Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesu Anabwera ndi Uthenga Wolimbikitsa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 1. Kodi uthenga umene Yohane analemba ukupita kwa ndani, ndipo masiku ano ndani amene ayenera kuchita chidwi ndi uthengawu?

      ALIYENSE amene amasonkhana ndi mpingo wa anthu a Mulungu masiku ano ayenera kuchita chidwi ndi uthenga umene uli m’mavesi otsatirawa. M’mavesi amenewa muli uthenga wosiyanasiyana ndipo ndi wofunika kwambiri panopa chifukwa “nthawi yoikidwiratu ili pafupi.” (Chivumbulutso 1:3) Tikatsatira mfundo za uthenga umenewu tidzapeza madalitso osatha. Uthengawu ukuyamba ndi mawu akuti: “Ine Yohane, ndikulembera mipingo 7 ya m’chigawo cha Asia. Kukoma mtima kwakukulu, ndi mtendere zikhale nanu kuchokera kwa ‘Iye amene alipo, amene analipo, ndi amene akubwera,’ ndiponso kuchokera kwa mizimu 7 yokhala pamaso pa mpando wake wachifumu. Komanso, kuchokera kwa Yesu Khristu.”—Chivumbulutso 1:4, 5a.

  • Yesu Anabwera ndi Uthenga Wolimbikitsa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 3. (a) Kodi mawu oyamba a Yohane akusonyeza kuti “kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere” zimachokera kuti? (b) Kodi ndi mawu ati a mtumwi Paulo amene akufanana ndi mawu oyamba a Yohane?

      3 “Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere” ndi makhalidwe osangalatsa kwambiri, makamaka tikadziwa kumene makhalidwewa akuchokera. Makhalidwewa amachokera kwa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa yemwenso ndi “Mfumu yamuyaya,” amene wakhalapo “kuyambira kalekale mpaka kalekale.” (1 Timoteyo 1:17; Salimo 90:2) Mtumwi Yohane anatchulanso “mizimu 7.” Zimenezi zikutanthauza kuti mzimu woyera, kapena kuti mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, ikugwira ntchito mokwanira. Mzimu woyerawu umachita zimenezi ukamathandiza anthu kumvetsa ulosi ndiponso kuthandiza anthu onse amene akutsatira zimene ulosiwo ukunena kuti apeze madalitso. Uthenga wa Yohane ukusonyezanso kuti “Yesu Khristu” ali ndi udindo wofunika kwambiri. Ponena za iye, Yohane analemba kuti: “Anali wodzaza ndi kukoma mtima kwakukulu ndi choonadi.” (Yohane 1:14) Choncho, m’mawu ake oyambirira, Yohane analemba mfundo zofanana ndi zimene mtumwi Paulo anatchula pomaliza kalata yake yachiwiri yopita kumpingo wa ku Korinto. Iye anati: “Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu, chikondi cha Mulungu, komanso mzimu woyera umene mukupindula nawo limodzi, zikhale nanu nonsenu.” (2 Akorinto 13:14) Tiyeni tiyesetse kuti mawu amenewa azigwiranso ntchito kwa aliyense wa ife amene amakonda choonadi masiku ano.—Salimo 119:97.

      “Mboni Yokhulupirika”

      4. Pofotokoza za Yesu Khristu, kodi Yohane anagwiritsa ntchito mayina ati, ndipo n’chifukwa chiyani mayina amenewa ali oyenerera?

      4 Yesu ndi waulemerero kwambiri m’chilengedwe chonse ndipo amaposedwa ndi Yehova yekha basi. Yohane anazindikira zimenezo ndipo anafotokoza za Yesu kuti ndi “‘Mboni Yokhulupirika,’ ‘Woyamba kubadwa kuchokera kwa akufa,’ ndiponso ‘Wolamulira wa mafumu a dziko lapansi.’” (Chivumbulutso 1:5b) Mofanana ndi mwezi kumwamba, iye wakhazikika monga Mboni yaikulu kwambiri yotsimikizira kuti Yehova ndiye Mulungu. (Salimo 89:37) Atatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika mpaka imfa yake yansembe, iye anali munthu woyamba kuukitsidwa n’kupatsidwa moyo wauzimu umene sungafe. (Akolose 1:18) Tsopano Yesu ali ndi Yehova kumwamba ndipo wakwezedwa kuposa mafumu onse a padziko lapansi. Wapatsidwanso “ulamuliro wonse . . . kumwamba ndi padziko lapansi.” (Mateyu 28:18; Salimo 89:27; 1 Timoteyo 6:15) M’chaka cha 1914, iye anaikidwa kukhala Mfumu yolamulira pakati pa mitundu ya anthu padziko lapansi.—Salimo 2:6-9.

      5. (a) Kodi Yohane anapitiriza bwanji kuyamikira Ambuye Yesu Khristu? (b) Ndani amene amapindula ndi mphatso ya moyo wangwiro wa Yesu, ndipo kodi Akhristu odzozedwa ali ndi mwayi wapadera wotani?

      5 Yohane anapitiriza kuyamikira Ambuye Yesu Khristu ndi mawu omutamanda akuti: “Kwa iye amene amatikonda, amenenso anatimasula ku machimo athu ndi magazi ake enieniwo, n’kutipanga kukhala mafumu ndi ansembe kwa Mulungu wake ndi Atate wake, kwa iyeyo kukhale ulemerero ndi mphamvu kwamuyaya. Ame.” (Chivumbulutso 1:5c, 6) Yesu anapereka moyo wake wangwiro n’cholinga choti anthu amene amam’khulupirira adzakhale ndi moyo wangwiro. Inunso amene mukuwerenga bukuli mukhoza kudzakhala ndi moyo wangwiro umenewo. (Yohane 3:16) Koma imfa yansembe ya Yesu inatsegula njira yoti Akhristu odzozedwa, monga Yohane, alandire madalitso apadera. Mulungu amawaona Akhristu amenewa kuti ndi olungama chifukwa cha nsembe ya Yesu ya dipo. Mofanana ndi Yesu, anthu a m’kagulu ka nkhosa sakhala ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo padziko lapansi, ndipo anabadwanso mwa mzimu wa Mulungu. Iwo akuyembekezera kudzaukitsidwa ndi kudzakhala mafumu ndi ansembe pamodzi ndi Yesu Khristu mu Ufumu wake. (Luka 12:32; Aroma 8:18; 1 Petulo 2:5; Chivumbulutso 20:6) Umenewutu ndi mwayi waukulu kwambiri, ndipo m’pake kuti Yohane analankhula mosangalala kuti ulemerero komanso mphamvu ndi za Yesu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena