Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 2/1 tsamba 14-19
  • “Amene Mungakhale Simunamuona Mumkonda”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Amene Mungakhale Simunamuona Mumkonda”
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zinthu Zimene Iwo Anamva
  • Mzimu Umene Iye Anasonyeza
  • Kudalira Kwake Mulungu Modzichepetsa
  • Kusonyeza Chikondi Chathu pa Iye
  • Kodi Mudzalabadira ku Chikondi cha Yesu?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • “Mudziwe Chikondi cha Khristu”
    Yandikirani Yehova
  • Taphunzitsidwa Kuchitira Umboni Mokwanira
    Nsanja ya Olonda—2005
  • “Yesu . . . Anawakonda Mpaka pa Mapeto a Moyo Wake”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 2/1 tsamba 14-19

“Amene Mungakhale Simunamuona Mumkonda”

“Amene mungakhale simunamuona mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka.”​—1 PETRO 1:8.

1. Ngakhale kuti kulibe aliyense padziko lapansi lerolino amene anaona Yesu, kodi anthu ena opembedza amayesa motani kuonetsa kudzipereka kwawo?

PALIBE munthu aliyense wamoyo padziko lapansi lerolino amene anaonapo Yesu Kristu. Komabe, anthu mamiliyoni ambiri amati amamkonda iye. Chaka chilichonse pa January 9, ku Manila, Philippines, fano lalikulu monga munthu la Yesu Kristu lonyamula mtanda amalikoka m’makwalala pachochitika chimene chatchedwa chionetsero chachikulu koposa ndi chochititsa chidwi cha chipembedzo chotchuka m’dzikolo. Anthu m’khamulo amakankhana ndi kubwanyulana; amakwerananso poyesetsa motengeka maganizo kukhudza fanolo. Ambiri amene amakhalapo pazimenezi kwenikweni amakopeka ndi ligubo lachikondwerero limenelo. Komabe, ena a iwo mosakayikira ali anthu amene amaganizadi kuti ali oyandikana kwambiri ndi Yesu. Iwo amavala korona kapena kupita kutchalitchi nthaŵi zonse monga umboni wa zimenezo. Komabe, kodi kupembedza mafano koteroko kungaonedwe monga kulambira koona?

2, 3. (a) Kodi ndani pakati pa otsatira a Yesu amene anamuonadi iye ndi kumumva akulankhula? (b) Ndaninso m’zaka za zana loyamba amene anakonda Yesu ndi kumkhulupirira, ngakhale kuti sanamuone maso ndi maso?

2 M’zaka za zana loyamba, panali zikwi zambiri m’zigawo za Roma za Yudeya, Samariya, Perea, ndi Galileya amene anaonadi Yesu Kristu maso ndi maso ndi kumumva akulankhula. Iwo anamvetsera pamene iye anali kufotokoza choonadi chokhudza mtima cha Ufumu wa Mulungu. Anali mboni zoona ndi maso za zozizwitsa zimene iye anachita. Ena a iwo anakhala ophunzira ake odzipereka, otsimikiza kuti iyeyo anali “Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.” (Mateyu 16:16) Komabe, aja amene mtumwi Petro analemberako kalata yake yoyamba youziridwa sanali pakati pa ameneŵa ayi.

3 Amene Petro analembera anali m’zigawo za Roma za Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bituniya​—zonsezo zinali m’dera la Turkey wamakono. Petro anawalembera kuti: “Amene mungakhale simunamuona mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero.” (1 Petro 1:1, 8) Kodi anafika motani pakumdziŵa Yesu Kristu moti nkumkonda ndi kumkhulupirira?

4, 5. Kodi anthu aja omwe sanamuonepo Yesu anadziŵa motani zochuluka ponena za iye moti nkumkonda ndi kumkhulupirira?

4 Zikuoneka kuti, ena a iwo analipo m’Yerusalemu pamene mtumwi Petro anapereka umboni kwa khamu lopezeka paphwando la Pentekoste mu 33 C.E. Phwandolo litatha, ophunzira ambiri anatsalira m’Yerusalemu kuti alandire malangizo ena kwa atumwi. (Machitidwe 2:9, 41, 42; yerekezerani ndi 1 Petro 1:1.) Pamaulendo obwerezabwereza aumishonale, mtumwi Paulo anachita utumiki wachangu pakatinso pa anthu amene anali kukhala m’dera limene Petro pambuyo pake anatumizako kalata yake yoyamba ya m’Baibulo yotchedwa dzina lake.​—Machitidwe 18:23; 19:10; Agalatiya 1:1, 2.

5 Kodi nchifukwa ninji anthuwo, amene sanamuonepo Yesu, anakopeka naye kwambiri? Nchifukwa ninji masiku ano mamiliyoni ena ambiri kuzungulira dziko amamkonda kwambiri?

Zinthu Zimene Iwo Anamva

6. (a) Mukanamumva Petro akuchitira umboni za Yesu pa Pentekoste wa 33 C.E., kodi mukanaphunziranji? (b) Kodi zimenezi zinawakhudza motani anthu ngati 3,000 omwe analipo?

6 Mukanakhalapo m’Yerusalemu pamene Petro analankhula kwa khamulo paphwando mu 33 C.E., kodi mukanaphunziranji ponena za Yesu? Mosakayikira konse zozizwitsa zimene anachita zinaonetsa kuti anatumidwa ndi Mulungu. Mukanaphunziranso kuti, ngakhale kuti anthu ochimwa anamupha Yesu, sanalinso m’manda koma anaukitsidwa nakwezedwa kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu. Ndi kuti Yesu analidi Kristu, Mesiya yemwe aneneri analemba za iye. Ndi kutinso mzimu woyera unatsanulidwa pa otsatira ake kudzera mwa Yesu Kristu kotero kuti iwo anakhoza kuchitira umboni mofulumira kwa anthu a m’mitundu yambiri wa zazikulu zimene Mulungu anali kuchita mwa Mwana wake. Ambiri omwe anamva Petro akulankhula panthaŵiyo analaswa mtima, ndipo anthu ngati 3,000 anabatizidwa monga ophunzira achikristu. (Machitidwe 2:14-42) Mukanakhalapo, kodi mukanachitapo kanthu motsimikiza choncho?

7. (a) Mukanakhalako ku Antiokeya pamene mtumwi Paulo analalikira konko, kodi mwina mukanaphunziranji? (b) Kodi nchifukwa ninji ena m’khamulo anakhulupirira nauzako ena uthenga wabwino?

7 Mukanakhalapo pamene mtumwi Paulo anali kuphunzitsa ku Antiokeya m’chigawo cha Galatiya cha Roma, kodi mukanaphunziranso chiyani ponena za Yesu? Mukanamumva Paulo akufotokoza kuti aneneri analosera kuti olamulira m’Yerusalemu ndiwo adzaweruzira Yesu ku imfa. Mukanamvanso za umboni wa oonako ndi maso wa kuuka kwa Yesu. Mukanachitadi chidwi ndi kufotokoza kwa Paulo kuti mwa kuukitsa Yesu kwa akufa, Yehova anatsimikiza kuti ameneyu analidi Mwana wa Mulungu. Ndipo kodi mtima wanu sukanakhudzika pophunzira kuti kukhululukira machimo, komwe kunatheka mwa chikhulupiriro mwa Yesu, kudzatsogolera ku moyo wosatha? (Machitidwe 13:16-41, 46, 47; Aroma 1:4) Atazindikira kufunika kwake kwa zimene anali kumva, ena ku Antiokeya anakhala ophunzira, nauzako ena mwachangu za uthenga wabwino, ngakhale kuti kuteroko kunatanthauza kuti adzakumana ndi chizunzo chachikulu.​—Machitidwe 13:42, 43, 48-52; 14:1-7, 21-23.

8. Mukanakhalapo pamsonkhano wa mpingo wa ku Efeso pamene analandira kalata imene Paulo anawalembera, kodi mukanaphunziranji?

8 Nanga bwanji ngati munali mumpingo wachikristu ku Efeso, m’chigawo cha Asiya cha ku Roma, pamene analandira kalata youziridwa ya Paulo kwa atumwi konko? Kodi iyo ikanakuphunzitsani chiyani ponena za mbali ya Yesu m’chifuno cha Mulungu? M’kalata imeneyo Paulo anafotokoza kuti mwa Kristu zinthu zonse zakumwamba ndi za padziko lapansi Mulungu adzazigwirizanitsanso, ndi kuti mphatso ya Mulungu mwa Kristu inafika kwa anthu a m’mitundu yonse, kutinso anthu, mmodzi ndi mmodzi, amene anali akufa pamaso pa Mulungu chifukwa cha zolakwa zawo anali kukhala amoyo mwa kukhulupirira Kristu, ndi kutinso chifukwa cha makonzedwe ameneŵa, kunalinso kotheka kuti anthu akhale ana okondedwa a Mulungu.​—Aefeso 1:1, 5-10; 2:4, 5, 11-13.

9. (a) Kodi nchiyani chingakuthandizeni kuzindikira ngati inu nokha mukumvetsa tanthauzo la zimene Paulo analembera Aefeso? (b) Kodi abale okhala m’zigawo za Roma amene Petro anatchula anakhudzidwa motani ndi zimene anali kuphunzira ponena za Yesu?

9 Kodi kuyamikira kwanu zonsezi kukanakulitsa chikondi chanu pa Mwana wa Mulungu? Kodi chikondicho chikanatsogoza moyo wanu wa tsiku ndi tsiku, monga momwe mtumwi Paulo analimbikitsira m’machaputala 4 mpaka 6 a Aefeso? Kodi chiyamikiro chimenecho chikanakusonkhezerani kupenda bwinobwino zinthu zanu zoyamba m’moyo wanu? Chifukwa cha kukonda kwanu Mulungu ndi kuyamikira Mwana wake, kodi mukanapanga masinthidwe ofunika kotero kuti kuchita chifuniro cha Mulungu kukanakhaladi chinthu chofunika koposa m’moyo wanu? (Aefeso 5:15-17) Ponena za mmene Akristu ku Asiya, Galatiya, ndi zigawo zina za Roma anakhudzidwira ndi zimene anali kuphunzira, mtumwi Petro anawalembera kuti: “Amene mungakhale simunamuona [Yesu Kristu] mumkonda; . . . pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero.”​—1 Petro 1:8.

10. (a) Kodi nchiyani mosakayikira chimene chinasonkhezera Akristu oyambirira kumkonda Yesu? (b) Ifenso tingapindule motani?

10 Panalinso china chimene mosakayikira chinasonkhezera Akristu oyambirira aja amene Petro analembera kukonda Mwana wa Mulungu. Chimenecho chinali chiyani? Nthaŵi imene Petro analemba kalata yake yoyamba, aŵiri a Mauthenga Abwino​—Mateyu ndi Luka​—analipo kale. Akristu a m’zaka za zana loyamba amene sanaonepo Yesu anaŵerenga nkhani za m’Mauthenga Abwino zimenezi. Ifenso tingatero. Mauthenga Abwino saali nkhani zopeka; ali ndi maumboni onse a mbiri yodalirika koposa. M’mbiri youziridwa imeneyo, timapezamo zochuluka zimene zimakulitsa chikondi chathu pa Mwana wa Mulungu.

Mzimu Umene Iye Anasonyeza

11, 12. Ponena za mzimu umene Yesu anasonyeza kwa anthu ena, kodi nchiyani chimakusonkhezerani kumkonda?

11 M’mbiri yolembedwa ya moyo wa Yesu imeneyo, timaphunziramo za njira imene iye anachitira ndi anthu ena. Mzimu umene anaonetsa ukukhudza mtima wa anthu ngakhale tsopano, zaka zoposa 1,960 pambuyo pa imfa yake. Munthu aliyense wamoyo akuvutika ndi zotsatira zake za uchimo. Mamiliyoni ambiri achitidwa mosalungama, akuvutika ndi matenda, kapena pazifukwa zina akhumudwa kowopsa. Kwa onse otero, Yesu akuti: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.”​—Mateyu 11:28-30.

12 Yesu anachitira chifundo osauka, anjala, ndi olira. Pamene mikhalidwe inafuna zimenezo, anadyetsa ngakhale makamu aakulu a anthu mozizwitsa. (Luka 9:12-17) Anawamasula ku miyambo yaukapolo. Anamangiriranso chikhulupiriro chawo m’makonzedwe a Mulungu othetsera kutsendereza kwa ndale ndi zachuma. Yesu sanaswe mzimu wa awo omwe anali otsenderezeka kale. Mwachifundo ndi chikondi, iye mwaluso analimbitsa ofatsa. Anatsitsimula aja omwe anali ngati bango lophwanyika lokhofoka ndi aja omwe anali ngati nyali yofuka ili pafupi kuzima. Mpaka lero, dzina lake limapereka chiyembekezo, ngakhale m’mitima ya amene sanamuonepo.​—Mateyu 12:15-21; 15:3-10.

13. Kodi nchifukwa ninji njira imene Yesu anachitira ndi ochimwa imakopa anthu?

13 Yesu sanavomereze kulakwa, koma anawachitirabe chifundo anthu omwe analakwa m’moyo wawo koma amenenso anaonetsa kulapa natembenukira kwa iye kuti awathandize. (Luka 7:36-50) Anali kukhala pansi ndi kudya chakudya ndi anthu onyozeka m’chitaganya ataona kuti zimenezo zidzampatsa mpata wowathandiza mwauzimu. (Mateyu 9:9-13) Chifukwa cha mzimu umene anaonetsa, anthu mamiliyoni ambiri omwe ali m’mikhalidwe yonga imeneyo amene sanamuonepo Yesu asonkhezereka kumdziŵa ndipo amkhulupirira.

14. Kodi chimakukopani nchiyani panjira imene Yesu anathandizira anthu odwala, opunduka, kapena ofedwa?

14 Njira imene Yesu anachitira ndi anthu odwala kapena opunduka imapereka umboni wa chikondi ndi chifundo chake ndiponso wa kukhoza kwake kuwapatsa mpumulo. Chifukwa chake, pamene mwamuna wina wakhate thupi lonse anafika kwa iye namchonderera kuti amthandize, Yesu sananyansidwe ndi maonekedwe ake. Ndipo sanauze mwamunayo kuti, ngakhale kuti anamchitira chifundo, matenda akewo anali oipa koposa ndi kuti palibe chimene akanachita kuti amthandize. Mwamunayo anachonderera kuti: “Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza.” Mosazengereza, Yesu anatambalitsa dzanja lake nakhudza mwamuna wakhateyo, naati: “Ndifuna; takonzedwa.” (Mateyu 8:2, 3) Nthaŵi inanso mkazi wina anafuna kuchira mwa kukhudza mphonje ya chovala chake mobisa. Yesu anachita naye mokoma mtima ndi motonthoza. (Luka 8:43-48) Ndipo pamene anakumana ndi maliro, anamvera chifundo mkazi wamasiye wachisoniyo amene anafedwa mwana wake wamwamuna mmodzi yekha. Ngakhale kuti Yesu anakana kugwiritsira ntchito mphamvu imene Mulungu anampatsa kudzipezera chakudya mozizwitsa, anaigwiritsira nchito mwaufulu kuukitsira munthu wakufayo nampereka kwa amake.​—Luka 4:2-4; 7:11-16.

15. Kodi kuŵerenga nkhani za Yesu ndi kuzisinkhasinkha kumakukhudzani motani?

15 Pamene tiŵerenga nkhani zimenezi ndi kusinkhasinkha za mzimu umene Yesu anasonyeza, chikondi chathu pa ameneyu yemwe anataya moyo wake waumunthu kuti ife tikhale ndi moyo kosatha chimakula. Ngakhale kuti sitinamuonepo, timakopeka naye, ndipo timafuna kulondola mapazi ake.​—1 Petro 2:21.

Kudalira Kwake Mulungu Modzichepetsa

16. Kodi Yesu makamaka anasumika maganizo pa yani, ndipo anatilimbikitsa kuchita chiyani?

16 Koposa zonse, Yesu anasumika maganizo ake ndi athu omwe pa Atate wake wakumwamba, Yehova Mulungu. Anasonyeza lamulo lalikulu koposa la m’Chilamulo, kuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” (Mateyu 22:36, 37) Analangiza ophunzira ake kuti: “Khulupirirani Mulungu.” (Marko 11:22) Pamene iwo anakumana ndi chiyeso cholimba pachikhulupiriro chawo, anawalimbikitsa kuti: “Pempherani kosaleka.”​—Mateyu 26:41, NW.

17, 18. (a) Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anadalira Atate wake modzichepetsa? (b) Nchifukwa ninji zimene anachita zili zofunika kwambiri kwa ife?

17 Yesu mwiniyo anapereka chitsanzo. Pemphero linali chinthu chofunika kwambiri m’moyo wake. (Mateyu 14:23; Luka 9:28; 18:1) Itafika nthaŵi yoti asankhe atumwi ake, Yesu sanadalire kuweruza kwake ayi, ngakhale kuti kale anali kuyang’anira angelo onse kumwamba. Modzichepetsa anachezera usiku wonse kupemphera kwa Atate wake. (Luka 6:12, 13) Pamene anali pafupi kugwidwa ndi kuphedwa, Yesu anatembenukiranso kwa Atate wake, napemphera ndi mtima wonse. Sanaganize kuti anali kumdziŵa bwino Satana ndi kuti akanalimbana mosavuta ndi chilichonse chimene woipayo akanadzetsa. Yesu anazindikira kuti sanafunikira kulephera. Kulephera kwake kukanadzetsa chitonzo chachikulu pa Atate wake! Ndipotu mtundu wa anthu, umene moyo wawo wamtsogolo unadalira pa nsembe imene Yesu anali kupereka, ukanatayikidwa kwambiri!

18 Yesu anapemphera kaŵirikaŵiri​—pamene anali ndi atumwi ake m’chipinda chapamwamba m’Yerusalemu ndiponso mwaphamphu m’munda wa Getsemane. (Mateyu 26:36-44; Yohane 17:1-26; Ahebri 5:7) Povutika pamtengo wozunzirapo, sanawachitire chipongwe aja omwe anali kumseka. M’malo mwake, anawapempherera iwowo amene anali kuchita zimenezo mosadziŵa, kuti: “Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziŵa chimene achita.” (Luka 23:34) Anasumika maganizo ake pa Atate wake, ‘napereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama.’ Mawu omaliza omwe ananena pamtengo wozunzirapo anali pemphero kwa Atate wake. (1 Petro 2:23; Luka 23:46) Tikuthokoza chotani nanga kuti, ndi chidaliro chonse pa Yehova, Yesu anamaliza ntchito yake mokhulupirika imene Atate wake anampatsa! Ngakhale kuti sitinamuonepo Yesu Kristu, timamkonda kwambiri chifukwa cha zimene anachita!

Kusonyeza Chikondi Chathu pa Iye

19. Posonyeza chikondi kwa Yesu, kodi ndi machitachita ati omwe tidzapeŵa osayenera konse?

19 Kodi tingaupereke motani umboni wakuti chikondi chomwe timati tili nacho sichimangothera m’mawu basi? Popeza Atate wake, amene Yesu anakonda, analetsa kupanga mafano ndiyeno kuwayesa zinthu zolambira, sitingalemekeze Yesu konse mwa kuvala fano lotero monga mkanda m’khosi mwathu kapena kulinyamula ndi kumayenda nalo m’khwalala. (Eksodo 20:4, 5; Yohane 4:24) Sitingakhale tikumlemekeza Yesu ngati ife tipita kumapemphero, ngakhale kangapo mlungu umodzi, pamene sitikuchita monga mwa ziphunzitso zake masiku ena m’mlunguwo. Yesu anati: “Iye wakukhala nawo malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga.”​—Yohane 14:21, 23; 15:10.

20. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zidzasonyeza ngati timamkondadi Yesu?

20 Kodi anatipatsa malamulo otani? Loyamba, kulambira Mulungu woona, Yehova, ndipo iye yekhayekha. (Mateyu 4:10; Yohane 17:3) Chifukwa cha mbali yake m’chifuno cha Mulungu, Yesu anaphunzitsanso kuti tiyenera kumkhulupirira monga Mwana wa Mulungu ndi kuti tizisonyeza zimenezo mwa kukana ntchito zoipa ndi mwa kuyenda m’kuunika. (Yohane 3:16-21) Anatilangiza kufunafuna Ufumu wa Mulungu choyamba ndi chilungamo chake, kuika zimenezi patsogolo pake pa nkhaŵa ya zosoŵa zakuthupi. (Mateyu 6:31-33) Analamula kuti tikondane wina ndi mnzake monga momwe anatikondera ife. (Yohane 13:34; 1 Petro 1:22) Ndipo anatituma kuti tikhale mboni za chifuno cha Mulungu, monganso iye. (Mateyu 24:14; 28:19, 20; Chivumbulutso 3:14) Ngakhale kuti sizinamuonepo Yesu, Mboni zake za Yehova mamiliyoni ngati asanu lerolino zimasonkezereka kusunga malamulo amenewo chifukwa chomkonda iye kwenikweni. Mfundo yakuti iwo sanamuone Yesu maso ndi maso siimafooketsa konse cholinga chawo cha kumvera. Zimakumbukira zimene Mbuye wawo anauza mtumwi Tomasi kuti: “Chifukwa wandiona Ine, wakhulupira; odala iwo akukhulupira, angakhale sanaona.”​—Yohane 20:29.

21. Kodi tidzapindula motani mwa kupezekapo pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu, chimene chidzakhalako chaka chino pa Sande, March 23?

21 Tikhulupirira mudzakhala pakati pa awo amene adzasonkhana padziko lonse pa Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova dzuŵa litaloŵa pa Sande, March 23, 1997, kukumbukira chikondi chachikulu koposa chimene Mulungu anasonyeza kwa mtundu wa munthu ndi kukumbukiranso imfa ya Mwana wake wokhulupirika, Yesu Kristu. Zimene zidzachitika ndi kunenedwa nthaŵiyo ziyenera kukulitsa chikondi chathu pa Yehova ndi Mwana wake, motero kukulitsa chikhumbo chathu chomvera malamulo a Mulungu.​—1 Yohane 5:3.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi aja amene buku la Petro woyamba linalembedwako anafika bwanji pomdziŵa Yesu ndi kumkonda?

◻ Kodi zinthu zina zimene Akristu oyambirira anamva zimene zimakusangalatsani nzotani?

◻ Ponena za mzimu umene Yesu anasonyeza, kodi nchiyani chimakulitsa chikondi chanu pa iye?

◻ Kodi nchifukwa ninji kudalira Mulungu modzichepetsa kwa Yesu kuli kofunika kwambiri kwa ife?

◻ Kodi tingasonyeze motani chikondi chathu pa Yesu Kristu?

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Timakopeka ndi Yesu chifukwa cha mzimu umene anasonyeza

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena