Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Utsogoleri Wokangalika wa Kristu Lerolino
    Nsanja ya Olonda—1987
    • Oyang’anira M’dzanja Lamanja la Kristu

      8, 9. (a) Kodi ndi masomphenya otani amene mtumwi Yohane analandira? (b) Kodi nchiyani chimene chidaimiridwa ndi zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri?

      8 Mtumwi Yohane, chiwalo cha bungwe lolamulira la mpingo Wachikristu woyambirira, analandira masomphenya mmene iye “anawona zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi, ndipo pakati pa zoikapo nyalizo wina wonga mwana wa munthu . . . Ndipo m’dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri.” Yesu Kristu analongosola kwa Yohane: “Chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziwona pa dzanja langa lamanja, ndi zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi: Nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri ndizo mipingo isanu ndi iwiri.”​—Chivumbulutso 1:12-20.

      9 Kuchitira ndemanga pa ndime imeneyi, bukhu la “Then Is Finished the Mystery of God” limanena kuti: “Kodi ‘angelo’ oterowo ali osawoneka ndi maso? Ayi. Mtumwi Yohane analandira bukhu lonse la Chivumbulutso kuchokera kwa Yesu Kristu kupyolera mwa m’ngelo wa kumwamba, ndipo chingakhale kusalingalira kumbali yake kumakhala akumlemberanso m’ngelo kumwamba, mu malo ake osawoneka. Iwo safuna uthengawu wolembedwa kwa mipingo isanu ndi iwiri ya mu Asia. Tanthauzo lenileni la liwu lakuti ‘m’ngelo’ liri ‘mthenga; wonyamula uthenga.’ . . . Popeza nyenyezi zophiphiritsira zisanu ndi ziwiri zimenezi zikuwonedwa ziri mu dzanja lamanja la Yesu, izo ziri m’chisamaliro chake ndi ulamuliro ndi pansi pa chitsogozo chake, ‘dzanja lamanja’ lake lopatsidwa mphamvu liri lokhoza kutsogoza ndi kutetezera iwo. . .. Ponena za ‘zoikapo nyali zisanu ndi ziWiri* mu masomphenya a ‘m’tsiku la Ambuye’ zinaimira mipingo yonse ya Akristu owona mu tsiku lino, ‘tsiku la Ambuye lenileni chiyambire 1914 C.E., chotero ‘nyenyezi zisanu ndi ziwiri’ zimaimira oyang’anira onse odzozedwa ndi mzimu, odzozedwa onga angelo a mipingo imeneyo lerolino.b—Masamba 102-4.

      10. Kodi ndi “chuma” chowonjezereka chotani chimene chaperekedwa ku chisamaliro cha kapolo?

      10 Oyang’anira odzozedwa amenewa m’dzanja lamanja la Kristu ali mbali ya “kapolo”amene Iye wamusankha kukhala “woyang’anira chuma chake.” Chifukwa chakuti Mbuye wa kapolo iyemwini wavekedwa ndi mathayo owonjezereka chiyambire 1914, “chuma chake chonse” chiyenera kuphatikizapo zinthu zochuluka zowonjezereka kaamba ka kapolo kusiyana ndi kale. Popeza chinthu chimodzi, monga “atumiki olowa m’malo mwa Kristu,” tsopano otsalira ali atumiki a Mfumu yolamulira yomalamulira pa Ufumu wokhazikitsidwa. (2 Akorinto 5:20) Iwo aikidwa oyang’anira a zinthu zonse zauzimu zomwe ziri za Mbuye wawo padziko lapansi. Iwo ayenera kutumikira m’kukwaniritsa maulosi omwe amagwira ntchito chiyambire chikhazikitsidwe cha Ufumuwo. Ichi chimaphatikizapokulalikira “mbiri imeneyi yabwino ya ufumu . . . mu dziko lonse lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni.” (Mateyu 24:14) Kuposa ndi kalelonse, iwo ayenera kupitiriza kupanga “ophunzira a anthu a mitundu yonse,” chotero kusonkhanitsa “khamu lalikulu” losawerengeka. (Mateyu 28:19, 20; Chivumbulutso 7:9) Inde, “zinthu zofunika za amitundu” zimenezi ziri mbali ya “chuma” chowonjezereka cha Kristu padziko lapansi.​—Hagai 2:7.

      11. (a) Kodi nchiyani chimene “chuma” chowonjezereka chimenechi chimayeneretsa? (b) Kodi ndani amene akutsogoza ntchito, ndipo motani?

      11 Izi zonse zimatanthauza ntchito yowonjezereka kwa “kapolo,” munda wokulira wa ntchito, wofutukulika m’chenicheni ku “dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu.” Iyo imafunikiranso malikulu okulira nth zipangizo za nthambi kaamba ka kuyang’anira ntchitoyo ndi kusindikiza ndi kugawira mabukhu kaamba ka kulalikira ndi phunziro laumwini. Mofanana ndi mu zana loyamba, ntchito imeneyi imachitika pansi pa utsogoleri wokangalika wa Yesu Kristu, amene mophiphiritsira ali “pakati pa zoikapo nyali,” kapena mipingo. Iye amatsogolera iwo kupyolera mwa oyang’anira odzozedwa, amene mophiphiritsira akuwasunga “m’dzanja lake lamanja.” (Chivumbulutso 1:13, 16) Mofanana ndi mu nthawi ya Akristu oyambirira, gulu la oyang’anira odzozedwa amenewa limapanga Bungwe Lolamulira lowoneka ndi maso la mpingo wa Kristu padziko lapansi. “Dzanja lamanja” lake lopatsidwa mphamvu limatsogoza amuna okhulupirika amenewo pamene amayang’anira ntchito ya Ufumu.

  • Utsogoleri Wokangalika wa Kristu Lerolino
    Nsanja ya Olonda—1987
    • b Kope la December 15, 1971, la Nsanja ya Olonda m’Chingelezi rnamveketaa bwino nsonga iyi mowonjezereka, ikumati: “Mosakaikira, osati kokha mkulu mmodzi, wansembe, woyang’anira kapena mbusa, koma ‘bungwe lonse la akulu* linali limene Ambuye wolemekezedwa, Yesu Kristu, analitcha ‘m’ngelo’ yemwe anaimiridwa ndi nyenyezi ya kumwamba. . . . ‘Bungwe la akulu’ (kapena ansembe) la kumeneko ku Aefeso linayenera kugwira ntchito monga nyenyezi mkupereka kuwala kwauzimu kuchokera kumwamba, pa mpingo umene mzimu woyera unawapanga abusa.”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena