-
Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
Zimene Baibulo limanena: ‘Mutulireni [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’—1 Petulo 5:7.
Mfundo yake: Mulungu akukupemphani kuti muzimasuka kumuuza chilichonse chimene chikukudetsani nkhawa.
Mulungu akhoza kukupatsani mtendere wa mumtima komanso mphamvu kuti muthe kupirira mavuto amene mukukumana nawo. (Afilipi 4:6, 7, 13) Mulungu amagwiritsa ntchito njira imeneyi pothandiza anthu omwe akumupempha kuti awathandize.—Salimo 55:22.
-
-
Kodi M’Baibulo Mungapezeke Mawu Omwe Angandilimbikitse?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
1 Petulo 5:7: ‘Mutulireni nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’
Mfundo yake: Mulungu amatidera nkhawa tikamavutika. Iye amatilimbikitsa kuti tizipemphera kwa iye n’kumuuza zomwe zikutidetsa nkhawa.
-