Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Muzinyansidwa ndi “Zinthu Zozama za Satana”
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 8. (a) Kodi Yesu anapereka uthenga wotani kwa “Yezebeli” wa ku Tiyatira? (b) Kodi azimayi ena achita zinthu zotani zosokoneza ena mumpingo masiku ano?

      8 Yesu anapitiriza kuuza akulu a mpingo wa ku Tiyatira kuti: “Ndamupatsa nthawi kuti alape, koma sakufuna kulapa dama lake. Taona! Ndatsala pang’ono kumudwalitsa kwambiri, ndipo ochita naye chigololo ndiwaponya m’masautso aakulu, kupatulapo ngati atalapa ntchito zawo zofanana ndi za mayiyo.” (Chivumbulutso 2:21, 22) Mofanana ndi Yezebeli, amene zikuoneka kuti ankalamulira mwamuna wake Ahabu, ndipo kenako anachitira mwano Yehu, yemwe anatumidwa ndi Mulungu kuti adzamuphe, azimayi oipawa mwina ankanyengerera amuna awo komanso akulu kuti azichita zinthu zoipa. Zikuoneka kuti akulu mumpingo wa Tiyatira ankalekerera khalidwe losokoneza langati la Yezebeli limeneli. Yesu anawachenjeza mwamphamvu Akhristu amenewa, ndipo masiku ano chenjezoli likupitanso ku mpingo wa padziko lonse wa anthu a Yehova. Masiku ano, azimayi ena osafuna kuuzidwa zochita ofanana ndi Yezebeli, anyengererapo amuna awo kuti akhale ampatuko ndipo afika ngakhale potengera ku khoti atumiki a Yehova okhulupirika.—Yerekezerani ndi Yuda 5-8.

  • Muzinyansidwa ndi “Zinthu Zozama za Satana”
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 10. (a) N’chifukwa chiyani Yezebeli ndi ana ake anayenera kupatsidwa chilango? (b) Kodi ndi zinthu zoopsa ziti zimene zimachitikira anthu amene ndi ana a Yezebeli, ndipo anthu amenewo ayenera kuchita chiyani?

      10 Popitiriza kufotokoza za “mayi uja Yezebeli,” Yesu anati: “Ana ake ndidzawapha ndi mliri wakupha, moti mipingo yonse idzadziwa kuti ineyo ndiye amene ndimafufuza impso ndi mitima, ndipo ndidzabwezera mmodzi ndi mmodzi wa inu malinga ndi ntchito zake.” (Chivumbulutso 2:23) Yesu anapatsa Yezebeli ndi ana ake nthawi yoti alape, koma iwo anapitirizabe khalidwe lawo lachiwerewere. Choncho anayenera kulangidwa. Pamenepa pali chenjezo lamphamvu kwa Akhristu masiku ano. Anthu amene amatsanzira Yezebeli, kaya ndi amuna kapena akazi, akudwala kwambiri mwauzimu. Iwo amakhala ana ake pophwanya mfundo za m’Baibulo zokhudza umutu ndi makhalidwe abwino, kapena posafuna kumva za ena n’kumanyalanyaza dongosolo limene gulu la Mulungu limachitira zinthu. Ngati munthu woteroyo ataitana akulu a mumpingo kuti amupempherere, “pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamulimbitsa.” Komabe iye ayenera kudzichepetsa n’kumachita zinthu zogwirizana ndi pempherolo. Ndipo aliyense asaganize kuti angapusitse Mulungu kapena Khristu poyesa kubisa khalidwe lachiwerewere kapena pochita utumiki mwakhama kwambiri kuti aphimbe tchimo.—Yakobo 5:14, 15.

  • Muzinyansidwa ndi “Zinthu Zozama za Satana”
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 13. Kodi chidzachitike n’chiyani kwa anthu amene ayamba kuchita zinthu zoipa chifukwa chotengera akazi osokoneza mumpingo?

      13 Mwana wa Mulungu, yemwe ndi Mthenga wa Yehova komanso Woweruza, anachita zinthu moyenera podzudzula Yezebeli wamakono n’kumutaya chifukwa chakuti akudwala, popeza matenda ake auzimu ndi osachiritsika. (Malaki 3:1, 5) Anthu amene ayamba kuchita zinthu zoipa chifukwa chotengera akazi osokoneza mumpingo amakumananso ndi masautso aakulu. Masautsowa akutanthauza chisoni chimene anthuwa amamva akachotsedwa mumpingo, n’kutayidwa kunja kwa mpingo wachikhristu ngati kuti afa. Anthu amenewa akapanda kulapa, kutembenuka, n’kubwereranso mumpingo, adzafa imfa yeniyeni ndi “mliri wakupha,” pa chisautso chachikulu kapena chisautsochi chisanafike. Komabe, Mulungu akhoza kuwalandiranso ngati atalapa moona mtima n’kusiya machimo awo onse.—Mateyu 24:21, 22; 2 Akorinto 7:10.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena