Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Dzina Lanu Lili M’buku la Moyo?
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 3. (a) Kodi “mngelo wa mpingo wa ku Sade” anayenera kukumbukira chiyani pa mfundo yakuti Yesu ali ndi “nyenyezi 7”? (b) Kodi Yesu anapereka uphungu wamphamvu wotani ku mpingo wa ku Sade?

      3 Yesu anakumbutsanso “mngelo wa mpingo wa ku Sade” kuti Yesuyo ali ndi “nyenyezi 7.” Iye ananyamula akulu a mpingowu m’dzanja lake lamanja, kusonyeza kuti ali ndi udindo wotsogolera akuluwo akamagwira ntchito yawo ya ubusa. Iwo anafunika kuyesetsa ndi mtima wonse kuti ‘adziwe bwino maonekedwe a ziweto zawo.’ (Miyambo 27:23) Motero, iwo anayenera kumvetsera mwatcheru mawu otsatira amene Yesu anawauza, akuti: “Khala maso, ndipo limbikitsa otsala amene atsala pang’ono kufa, chifukwa ndapeza kuti ntchito zako sizinachitidwe mokwanira pamaso pa Mulungu wanga. Choncho, pitiriza kukumbukira zimene unalandira ndi zimene unamva. Pitiriza kuzitsatira, ndipo ulape. Ndithudi, ukapanda kudzuka, ndidzabwera ngati mbala, ndipo sudzadziwa ngakhale pang’ono ola limene ndidzafike kwa iwe.”—Chivumbulutso 3:2, 3.

      4. Kodi mawu a Petulo akanathandiza bwanji mpingo wa ku Sade kuti ‘ulimbikitse otsala’?

      4 Akulu a mpingo wa ku Sade anafunika kukumbukira chimwemwe chimene anali nacho poyamba atangophunzira kumene choonadi ndiponso madalitso amene analandira. Koma tsopano iwo anali akufa pa ntchito zauzimu. Nyale ya mpingo wawo inali itatsala pang’ono kuzima chifukwa iwo sankagwira ntchito zosonyeza chikhulupiriro. Zaka zingapo m’mbuyomu, mtumwi Petulo analemba makalata opita kumipingo ya ku Asia (mwina kuphatikizapo wa ku Sade). Iye analemba makalatawo pofuna kulimbikitsa mipingoyo kuti iziyamikira uthenga wabwino umene Akhristu anaulandira. Ndiponso uthengawo unalengezedwa “mwa mzimu woyera wotumizidwa kuchokera kumwamba,” monga mmene zinalili m’masomphenya a Yohane. M’masomphenyawo, mizimu 7 inkaimira “mzimu woyera wotumizidwa kuchokera kumwamba” umenewu. Kenako Petulo anakumbutsanso Akhristu a ku Asia kuti iwo anali ‘fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera, anthu odzakhala chuma chapadera, kuti alengeze makhalidwe abwino kwambiri a amene anawaitana kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.’ (1 Petulo 1:12, 25; 2:9) Kuganizira mozama mfundo za choonadi zimenezi kukanathandiza mpingo wa ku Sade kuti ulape ndiponso kuti ‘ulimbikitse otsala.’—Yerekezerani ndi 2 Petulo 3:9.

      5. (a) Kodi zinthu zinali bwanji ndi Akhristu a mpingo wa ku Sade pa nkhani yoyamikira choonadi? (b) Kodi chikanachitika n’chiyani Akhristu a mpingo wa ku Sade akanapanda kumvera malangizo a Yesu?

      5 Pa nthawiyi, kuyamikira ndi kukonda kwawo choonadi kunali kutachepa ngati moto umene watsala pang’ono kuzima. Ndi anthu ochepa chabe mumpingowo omwe anali ngati nkhuni zoyaka. Yesu anawalimbikitsa kuti akolezerenso moto umenewu n’cholinga choti mpingowo ukhalenso ndi moyo mwauzimu. Iye anawauzanso kuti alape machimo awo amene ankawachita chifukwa chonyalanyaza malangizo a Mulungu. (Yerekezerani ndi 2 Timoteyo 1:6, 7.) Akhristu a mpingo wa ku Sade anayenera kuchita zimenezi kuti Yesu pobwera mwadzidzidzi “ngati mbala” kudzapereka chiweruzo, adzawapeze atakonzeka.—Mateyu 24:43, 44.

  • Kodi Dzina Lanu Lili M’buku la Moyo?
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 7. N’chifukwa chiyani Akhristu masiku ano ayenera kukhala maso?

      7 Sikuti Akhristu ankangofunika kukhala maso kumayambiriro kwa tsiku la Ambuye kokha basi. Yesu anapereka chenjezo lamphamvu mu ulosi wake waukulu wonena za “chizindikiro chosonyeza kuti zinthu zonsezi zili m’nthawi yake yamapeto.” Iye anati: “Kunena za tsikulo kapena ola lake, palibe amene akudziwa . . . Khalani maso, khalani tcheru, pakuti simukudziwa pamene nthawi yoikidwiratu idzafika. Koma zimene ndikuuza inuzi ndikuuza onse, Khalani maso.” (Maliko 13:4, 32, 33, 37) Choncho mpaka pano, aliyense wa ife, kaya ndi wodzozedwa kapena wa khamu lalikulu, ayenera kukhala maso ndiponso ayenera kuyesetsa kuti asagone mwauzimu. Tiyeni tiyesetse kuti tsiku la Yehova likadzabwera “ngati mbala usiku,” tidzapezeke tili maso kuti tidzalandire madalitso.—1 Atesalonika 5:2, 3; Luka 21:34-36; Chivumbulutso 7:9.

      8. Kodi Akhristu odzozedwa masiku ano amalimbikitsa bwanji anthu a Mulungu kuti asafe mwauzimu?

      8 Akhristu odzozedwa masiku ano ali maso ndipo akuthandiza anthu a Mulungu kuti asafe mwauzimu. Kuti zimenezi zitheke, iwo amakonza misonkhano yosiyanasiyana ikuluikulu padziko lonse chaka chilichonse. M’chaka china posachedwapa, chiwerengero cha anthu amene anafika pa misonkhano ya chigawo, yomwe inalipo 2,981, chinali 10,953,744, ndipo anthu 122,701 anabatizidwa. Kwa zaka zoposa 100, Akhristu odzozedwa akhala akugwiritsa ntchito magazini a Nsanja ya Olonda polengeza dzina ndi cholinga cha Yehova. Komanso pofuna kulimbikitsa Akhristu a Mboni za Yehova amene anazunzidwa kwambiri pa nthawi ya nkhondo ziwiri zikuluzikulu za padziko lonse, m’magazini a Nsanja ya Olonda munasindikizidwa nkhani zosiyanasiyana zolimbikitsa. Zina mwa nkhanizi zinali zakuti “Anthu Olimba Mtima Amakhala Odala” (1919), “Tigwire Ntchito Mwakhama” (1925), ndiponso “Kuzunzidwa Sikunalepheretse Ntchito Yolalikira” (1942).

      9. (a) Kodi Akhristu onse ayenera kudzifunsa mafunso otani? (b) Kodi magazini a Nsanja ya Olonda analimbikitsa bwanji Akhristu?

      9 Masiku ano, m’pofunika kwambiri kuti Akhristu m’mipingo yonse apitirize kudzifufuza ngati mmene Akhristu a mpingo wa ku Sade anayenera kuchitira. Aliyense ayenera kudzifunsa kuti: Kodi ‘ntchito zanga ndikuzichita mokwanira pamaso pa Mulungu wanga’? Kodi ineyo ndimapewa kuweruza ena, ndiponso ndimayesetsa kukhala ndi mtima wololera kuvutikira ena komanso kutumikira Mulungu ndi mtima wonse? M’magazini a Nsanja ya Olonda munatuluka nkhani zosiyanasiyana zothandiza munthu kuganizira mafunso amenewa. Mwachitsanzo, panali nkhani yakuti “Kodi Mukutsatira Khristu ndi Mtima Wonse?” komanso yakuti, “Musasiye ‘Chikondi Chimene Munali Nacho Poyamba.’”a Popeza tili ndi nkhani zolimbikitsa za m’Malemba zimenezi, tiyeni tizifufuza zolinga za mumtima mwathu ndipo tizipemphera kuti Yehova atithandize kukhala ndi mtima wosagawanika komanso kuti tiziyenda modzichepetsa pamaso pake.—Salimo 26:1-3; 139:23, 24.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena