-
‘Mulungu Anakondwera Naye’Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2017 | Na. 1
-
-
INOKI ‘ANALOSERA ZA IWO’
Chifukwa choti anthu ambiri ankachita zoipa n’kutheka kuti Inoki ankaona kuti analibe anzake otumikira nawo Mulungu. Komatu Yehova Mulungu ankamuona kuti ndi wofunika. Tsiku lina Yehova analankhula ndi mtumiki wake wokhulupirikayu n’kumupatsa uthenga woti akauze anthu ena. Choncho Inoki anakhala mneneri wa Yehova ndipo ndi mneneri woyamba yemwe uthenga wake ukupezeka m’Baibulo. Izi zili choncho chifukwa patapita zaka zambiri, Yuda, yemwe anali m’bale wake wa Yesu, analemba uthengawo m’buku lake la m’Baibulo.a
Uthenga wa Inoki unali wakuti: “Taonani! Yehova anabwera ndi miyandamiyanda ya oyera ake, kudzapereka chiweruzo kwa onse, ndi kudzagamula kuti onse osaopa Mulungu apezeka ndi mlandu chifukwa cha ntchito zawo zonyoza Mulungu zimene anazichita mosaopa Mulungu, komanso chifukwa cha zinthu zonse zonyoza koopsa zimene ochimwa osaopa Mulungu anamunenera.” (Yuda 14, 15) Mukhoza kuona kuti Inoki analankhula uthenga wakewu ngati kuti zinthuzo zinali zitachitika kale. Umu ndi mmene maulosi ambiri analembedwera. Aneneriwo ankafotokoza chonchi chifukwa choti sankakayikira ngakhale pang’ono kuti zimene akunenazo zidzachitikadi.—Yesaya 46:10.
Inoki ankauza anthu uthenga wa Mulungu molimba mtima ngakhale kuti ankadana naye
Kodi mukuganiza kuti Inoki ankamva bwanji pamene ankauza anthu ena za uthengawu? Uthengawu unali wamphamvu kwambiri chifukwa anagwiritsa ntchito mawu akuti “osaopa Mulungu” kangapo podzudzula anthuwo komanso pofotokoza zimene ankachita. Uthengawu unasonyeza kuti kungoyambira nthawi imene Adamu ndi Hava anatulutsidwa mu Edeni, zinthu zinali zikungoipiraipirabe. Unachenjezanso anthu kuti Yehova adzabwera ndi angelo ake ambirimbiri kuti adzawononge anthu oipa onse. Ngakhale kuti Inoki anali yekha, anauza anthu uthengawu molimba mtima. Pa nthawiyi n’kuti Lameki ali mwana ndipo ngati anaona agogo ake akuchita zinthu molimba mtima chonchi, ayenera kuti anadabwa kwambiri.
Tikaganizira zimene Inoki anachita tingachite bwino kudzifunsa ngati timaona zinthu za m’dzikoli mmene Mulungu amazionera. Uthenga umene Inoki anapereka ukukhudzanso anthu amasiku ano. Mogwirizana ndi zimene Inoki anachenjeza, Yehova anabweretsa Chigumula chachikulu chimene chinawononga anthu oipa a m’nthawi ya Nowa. Zimene zinachitikazi zikusonyeza zimene zidzachitikenso m’tsogolo. (Mateyu 24:38, 39; 2 Petulo 2:4-6) Mofanana ndi nthawi ya Nowa, Mulungu limodzi ndi angelo ake ambirimbiri ndi okonzeka kuperekanso chiweruzo kwa anthu onse oipa. Choncho aliyense wa ife ayenera kumvera chenjezo la Inoki komanso kuthandiza nawo pochenjeza anthu ena. N’kutheka kuti achibale komanso anzathu sangagwirizane ndi zimene tikuchita ndipo tikhoza kumva ngati tili tokhatokha. Koma Yehova sanasiye Inoki ndipo sangasiyenso atumiki ake okhulupirika masiku ano.
-
-
‘Mulungu Anakondwera Naye’Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2017 | Na. 1
-
-
a Akatswiri ena a Baibulo amanena kuti uthenga wa Inoki umene Yuda analemba anautenga m’buku lakuti Buku la Inoki. Koma Yuda sakanatenga uthengawu m’bukuli chifukwa nkhani zambiri za m’bukuli ndi zongopeka komanso si zoona kuti linalembedwa ndi Inoki ndipo silikudziwika kumene linachokera. N’zoona kuti bukuli lili ndi uthenga wa Inoki koma mwina olemba ake anautenga m’zolemba zina zakale kapena anachita kuuzidwa ndi anthu ena. N’kutheka kuti uthenga wa Inoki umene Yuda analembawu anautenganso kumene olemba Buku la Inoki anatenga uthengawu. Apo ayi, mwina anamva kwa Yesu, yemwe anali kumwamba pamene Inoki anali ndi moyo.
-