Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Kapolo Wokhulupirika” Wapambana Mayeso!
    Nsanja ya Olonda—2004 | March 1
    • 15, 16. (a) Kodi nthaŵi yoŵerengerana inali liti? (b) Kodi akapolo okhulupirika anapatsidwa mwayi watsopano wotani wochita “malonda”?

      15 Fanizoli limapitiriza kuti: “Ndipo itapita nthaŵi yaikulu, anabwera mbuye wa akapolo awo, naŵerengera nawo pamodzi.” (Mateyu 25:19) Mu 1914​—patathadi nthaŵi yaitali kuchokera mu 33 C.E.​—Kristu Yesu anayamba kukhalapo kwake monga Mfumu. Patatha zaka zitatu ndi theka, mu 1918, iye anabwera m’kachisi wauzimu wa Mulungu ndi kukwaniritsa mawu a Petro, akuti: “Yafika nthaŵi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu.” (1 Petro 4:17; Malaki 3:1) Inali nthaŵi yoti aŵerengerane.

  • “Kapolo Wokhulupirika” Wapambana Mayeso!
    Nsanja ya Olonda—2004 | March 1
    • Mu Mateyu chaputala 24 ndi 25, Yesu ananena za ‘kudza’ ndi matanthauzo osiyanasiyana. Sakuchita kufunika kusintha malo kuti ‘adze.’ M’malomwake, iye ‘akudza’ m’lingaliro la kuika maganizo ake pa anthu kapena otsatira ake ndipo nthaŵi zambiri n’cholinga chopereka chiweruzo. Motero, mu 1914 ‘anadza’ kuti ayambe kukhalapo monga Mfumu yoikidwa. (Mateyu 16:28; 17:1; Machitidwe 1:11) Mu 1918 ‘anadza’ monga mthenga wa chipangano ndi kuyamba kuweruza anthu omwe ankanena kuti akutumikira Yehova. (Malaki 3:1-3; 1 Petro 4:17) Pa Armagedo, “adzadza” kudzaweruza adani a Yehova.​—Chivumbulutso 19:11-16.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena