‘Kodi Ndiyenera Kubatizidwa?’
PAZOSANKHA zonse zimene timafunikira kupanga m’moyo, mwinamwake palibe chimene chiri chofunika koposa ichi: ‘Kodi ndiyenera kubatizidwa?’ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri? Chifukwa chakuti chosankha chathu ponena za funso limeneli chiri ndi chiyambukiro chachindunji osati chabe panjira yathu ya moyo tsopano komanso paubwino wathu wosatha.
Kodi mwayang’anizana ndi chosankha chimenechi? Mwinamwake mwakhala mukuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kwanthaŵi yakutiyakuti. Kapena makolo anu akhala akukuphunzitsani Malemba kuyambira paukhanda. Tsopano mwafika pamsikhu umene muyenera kudzisankhira zimene muyenera kuchita. Kuti musankhe moyenera, mudzafunikira kumvetsetsa zimene ubatizo umaphatikizapo ndi amene ayenera kubatizidwa.
Zimene Ubatizo Umaphatikizapo
Mofanana ndi phwando laukwati, ubatizo ndiwo dzoma limene limasonyeza unansi. Ponena za phwando la ukwati, mwamuna ndi mkazi ophatikizidwawo amakhala atakulitsa kale unansi wawo wathithithi. Dzoma laukwatilo limangodziŵikitsa poyera zimene zavomerezedwa kale mtseri, ndiko kuti, aŵiriwo tsopano akuloŵa mumgwirizano waukwati weniweniwo. Limatseguliranso mipata ya maubwino amene okwatiranawo adzasangalala nawo ndi kudzetsa mathayo amene ayenera kuwachita pamodzi m’moyo wawo.
Mkhalidwe umenewu ngofanana kwambiri ndi ubatizo. Pamene tiphunzira Baibulo, timazindikira zinthu zabwino zimene Yehova watichitira. Iye watipatsa osati moyo wathu wokha ndi zinthu zonse zomwe timafunikira kuuchirikiza komanso Mwana wake wobadwa yekha kutsegulira njira anthu ochimwa kuloŵa Naye muunansi ndi kupeza moyo wamuyaya m’paradaiso wa padziko lapansi. Pamene tilingalira zonsezi, kodi sitimasonkhezeredwa kuchitapo kanthu?
Kodi tingachitenji? Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, akutiuza kuti: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge [mtengo wake wozunzirapo, NW], nanditsate ine.” (Mateyu 16:24) Inde, tingakhale ophunzira a Yesu Kristu, tikumatsatira chitsanzo chake pochita chifuno cha Atate wake, Yehova. Komabe, kutero, kumafunikiritsa ‘kudzikana’ kwathu, ndiko kuti, kusankha modzifunira kuika chifuniro cha Mulungu patsogolo pa chifuniro chathu; zimenezi zimaphatikizapo kupereka, kapena kupatulira, moyo wathu kuchita chifuniro chake. Kuti tidziŵikitse chosankha chodzifunira ndi chamtseri chimenechi, dzoma lapoyera limachitidwa. Dzoma limenelo ndilo ubatizo wa m’madzi kusonyeza mwapoyera kudzipatulira kwathu kwa Mulungu.
Kodi Ndani Ayenera Kubatizidwa?
Yesu Kristu analangiza otsatira ake ‘kupita ndi kukapanga ophunzira a anthu a mitundu yonse, kumawabatiza m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la mzimu woyera, kuwaphunzitsa kusunga zonse zimene anali atawalamulira.’ (Mateyu 28:19, 20) Mwachiwonekere, mlingo wakutiwakuti wa kukula msinkhu kwa maganizo ndi mtima zimafunika kwa awo amene ati abatizidwe. Kupyolera mwa phunziro lawo laumwini la Mawu a Mulungu, azindikira kufunika kwa ‘kulapa ndi kutembenuka’ panjira yawo ya moyo yakale. (Machitidwe 3:19) Pamenepo, iwo awona kufunika kwa kuyamba ntchito yaulaliki yochitidwa ndi Yesu Kristu, kukhala ophunzira ake. Zonsezi zachitika sitepe la ubatizo lisanachitike.
Kodi inu mwafika pamfundo imeneyi m’kukula kwanu kwauzimu? Kodi mumakhumba kutumikira Mulungu? Ngati ndichoncho, lingalirani mwapemphero chochitika cholembedwa m’Baibulo cha mfule wa ku Aitiyopiya, cholembedwa pa Machitidwe chaputala 8. Pamene maulosi onena za Yesu Mesiyayo anafotokozedwa kwa mwamuna ameneyu, anasinkhasinkha m’maganizo mwake ndi mtima ndiyeno anafunsa kuti: “Chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?” Mwachiwonekere panalibe chomletsa; chotero anabatizidwa.—Machitidwe 8:26-38.
Lerolino ambiri akufunsa funso lofananalo: “Chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?” Monga chotulukapo, anthu atsopano odzipereka 300,945 anabatizidwa mu 1991. Zimenezi zinadzetsa chisangalalo chachikulu kwa anthu onse a Yehova, ndipo akulu m’mipingo ngokondwera kuthandiza anthu ena owongoka mitima kupita patsogolo ndi kukwaniritsa ziyeneretso za ubatizo.
Komabe, mwinamwake akulu a mpingo wanu angapereke lingaliro lakuti muyembekezere. Kapena, ngati muli wachichepere, makolo anu angakulangizeni kuyembekezera. Pamenepo chiyani? Musalefulidwe maganizo. Kumbukirani kuti kuloŵa muunansi wachindunji ndi Wammwambamwamba ndiko nkhani yaikulu kwambiri. Miyezo yapamwamba iyenera kufitsidwa ndi kusungidwa. Chotero mverani malingaliro operekedwa ndipo agwiritsireni ntchito ndi mtima wonse. Ngati simukumvetsetsa zifukwa zoperekedwazo, musachite manyazi, koma funsani kufikira mutamvetsetsa makonzedwe amene muyenera kuchita.
Kumbali ina, anthu ena angazengereze kupanga sitepe lalikululo, monga momwe amalitchulira. Kodi ndinu mmodzi wa iwo? Ndithudi, pangakhale zifukwa zotsimikizirika chifukwa chake mumazengerezera kudzipatulira ndi ubatizo. Koma ngati muli woyenerera ndipo mukukayikirabe, kuli bwino kudzifunsa kuti: “Chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?” Pendani mkhalidwewo mwapemphero ndi kuwona ngati pali chifukwa choyenera chokuchititsani kuzengereza kuyankha chiitano cha Yehova cha kuloŵa muunansi wanu naye.
‘Ndikali Wachichepere’
Ngati muli wachichepere, mungakhale mukuganiza kuti, ‘Ndikali wachichepere.’ Nzowona kuti malinga ngati achichepere akhala omvera ndi kulabadira makolo awo Achikristu ndi kugwiritsira ntchito Malemba monga momwe angathere, angakhale ndi chidaliro chakuti Yehova amawawona kukhala “oyera.” Kwenikweni, Baibulo limatiuza kuti chivomerezo cha Mulungu pa makolo olungama chimafikira ana awo odalirabe pa iwo. (1 Akorinto 7:14) Komabe, palibe malire a usinkhu amene akuperekedwa m’Baibulo pamene pamathera nyengo ya kudalira pamakolo. Chifukwa chake, kuli kofunika kwa achichepere Achikristu kulingalira mwamphamvu funsoli: ‘Kodi ndiyenera kubatizidwa?’
Baibulo limalimbikitsa achichepere ‘kukumbukira Mlengi wawo Wamkulu m’masiku aunyamata wawo.’ (Mlaliki 12:1) Ponena za zimenezi, tiri ndi chitsanzo cha Samueli wachichepere, amene “anatumikira pamaso pa Yehova akali mwana.” Palinso chitsanzo cha Timoteo, amene kuyambira paukhanda anakhulupirira chowonadi chimene anaphunzitsidwa ndi amake ndi agogo ŵake.—1 Samueli 2:18; 2 Timoteo 1:5; 3:14, 15.
Mofananamo lerolino, achichepere ambiri apatulira miyoyo yawo kutumikira Yehova. Akifusa, wa zaka 15, ananena kuti nkhani ina ya m’Msonkhano Wautumiki inamthandiza kupanga chosankha cha kubatizidwa. Ayumi anabatizidwa pamene anali ndi zaka khumi. Iye anafuna kutumikira Yehova chifukwa chakuti anafikadi pakumkonda. Tsopano ali ndi zaka 13 ndipo wawona phunziro lake la Baibulo, limene lafikiranso pakukonda Yehova, likubatizidwa pausinkhu wa zaka 12. Mlongo wake wamng’ono wa Ayumi, Hikaru anabatizidwanso pausinkhu wa zaka khumi. “Ena ananena kuti ndinali wamng’ono kwambiri,” akukumbukira motero, “koma Yehova anadziŵa mmene ndinamvera. Ndinatsimikizira kubatizidwa pamene ndinasankha kupatulira moyo wanga kumtumikira ndi zonse ndinali nazo.”
Chitsanzo cha makolo chinakhalanso chosonkhezera, monga momwe chokumana nacho cha mlongo wina wachichepere chikusonyezera. Atate ŵake analetsa amake kuphunzira naye Baibulo ndi mlongo wake ndi mphwake. Ankawamenya ndi kuwatenthera mabuku. Koma chifukwa cha chipiriro cha amawo ndi chikhulupiriro, anawo ankawona kufunika kwa kutumikira Yehova Mulungu. Msungwana wachichepereyu anabatizidwa pausinkhu wa zaka 13, ndipo mlongo wake ndi mphwake atsatira chitsanzo chake.
‘Ndine Wokalamba Kwambiri’
Wamasalmo anati: “Okalamba pamodzi ndi ana: alemekeze dzina la Yehova.” (Salmo 148:12, 13) Inde, okalamba ayeneranso kuzindikira kufunika kwawo kwa kuima kumbali ya Yehova. Komabe, okalamba ena, amakhoterera kukupeŵa kusintha. Iwo amalingalira kuti “mbatata ikakhota siwongoka.” Komabe, kumbukirani kuti Abrahamu wokhulupirika anali ndi zaka 75 zakubadwa pamene Yehova anamuuza kuti: “Tuluka kudziko lako ndi kwa abale ako, ndipo tiye kudziko limene ndidzakusonyeza iwe.” (Machitidwe 7:3; Genesis 12:1, 4) Mose anali ndi zaka 80 pamene Yehova anamtuma kuti: “Utulutse anthu anga . . . m’Aigupto.” (Eksodo 3:10) Anthu ameneŵa ndi ena anali atakhazikika bwino lomwe m’moyo wawo pamene anapemphedwa ndi Yehova kusonyeza chikondi chawo ndi kudzipatulira kwa iye. Sanazengereze kulabadira pempho la Yehova.
Bwanji za lerolino? Shizumu anali Mbuddha kwa zaka 78 pamene anayamba kuphunzira Baibulo. Banja lake linamtsutsa, osamlola ngakhale kuphunzirira m’nyumba mwake. Pambuyo pa chaka chimodzi chokha, anawona kufunika kwa kudzipatulira kwa Yehova, ndipo anabatizidwa. Kodi nchifukwa ninji anasintha? Iye anati: “Kwazaka zambiri ndinapusitsidwa ndi chipembedzo chonyenga, ndipo ndinafuna kupitirizabe kulandira chowonadi kosatha kwa Yehova.”
‘Chimene Chikupulumutsani Tsopano’
Nthaŵi ikutha. Miyoyo, kuphatikizapo wanu, iri pachiswe. Nkofunika mofulumira kuti mulingalire mwamphamvu nkhani ya kudzipatulira kwa Yehova ndi kukusonyeza mwa ubatizo wa m’madzi. Mtumwi Petro anagogomezera zimenezi mwa kunena kuti: “Chimenenso . . . chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo.” Iye anapitiriza kufotokoza kuti ubatizo “kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi” (munthu amakhala atachita kale zimenezo asanayenerere ubatizo) “komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu.”—1 Petro 3:21.
Pokhala atakwaniritsa zofunikira za Yehova, wophunzira wobatizidwayo amakhala ndi chikumbumtima chabwino. Mwa kupitirizabe kuchita zomwe angathe potumikira Yehova, amakhala ndi mtendere wa maganizo ndi chikhutiro. (Yakobo 1:25) Koposa zonsezo, angayang’ane mtsogolo ndi chidaliro kumadalitso osatha ochokera kwa Yehova m’dongosolo latsopano likudzalo. Limenelo likhaletu gawo lanu pamene mukulabadira motsimikizira funso lakuti: ‘Kodi ndiyenera kubatizidwa?’
[Chithunzi patsamba 21]
Samueli anatumikira pamaso pa Yehova ali mwana
[Chithunzi patsamba 22]
Mose anali wa zaka 80 pamene anatumidwa ndi Yehova
[Zithunzi patsamba 23]
Lerolino achichepere ndi achikulire omwe amene amabatizidwa angayang’ane mtsogolo kumadalitso osatha m’dongosolo latsopano la Mulungu