-
Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa MulunguMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
2. Kodi munthu aliyense akhoza kupeza Baibulo?
Anthu a ‘m’dziko lililonse, fuko lililonse, chilankhulo chilichonse ndi mtundu uliwonse’ akhoza kupeza uthenga wabwino wa m’Baibulo. (Werengani Chivumbulutso 14:6.) Mulungu anaonetsetsa kuti Baibulo lizipezeka m’zilankhulo zambiri kuposa buku lina lililonse. Pafupifupi munthu aliyense akhoza kupeza Baibulo ndipo zilibe kanthu kuti amakhala kuti kapena amalankhula chilankhulo chiti.
-
-
Kodi Angelo Ndi Ndani, Nanga Amachita Zotani?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
4. Angelo amathandiza anthu kuphunzira zokhudza Yehova
Angelo a Mulungu salalikira mwachindunji kwa anthu. M’malomwake amatsogolera atumiki a Mulungu kwa anthu amene akufuna kuphunzira. Werengani Chivumbulutso 14:6, 7, kenako mukambirane mafunso awa:
N’chifukwa chiyani timafunikira kuthandizidwa ndi angelo tikamalalikira?
Kodi mukumva bwanji mukaganizira kuti angelo angakutsogolereni kwa anthu amene akufuna kuphunzira Baibulo? N’chifukwa chiyani mukumva choncho?
-