Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yohane Anaona Yesu Ali mu Ulemerero Wake
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 5. (a) Kodi Yohane anamva mawu omulamula kuchita chiyani? (b) N’chifukwa chiyani zinali zosavuta kutumiza mpukutu m’dera limene munali “mipingo 7”?

      5 Yohane asanaone chilichonse m’masomphenya oyambawa anamva mawu amphamvu. Iye anati: “Ndinamva mawu amphamvu ngati kulira kwa lipenga. Mawuwo anali akuti: ‘Zimene uone, lemba mumpukutu ndi kuutumiza kumipingo 7 yotsatirayi: wa ku Efeso, wa ku Simuna, wa ku Pegamo, wa ku Tiyatira, wa ku Sade, wa ku Filadefiya, ndi wa ku Laodikaya.’” (Chivumbulutso 1:10b, 11) Yohane anamva mawu amphamvu ngati kulira kwa lipenga komanso osonyeza kuti akuchokera kwa munthu waulamuliro, omuuza kuti alembe mauthenga opita “kumipingo 7.” Iye anali atatsala pang’ono kulandira mauthenga osiyanasiyana ndiponso kulemba zinthu zimene aone ndi kumva. Kumbukirani kuti mipingo imene inatchulidwa m’masomphenyawa inalipodi m’nthawi ya Yohane. Mipingo yonseyi inali ku Asia Minor, kutsidya lina la nyanja, kuchokera pachilumba cha Patimo. Anthu a m’mipingoyi ankayenderana mosavuta chifukwa m’derali munali misewu yabwino kwambiri imene Aroma anamanga. Choncho zinali zosavuta kuti munthu amene watumidwa kukapereka mpukutu ayende kuchokera kumpingo wina kupita kumpingo wina. Mipingo 7 imeneyi ingafanane ndi mbali imodzi ya dera limene woyang’anira dera wa Mboni za Yehova amayendera masiku ano.

  • Yohane Anaona Yesu Ali mu Ulemerero Wake
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • [Zithunzi patsamba 23]

      Zinthu zakale zimene zinapezeka m’mizinda imene munali mipingo 7 imeneyi zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena. M’mizinda imeneyi, Akhristu a m’nthawi ya atumwi analandira mauthenga olimbikitsa a Yesu amene amalimbikitsanso mipingo padziko lonse masiku ano

      PEGAMO

      SIMUNA

      TIYATIRA

      SADE

      EFESO

      FILADEFIYA

      LAODIKAYA

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena