-
N’chifukwa Chiyani Utumiki wa ku Nyumba ndi Nyumba Uli Wofunika Kwambiri Masiku Ano?Nsanja ya Olonda—2008 | July 15
-
-
16, 17. (a) Kodi n’chiyani chimene chidzakhala chitachitika “chisautso chachikulu” chisanathe? (b) Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?
16 Nthawi ingadzafike pamene uthenga umene timalalikira udzakhala ngati “mfuu yaikulu” ya nkhondo. M’buku la Chivumbulutso, mauthenga amphamvu a chiweruzo akuwasonyeza monga “matalala aakulu, lililonse lolemera pafupifupi makilogalamu 20.” Ndipo lemba la Chivumbulutso 16:21 limati: “Mliriwo unali waukulu modabwitsa.” Pakali pano, sitikudziwa kuti utumiki wa ku nyumba ndi nyumba udzakhala wofunika motani pa ntchito yolengeza mauthenga omaliza achiweruzo. Koma chimene tikudziwa n’chakuti “chisautso chachikulu” chisanathe, dzina la Yehova lidzakhala litadziwika kwambiri kuposa kale lonse.—Chiv. 7:14; Ezek. 38:23.
-