Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Labadirani Malonjezo a Mulungu mwa Kusonyeza Chikhulupiriro
    Nsanja ya Olonda—1993 | July 15
    • 4. Kodi ndimikhalidwe iti imene tiyenera kuwonjezera pachikhulupiriro chathu?

      4 Kukhulupirira malonjezo a Yehova ndi kuyamikira ufulu wathu wopatsidwa ndi Mulungu ziyenera kutisonkhezera kuchita zomwe tingathe kuti tikhale Akristu ochita bwino. Petro anati: “Pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pachikhulupiriro chanu, ndi paukoma [chidziŵitso, NW]; ndi [pachidziŵitso, NW] chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro [kudzipereka kwaumulungu, NW]; ndi [pakudzipereka kwamulungu, NW] chikondi cha pa abale; ndi pachikondi cha pa abale chikondi.” (2 Petro 1:5-7) Motero Petro amatipatsa mpambo umene tingachite bwino kuuloŵeza mumtima. Tiyeni tipende mikhalidwe imeneyi.

  • Labadirani Malonjezo a Mulungu mwa Kusonyeza Chikhulupiriro
    Nsanja ya Olonda—1993 | July 15
    • 9. (a) Kodi kudzipereka kwaumulungu nchiyani? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuwonjezera kukonda abale pakudzipereka kwathu kwaumulungu? (c) Kodi tingawonjezerepo motani kukonda kwathu abale?

      9 Pachipiriro chathu, tiyenera kuwonjezeranso kudzipereka kwaumulungu​—mantha a ulemu, kulambira, ndi kutumikira Yehova. Chikhulupiriro chathu chimakula pamene tichita kudzipereka kwaumulungu ndi kuona mmene Yehova amachitira ndi anthu ake. Komabe, kuti tisonyeze umulungu, tifunikira kukonda abale. Ndiiko komwe, “iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.” (1 Yohane 4:20) Mitima yathu iyenera kutisonkhezera kusonyeza chikondi chowona kwa atumiki ena a Yehova ndi kufuna kuwachitira zabwino nthaŵi zonse. (Yakobo 2:14-17) Koma kodi nchifukwa ninji tikuuzidwa kuwonjezera chikondi pakukonda kwathu abale? Mwachiwonekere Petro anatanthauza kuti tiyenera kusonyeza chikondi kwa anthu onse, osati abale athu okha. Makamaka chikondi chimenechi chimasonyezedwa mwa kulalikira mbiri yabwino ndi kuthandiza anthu mwauzimu.​—Mateyu 24:14; 28:19, 20.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena