Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Tayani Nkhaŵa Yanu Yonse pa Yehova
    Nsanja ya Olonda—1994 | November 15
    • 8, 9. Kodi ndi chitonthozo chotani chimene chingapezedwe mu 1 Petro 5:6-11?

      8 Petro anawonjezera kuti: “Potero dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthaŵi yake akakukwezeni; ndi kutaya pa Iye nkhaŵa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu. Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire; ameneyo mumkanize okhazikika m’chikhulupiriro, podziŵa kuti zoŵaŵa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko. Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kuloŵa ulemerero wake wosatha mwa Kristu, mutamva zoŵaŵa kanthaŵi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu. Kwa Iye kukhale mphamvu ku nthaŵi za nthaŵi. Amen.”​—1 Petro 5:6-11.

  • Tayani Nkhaŵa Yanu Yonse pa Yehova
    Nsanja ya Olonda—1994 | November 15
    • 10. Kodi 1 Petro 5:6, 7 amakhudza mikhalidwe itatu iti imene ingatithandize kuchepetsa nkhaŵa?

      10 Petro Woyamba 5:6, 7 amakhudza mikhalidwe itatu imene ingatithandize kulimbana ndi nkhaŵa. Umodzi ndiwo kufatsa, kapena “kudzichepetsa.” Vesi 6 limatha ndi mawu akuti “panthaŵi yake,” likumapereka lingaliro la kufunika kwa kuleza mtima. Vesi 7 limasonyeza kuti ife tingataye nkhaŵa yathu yonse pa Mulungu ndi chidaliro ‘pakuti iye asamalira ife,’ ndipo mawu amenewo amalimbikitsa kukhulupirira Yehova kotheratu. Chotero tiyeni tione mmene kufatsa, chipiriro, ndi kukhulupirira Mulungu kotheratu zingathandizire kuchepetsa nkhaŵa.

      Mmene Kufatsa Kungathandizire

      11. Kodi ndimotani mmene kufatsa kungatithandizire kulimbana ndi nkhaŵa?

      11 Ngati tili ofatsa, tidzavomereza kuti malingaliro a Mulungu ali apamwamba kuposa a ife eni. (Yesaya 55:8, 9) Kufatsa kumatithandiza kuzindikira kufinimpha maganizo kwathu poyerekezera ndi malingaliro akuya a Yehova. Iye amaona zinthu zimene sitidziŵa, monga momwe nkhani ya munthu wolungamayo Yobu imasonyezera. (Yobu 1:7-12; 2:1-6) Mwa kudzichititsa kukhala ofatsa “pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu,” timavomereza malo athu otsika poyerekezera ndi a Mfumu Yam’mwambamwamba. Zimenezi nazonso, zimatithandiza kulimbana ndi mikhalidwe imene iye amalola. Mitima yathu ingakhumbe kupeza mpumulo panthaŵi yomweyo, koma popeza kuti mikhalidwe ya Yehova njolinganizika bwino kwambiri, amadziŵa bwino lomwe nthaŵi ndi mmene adzachitirapo kanthu kaamba ka ife. Pamenepo, ife mofanana ndi ana, tiyeni tigwiritsitse zolimba mkono wa Yehova wamphamvuwo modzichepetsa, tili ndi chidaliro chakuti iye adzatithandiza kulimbana ndi nkhaŵa zathu.​—Yesaya 41:8-13.

      12. Kodi nchiyani chimene chidzachitikira nkhaŵa ya chisungiko cha zachuma ngati tigwiritsira ntchito mofatsa mawu a Ahebri 13:5?

      12 Kufatsa kumaphatikizapo kufunitsitsa kugwiritsira ntchito uphungu wa Mawu a Mulungu, umene kaŵirikaŵiri ungachepetse nkhaŵa. Mwachitsanzo, ngati nkhaŵa yathu yakhalapo chifukwa cha kuloŵa mwakuya m’kulondola zinthu zakuthupi, kungakhale bwino kwa ife kulingalira za uphungu wa Paulo wakuti: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti [Mulungu] anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” (Ahebri 13:5) Mwa kugwiritsira ntchito modzichepetsa uphungu wotero, ambiri adziwonjola pa nkhaŵa yaikulu ya chisungiko cha zachuma. Ngakhale kuli kwakuti mkhalidwe wawo wa ndalama sunawongokere, zimenezi sizimalamulira malingaliro awo kuti ziwaloŵetse m’ngozi yauzimu.

      Mbali ya Kuleza Mtima

      13, 14. (a) Ponena za kupirira moleza mtima, kodi ndi chitsanzo chotani chimene munthuyo Yobu anapereka? (b) Kodi kuyembekezera Yehova moleza mtima kungatichitirenji?

      13 Mawu akuti “panthaŵi yake” pa 1 Petro 5:6 amapereka lingaliro la kufunika kwa kupirira moleza mtima. Nthaŵi zina vuto limapitirizabe kwanthaŵi yaitali, ndipo zimenezo zingawonjezere nkhaŵa. Pamenepo mpamene makamaka timafunikira kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova. Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Yobu anatayikiridwa ndi chuma, anatayikiridwa ndi ana khumi mu imfa, anadwala nthenda yonyansa, ndipo anaimbidwa mlandu molakwa ndi otonthoza onyenga. Ndithudi pangakhale nkhaŵa mwachibadwa m’mikhalidwe yotero.

      14 Mulimonse mmene zinalili, Yobu anali chitsanzo chabwino cha kupirira moleza mtima. Ngati tili pansi pa chiyeso chachikulu cha chikhulupiriro, mwina tingafunikire kuyembekezera mpumulo, monga momwedi iye anachitira. Koma Mulungu anachitapo kanthu m’malo mwake, potsirizira pake akumachotsera Yobu mavuto ake ndi kumfupa moŵirikiza. (Yobu 42:10-17) Kuyembekezera pa Yehova moleza mtima kumakulitsa chipiriro chathu ndi kusonyeza kuya kwa kudzipereka kwathu kwa iye.​—Yakobo 1:2-4.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena