Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mfumu Yankhondo Idzapambana pa Aramagedo
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 22. Kodi Yohane anati chiyani pofotokoza mwachidule zimene zidzachitike pa nkhondo yomalizayi?

      22 Kenako Yohane akufotokoza mwachidule zimene zidzachitike pa nkhondo yomalizayi. Iye akuti: “Ndipo ndinaona chilombo, mafumu a dziko lapansi, ndi magulu awo ankhondo atasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi wokwera pahatchi uja ndi gulu lake lankhondo. Koma chilombocho chinagwidwa limodzi ndi mneneri wonyenga uja, amene anachita zizindikiro pamaso pa chilombocho. Zizindikiro zimenezi anasocheretsa nazo olandira chizindikiro cha chilombo ndi olambira chifaniziro chake. Adakali amoyo, onse awiri anaponyedwa m’nyanja ya moto yoyaka ndi sulufule. Koma ena onse anaphedwa ndi lupanga lalitali la wokwera pahatchi, limene linatuluka m’kamwa mwake lija. Ndipo mbalame zonse zinakhuta minofu yawo.”—Chivumbulutso 19:19-21.

  • Mfumu Yankhondo Idzapambana pa Aramagedo
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 24. (a) Kodi chilombo ndi mneneri wonyenga adzalandira chiweruzo chotani, ndipo mfundo yakuti iwo adakali “amoyo” ikutanthauza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti ‘nyanja ya moto’ ndi yophiphiritsa?

      24 Chilombo cha mitu 7 ndi nyanga 10 chotuluka m’nyanja, chimene chikuimira maulamuliro andale amene Satana wakhazikitsa, chidzawonongedwa pamodzi ndi mneneri wonyenga, amene akuimira ulamuliro wa 7 wamphamvu kwambiri padziko lonse. (Chivumbulutso 13:1, 11-13; 16:13) Chilombochi komanso mneneri wonyengayu adzaponyedwa “m’nyanja ya moto” adakali “amoyo,” kapena kuti akuchitabe zinthu mogwirizana, potsutsana ndi anthu a Mulungu padziko lapansi. Kodi nyanja ya motoyi ndi nyanja yeniyeni? Ayi ndi yophiphiritsa, chifukwa chilombocho komanso mneneri wonyengayu n’zophiphiritsanso. Choncho nyanja ya moto ikuimira chiwonongeko chotheratu chomwenso ndi chomaliza, kutanthauza kuti owonongedwawo sadzakhalaponso mpaka kalekale. N’chifukwa chake pamapeto pake imfa ndi Manda, komanso Mdyerekezi weniweniyo adzaponyedwe m’nyanja imeneyi. (Chivumbulutso 20:10, 14) Choncho nyanja imeneyi si ng’anjo ya moto, kumene anthu ena amaganiza kuti anthu oipa amakazunzika kwamuyaya. Zili choncho chifukwa Yehova amanyansidwa ndi chiphunzitso chakuti anthu oipa amakazunzika kwamuyaya m’ng’anjo ya moto.—Yeremiya 19:5; 32:35; 1 Yohane 4:8, 16.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena