-
Khalani Oŵerenga Achimwemwe a Buku la ChivumbulutsoNsanja ya Olonda—1999 | December 1
-
-
16. N’chifukwa chiyani machaputala omalizira a Chivumbulutso makamaka alili opatsa chimwemwe?
16 Oŵerenga achimwemwe a buku la Chivumbulutso amasangalala kwabasi pamene aŵerenga machaputala omalizira amene amafotokoza chiyembekezo chathu chaulemerero cha kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, zimene zikutanthauza boma lakumwamba lolungama la Ufumu lolamulira anthu atsopano, oyeretsedwa, zonse zodzetsa chitamando kwa “Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 21:22) Pamene masomphenya osangalatsa osiyanasiyanawo anali kutha, mngelo wamithengayo anati kwa Yohane: “Mawu aŵa ali okhulupirika ndi oona; ndipo Ambuye, Mulungu wa mizimu ya aneneri, anatuma mngelo wake kukaonetsera akapolo ake zimene ziyenera kuchitika msanga. Ndipo taonani, ndidza msanga. Wodala iye amene asunga mawu a chinenero cha buku ili.”—Chivumbulutso 22:6, 7.
-
-
Khalani Oŵerenga Achimwemwe a Buku la ChivumbulutsoNsanja ya Olonda—1999 | December 1
-
-
18, 19. (a) N’chifukwa chiyani Yesu ayenera kudzabe, ndipo n’chiyembekezo chotani chomwe Yohane anasonyeza chomwe ifenso tili nacho? (b) Kodi Yehova ‘azadzabe’ ndi cholinga chotani?
18 Nthaŵi zingapo, Yesu akulengeza m’buku la Chivumbulutso kuti: ‘Ndidza msanga.’ (Chivumbulutso 2:16; 3:11; 22:7, 20a) Ayenera kudzabe kudzaweruza Babulo Wamkulu, dongosolo landale la Satana, ndi anthu onse amene akukana kugonjera uchifumu wa Yehova, umene tsopano ukuchitidwa mwa Ufumu Waumesiya. Tikugwirizana ndi mtumwi Yohane ponena kuti: “Amen; idzani, Ambuye Yesu.”—Chivumbulutso 22:20b.
-