Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 2/15 tsamba 21-24
  • Kuwamasula Mwauzimu Andende

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuwamasula Mwauzimu Andende
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Mmene Akuchitira Ntchitoyo
  • Programu Yopambana Yowongolera Khalidwe
  • Islas Marías
Nsanja ya Olonda—1997
w97 2/15 tsamba 21-24

Kuwamasula Mwauzimu Andende

“TIMAKUDIKIRANITU.” “Kangapo ndithu, usiku ndimakulotani mutafika.” “Zikomo kuti mwapereka wina womadzatichezera kaŵirikaŵiri.” “Tikuyamikira dalitso lililonse limene mosayenerera timalandira kwa Yehova ndi gulu lake ndi chakudya chauzimu chimene amapereka panthaŵi yoyenera.”

Kodi chiyamiko chimenechi chinasonyezedwa chifukwa chanji? Ameneŵa ndi mawu a akaidi obindikira m’ndende zosiyanasiyana ku Mexico. Akuyamikira kuti Mboni za Yehova zikuwasamala mwanjira imene yawapatsa ufulu wauzimu ngakhalebe ali m’ndende. Ku Mexico kuli ndende 42 zimene Mboni za Yehova kaŵirikaŵiri zimatumikirako popereka zosoŵa zauzimu kwa akaidi. Malo ameneŵa amatchedwa Centro Readaptación Social (Malo Owongolera Khalidwe). Mu zina za ndende zimenezi, mumachitikira misonkhano yachikristu kaŵirikaŵiri ndi zotulukapo zabwino. Mwachitsanzo, panthaŵi ina, anthu 380 anapezeka pamsonkhano m’malo ameneŵa. Panthaŵiyo maphunziro a Baibulo okwanira 350 anali kuchitidwa. Okwanira 37 anayenerera kuyamba kulalikira, ndi 32 anapatulira moyo wawo kwa Yehova, nasonyeza zimenezo mwa ubatizo wa m’madzi.

Mmene Akuchitira Ntchitoyo

Kodi Mboni za Yehova zimaichita motani ntchito yawo yolalikira m’malo ameneŵa? Choyamba amapempha kwa akuluakulu kalata yachilolezo yoloŵera m’ndendemo, akumafotokoza chifuno chakuchezetsako​—kukaphunzitsa akaidi mmene angawongolerere moyo wawo ndi kutumikira Mulungu mwanjira yomkondweretsa.

Nthaŵi zonse akuluakulu amapereka chilolezocho. Akuluakulu ameneŵa amayamikira malangizo a Baibulo omwe akaidiwo amapatsidwa. Akuluakulu a ndendewo azindikira kuti Mboni za Yehova zimamvera malamulo achisungiko okhazikitsidwa m’malo ameneŵa. Amawalola atumiki okachezawo kuchitira misonkhano yawo m’maofesi, m’zipinda zodyera, ndi m’zipinda zogwirira ntchito. Pamalo ena, Mboni zinaloledwa ngakhale kumanga Nyumba ya Ufumu yaing’ono, monga momwe chikusonyezera chokumana nacho chotsatira chosimbidwa ndi woyang’anira woyendayenda kummwera chakummaŵa kwa Mexico.

“Kuchiyambi kwa 1991 tinayamba kuchezera ndende ya ku Tehuantepec, Oaxaca, kumene tinapeza njala yaikulu yauzimu. Mwamsanga tinayambitsa maphunziro a Baibulo 27. Titaona chidwi cha akaidiwo, tinalinganiza misonkhano yampingo isanu. Mmodzi wa akaidiwo, yemwe anasonyeza kukonda Yehova kwambiri, anaganiza kuti angomanga Nyumba ya Ufumu yaing’ono mkati momwemo kuti azichitiramo misonkhano. Anakamfikira mkulu wa ndende ndi kumpempha chilolezo, ndipo akuluakuluwo anamlola. Kuchiyambi kwa December 1992, akaidi asanu ndi mmodzi anayenerera kukhala ofalitsa uthenga wabwino. Chifukwa cha kupita kwawo patsogolo, tinakonza kuti tichitire Chikumbutso m’ndende momwemo. Tinapempha chilolezo kwa mkulu wa ndende kuti tibwere ndi zizindikiro​—mkate ndi vinyo​—ndipo titakambitsirana kwa maola anayi, anatilola.

“Ndiye zinachitika kuti pa April 3, 1993 (masiku atatu phwando la Chikumbutso lisanachitike), andende ena anamasulidwa. Pamene wina yemwe anali wofalitsa analandira makalata ake ommasula, analankhula ndi mkulu wa ndende kumpempha chilolezo choti akhalebe mpaka phwando la Chikumbutso litatha. Ichi chinamdabwitsa mkuluyo kwabasi, chifukwa pempho loterolo silimakhalapo wambawamba iyayi, koma poona kuti mkaidiyo anali wofunitsitsa kukhalapo pa Chikumbutso m’ndendemo, anamvomereza. Pa Chikumbutsopo panali anthu 53 omwe anagwetsa misozi yachisangalalo programuyo itatha. Tinavomerezana kulitcha gulu limeneli kuti ‘Ufulu wa Cereso’ chifukwa ngomasuka m’lingaliro lauzimu.”

M’malo ameneŵa ntchito ya Mboni za Yehova amaiyamikira kwambiri. Pa imodzi ya ndende zimenezi, munthu wina woyang’anira amanena poyera kuti kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova ndiwo “mankhwala” owongolera msanga khalidwe la akaidi.

Programu Yopambana Yowongolera Khalidwe

Ntchito ya Mboni za Yehova yathandiza kuwongolera khalidwe la akaidi ambiri. Pamene zili zoona kuti aja amene anakhalapo m’ndende akamasulidwa kaŵirikaŵiri amayambanso moyo waupandu, aja amene analandiradi uthenga wa Mawu a Mulungu amasinthiratu. Kusandulizika kwawo kukutikumbutsa mawu a Mtumwi Paulo akuti: “Adama . . . , kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere. Koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa; koma munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.”​—1 Akorinto 6:9-11.

Kusintha kwakukulu kwa umunthu wawo kumaonekera pamene akufotokoza maganizo awo. Miguel, yemwe ali m’ndende ya Campeche ku Campeche City, anafotokoza motere: “Lero ndinganene ndi chimwemwe kuti ndikudziŵerengera pakati pa nkhosa zina zokhala ndi chiyembekezo cholembedwa pa 2 Petro 3:13 ndi pa Mateyu 5:5.” José, yemwe ali mu Koben, ndende ya mu Campeche anathirira ndemanga kuti: “Ngakhale ndili mkaidi ndipo upandu wanga ngwaukulu kwambiri, ndikuzindikira kuti Yehova ngwachifundo ndipo amamvetsera mapemphero ndi mapembedzero anga. Angandikhululukire zolakwa zanga ndi kundipatsa mpata woti ndithe mbali yotsala ya moyo wanga ndikumagaŵana ndi ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Tikuyamikira akulu athu chifukwa cha nthaŵi imene amakhala nayo kudzatichezera m’ndende kuti tipindule ndi malonjezo a Ufumu wa Mulungu. Ndi madalitso abwinotu amenewo! Ndinganenenso kuti ndine mkaidi ngati? Ayi, Yehova wandipatsa ufulu wauzimu umene ndinafuna.”

Kodi nchiyani chimachititsa kuti ambanda, ochita mizambi, otentha nyumba, ambala, ndi ena asinthe nkukhala Akristu amoyo wabwino? Malinga ndi anthu ake omwewo, ndiyo mphamvu yosanduliza ya Mawu a Mulungu ndiponso mayanjano abwino ndi anthu odziperekadi. Nkhani ya Tiburcio, wobindikira m’ndende ku Mazatlán, Sinaloa, imasonyeza kupambana kwa programu yowongolera khalidwe imeneyi. Anali m’ndende mu Concordia, Sinaloa, kumene anali ndi mavuto chifukwa chaukali wake. Mkazi wake anali mmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo anali kumchita nkhanza kwambiri, ngakhale pamene anabwera kudzamchezera kundende. Anali kuleza mtima ndipo sanaleke kumakamchezera, choncho mwamunayo anampempha kuti ambweretsere buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso Padziko Lapansi, limene anayamba kuliŵerenga payekha.a Kenako anapempha kuti wina azibwera kundendeko kudzamphunzitsa. Anayamba kupita patsogolo mwauzimu, ndipo maunansi ake ndi ena anayamba kuwongokera. Anatumizidwa ku Mazatlán kumene kulinso gulu lina lophunzira Baibulo, ndipo tsopano ndi wofalitsa. Iye akuti: “Tsopano ndikuyamikira kuti ndikumvetsera choonadi cha Baibulo konkuno, ndikumayembekezera kuti mtsogolo posachedwapa ndimasulidwa, ndipo ndidzatha kumapezeka pamisonkhano yonse yaikulu ndi yampingo, limodzi ndi mkazi wanga ndi ana anga.”

Ndiponso pali Conrado, yemwe akuyamikira kwambiri chifukwa cha kusintha kumene wachita pamoyo wake. Mavuto am’banja lake anali aakulu kwakuti mkazi wake anamthaŵa. Ndiye anafunafuna chitonthozo mwa anamgoneka. Posakhalitsa anayamba kugulitsa anamgoneka. Anagwidwa ndi kuŵeruzidwa kuti aloŵe m’ndende chifukwa chonyamula mtokoma wachamba ndi cocaine. M’ndendemo munali kagulu kophunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo anampempha kuti aziphunzira nawo. Akufotokozano maganizo ake motere: “Ndinachita chidwi ndi mmene misonkhano inachitikira mwadongosolo, programu yofufuza mwa kugwiritsira ntchito zofalitsa, ndi kuti chilichonse chinazikidwa pa Baibulo. Nthaŵi yomweyo ndinapempha phunziro la Baibulo ndipo ndinayamba kupezeka pamisonkhano.” Mmenemo munali mu January 1993. Tsopano Conrado anatuluka m’ndende ndipo akupitabe patsogolo mumpingo wachikristu.

Islas Marías

Ku Mexico kuli ndende ina yowopsa yazisumbu zinayi zotchedwa Islas Marías. Akaidi amayendayenda pazisumbu zachibalozo kumene anawabindikira. Ena amakhala kumeneko ndi akazi ndi ana awo.

Kumeneko kuli mpingo waung’ono. Abale atatu amapitako kamodzi pamwezi kuchokera ku Mazatlán, kukathandiza kuchititsa misonkhano, kupereka mabuku, ndi kulimbikitsa. Nthaŵi zina woyang’anira dera amakawachezetsanso. Avareji ya osonkhana imakhala pakati pa 20 ndi 25. Kuli ofalitsa obatizidwa anayi ndi osabatizidwa aŵiri. Woyang’anira woyendayenda anatero kuti “ena amayenda makilomita 17 [mamailosi 10] kuti akapezeke pamisonkhano pa Sande ndipo amachoka pamsonkhanopo mwachangu kuti abwerere kukapezekapo poitana maina awo. Kuyenda mofulumira kumatenga maola aŵiri kukafika.” Mmodzi wa abalewo, yemwe anaphunzira choonadi m’ndende momwemo, posachedwapa anati: “Ndinali kukhumba kutuluka mwamsanga, koma tsopano zingakhale pamene Yehova afunira, popeza ndili ndi ntchito yochuluka yoti ndichite mkati mommuno.”

Tili okondwa kuona kuti choonadi chili ndi mphamvu yomasula oona mtima omwe akufunafuna njira zomkondweretsera Yehova. Pa ameneŵa, oposa khumi ndi aŵiri omwe anaphunzira choonadi m’ndende anamasulidwa, nabatizidwa, ndipo tsopano ali ndi moyo wolemekezeka monga atumiki a Mulungu, ena akhala ngakhale akulu mumpingo. Mphamvu ya Baibulo yochiritsa mitima ndi kusanduliza anthu yasonyezedwa modabwitsa. Anthu ameneŵa omwe anawabindikirapo m’ndende chifukwa cha kulakwa, pamene aloŵa njira ya kuunika kwa Mawu a Mulungu, amapeza ufulu weniweni umene Yesu analonjeza pamene anati: “Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”​— Yohane 8:32; Salmo 119:105.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 23]

Ambiri anapindula ndi choonadi chachikristu chimene anaphunzira m’ndende

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena