumakhululukira ena ndi mtima wonse?

      ZOMWE TAPHUNZIRA

      Mungathandize kuti mpingo upitirizebe kuchita zinthu mogwirizana mukamakhululuka komanso mukamayesetsa kukonda abale ndi alongo anu onse.

      Kubwereza

      • Kodi mungathetse bwanji mtima watsankho?

      • Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mwasemphana maganizo ndi Mkhristu mnzanu?

      • Kodi inuyo mukufuna kutsanzira Yehova pa nkhani yokhululukira ena? N’chifukwa chiyani mukutero?

      Zoti Muchite

      ONANI ZINANSO

      Onani mmene fanizo lina limene Yesu ananena lingatithandizire kuti tizipewa kuweruza anthu ena.

      Chotsa Mtanda wa Denga M’diso Lako (6:56)

      Kodi tiyenera kupepesa ngakhale tikuona kuti sitinalakwitse chilichonse?

      “Kupepesa​—Njira Yothandiza Yopezera Mtendere” (Nsanja ya Olonda, November 1, 2002)

      Onani zimene zathandiza ena kuti azichita zinthu mopanda tsankho.

      Musamaweruze Ena Potengera M’mene Akuonekera (5:06)

      Onani mmene mungathetsere kusamvana ngati mwasemphana maganizo ndi munthu wina kuti musasokoneze mtendere mumpingo.

      “Kodi Mumathetsa Nkhani Mwachikondi Mukasemphana Maganizo?” (Nsanja ya Olonda, May 2016)

      a Mawu Akumapeto 6 akufotokoza mmene chikondi chimathandizira Akhristu kupewa kufalitsa matenda opatsirana.

      b Mawu Akumapeto 7 akufotokoza zimene mungachite kuti muthetse kusamvana pa nkhani zokhudza bizinesi ndiponso malamulo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena