Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 12/15 tsamba 25-29
  • Kodi Muli ndi Lingaliro Laumulungu pa Moŵa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Muli ndi Lingaliro Laumulungu pa Moŵa?
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Lingaliro Lopanda Umulungu
  • Kodi Kupambanitsa Kumayambira Pati?
  • Tetezerani Kulingalira Kwanu
  • Kodi Nchiyani Chimaumba Lingaliro Lanu pa Moŵa?
  • Peŵani Kukhumudwitsa Ena
  • Akristu Ngosiyana Moonekeratu
  • Kodi Kumwa Mowa N’kulakwa?
    Galamukani!—2006
  • Mowa Umafunika Kusamala Nawo
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Mumayendera Maganizo a Yehova pa Nkhani ya Mowa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Zakumwa Zoledzeretsa Nchiyani Chomwe Chiri Kawonedwe Kachikristu ka Izo?
    Nsanja ya Olonda—1987
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 12/15 tsamba 25-29

Kodi Muli ndi Lingaliro Laumulungu pa Moŵa?

PAFUPIFUPI zaka 20 zapitazo, ofukula za m’mabwinja anafukula nyumba yakale ya njerwa zadothi pafupi ndi tauni ya Urmia, Iran. Anapezamo chikho chadothi chimene, malinga ndi kunena kwa asayansi, chili ndi zaka zikwi zambiri, cha nthaŵi pamene midzi ina ya anthu yakale kwambiri inakhazikitsidwa. Posachedwapa njira zamakono zinagwiritsiridwa ntchito posanthula chikhocho. Asayansi anadabwa kupeza mkati mwake umboni wa makemikolo wakale koposa wa kupanga vinyo.

Baibulo nalonso limanena motsimikiza kuti kuyambira nthaŵi zakale anthu akhala ali kumwa vinyo, moŵa, ndi zakumwa zina zoledzeretsa. (Genesis 27:25; Mlaliki 9:7; Nahumu 1:10) Monga momwe zilili ndi zakudya zina, Yehova amatipatsa chosankha aliyense payekha​—kumwa kapena kusamwa moŵa. Yesu kaŵirikaŵiri anali kumwa vinyo pachakudya chake. Yohane Mbatizi sanali kumwa moŵa.​—Mateyu 11:18, 19.

Baibulo sililola kumwa kwambiri. Kuledzera kuli kuchimwira Mulungu. (1 Akorinto 6:9-11) Mogwirizana ndi zimenezi, Mboni za Yehova sizimalola aliyense amene akhala chidakwa chosalapa kuti akhalebe mumpingo wachikristu. Awo amene ali mumpingo amene asankha kumwa moŵa ayenera kutero modzisunga.​—Tito 2:2, 3.

Lingaliro Lopanda Umulungu

Anthu ambiri lerolino alibe lingaliro laumulungu pa moŵa. Nkosavuta kuona kuti Satana akusonkhezera kululuza chakumwa chakale chimenechi. Mwachitsanzo, m’zisumbu zina za ku South Pacific, nkwachizoloŵezi kwa amuna kukumana pamodzi kudzamwa chakumwa chovundika chochuluka chopangidwa panyumba. Nyengo zimenezi zimatha maola angapo ndipo amakhala nazo kaŵirikaŵiri​—amuna ambiri amachita zimenezi tsiku ndi tsiku. Ena amachiyesa mbali ya mwambo chabe. Nthaŵi zina iwo amamwa moŵa ndi kachasu m’malo mwa​—kapena kuwonjezera pa​—chakumwa chakumeneko chopangidwa panyumba. Kaŵirikaŵiri pamakhala kuledzera.

M’dziko linanso la ku Pacific, kumwa moŵa modzisunga kwa amuna sikumatchulidwa nkomwe. Kaŵirikaŵiri, pamene akumwa, amamwa kuti aledzere. Kwenikweni, patsiku lamalipiro gulu la amuna limakumana ndi kugula makatoni angapo a moŵa, katoni iliyonse yokhala ndi mabotolo 24. Amaleka kumwa kokha pamene moŵa watha. Chifukwa cha zimenezo, kuledzera poyera nkofala kwambiri.

Zakumwa zovundika, zonga uchema ndi moŵa wina wophikidwa kumaloko, amazigwiritsira ntchito mwamwambo m’maiko a mu Afirika. Mwambo kumalo ena umafuna kuti pamene akuchezetsa alendo, ayenera kuwapatsa moŵa. Wochezetsa alendoyo mwamwambo amapereka chakumwa chochuluka chimene mlendo wake sangachimalize. Kumalo ena mwambo ndiwo wakuti amapatsa mlendo aliyense mabotolo 12 a moŵa.

Makampani ambiri a ku Japan amalinganiza maulendo apabasi kaamba ka antchito awo. Amapita ndi moŵa wochuluka, ndipo kuledzera sikumaonedwa ngati nkhani yaikulu. Ena a maulendo okacheza ameneŵa a makampani amatenga masiku aŵiri kapena atatu. Malinga ndi kunena kwa magazini a Asiaweek, ku Japan, “kuyambira alimi a mpunga mpaka andale olemera, umuna wa munthu mwamwambo umapimidwa ndi unyinji wa kachasu amene angamwe.” Machitidwe ofananawo akuonedwa m’maiko enanso a ku Asia. Asiaweek ikunena kuti “anthu a ku South Korea tsopano amamwa kachasu wochuluka pa munthu mmodzi kuposa amene amamwa a kwina kulikonse m’dziko.”

Kumwetsa moŵa pamapwando kwakhala chizoloŵezi chofala m’makoleji a ku United States. Malinga ndi kunena kwa The Journal of the American Medical Association, “ochuluka amene amamwetsa moŵa pamapwando samadziona kuti ali ndi vuto.”a Zimenezi sizikudabwitsa chifukwa chakuti m’maiko ambiri ofalitsa nkhani amachirikiza kumwa kuti kuli kosangalatsa, kwamakono, ndi mchitidwe wa odziŵa zambiri. Nthaŵi zambiri mabodza ameneŵa kwenikweni amapangidwira achichepere.

Ku Britain, unyinji wa moŵa womwedwa waŵirikiza kaŵiri m’nyengo ya zaka 20, ndipo kumwa kachasu wamkali kwambiri kwaŵirikiza katatu. Akumwa moŵa akuyamba adakali achichepere kwambiri, ndipo akazi ambiri akumwa moŵa. Mkhalidwe wofananawo ukupezeka m’maiko a ku Eastern Europe ndi Latin-America. Zimenezi zimasonyezedwa ndi ziŵerengero zomakwera mofanana za uchidakwa ndi imfa za m’ngozi za pamsewu zimene moŵa umachititsa. Ndithudi, kumwetsa moŵa padziko lonse kwawonjezeka mosakayikira konse.

Kodi Kupambanitsa Kumayambira Pati?

Lingaliro la Baibulo pa moŵa nlolinganizika. Kumbali ina, Malemba amanena kuti vinyo uli mphatso yochokera kwa Yehova Mulungu ‘yokondweretsa mtima wa munthu.’ (Salmo 104:1, 15) Ndiyeno kumbali inanso, potsutsa kupambanitsa Baibulo limagwiritsira ntchito mawu akuti “kuledzera,” “maledzero, madyerero, mamwaimwa,” ‘kumwetsa vinyo,’ ndi ‘kukodwa nacho chikondi cha pavinyo.’ (Luka 21:34; 1 Petro 4:3; 1 Timoteo 3:8; Tito 2:3) Koma kodi ‘kumwetsa vinyo’ kumayambira pati? Kodi ndi motani mmene Mkristu angalidziŵire lingaliro laumulungu pa moŵa?

Nkosavuta kudziŵa kuti munthu waledzera. Zotulukapo zake zalongosoledwa m’Baibulo ndi mawu akuti: “Ndani ali ndi chisoni? Ndani asauka? Ndani ali ndi makangano? Ndani ang’ung’udza? Ndani alasidwa chabe? Ndani afiira maso? Ngamene achedwa pali vinyo, napita kukafunafuna vinyo wosanganizidwa. . . . Maso ako adzaona zachilendo, mtima wako udzalankhula zokhota.”​—Miyambo 23:29-33.

Kumwa moŵa kopambanitsa kungachititse kusokonezeka maganizo, kuona zideruderu, kusazindikira zomwe zikuchitika, ndi matenda ena a m’maganizo ndi m’thupi. Mosonkhezeredwa ndi moŵa, munthu angalephere kulamulira khalidwe lake, akumadzivulaza yekha kapena kuvulaza ena. Anthu amadziŵa kuti zidakwa zimakhala ndi khalidwe lopusa, lachipongwe, kapena lachiwerewere.

Kumwa mpaka kuledzera, ndi kukhala ndi zotulukapo zotchulidwazo, kulidi kumwa mopambanitsa. Komabe, munthu akhoza kusonyeza kusadzisunga popanda kusonyeza zizindikiro zake zonse za kuledzera. Ndiye chifukwa chake pamakhala kusamvana pa nkhani yakuti kaya munthu wamwa mopambanitsa. Kodi malire a kudzisunga ndi kupambanitsa ali pati?

Tetezerani Kulingalira Kwanu

Baibulo silimaika malire mwa kutchula unyinji wa moŵa umene uyenera kukhala m’mwazi kapena muyezo wina uliwonse. Unyinji wa moŵa umene munthu aliyense angamwe asanaledzere umasiyanasiyana. Komabe, Akristu onse ayenera kutsatira mapulinsipulo a Baibulo ndipo angatithandize kukhala ndi lingaliro laumulungu pa moŵa.

Lamulo loyamba, Yesu anatero, ndilo ‘kukonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.’ (Mateyu 22:37, 38) Moŵa umayambukira malingaliro mwachindunji, ndipo kupambanitsa kudzakulepheretsani kumvera lamulo lalikulu koposa onse limeneli. Ukhoza kudodometsa kwambiri kuweruza kwabwino, nzeru yothetsera mavuto, kudziletsa, ndi ntchito zina zofunika za maganizo. Malemba amatipatsa uphungu wakuti: “Sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira; ndipo mtima wako udzatengapo moyo, ndi khosi lako chisomo.”​—Miyambo 3:21, 22.

Mtumwi Paulo akuchonderera Akristu kuti: “Mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yoyera, yolandirika kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika ndi mphamvu yanu ya kulingalira.” (Aroma 12:1, NW) Kodi Mkristu angakhale ‘wolandirika kwa Mulungu’ ngati amamwa moŵa mpaka kufooketsa ‘mphamvu yake ya kulingalira’? Nthaŵi zambiri, wakumwa mosadzisunga thupi lake limayamba kuzoloŵera moŵa pang’onopang’ono. Angalingalire kuti kumwa kwake kopambanitsa​—kwa iye​—sikuli uchidakwa. Komabe, angayambe kumadalira moŵa mosayenera. Kodi munthu woteroyo angapereke thupi lake monga “nsembe yamoyo, yoyera”?

Unyinji uliwonse wa moŵa umene udodometsa “nzeru [yanu] yeniyeni ndi kulingalira” monga Mkristu ndi moŵa wopambanitsa kwa inu.

Kodi Nchiyani Chimaumba Lingaliro Lanu pa Moŵa?

Mkristu ayenera kusanthula kuti aone ngati maganizo ake ponena za kumwa akuyambukiridwa ndi khalidwe lomwe lafala kapena miyambo. Ponena za moŵa, ndithudi simuyenera kuzika zosankha zanu pa khalidwe lofala kapena mabodza a ofalitsa nkhani. Pofufuza maganizo anu, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikusonkhezeredwa ndi zimene anthu amalandira? Kapena kodi kumwa kwanga kumatsogozedwa ndi mapulinsipulo a Baibulo?’

Ngakhale kuti Mboni za Yehova si anthu otsutsa chikhalidwe, iwo amadziŵa kuti Yehova amada machitachita ochuluka ochitidwa ndi anthu ambiri lerolino. Maiko ena amalola kuchotsa mimba, kuikidwa mwazi, umathanyula, kapena mitala. Komabe, Akristu amatsatira lingaliro la Mulungu pa zinthu zimenezi. Inde, lingaliro laumulungu lidzasonkhezera Mkristu kuda machitachita ameneŵa ngakhale ngati amalandiridwa kapena samalandiridwa monga mwambo.​—Salmo 97:10.

Baibulo limanena za “chifuno cha amitundu,” chimene chimaphatikizapo “maledzero” ndi “mamwaimwa.” Liwulo “mamwaimwa” limapereka lingaliro la macheza amene anali kulinganizidwa ndi chifuno chachikulu cha kumwa moŵa wochuluka. Zikuchita ngati m’nthaŵi za Baibulo ena amene ankanyada kuti akanakhoza kumwa moŵa wambiri popanda kuledzera ankayesa kumwa kuposa ena, kapena ankayesa kuona amene akanamwa koposa onse. Mtumwi Petro akunena kuti khalidweli ndilo ‘kusefukira kwa chitayiko’ kumene Akristu olapa satengamonso mbali.​—1 Petro 4:3, 4.

Kodi kungakhale bwino kwa Mkristu kutengera lingaliro lakuti malinga ngati sanaledzere, palibe kanthu ndi kumene anamwera, nthaŵi yake, kapena unyinji wa zimene anamwa? Tingafunse kuti, Kodi limeneli ndi lingaliro laumulungu? Baibulo limanena kuti: “Mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.” (1 Akorinto 10:31) Gulu la amuna amene akumana kuti amwe poyera moŵa wochuluka mwinamwake sangaledzere onse, koma kodi khalidwe lawo lidzapereka ulemerero kwa Yehova? Baibulo limachenjeza kuti: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.”​—Aroma 12:2.

Peŵani Kukhumudwitsa Ena

Chochititsa chidwi nchakuti, nthaŵi zambiri anthu amene amalekerera kupambanitsa amanyansidwa nako pamene chidakwa anena kuti ali munthu wa Mulungu. M’mudzi wina waung’ono ku South Pacific, munthu wina anati: “Anthu inu ndimakukhumbirani. Mumalalikira choonadi. Koma vuto limene timaonapo ndilo lakuti amuna a kwanu amamwa kwambiri kachasu.” Malinga ndi malipoti, amunawo sanaledzere, komabe si ambiri m’mudzimo amene anadziŵa zimenezo. Anthu openyerera angangogamula kuti monga amuna ena ochuluka amene amakhala pamapwando a moŵa, Mboninso zimaledzera. Kodi mtumiki wachikristu amene amakhala pamapwando aatali a moŵa akhoza kukhalabe ndi mbiri yabwino ndi kutsiriza utumiki wake wapoyera ndi ufulu wa kulankhula?​—Machitidwe 28:31.

Lipoti lochokera ku dziko lina la ku Ulaya limasonyeza kuti nthaŵi zina abale ndi alongo ena amafika pa Nyumba ya Ufumu akumanunkha kwambiri moŵa mkamwa mwawo. Zimenezi zavutitsa zikumbumtima za ena. Baibulo limapereka uphungu wakuti: “Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusachita chinthu chilichonse chakukhumudwitsa mbale wako.” (Aroma 14:21) Lingaliro laumulungu pa moŵa lidzasonkhezera Mkristu wokula msinkhu kukhala wosamala kwambiri ndi zikumbumtima za ena, ngakhale ngati kungafune kusamwa moŵa m’mikhalidwe ina.

Akristu Ngosiyana Moonekeratu

Mwachisoni, dzikoli lachita zambiri zolakwira Yehova mwa kululuza zinthu zabwino zimene wapatsa anthu kuphatikizapo moŵa. Mkristu wodzipatulira aliyense ayenera kuyesayesa kupeŵa malingaliro osakhala aumulungu ofalawa. Chotero anthu adzatha “kuzindikira [kusiyana, NW] pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.”​—Malaki 3:18.

Ponena za moŵa, “kusiyana” pakati pa Mboni za Yehova ndi dziko kuyenera kukhala koonekeratu. Kumwa moŵa sindiko chinthu chachikulu m’moyo wa Akristu oona. Iwo samayesa kuona unyinji wa moŵa umene angamwe asanaledzere, ndipo kutsala pango’ono kwambiri kuledzera; ndiponso samalola moŵa kuwononga kapena m’njira ina iliyonse kusokoneza kutumikira kwawo Mulungu ndi moyo wawo wonse ndiponso ndi maganizo osasokonezeka.

Monga gulu, Mboni za Yehova zili ndi lingaliro laumulungu pa moŵa. Bwanji ponena za inu? Aliyense wa ife angadalire pa madalitso a Yehova pamene titsatira chilangizo cha Baibulo chakuti ‘tikane chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m’dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza.’​—Tito 2:12.

[Mawu a M’munsi]

a “Kumwetsa moŵa pamapwando kunalongosoledwa kuti ndiko kumwa mabotolo asanu kapena kuposapo motsatizana kwa amuna ndipo mabotolo anayi kapena kuposapo motsatizana kwa akazi.”​—The Journal of the American Medical Association.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 28]

Mvetserani Okondedwa Anu

Wakumwa mosadzisunga nthaŵi zambiri ndiye amakhala wotsirizira kuzindikira kuti ali ndi vuto. Achibale, mabwenzi, ndi akulu achikristu sayenera kuzengereza kupereka thandizo kwa okondedwa amene alibe kudzisunga. Ndiyenonso, ngati okondedwa afotokoza nkhaŵa zawo ponena za kamwedwe kanu ka moŵa, ayenera kuti ali ndi zifukwa zabwino. Lingalirani zimene akunena.​—Miyambo 19:20; 27:6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena