-
Abusa, Tsanzirani Abusa AakuluNsanja ya Olonda—2013 | November 15
-
-
4. Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino?
4 Ndiyeno kodi abusawa ayenera kuweta bwanji nkhosa za Mulungu? Akhristu onse amauzidwa kuti ‘azimvera amene akutsogolera pakati pawo.’ Pomwe akulu amalangizidwa kuti ‘asamachite ufumu pa anthu amene ali cholowa chochokera kwa Mulungu.’ (Aheb. 13:17; werengani 1 Petulo 5:2, 3.) Ndiyeno funso n’kumati, Kodi akulu angatsogolere bwanji nkhosa popanda kuchita ufumu? Kapena tifunse kuti, Kodi akulu angatani kuti azikwaniritsa udindo umene Mulungu wawapatsa woyang’anira nkhosa zake popanda kupitirira malire?
-
-
Abusa, Tsanzirani Abusa AakuluNsanja ya Olonda—2013 | November 15
-
-
9. Kodi Yesu analimbikitsa ophunzira ake kupewa mtima wotani?
9 Pa nthawi ina, Yakobo ndi Yohane anasonyeza kuti sankaona udindo wa abusa mmene Yesu ankauonera. Atumwi awiriwa ankafuna kukhala ndi malo apamwamba mu Ufumu. Koma Yesu anawathandiza powauza kuti: “Inu mukudziwa kuti olamulira a anthu a mitundu ina amapondereza anthu awo ndipo akuluakulu amasonyeza mphamvu zawo pa iwo. Sizili choncho pakati panu, koma aliyense wofuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala mtumiki wanu.” (Mat. 20:25, 26) Atumwiwo anafunika kupewa mtima wofuna ‘kuchita ufumu’ kapena wofuna ‘kusonyeza mphamvu zawo kwa ena.’
10. (a) Kodi Yesu amafuna kuti akulu aziweta bwanji nkhosa? (b) Kodi Paulo anapereka chitsanzo chotani pa nkhaniyi?
10 Yesu amafuna kuti akulu azimutsanzira poweta nkhosa. Iwo ayenera kuchita zinthu ndi Akhristu monga atumiki anzawo osati mabwana awo. Umenewu ndi mtima umene mtumwi Paulo anali nawo. Tikutero chifukwa chakuti analangiza akulu a ku Efeso kuti: “Inu mukudziwa bwino mmene ndinali kukhalira nanu nthawi zonse kuchokera tsiku loyamba limene ndinaponda m’chigawo cha Asia. Ndinali kutumikira Ambuye monga kapolo, modzichepetsa kwambiri.” Paulo ankafuna kuti akuluwo azithandiza Akhristu anzawo modzipereka ndiponso modzichepetsa. Iye anati: “M’zinthu zonse ndakuonetsani kuti mwa kugwira ntchito molimbika chomwechi, muthandize ofookawo.” (Mac. 20:18, 19, 35) Paulo anauza Akhristu a ku Korinto kuti iye sanali wolamulira chikhulupiriro chawo koma anali wantchito mnzawo kuti akhale ndi chimwemwe. (2 Akor. 1:24) Apatu Paulo anapereka chitsanzo chabwino kwa akulu pa nkhani ya kudzichepetsa ndiponso kudzipereka.
-
-
Abusa, Tsanzirani Abusa AakuluNsanja ya Olonda—2013 | November 15
-
-
“MUKHALE ZITSANZO KWA GULU LA NKHOSA”
Akulu amathandiza mabanja awo kukonzekera utumiki (Onani ndime 13)
13, 14. Kodi mkulu angakhale chitsanzo chabwino m’njira ziti?
13 Mtumwi Petulo atalangiza akulu mumpingo kuti ‘asamachite ufumu pa anthu amene ali cholowa chochokera kwa Mulungu,’ anawalimbikitsa kuti ‘akhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa.’ (1 Pet. 5:3) Kodi akulu angakhale bwanji zitsanzo kwa nkhosa? Tiyeni tione zinthu ziwiri zofunika kwa m’bale amene “akuyesetsa kuti akhale woyang’anira.” Choyamba, ayenera kukhala “woganiza bwino.” Izi zikutanthauza kuti ayenera kumvetsa mfundo za m’Mawu a Mulungu komanso ayenera kudziwa mmene angazigwiritsire ntchito pa moyo wake. Azichita zinthu moleza mtima ndipo asamapupulume posankha zochita. Chachiwiri, ayenera kukhala “woyang’anira bwino banja lake.” Izi zikutanthauza kuti ngati mkulu ali ndi banja, ayenera kupereka chitsanzo pa nkhani yoyang’anira banja lake chifukwa “ngati munthu sadziwa kuyang’anira banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalire bwanji?” (1 Tim. 3:1, 2, 4, 5) Abale ndi alongo mumpingo akaona kuti akulu akuchita zimenezi amawadalira ndi kuwalemekeza kwambiri.
14 Akulu angakhalenso chitsanzo chabwino kwa Akhristu anzawo ngati amatsogolera pa ntchito yolalikira. Pa nkhani imeneyi, Yesu anapereka chitsanzo kwa oyang’anira. Kulalikira uthenga wabwino inali ntchito yofunika kwambiri kwa Yesu. Iye anaphunzitsanso ophunzira ake kuti azigwira ntchito imeneyi. (Maliko 1:38; Luka 8:1) Masiku ano, abale ndi alongo amasangalala akayenda limodzi ndi akulu mu utumiki. Iwo amaona khama la akuluwo pa ntchito yofunikayi ndipo amaphunzira zambiri akamaona mmene akuphunzitsira. Anthu mumpingo akaona akulu akulalikira uthenga wabwino mwakhama, ngakhale kuti amakhala otanganidwa kwambiri, amalimbikitsidwa ndipo amatengera chitsanzo chawo. Akulu akhoza kuperekanso chitsanzo chabwino akamakonzekera bwino misonkhano yampingo komanso kugwira nawo ntchito zina monga kuyeretsa ndi kukonza Nyumba ya Ufumu.—Aef. 5:15, 16; werengani Aheberi 13:7.
Oyang’anira amapereka chitsanzo chabwino mu utumiki (Onani ndime 14)
-