Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa Mulungu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 1. Ngati anthu ndi amene analemba Baibulo, n’chifukwa chiyani tinganene kuti mlembi wake wamkulu ndi Mulungu?

      Baibulo linalembedwa ndi anthu 40 kwa zaka pafupifupi 1,600 kuchokera mu 1513 B.C.E., kufika mu 98 C.E. Anthu amene analembawa moyo wawo unali wosiyanasiyana. Ngakhale zili choncho, mabuku ake onse ndi ogwirizana. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? N’chifukwa chakuti Mlembi Wamkulu wa Baibulo ndi Mulungu. (Werengani 1 Atesalonika 2:13.) Anthuwo sanalembe maganizo awo. Koma “analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.”a (2 Petulo 1:21) Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera pouzira kapena kuti kuchititsa amuna amenewa kuti alembe maganizo ake.​—2 Timoteyo 3:16.

  • Kodi Yehova Ndi Wotani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
    • 4. Mzimu woyera ndi mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito

      Zithunzi: Zomwe Mulungu anachita pogwiritsa ntchito mzimu woyera. 1. Mapulaneti ndi zinthu zina za m’chilengedwe. 2. Munthu akulemba mawu ouziridwa ndi Mulungu pampukutu.

      Yehova amagwiritsa ntchito mzimu woyera ngati mmene ifeyo timagwiritsira ntchito manja athu. Baibulo limasonyeza kuti mzimu woyera si munthu, koma ndi mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito. Werengani Luka 11:13, ndi Machitidwe 2:17, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

      • Mulungu ‘amatsanulira’ mzimu wake woyera kwa anthu amene amamupempha. Kodi inuyo mukuganiza kuti mzimu woyera ndi munthu kapena ndi mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito? N’chifukwa chiyani mukutero?

      Yehova amagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti apange zinthu zodabwitsa kwambiri. Werengani Salimo 33:6 ndi 2 Petulo 1:​20, 21, kenako mukambirane funso ili:

      • Kodi Yehova anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera m’njira zina ziti?

      Zithunzi: Zomwe Mulungu anachita pogwiritsa ntchito mzimu woyera. 1. Mapulaneti ndi zinthu zina za m’chilengedwe. 2. Munthu akulemba mawu ouziridwa ndi Mulungu pampukutu.
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena