-
Mafunso Ochokera kwa OwerengaNsanja ya Olonda—2015 | May 15
-
-
Nanga kodi “Gogi ndi Magogi” otchulidwa pa Chivumbulutso 20:8 ndi ndani? Zaka 1,000 zikadzatha, anthu amene adzasiye kutumikira Yehova adzakhalanso ndi mtima wachiwembu ngati wa “Gogi wa kudziko la Magogi.” Ndiye paja tanena kale kuti Gogi wa kudziko la Magogi ndi mitundu ya anthu imene idzaukire anthu a Mulungu chakumapeto kwa chisautso chachikulu. Ndiyeno zimene zidzachitikire “Gogi wa kudziko la Magogi” zidzafanana ndi zimene zidzachitikire “Gogi ndi Magogi.” Onse adzawonongedwa ndipo sadzakhalakonso. (Chiv. 19:20, 21; 20:9) Malinga ndi zimene tanenazi, “Gogi ndi Magogi” akuimira anthu onse amene adzasiye kutumikira Mulungu pambuyo pa zaka 1,000.
-