Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kumalizitsa Mkwiyo wa Mulungu
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 6. Kodi chinachitika n’chiyani mbale yachitatu itakhuthulidwa, ndipo panamveka mawu otani a mngelo ndiponso a guwa lansembe?

      6 Mbale yachitatu ya mkwiyo wa Mulungu, mofanana ndi kulira kwa lipenga lachitatu, inakhudza mitsinje ndi akasupe a madzi. Yohane anati: “Mngelo wachitatu anathira mbale yake pamitsinje ndi pa akasupe amadzi, ndipo zonse zinasanduka magazi. Ndiye ndinamva mngelo wokhala ndi ulamuliro pa madzi akunena kuti: ‘Inu Amene mulipo ndi amene munalipo, inu Wokhulupirika, ndinu wolungama chifukwa mwapereka zigamulo zimenezi, pakuti iwo anakhetsa magazi a oyera ndi a aneneri. Ndipo inu mwawapatsa magazi kuti amwe, ndipo n’zowayenereradi.’ Kenako ndinamva guwa lansembe likunena kuti: ‘Inde, Yehova Mulungu, inu Wamphamvuyonse, zigamulo zanu n’zoona ndi zolungama.’”—Chivumbulutso 16:4-7.

  • Kumalizitsa Mkwiyo wa Mulungu
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 10. Kodi “mngelo wokhala ndi ulamuliro pa madzi” ananena kuti chiyani, ndipo “guwa lansembe” linapereka umboni wina wotani?

      10 “Mngelo wokhala ndi ulamuliro pa madzi,” kutanthauza mngelo amene anakhuthulira mbale imeneyi pamadzi, anatamanda Yehova kuti ndiye Woweruza wa Chilengedwe Chonse, ndipo zigamulo zake zolungama n’zosasinthika. Choncho, ponena za chigamulo cha Mulungu pa nkhani imeneyi, mngeloyo anati: “N’zowayenereradi.” Mosakayikira, kwa zaka masauzande ambiri mngelo ameneyu anadzionera yekha anthu otsatira ziphunzitso zonyenga ndiponso nzeru za anthu a m’dziko loipali akukhetsa magazi a anthu ambiri ndiponso akuzunza anthu ochuluka. Choncho iye akudziwa kuti chigamulo cha Yehova n’cholondola. Ngakhale “guwa lansembe” la Mulungu linalankhula. Lemba la Chivumbulutso 6:9, 10 limafotokoza kuti miyoyo ya anthu amene anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo ili pansi pa guwa lansembe limenelo. Chotero “guwa lansembe” likupereka umboni wina wamphamvu wosonyeza kuti zigamulo za Yehova ndi zolungama.a Ndipotu m’poyenera kuti anthu amene akhetsa magazi ochuluka ndiponso kuwagwiritsira ntchito molakwika, nawonso akakamizidwe kumwa magazi, monga chizindikiro chakuti Yehova adzawaweruza kuti afe.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena