-
Zinthu Zimene Ziyenera Kuchitika PosachedwapaMapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
-
-
Njira Yotumizira Uthenga
5. Kodi uthenga wa m’buku la Chivumbulutso unaperekedwa bwanji kwa mtumwi Yohane ndiponso kumipingo?
5 Lemba la Chivumbulutso 1:1b, 2 limapitiriza kuti: “Yesuyo anatumiza mngelo wake kuti adzapereke Chivumbulutsocho mwa zizindikiro kwa kapolo wake Yohane. Yohaneyo anachitira umboni mawu a Mulungu, ndiponso umboni umene Yesu Khristu anapereka, kutanthauza zonse zimene anaona.” Apa zikusonyeza kuti Yohane analandira uthenga wouziridwa kudzera mwa mngelo. Yohane analemba uthengawo mumpukutu, n’kuutumiza kumipingo imene inalipo pa nthawiyo. Ndife oyamikira kuti Mulungu anaonetsetsa kuti uthenga umenewo usungidwe mpaka lero kuti uzilimbikitsa mipingo pafupifupi 100,000 ya atumiki ake ogwirizana padziko lonse lapansi.
6. Kodi Yesu anasonyeza kuti ndi njira iti imene adzagwiritse ntchito popereka chakudya chauzimu kwa ‘akapolo’ ake masiku ano?
6 M’nthawi ya Yohane, Mulungu anali ndi njira yotumizira uthenga wa m’buku la Chivumbulutso ndipo anagwiritsira ntchito Yohaneyo potumiza uthengawo padziko lapansi. Masiku anonso Mulungu ali ndi njira yoperekera chakudya chauzimu kwa ‘akapolo’ ake. Mu ulosi wake waukulu wonena za mapeto a nthawi ino, Yesu anasonyeza kuti njira imene adzagwiritse ntchito popereka chakudya padziko lapansi ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa chakudya pa nthawi yoyenera.” (Mateyu 24:3, 45-47) Iye amagwiritsira ntchito kapolo ameneyu, yemwe ndi Akhristu odzozedwa, pofotokoza matanthauzo a ulosi.
7. (a) Kodi zizindikiro za m’buku la Chivumbulutso ziyenera kutikhudza bwanji? (b) Kodi ena mwa Akhristu odzozedwa agwira nawo kwa nthawi yaitali bwanji ntchito yokwaniritsa masomphenya a m’buku la Chivumbulutso?
7 Mtumwi Yohane analemba kuti Yesu anapereka uthenga wa m’buku la Chivumbulutso “mwa zizindikiro.” Zizindikiro zimenezi n’zochititsa chidwi komanso n’zosangalatsa kwambiri kuziphunzira. Zizindikirozi zikusonyeza zochitika zikuluzikulu zimene zingatithandize kukhala akhama polengeza ulosi ndiponso matanthauzo a ulosiwo. M’buku la Chivumbulutso muli masomphenya ambiri osangalatsa ndi ochititsa chidwi, ndipo Yohane ankachita nawo zinthu zimene ankaonazo koma nthawi zina ankangoonerera. Akhristu odzozedwa akusangalala kuti mzimu wa Mulungu wawaululira matanthauzo a masomphenyawa kuti iwonso afotokozere anthu ena. Ndipo ena mwa iwo agwira nawo kwa zaka zambiri ntchito yokwaniritsa masomphenya amenewa.
-
-
Zinthu Zimene Ziyenera Kuchitika PosachedwapaMapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
-
-
9. (a) Kodi Akhristu odzozedwa asonyeza motani mtima wofanana ndi wa Yohane? (b) Kodi Yohane watisonyeza bwanji njira yotithandiza kukhala osangalala?
9 Yohane anali wokhulupirika polengeza uthenga umene Mulungu anam’patsa kudzera mwa Yesu Khristu. Iye anafotokoza mwatsatanetsatane zinthu “zonse zimene anaona.” Akhristu odzozedwa amapempha Mulungu ndi Yesu Khristu mwakhama kuti awathandize kumvetsa bwino ulosi, n’cholinga choti nawonso auze anthu a Mulungu mfundo zake mwatsatanetsatane. Pofuna kuthandiza mpingo wa Akhristu odzozedwa (ndiponso khamu lalikulu la padziko lonse limene Mulungu adzalipulumutse pa chisautso chachikulu) kupeza njira imene ingawathandize kukhala osangalala, Yohane analemba kuti: ‘Wodala ndi munthu amene amawerenga mokweza, ndiponso anthu amene akumva mawu a ulosi umenewu, komanso amene akusunga zolembedwamo, pakuti nthawi yoikidwiratu ili pafupi.’—Chivumbulutso 1:3.
-