-
Kodi Angelo Ndi Ndani, Nanga Amachita Chiyani?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
2. Kodi Satana ndi ziwanda zake ndi ndani?
Angelo ena anasankha kusiya kumvera Yehova. Mngelo amene anayambirira kuchita zimenezi ndi amene amatchedwa kuti “Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 12:9) Satana ankafuna kuti azilamulira ena, choncho anapusitsa Adamu ndi Hava ndipo kenako anadzapusitsanso angelo ena kuti asiye kumvera Mulungu. Angelo amene anasankha kupandukira Mulunguwa amatchedwa ziwanda. Popeza kuti angelowa anali kumwamba, Yehova anawathamangitsira padziko lapansi ndipo akuyembekezera kuwonongedwa posachedwapa.—Werengani Chivumbulutso 12:9, 12.
3. Kodi Satana ndi ziwanda zake amapusitsa bwanji anthu?
Satana ndi ziwanda zake amapusitsa anthu ambiri kuti azichita zamizimu. Kuchita zimenezi n’koopsa kwambiri chifukwa amawachititsa kukhulupirira kuti angalankhulane ndi anthu amene anamwalira. Mwachitsanzo, anthu ena akakhala ndi vuto amapita kukakumana ndi okhulupirira nyenyezi, olosera zam’tsogolo kapenanso asing’anga. Anthu ena akadwala amakafunafuna mankhwala kwa anthu ochita zamizimu. Satana ndi ziwanda zake amapangitsanso anthu kukhulupirira kuti akhoza kulankhulana ndi anthu amene anamwalira. Koma Yehova amatichenjeza kuti: “Musatembenukire kwa olankhula ndi mizimu ndipo musafunsire olosera zam’tsogolo.” (Levitiko 19:31) Iye amatiuza zimenezi chifukwa amafuna kutiteteza kwa Satana ndi ziwanda zake, omwe ndi adani a Mulungu ndipo amafuna kutipweteka.
-
-
Ufumu wa Mulungu Ukulamulira PanopaMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
2. Kodi kuchokera mu 1914, ndi zinthu ziti zomwe zakhala zikuchitika padzikoli, nanga anthu akhala akusonyeza makhalidwe otani?
Ophunzira a Yesu anafunsa kuti: “Kodi . . . chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?” (Mateyu 24:3) Poyankha, Yesu anawafotokozera zinthu zambiri zimene zidzachitike iye akadzayamba kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kumwamba. Zina mwa zinthu zimenezi ndi monga nkhondo, njala komanso zivomezi. (Werengani Mateyu 24:7.) Baibulo linaloseranso kuti ‘m’masiku otsiriza’ anthu adzakhala ndi makhalidwe oipa omwe adzachititse kuti moyo ukhale wovuta kwambiri. (2 Timoteyo 3:1-5) Zinthu zimenezi zakhala zikuchitika kwambiri kuyambira mu 1914.
3. N’chifukwa chiyani padzikoli pakuchitika zinthu zoipa kwambiri kungochokera pamene Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira?
Yesu atangokhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, anapita kukamenyana ndi Satana komanso ziwanda zake. Satana anagonja pa nkhondoyi. Baibulo limanena kuti: “Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.” (Chivumbulutso 12:9, 10, 12) Satana ndi wokwiya kwambiri chifukwa akudziwa kuti awonongedwa posachedwapa. Iye ndi amene akuchititsa kuti padzikoli pakhale mavuto ambiri chonchi. Zimenezi zikutithandiza kumvetsa chifukwa chake zinthu zafika poipa kwambiri padzikoli. Koma chosangalatsa n’chakuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto onsewa.
-
-
Ufumu wa Mulungu Ukulamulira PanopaMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
5. Dzikoli lasintha kwambiri kuyambira mu 1914
Yesu ananeneratu zinthu zomwe zidzachitike padzikoli akadzangokhala Mfumu. Werengani Luka 21:9-11, kenako mukambirane funso ili:
Pa zinthu zimene zatchulidwa palembali, ndi ziti zimene inuyo munaona zikuchitika kapena kumva kuti zachitika?
Mtumwi Paulo anafotokoza makhalidwe amene anthu adzakhale nawo m’masiku otsiriza. Werengani 2 Timoteyo 3:1-5, kenako mukambirane funso ili:
Malinga ndi lembali, ndi makhalidwe ati amene inuyo mukuona kuti anthu akusonyeza kwambiri masiku ano?
-