Mutu 11
Kodi Dzina Lanu Lili M’buku la Moyo?
SADE
1. Kodi moyo wauzimu wa mpingo wa ku Sade unali wotani, ndipo Yesu anayamba bwanji uthenga wake wopita kumpingowu?
MPINGO wotsatira umene unalandira uthenga wa Yesu amene anali mu ulemerero wake, unali wa ku Sade. Mpingowu unali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 50 kum’mwera kwa mzinda wamakono wa Akhisar (Tiyatira). M’zaka za m’ma 500 B.C.E., mzinda wotchuka wa Sade unali likulu la ufumu wa Lidiya ndipo Mfumu Kolosase, yomwe inali yolemera kwambiri, inkakhala mumzinda umenewu. Koma pofika m’nthawi ya Yohane, mzindawu unali pa mavuto aakulu, ndipo sunalinso wotchuka ngati mmene unalili mu ulamuliro wa Kolosase. Nawonso mpingo wachikhristu umene unali kumeneko unali utasauka mwauzimu. Ndipo kwa nthawi yoyamba, Yesu sanayambe ndi mawu oyamikira popereka uthenga wake. Koma iye ananena kuti: “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Sade, lemba kuti: Izi ndi zimene akunena iye amene ali ndi mizimu 7 ya Mulungu, ndi nyenyezi 7. ‘Ndikudziwa ntchito zako, kuti uli ndi dzina lakuti uli moyo, pamene ndiwe wakufa.’”—Chivumbulutso 3:1.
2. (a) Kodi mfundo yakuti Yesu ali “ndi mizimu 7” inatanthauza chiyani kwa Akhristu a ku Sade? (b) Kodi mpingo wa ku Sade unali ndi mbiri yotani, koma zoona zake zinali zotani?
2 N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti iye “ali ndi mizimu 7”? Chifukwa chakuti mizimu imeneyi ikuimira mzimu woyera wa Yehova umene ukugwira ntchito mokwanira. Kenako, Yohane anatchula mizimuyi kuti “ndi maso 7.” Zimenezi zikusonyeza kuti mzimu woyera wa Mulungu unapatsa Yesu mphamvu zoti azitha kuona zinthu zobisika. (Chivumbulutso 5:6) Choncho, iye amatha kuulula zinthu zobisika ndiponso kuthana ndi vuto lililonse. (Mateyu 10:26; 1 Akorinto 4:5) Mpingo wa ku Sade unali ndi mbiri yakuti unali wolimba komanso wakhama potumikira Mulungu. Koma Yesu anaona kuti mpingo umenewu unali wakufa mwauzimu. Zikuoneka kuti Akhristu ambiri mumpingowu analibenso chidwi pa zinthu zauzimu ndipo anakhala ngati mmene analili asanakhale Akhristu.—Yerekezerani ndi Aefeso 2:1-3; Aheberi 5:11-14.
3. (a) Kodi “mngelo wa mpingo wa ku Sade” anayenera kukumbukira chiyani pa mfundo yakuti Yesu ali ndi “nyenyezi 7”? (b) Kodi Yesu anapereka uphungu wamphamvu wotani ku mpingo wa ku Sade?
3 Yesu anakumbutsanso “mngelo wa mpingo wa ku Sade” kuti Yesuyo ali ndi “nyenyezi 7.” Iye ananyamula akulu a mpingowu m’dzanja lake lamanja, kusonyeza kuti ali ndi udindo wotsogolera akuluwo akamagwira ntchito yawo ya ubusa. Iwo anafunika kuyesetsa ndi mtima wonse kuti ‘adziwe bwino maonekedwe a ziweto zawo.’ (Miyambo 27:23) Motero, iwo anayenera kumvetsera mwatcheru mawu otsatira amene Yesu anawauza, akuti: “Khala maso, ndipo limbikitsa otsala amene atsala pang’ono kufa, chifukwa ndapeza kuti ntchito zako sizinachitidwe mokwanira pamaso pa Mulungu wanga. Choncho, pitiriza kukumbukira zimene unalandira ndi zimene unamva. Pitiriza kuzitsatira, ndipo ulape. Ndithudi, ukapanda kudzuka, ndidzabwera ngati mbala, ndipo sudzadziwa ngakhale pang’ono ola limene ndidzafike kwa iwe.”—Chivumbulutso 3:2, 3.
4. Kodi mawu a Petulo akanathandiza bwanji mpingo wa ku Sade kuti ‘ulimbikitse otsala’?
4 Akulu a mpingo wa ku Sade anafunika kukumbukira chimwemwe chimene anali nacho poyamba atangophunzira kumene choonadi ndiponso madalitso amene analandira. Koma tsopano iwo anali akufa pa ntchito zauzimu. Nyale ya mpingo wawo inali itatsala pang’ono kuzima chifukwa iwo sankagwira ntchito zosonyeza chikhulupiriro. Zaka zingapo m’mbuyomu, mtumwi Petulo analemba makalata opita kumipingo ya ku Asia (mwina kuphatikizapo wa ku Sade). Iye analemba makalatawo pofuna kulimbikitsa mipingoyo kuti iziyamikira uthenga wabwino umene Akhristu anaulandira. Ndiponso uthengawo unalengezedwa “mwa mzimu woyera wotumizidwa kuchokera kumwamba,” monga mmene zinalili m’masomphenya a Yohane. M’masomphenyawo, mizimu 7 inkaimira “mzimu woyera wotumizidwa kuchokera kumwamba” umenewu. Kenako Petulo anakumbutsanso Akhristu a ku Asia kuti iwo anali ‘fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera, anthu odzakhala chuma chapadera, kuti alengeze makhalidwe abwino kwambiri a amene anawaitana kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.’ (1 Petulo 1:12, 25; 2:9) Kuganizira mozama mfundo za choonadi zimenezi kukanathandiza mpingo wa ku Sade kuti ulape ndiponso kuti ‘ulimbikitse otsala.’—Yerekezerani ndi 2 Petulo 3:9.
5. (a) Kodi zinthu zinali bwanji ndi Akhristu a mpingo wa ku Sade pa nkhani yoyamikira choonadi? (b) Kodi chikanachitika n’chiyani Akhristu a mpingo wa ku Sade akanapanda kumvera malangizo a Yesu?
5 Pa nthawiyi, kuyamikira ndi kukonda kwawo choonadi kunali kutachepa ngati moto umene watsala pang’ono kuzima. Ndi anthu ochepa chabe mumpingowo omwe anali ngati nkhuni zoyaka. Yesu anawalimbikitsa kuti akolezerenso moto umenewu n’cholinga choti mpingowo ukhalenso ndi moyo mwauzimu. Iye anawauzanso kuti alape machimo awo amene ankawachita chifukwa chonyalanyaza malangizo a Mulungu. (Yerekezerani ndi 2 Timoteyo 1:6, 7.) Akhristu a mpingo wa ku Sade anayenera kuchita zimenezi kuti Yesu pobwera mwadzidzidzi “ngati mbala” kudzapereka chiweruzo, adzawapeze atakonzeka.—Mateyu 24:43, 44.
Adzabwera “Ngati Mbala”
6. Kodi Yesu anabwera bwanji “ngati mbala” mu 1918, ndipo anapeza zinthu zili bwanji pakati pa anthu amene ankati ndi otsatira ake?
6 Chenjezo limene Yesu anapereka, lakuti adzabwera “ngati mbala” likufika m’nthawi yathu ino. Chenjezoli linagwira ntchito mwapadera kwa Akhristu amene anakhala ndi moyo mpaka kufika m’tsiku la Ambuye. Patangopita nthawi yochepa kuchokera m’chaka cha 1914, ulosi wa Malaki unakwaniritsidwa. Ulosiwo ndi wakuti: “‘Mwadzidzidzi, Ambuye woona, amene anthu inu mukumufunafuna, adzabwera kukachisi Wake. Adzabwera ndi mthenga wa pangano amene mukumuyembekezera mosangalala. Iye adzabwera ndithu,’ watero Yehova wa makamu.” (Malaki 3:1; Chivumbulutso 1:10) Monga “mthenga wa pangano,” Yesu anabwera kudzayendera ndi kuweruza anthu amene ankati ndi otsatira ake. (1 Petulo 4:17) Pa nthawiyo mu 1918, Matchalitchi Achikhristu anawapeza kuti anapha nawo anthu ambiri pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse ndipo anali akufa mwauzimu. Ngakhalenso Akhristu oona, amene ankalalikira mwakhama nkhondo isanayambe, anali atayamba kuwodzera mwauzimu. Akulu ena amene ankatsogolera mpingo pa nthawiyo anatsekeredwa m’ndende, ndipo ntchito yolalikira inatsala pang’ono kuimiratu. M’chaka chotsatira, mzimu wa Yehova unathandiza Akhristuwa kuti akhale maso, koma ena anapitirizabe kuwodzera mwauzimu. Mofanana ndi anamwali opusa a m’fanizo la Yesu, Akhristu ena anali asanakonzeke mwauzimu kuti ayambirenso kutumikira Yehova. Koma n’zosangalatsa kuti panali ena ofanana ndi anamwali ochenjera, amene anamvera chenjezo la Yesu lakuti: “Chotero khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.”—Mateyu 25:1-13.
7. N’chifukwa chiyani Akhristu masiku ano ayenera kukhala maso?
7 Sikuti Akhristu ankangofunika kukhala maso kumayambiriro kwa tsiku la Ambuye kokha basi. Yesu anapereka chenjezo lamphamvu mu ulosi wake waukulu wonena za “chizindikiro chosonyeza kuti zinthu zonsezi zili m’nthawi yake yamapeto.” Iye anati: “Kunena za tsikulo kapena ola lake, palibe amene akudziwa . . . Khalani maso, khalani tcheru, pakuti simukudziwa pamene nthawi yoikidwiratu idzafika. Koma zimene ndikuuza inuzi ndikuuza onse, Khalani maso.” (Maliko 13:4, 32, 33, 37) Choncho mpaka pano, aliyense wa ife, kaya ndi wodzozedwa kapena wa khamu lalikulu, ayenera kukhala maso ndiponso ayenera kuyesetsa kuti asagone mwauzimu. Tiyeni tiyesetse kuti tsiku la Yehova likadzabwera “ngati mbala usiku,” tidzapezeke tili maso kuti tidzalandire madalitso.—1 Atesalonika 5:2, 3; Luka 21:34-36; Chivumbulutso 7:9.
8. Kodi Akhristu odzozedwa masiku ano amalimbikitsa bwanji anthu a Mulungu kuti asafe mwauzimu?
8 Akhristu odzozedwa masiku ano ali maso ndipo akuthandiza anthu a Mulungu kuti asafe mwauzimu. Kuti zimenezi zitheke, iwo amakonza misonkhano yosiyanasiyana ikuluikulu padziko lonse chaka chilichonse. M’chaka china posachedwapa, chiwerengero cha anthu amene anafika pa misonkhano ya chigawo, yomwe inalipo 2,981, chinali 10,953,744, ndipo anthu 122,701 anabatizidwa. Kwa zaka zoposa 100, Akhristu odzozedwa akhala akugwiritsa ntchito magazini a Nsanja ya Olonda polengeza dzina ndi cholinga cha Yehova. Komanso pofuna kulimbikitsa Akhristu a Mboni za Yehova amene anazunzidwa kwambiri pa nthawi ya nkhondo ziwiri zikuluzikulu za padziko lonse, m’magazini a Nsanja ya Olonda munasindikizidwa nkhani zosiyanasiyana zolimbikitsa. Zina mwa nkhanizi zinali zakuti “Anthu Olimba Mtima Amakhala Odala” (1919), “Tigwire Ntchito Mwakhama” (1925), ndiponso “Kuzunzidwa Sikunalepheretse Ntchito Yolalikira” (1942).
9. (a) Kodi Akhristu onse ayenera kudzifunsa mafunso otani? (b) Kodi magazini a Nsanja ya Olonda analimbikitsa bwanji Akhristu?
9 Masiku ano, m’pofunika kwambiri kuti Akhristu m’mipingo yonse apitirize kudzifufuza ngati mmene Akhristu a mpingo wa ku Sade anayenera kuchitira. Aliyense ayenera kudzifunsa kuti: Kodi ‘ntchito zanga ndikuzichita mokwanira pamaso pa Mulungu wanga’? Kodi ineyo ndimapewa kuweruza ena, ndiponso ndimayesetsa kukhala ndi mtima wololera kuvutikira ena komanso kutumikira Mulungu ndi mtima wonse? M’magazini a Nsanja ya Olonda munatuluka nkhani zosiyanasiyana zothandiza munthu kuganizira mafunso amenewa. Mwachitsanzo, panali nkhani yakuti “Kodi Mukutsatira Khristu ndi Mtima Wonse?” komanso yakuti, “Musasiye ‘Chikondi Chimene Munali Nacho Poyamba.’”a Popeza tili ndi nkhani zolimbikitsa za m’Malemba zimenezi, tiyeni tizifufuza zolinga za mumtima mwathu ndipo tizipemphera kuti Yehova atithandize kukhala ndi mtima wosagawanika komanso kuti tiziyenda modzichepetsa pamaso pake.—Salimo 26:1-3; 139:23, 24.
“Mayina Angapo”
10. Kodi Yesu anaona zinthu ziti zolimbikitsa mumpingo wa ku Sade, ndipo zimenezi ziyenera kutikhudza motani?
10 Mawu otsatira amene Yesu anauza mpingo wa ku Sade anali olimbikitsa kwambiri. Iye anati: “Ngakhale zili choncho, uli ndi mayina angapo mu Sade a anthu amene sanaipitse malaya awo akunja. Amenewa adzayenda ndi ine atavala malaya oyera, chifukwa ndi oyenerera. Choncho amene wapambana pa nkhondo adzavekedwa malaya akunja oyera. Ndipo sindidzafafaniza dzina lake m’buku la moyo, koma ndidzavomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake.” (Chivumbulutso 3:4, 5) Mawu amenewatu ndi osangalatsa ndipo akutilimbikitsa kuti tipitirizebe kukhala anthu okhulupirika. Ngati akulu atayamba kulekerera zinthu zoipa mumpingo, mpingo wonse ungathe kugona tulo tofa nato mwauzimu. Komabe, Akhristu ena mumpingomo angayesetse molimba mtima kuti apitirizebe kukhala oyera ndiponso osadetsedwa n’cholinga choti akhalebe ndi dzina labwino pamaso pa Yehova.—Miyambo 22:1.
11, 12. (a) Ngakhale pa nthawi imene kunali mpatuko waukulu, n’chifukwa chiyani tinganene kuti Akhristu ena anali ngati Akhristu “angapo” okhulupirika a ku Sade? (b) Kodi ndi zinthu zosangalatsa ziti zimene zinachitikira Akhristu amene anali ngati tirigu m’tsiku la Ambuye?
11 Apa n’zoonekeratu kuti “malaya akunja” amenewo akutanthauza chizindikiro chothandiza kuti munthu azidziwika kuti ndi Mkhristu wolungama. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 16:15; 19:8.) Yesu ayenera kuti anasangalala ataona kuti “mayina angapo,” kapena kuti Akhristu angapo odzozedwa a mumpingo wa ku Sade, akupitirizabe kukhala ndi chizindikiro chimenechi ngakhale kuti Akhristu ambiri mumpingowo anafooka mwauzimu. Zimenezi n’zofanana ndi zimene zinkachitika kwa zaka mahandiredi ambiri pa nthawi imene kunali mpatuko waukulu. Pa nthawiyo, anthu ambiri amene ankati ndi Akhristu analowerera kwambiri mu Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonyenga zonse pamodzi. Komabe kwa nthawi yonseyo, payenera kuti pankapezeka anthu ena ochepa amene ankayesetsa kuchita chifuniro cha Yehova ngakhale kuti panali zovuta zambiri. Anthu amenewa anali olungama ndipo anali ngati tirigu amene wabisika ndi namsongole, kutanthauza mpatuko.—Chivumbulutso 17:3-6; Mateyu 13:24-29.
12 Yesu analonjeza kuti iye adzakhala ndi Akhristu ofanana ndi tirigu amenewa “masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” Iye amawadziwa bwino komanso amadziwa mbiri yawo yabwino. (Mateyu 28:20; Mlaliki 7:1) Akhristu “angapo” okhulupirika amene anali ndi moyo pamene tsiku la Ambuye linkayamba ayenera kuti anasangalala kwambiri. Kenako iwo analekanitsidwa ndi Matchalitchi Achikhristu omwe ndi akufa mwauzimu ndipo anawasonkhanitsira mumpingo wolungama, wofanana ndi mpingo wa ku Simuna.—Mateyu 13:40-43.
13. Mofanana ndi Akhristu a ku Sade, kodi Akhristu odzozedwa amene “sanaipitse malaya awo akunja” amalandira madalitso otani?
13 Akhristu a ku Sade amene anali okhulupirika mpaka mapeto ndipo sanadetse chizindikiro chawo chachikhristu, analandira madalitso amene ankayembekezera. Ufumu wa Yesu, yemwe ndi Mesiya, utayamba mu 1914, iwo anayamba kuukitsidwa n’kupatsidwa moyo wauzimu. Komanso popeza iwo anapambana pa nkhondo, anavekedwa malaya oyera akunja monga chizindikiro choti ndi opanda uchimo komanso olungama. Iwo analandira madalitso amene adzasangalale nawo kosatha chifukwa anayenda mumsewu wopanikiza wopita ku moyo.—Mateyu 7:14; onaninso Chivumbulutso 6:9-11.
Mayina Awo Adzakhala M’buku la Moyo Kwamuyaya
14. Kodi ‘buku la moyo’ n’chiyani ndipo m’bukuli mumalembedwa mayina a ndani?
14 Kodi ‘buku la moyo’ n’chiyani ndipo ndi anthu otani amene mayina awo sadzafafanizidwa m’bukuli? Buku, kapena kuti mpukutu wa moyo, likutanthauza m’ndandanda wa atumiki a Yehova amene ali oyenerera kudzalandira mphoto ya moyo wosatha. (Malaki 3:16) Mayina a m’buku la moyo amene buku la Chivumbulutso likutchula, ndi a Akhristu odzozedwa. Koma m’buku la moyoli mulinso mayina a anthu amene ali oyenerera kudzalandira moyo wosatha padziko lapansi. Ngakhale zili choncho, mayina akhoza ‘kufafanizidwa’ m’buku la moyo limeneli. (Ekisodo 32:32, 33) Komabe, Akhristu odzozedwa amene mayina awo amakhalabe m’bukuli mpaka imfa yawo, amalandira moyo umene sungafe kumwamba. (Chivumbulutso 2:10) Mayina amenewa ndi amene Yesu amawavomereza pamaso pa Atate wake ndiponso pamaso pa angelo. Imeneyitu ndi mphoto yamtengo wapatali kwambiri.
15. Kodi anthu a m’khamu lalikulu ayenera kuchita chiyani kuti mayina awo asadzafafanizidwe m’buku la moyo?
15 Anthu a m’khamu lalikulu, amenenso mayina awo alembedwa m’buku la moyo, adzatuluka m’chisautso chachikulu ali ndi moyo. Iwo akadzakhalabe okhulupirika mu ulamuliro wonse wa Yesu wa zaka 1,000, ndiponso akadzapirira chiyeso chomaliza, adzalandira moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. (Danieli 12:1; Chivumbulutso 7:9, 14; 20:15; 21:4) Zimenezi zikadzachitika, ndiye kuti mayina awo sadzafafanizidwanso m’buku la moyo. Popeza mwadziwa uthenga umene unatumizidwa kudzera mwa mzimu woyera, simuyenera kuzengereza kuchita zimene Yesu akutipempha mobwerezabwereza kuti: “Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo.”—Chivumbulutso 3:6.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Nsanja ya Olonda ya April 15, 2010, ndiponso ya June 15, 2008.
[Chithunzi patsamba 57]
Yesetsani kuti dzina lanu likhalebe m’buku la moyo