Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
    • Mutu 5

      Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake

      1, 2. Kodi nkwayani kumene makolo ayenera kufunako chithandizo cholerera ana awo?

      “ANA ndiwo cholandira cha kwa Yehova,” linatero kholo lina loyamikira pafupifupi zaka 3,000 kalelo. (Salmo 127:3) Ndithudi, chisangalalo cha kukhala kholo ndicho mphotho yochokera kwa Mulungu, imene okwatirana ochuluka ali nayo. Komabe, awo amene amakhala ndi ana posapita nthaŵi amazindikira kuti pamene ukholo umadzetsa chisangalalo, umafikanso ndi mathayo.

      2 Makamaka lerolino, kulera ana ndi ntchito yaikulu kwambiri. Komabe, ambiri akuchita mwachipambano, ndipo wamasalmo wouziridwa amasonyeza njira yake mwakunena kuti: “Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe.” (Salmo 127:1) Pamene mutsatira kwambiri malangizo a Yehova, mpamenenso mumakhala kholo labwino kwambiri. Baibulo limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako.” (Miyambo 3:5) Kodi muli wofunitsitsa kumvetsera uphungu wa Yehova pamene mukuyamba ntchito yanu ya zaka 20 yolera mwana?

      KULANDIRA LINGALIRO LA BAIBULO

      3. Kodi atate ali ndi thayo lotani pa kulera ana?

      3 M’nyumba zambiri kuzungulira dziko lonse, amuna amaona ntchito yophunzitsa ana kukhala ya mkazi. Nzoona kuti Mawu a Mulungu amasonyeza kuti ntchito yaikulu ya tate ndiyo kusamalira banja. Komabe, limanenanso kuti iye alinso ndi mathayo panyumba. Baibulo limati: “Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda; pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.” (Miyambo 24:27) M’lingaliro la Mulungu, atate ndi amayi ali ogwirira ntchito pamodzi pa kuphunzitsa ana.—Miyambo 1:8, 9.

      4. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuona ana aamuna kukhala ofunika kuposa aakazi?

      4 Kodi mumawaona motani ana anu? Malipoti amanena kuti ku Asia “makanda achikazi kaŵirikaŵiri samalandiridwa ndi manja aŵiri [atabadwa].” Zikumveka kuti kusaŵerengera ana aakazi kudakalipo ku Latin America, ngakhale pakati pa “mabanja ophunzira bwino.” Komabe choonadi nchakuti, atsikana saali ana otsikirapo. Yakobo, tate wotchuka wa m’nthaŵi zakale, analongosola ana ake onse, kuphatikizapo ana aakazi obadwa kufikira nthaŵiyo, monga ‘ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu [ine].’ (Genesis 33:1-5; 37:35) Mofananamo, Yesu anadalitsa “tiana” (anyamata ndi atsikana) timene anthu anabweretsa kwa iye. (Mateyu 19:13-15) Tingakhale otsimikiza kuti iye anasonyeza lingaliro la Yehova.—Deuteronomo 16:14.

      5. Kodi nzotani zimene okwatirana ayenera kulingalira posankha ukulu wa banja lawo?

      5 Kodi kumene mumakhala anthu amayembekezera mkazi kubala ana ambiri malinga ndi mmene angakhozere? Kwenikweni, nkhani ya chiŵerengero cha ana ili chosankha cha aŵiri okwatirana. Bwanji ngati makolowo alibe njira yodyetsera ana ambiri, kuwaveka, ndi kuwapereka kusukulu? Ndithudi, okwatiranawo ayenera kulingalira zimenezi pamene akambitsirana za ukulu wa banja limene akufuna. Okwatirana ena amene amalephera kusamalira ana awo onse, amakawasungitsa kwa achibale kuti awalere. Kodi kachitidwe kameneka nkabwino? Osati kwenikweni. Ndipo sikamachotsera makolowo thayo lawo kulinga kwa ana awo. Baibulo limati: “Ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye.” (1 Timoteo 5:8) Okwatirana anzeru amayesa kulinganiza ukulu wa “banja” lawo kotero kuti ‘adzisungire mbumba zawo.’ Kodi iwo ayenera kugwiritsira ntchito njira zoletsa kubala kuti achite zimenezo? Iyinso ndi nkhani ya chosankha chawo, ndipo ngati okwatirana asankha kuchita zimenezo, njira imene adzagwiritsira ntchito ilinso chosankha chawo. “Yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.” (Agalatiya 6:5) Komabe, njira yoletsa kubala imene imaloŵetsamo mtundu uliwonse wa kuchotsa mimba imawombana ndi mapulinsipulo a Baibulo. Yehova Mulungu ali “chitsime cha moyo.” (Salmo 36:9) Motero, kuwononga moyo pambuyo pakuti wapangika kale kumasonyeza kupanda ulemu kwakukulu kulinga kwa Yehova ndipo ndi mbanda imeneyo.—Eksodo 21:22, 23; Salmo 139:16; Yeremiya 1:5.

      KUKWANIRITSA ZOFUNIKA ZA MWANA WANU

      6. Kodi kuphunzitsa mwana kuyenera kuyamba liti?

      6 Miyambo 22:6 imati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake.” Kuphunzitsa ana ndiko ntchito ina yaikulu ya makolo. Komabe, kodi kuphunzitsa kumeneko kuyenera kuyamba liti? Mwamsanga kwambiri. Mtumwi Paulo ananena kuti Timoteo anaphunzitsidwa “kuyambira ukhanda.” (2 Timoteo 3:15) Liwu lachigiriki logwiritsiridwa ntchito pano lingatanthauze khanda laling’ono kapena ngakhale mwana wosabadwa. (Luka 1:41, 44; Machitidwe 7:18-20) Chotero, Timoteo anaphunzitsidwa kuyambira pamene anali wamng’ono kwambiri—ndipo zimenezo zinali zoyenera. Ukhanda ndiyo nthaŵi yabwino yoyambirapo kuphunzitsa mwana. Ngakhale khanda laling’ono limafuna kudziŵa zinthu.

      7. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwa makolo onse aŵiri kukulitsa unansi wabwino ndi khanda? (b) Kodi panali unansi wotani pakati pa Yehova ndi Mwana wake wobadwa yekha?

      7 “Pamene ndinaona khanda langa nthaŵi yoyamba,” akutero mayi wina, “ndinalikonda pomwepo.” Amateronso amayi ambiri. Chikondi champhamvu pakati pa mayi ndi khanda chimakula pamene akhala pamodzi pambuyo pa kubadwa. Kuyamwitsa kumawonjezeranso chikondano chawo. (Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 2:7.) Kusisita khanda kwa mayi ndi kulankhula nalo kuli kofunika kwambiri pa kukwaniritsa zofunika za khanda za maganizo. (Yerekezerani ndi Yesaya 66:12.) Koma bwanji ponena za tate? Iyenso ayenera kukhala ndi unansi waukulu ndi mwana wake watsopanoyo. Yehova mwiniyo ali chitsanzo pa zimenezi. M’buku la Miyambo, timauzidwa za unansi wa Yehova ndi Mwana wake wobadwa yekha, amene amanenedwa kukhala atanena kuti: “Mulungu anali nane poyamba njira yake, . . . ndinamsekeretsa tsiku ndi tsiku.” (Miyambo 8:22, 30; Yohane 1:14) Mofananamo, tate wabwino amakulitsa unansi wabwino ndi wachikondi kwa mwana wake kuyambira pachiyambi penipeni pa moyo wa mwanayo. “Sonyezani chikondi chochuluka,” linatero kholo lina. “Palibe mwana amene anafapo ndi kumkumbatira ndi kupsompsona kochuluka.”

      8. Kodi ndi chisonkhezero cha maganizo chotani chimene makolo ayenera kupereka kwa makanda mwamsanga kwambiri?

      8 Koma makanda amafunikira zambiri. Kungoyambira pa kubadwa, ubongo wawo umakhala wokonzekera kulandira chidziŵitso ndi kuchisunga, ndipo chachikulu chimachokera kwa makolo. Titenge chitsanzo cha chinenero. Ofufuza akunena kuti mmene mwana amaphunzirira bwino kulankhula ndi kuŵerenga “kumadalira kwambiri pa zochita zapaukhanda pakati pa mwanayo ndi makolo ake.” Lankhulani ndi mwana wanu ndi kumuŵerengera kuyambira paukhanda. Posapita nthaŵi adzafuna kukutsanzirani, ndipo mwamsanga mudzakhala mukumthandiza kuŵerenga. Mwachionekere, adzayamba kuŵerenga asanaloŵe sukulu. Zimenezo zidzakhala zothandiza kwambiri ngati mukukhala m’dziko kumene aphunzitsi ali ochepa ndi ana ali ochuluka kwambiri m’kalasi.

      9. Kodi nchiyani chimene chili chonulirapo chachikulu koposa chimene makolo ayenera kukumbukira?

      9 Nkhaŵa yoyambirira ya makolo achikristu iyenera kukhala kukwaniritsa zofunika zauzimu za mwana wawo. (Onani Deuteronomo 8:3.) Ndi chonulirapo chotani? Cha kuthandiza mwana wawo kukhala ndi umunthu wonga wa Kristu, ndiko kuti, kuvala “umunthu watsopano.” (Aefeso 4:24, NW) Kuti achite zimenezi ayenera kulingalira za zinthu zomangira zoyenera ndi njira zomangira zoyenera.

      PHUNZITSANI MWANA WANU MWACHANGU

      10. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene ana afunikira kukulitsa?

      10 Kulimba kwa nyumba kumadalira kwambiri pa mtundu wa zomangira zogwiritsiridwa ntchito. Mtumwi Paulo ananena kuti zomangira zabwino kwambiri za umunthu wachikristu ndizo “golidi, siliva, miyala ya mtengo wake.” (1 Akorinto 3:10-12) Zimenezi zimaimira mikhalidwe yonga chikhulupiriro, nzeru, luntha, kukhulupirika, ulemu, ndi kuyamikira Yehova ndi malamulo ake mwachikondi. (Salmo 19:7-11; Miyambo 2:1-6; 3:13, 14) Kodi ndi motani mmene makolo angathandizire ana awo kukulitsa mikhalidwe imeneyi kuyambira paubwana weniweni? Mwa kutsatira njira imene inaperekedwa kalelo.

      11. Kodi makolo achiisrayeli anathandiza motani ana awo kukulitsa umunthu waumulungu?

      11 Mtundu wa Israyeli utakhala pafupi kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Yehova anauza makolo achiisrayeli kuti: “Mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:6, 7) Inde, makolo afunikira kukhala zitsanzo, mabwenzi, olankhulana nawo, ndi aphunzitsi.

      12. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti makolo akhale zitsanzo zabwino?

      12 Khalani chitsanzo. Choyamba, Yehova anati: “Mawu awa . . . azikhala pamtima panu.” Ndiyeno anawonjeza kuti: “Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu.” Chotero mikhalidwe yaumulungu choyamba iyenera kukhala mumtima mwa kholo. Kholo liyenera kukonda choonadi ndi kukhala ndi moyo mogwirizana nacho. Ndiyo njira yokha imene angafikire mtima wa mwana wawo. (Miyambo 20:7) Chifukwa ninji? Chifukwa ana amasonkhezeredwa kwambiri ndi zimene amaona kuposa zimene amamva.—Luka 6:40; 1 Akorinto 11:1.

      13. Posamalira ana awo, kodi ndi motani mmene makolo achikristu angatengere chitsanzo cha Yesu?

      13 Khalani bwenzi. Yehova anauza makolo mu Israyeli kuti: ‘Lankhulani ndi ana anu pamene mukhala pansi m’nyumba mwanu ndi pamene mukuyenda panjira.’ Izi zimafuna kupatula nthaŵi yomakhala ndi ana mosasamala kanthu kuti makolo ali otanganitsidwa motani. Mwachionekere Yesu anaona kuti ana anafunikira nthaŵi imeneyi. Mkati mwa masiku omalizira a utumiki wake, anthu “analinkudza nato kwa Iye tiana, kuti [Iye] akatikhudze.” Kodi Yesu anachitanji? “Anatiyangata, natidalitsa.” (Marko 10:13, 16) Tangolingalirani, maola omalizira a moyo wa Yesu anali kutha. Chikhalirechobe, iye anapatula nthaŵi napereka chisamaliro chake pa tiana timeneti. Phunziro labwino kwenikweni!

      14. Kodi nchifukwa ninji kuli kopindulitsa kwa makolo kupatula nthaŵi yokhala ndi mwana wawo?

      14 Khalani wolankhulana naye. Kukhala pamodzi ndi mwana wanu kudzakuthandizani kulankhulana naye. Pamene mulankhulana naye kwambiri, mpamenenso mudzazindikira bwino kakulidwe ka umunthu wake. Komabe, kumbukirani kuti kulankhulana kumaloŵetsamo zoposa kulankhula chabe. “Ndinakulitsa luso la kumvetsera,” anatero mayi wina ku Brazil, “kumvetsera ndi mtima wanga.” Kuleza mtima kwake kunabala zipatso pamene mwana wake wamwamuna anayamba kukambitsirana naye zakukhosi kwake.

      15. Kodi tiyenera kukumbukiranji ponena za zosangulutsa?

      15 Ana amafunikira “mphindi yakuseka . . . ndi mphindi yakuvina,” ndiyo mphindi yakusanguluka. (Mlaliki 3:1, 4; Zekariya 8:5) Kusanguluka kumakhala kopindulitsa kwambiri pamene makolo ndi ana akuchitira pamodzi. Nkomvetsa chisoni kuti m’mabanja ambiri kusanguluka kumatanthauza kupenyerera wailesi yakanema basi. Pamene maprogramu ena apawailesi yakanema angakhale okondweretsa, ambiri amawononga makhalidwe abwino, ndipo kupenyerera wailesi yakanema kumaletsa kulankhulana m’banja. Chifukwa chake, bwanji osachita kanthu kena kothandiza limodzi ndi ana anu? Imbani, chitani maseŵero, chezerani mabwenzi, kachezeni kumalo osangalatsa. Machitachita oterowo amalimbikitsa kulankhulana.

      16. Kodi nchiyani chimene makolo ayenera kuphunzitsa ana awo ponena za Yehova, ndipo kodi ayenera kuchita motani zimenezo?

      16 Khalani mphunzitsi. “Muziwaphunzitsa mwachangu [mawu awa] kwa ana anu,” anatero Yehova. Nkhani yake imasonyeza zimene muyenera kuphunzitsa ndi mmene muyenera kuphunzitsira. Choyamba, “muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.” (Deuteronomo 6:5) Ndiyeno, ‘mawu aŵa . . . muziwaphunzitsa mwachangu.’ Perekani chilangizo chokulitsa chikondi cha mtima wonse pa Yehova ndi malamulo ake. (Yerekezerani ndi Ahebri 8:10.) Mawu akuti “phunzitsa mwachangu” amatanthauza kuphunzitsa mobwerezabwereza. Chotero Yehova kwenikweni akukuuzani kuti njira yaikulu yothandizira ana anu kukulitsa umunthu waumulungu ndiyo kulankhula za iye nthaŵi zonse. Zimenezi zimaphatikizapo kuphunzira nawo Baibulo nthaŵi zonse.

      Zithunzi patsamba 57

      Makolo, khalani zitsanzo, mabwenzi, olankhulana nawo, ndi aphunzitsi

      17. Kodi makolo angafunikire kukulitsa chiyani mwa mwana wawo? Nchifukwa ninji?

      17 Makolo ambiri amadziŵa kuti kuloŵetsa chidziŵitso mumtima wa mwana si kopepuka. Mtumwi Petro analimbikitsa Akristu anzake kuti: “Monga makanda obadwa chatsopano, kulitsani chilakolako cha mkaka wosasukuluka wa mawu.” (1 Petro 2:2, NW) Mawu akuti “kulitsani chilakolako” amapereka lingaliro lakuti ambiri samakhala ndi njala yachibadwa ya chakudya chauzimu. Makolo angafunikire kupeza njira zokulitsira chilakolako chimenecho mwa mwana wawo.

      18. Kodi ndi njira zina zotani zophunzitsira za Yesu zimene makolo akulimbikitsidwa kutsanzira?

      18 Yesu anafika anthu pamtima mwa kugwiritsira ntchito mafanizo. (Marko 13:34; Luka 10:29-37) Njira yophunzitsira imeneyi imagwira ntchito kwambiri kwa ana. Phunzitsani mapulinsipulo a Baibulo mwa nkhani zokopa ndi zokondweretsa, mwinamwake zija zopezeka mu Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo.a Chititsani anawo kuloŵetsedwamo. Aloleni kugwiritsira ntchito luntha lawo mwa kulemba zithunzi za zinthu za m’Baibulo ndi kuchita maseŵero a zochitikazo. Yesu anagwiritsiranso ntchito mafunso. (Mateyu 17:24-27) Tsanzirani njira ya kaphunzitsidwe kake paphunziro lanu la banja. M’malo mwakungotchula lamulo la Mulungu, funsani mafunso onga akuti, Kodi nchifukwa ninji Yehova anatipatsa lamulo ili? Kodi nchiyani chimene chidzachitika ngati tilisunga? Kodi chidzachitika nchiyani ngati sitilisunga? Mafunso oterowo amathandiza mwana kulingalira ndi kuona kuti malamulo a Mulungu amathandiza ndipo ali abwino.—Deuteronomo 10:13.

      19. Ngati makolo atsatira mapulinsipulo a Baibulo pochita ndi ana awo, kodi ndi mapindu aakulu otani amene anawo angapeze?

      19 Mwa kukhala chitsanzo, bwenzi, wolankhulana naye, ndi mphunzitsi, mungathandize mwana wanu kuyambira m’zaka zake zaukhanda kukulitsa unansi wapafupi ndi Yehova Mulungu. Unansi umenewu udzalimbikitsa mwana wanu kukhala Mkristu wachimwemwe. Adzayesayesa kusunga chikhulupiriro chake ngakhale poyang’anizana ndi chisonkhezero cha mabwenzi ndi mayesero. Mthandizeni nthaŵi zonse kuyamikira unansi wamtengo wapatali umenewu.—Miyambo 27:11.

      CHILANGO—CHOFUNIKA CHACHIKULU

      20. Kodi chilango nchiyani, ndipo chiyenera kuperekedwa motani?

      20 Chilango ndicho kuphunzitsa kumene kumawongolera maganizo ndi mtima. Chimafunikira kwa ana nthaŵi ndi nthaŵi. Paulo akulangiza atate ‘kupitiriza kulera [ana awo] m’chilango cha Yehova ndi kuwawongolera maganizo m’njira yake.’ (Aefeso 6:4, NW) Makolo ayenera kulanga mwa chikondi, monga momwe Yehova amachitira. (Ahebri 12:4-11) Chilango chozikidwa pa chikondi chingaperekedwe mwa kukambitsirana. Chifukwa chake, timauzidwa kuti “imvani mwambo [“chilango,” NW].” (Miyambo 8:33) Kodi chilango chiyenera kuperekedwa motani?

      21. Kodi ndi mapulinsipulo ati amene makolo ayenera kukumbukira polanga ana awo?

      21 Makolo ena amaganiza kuti kulanga ana awo kumangotanthauza kulankhula kwa iwo ndi mawu owopseza, kuwakalipira, kapena ngakhale kuwatukwana. Komabe, pankhani imodzimodziyo, Paulo akuchenjeza kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu.” (Aefeso 6:4) Akristu onse akulimbikitsidwa kukhala ‘odekha kwa onse . . . akumalangiza mofatsa otsutsa.’ (2 Timoteo 2:24, 25, NW) Pamene kuli kwakuti makolo achikristu amazindikira kufunika kwa kukhala okhwima, amayesa kukumbukira mawu ameneŵa polanga ana awo. Komabe, nthaŵi zina mawu okha samakhala okwanira, ndipo mtundu wina wa chilango ungakhale wofunika.—Miyambo 22:15.

      22. Ngati mwana afunikira kupatsidwa chilango chamkwapulo, kodi ayenera kuthandizidwa kudziŵanji?

      22 Ana osiyanasiyana amafunikira mitundu yosiyanasiyana ya chilango. Ena “sangalangizidwe ndi mawu.” Kwa iwo, chilango chamkwapulo choperekedwa panthaŵi zina chifukwa cha kusamvera kwawo chingakhale chopulumutsa moyo. (Miyambo 17:10; 23:13, 14; 29:19) Komabe, mwana ayenera kudziŵa chifukwa chake akulangidwa. “Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru.” (Miyambo 29:15; Yobu 6:24) Ndiponso, chilango chamkwapulo chiyenera kukhala ndi malire. “Ndidzakulanga pamlingo woyenera,” anatero Yehova kwa anthu ake. (Yeremiya 46:28b, NW) Baibulo silimavomereza konse kukwapula kwaukali kapena kumenya kowopsa, kumene kungachititse mwana mikwingwirima ndipo ngakhale kumvulaza.—Miyambo 16:32.

      23. Kodi mwana ayenera kuzindikiranji pamene alangidwa ndi makolo ake?

      23 Pamene Yehova anachenjeza anthu ake kuti adzawalanga, choyamba anati: “Usawope . . . pakuti Ine ndili ndi iwe.” (Yeremiya 46:28a) Mofananamo, chilango chaukholo choyenera chilichonse sichiyenera kuchititsa mwana kudziona kukhala wosafunika. (Akolose 3:21) M’malo mwake, mwanayo ayenera kuona kuti chilangocho chikuperekedwa chifukwa chakuti khololo lili ‘ndi iye,’ kuti lili kumbali yake.

      TETEZERANI MWANA WANU KU NGOZI

      24, 25. Kodi ana ayenera kutetezeredwa ku chiwopsezo chachikulu chotani chomwe chilipo masiku ano?

      24 Achikulire ambiri amayang’ana kumbuyo ku ubwana wawo ndi kuona kuti inali nthaŵi yakusangalala. Amakumbukira mmene anali kumvera kukhala otetezereka ndi okondedwa ndi makolo awo, chitsimikiziro chakuti anali okonzeka kuwasamalira zivute zitani. Makolo amafuna ana awo kumva chimodzimodzi, koma m’dziko lamakono loipali, kutetezera ana nkovutirapo kuposa mmene kunalili kale.

      25 Chiwopsezo chachikulu chimene chakhalapo m’zaka zaposachedwapa ndicho kugona ana. Ku Malaysia, malipoti a ana ogonedwa anawonjezereka kanayi panyengo ya zaka khumi. Ku Germany pafupifupi ana 300,000 amagonedwa chaka chilichonse, pamene m’dziko lina la ku South America, malinga ndi kufufuza kwina, chiŵerengero chowopsa cha pachaka chinafika pafupifupi 9,000,000! Mwatsoka lake, ochuluka a ana ameneŵa amagonedwa m’nyumba mwawo mwenimwenimo ndi anthu amene amadziŵa ndi kuwakhulupirira. Koma ana ayenera kupeza chitetezo chachikulu kwa makolo awo. Kodi ndi motani mmene makolo angakhalire otetezera?

      26. Kodi ndi njira zina zotani zimene ana angakhalire otetezereka, ndipo ndi motani mmene chidziŵitso chingatetezerere mwana?

      26 Popeza kuti zochitika zimasonyeza kuti ana amene samadziŵa zochuluka za kugonana ndiwo ali pangozi yaikulu kwa ogona ana, njira yaikulu yowatetezera nayo ndiyo kuphunzitsa mwana, ngakhale pamene adakali wamng’ono. Chidziŵitso chingamtetezere “ku njira yoipa, kwa anthu onena zokhota.” (Miyambo 2:10-12) Chidziŵitso chotani? Chidziŵitso cha mapulinsipulo a Baibulo, onena za mkhalidwe wabwino ndi woipa. Chidziŵitsonso chakuti achikulire ena amachita zinthu zoipa ndi kuti wachichepere sayenera kumvera pamene anthu amuuza kuchita zosayenera. (Yerekezerani ndi Danieli 1:4, 8; 3:16-18.) Chilangizo chimenecho chisakhale cha nthaŵi imodzi chabe. Ana ambiri amakumbukira bwino chilangizo pamene chiphunzitsidwa kwa iwo mobwerezabwereza. Pamene ana akulirapo, tate ayenera kuyamba kupatsa ulemu mwana wamkazi, mayinso mwana wake wamwamuna—mwakutero adzakulitsa lingaliro la mwana la kuzindikira chimene chili choyenera. Ndiponso, chitetezo china chabwino koposa pa nkhanza ya kugonedwa kwa ana ndicho chiyang’aniro chatcheru cha inu makolo.

      FUNANI CHITSOGOZO CHA MULUNGU

      27, 28. Kodi ndani amene ali Magwero aakulu koposa a chithandizo kwa makolo pamene ayang’anizana ndi vuto la kulera mwana?

      27 Zoona, kuphunzitsa mwana kuyambira paukhanda wake kulidi kovuta, koma makolo okhulupirira sayenera kulimbana ndi vutolo paokha. Kale m’masiku a Oweruza, pamene mwamuna wotchedwa Manowa anadziŵa kuti adzakhala tate, anapempha chitsogozo cha Yehova pakulera mwana wake. Yehova anayankha mapemphero ake.—Oweruza 13:8, 12, 24.

      28 Mwa njira imodzimodzi lerolino, pamene makolo okhulupirira alera ana awo, iwonso angalankhule kwa Yehova m’pemphero. Kukhala kholo ndi ntchito yaikulu, koma kumadzetsa mphotho zazikulu. Okwatirana achikristu ku Hawaii anati: “Muli ndi zaka 12 zakuchita ntchito yanu zisanafike zaka zovuta zaunyamata kuyambira 13 mpaka 19. Koma ngati mwalimbikira kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo, imeneyo imakhala nthaŵi yotuta chisangalalo ndi mtendere pamene iwo asankha kutumikira Yehova ndi mtima wonse.” (Miyambo 23:15, 16) Pamene mwana wanu apanga chosankha chimenecho, inunso mudzasonkhezereka kunena kuti: “Ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova.”

      a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

      KODI MAPULINSIPULO A BAIBULO AŴA ANGATHANDIZE MOTANI . . . MAKOLO KUPHUNZITSA ANA AWO?

      Khulupirirani Yehova.—Miyambo 3:5.

      Samalirani thayo lanu.—1 Timoteo 5:8.

      Yehova ali Atate wachikondi.—Miyambo 8:22, 30.

      Makolo ali ndi thayo la kuphunzitsa ana awo.—Deuteronomo 6:6, 7.

      Chilango nchofunika.—Aefeso 6:4.

      CHILANGO CHOGWIRA NTCHITO

      Mtundu umodzi wothandiza wa chilango ndiwo kuchititsa ana kuona kuipa kwa zotulukapo za kusamvera. (Agalatiya 6:7; yerekezerani ndi Eksodo 34:6, 7.) Ngati, mwachitsanzo, mwana wanu aipitsa malo, kumchititsa kuyeretsa iye mwini kungampatse phunziro lamphamvu. Kodi wachitira wina choipa? Kumuuza kuti apepese kungawongolere mkhalidwe wake wosayenera. Mtundu wina wa chilango ndiwo kummana mwaŵi winawake kwakanthaŵi kuti atengepo phunziro lofunika. Mwa njira imeneyi mwanayo amaphunzira nzeru ya kutsatira mapulinsipulo olungama.

  • Sonyezani chikondi ndi chiyamikiro kwa ana anu
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
    • Mutu 6

      Thandizani Wachinyamata Wanu Kukula Bwino

      1, 2. Kodi ndi zovuta zotani ndi zisangalalo zimene zimadza ndi zaka zaunyamata?

      KUKHALA ndi wachinyamataa panyumba nkosiyana kwambiri ndi kukhala ndi wazaka zisanu kapena ngakhale wazaka khumi. Zaka zaunyamata zimadza ndi ziyeso zake ndi zovuta zake, koma zikhozanso kubweretsa zisangalalo ndi mphotho. Zitsanzo monga Yosefe, Davide, Yosiya, ndi Timoteo zimasonyeza kuti achichepere angachite zinthu mwanzeru ndi kukhala ndi unansi wabwino ndi Yehova. (Genesis 37:2-11; 1 Samueli 16:11-13; 2 Mafumu 22:3-7; Machitidwe 16:1, 2) Achinyamata ambiri lerolino asonyeza zimenezo. Mwachionekere, muyenera kudziŵa ena a iwo.

      2 Komabe, kwa ena zaka zaunyamata zimakhala zovutitsa. Achichepere omasinkhuka amakhala ndi maganizo akukondwa, nthaŵi zina akupsinjika. Anyamata ndi atsikana a zaka zimenezi angafune kukhala ndi ufulu wokulirapo, ndipo angaipidwe ndi ziletso zimene makolo angaike pa iwo. Komabe, achichepere oterowo adakali osadziŵa zambiri ndipo amafunikira thandizo la makolo achikondi ndi oleza mtima. Inde, zaka zaunyamata zingakhale zosangalatsa, koma zingakhalenso zothetsa nzeru—ponse paŵiri kwa makolo ndi kwa achinyamata omwe. Kodi achichepere angathandizidwe motani m’zaka zimenezi?

      3. Kodi ndi m’njira yotani imene makolo angapatsire mwana wawo womasinkhuka mwaŵi wabwino koposa m’moyo?

      3 Makolo amene amatsatira uphungu wa Baibulo amapatsa mwana wawo womasinkhukayo mwaŵi wabwino koposa wakupyola mwachipambano m’mayesero amenewo ndi kukhala wachikulire wanzeru. M’maiko onse ndipo kuyambira kale lonse, makolo ndi achinyamata amene anagwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo chapamodzi adalitsidwa ndi chipambano.—Salmo 119:1.

      KULANKHULANA KOONA MTIMA NDI KOMASUKA

      Chithunzi patsamba 67

      Patulani nthaŵi pamene wachinyamata wanu akufuna kulankhula nanu

      4. Kodi nchifukwa ninji upo wakukambitsirana uli wofunika kwambiri m’zaka zaunyamata?

      4 Baibulo limati: “Zolingalira zizimidwa popanda upo.” (Miyambo 15:22) Ngati upo wakukambitsirana unali wofunika pamene ana anali aang’ono, koposa kotani nanga m’zaka zaunyamata—pamene achichepere mwachionekere amakhala nthaŵi yochepa panyumba ndi kuthera nthaŵi yochuluka ali ndi mabwenzi akusukulu kapena anzawo ena. Ngati palibe upo wakukambitsirana—kulankhulana koona mtima ndi komasuka pakati pa ana ndi makolo—achinyamata angakhale alendo m’nyumba. Chotero kodi ndi motani mmene njira zolankhulana zingakhalire zotseguka?

      5. Kodi achinyamata akulimbikitsidwa kuiona motani nkhani ya kulankhulana ndi makolo awo?

      5 Ponse paŵiri achinyamata ndi makolo ayenera kuchita mbali zawo pazimenezi. Zoona, achichepere omasinkhuka angakupeze kukhala kovuta kulankhula ndi makolo awo koposa pamene anali aang’ono. Komabe, kumbukirani kuti “popanda upo wanzeru anthu amagwa; koma pochuluka aphungu pali chipulumutso.” (Miyambo 11:14) Mawu ameneŵa amagwira ntchito kwa onse, achichepere ndi achikulire omwe. Achinyamata amene amadziŵa zimenezi adzazindikira kuti adakafunikirabe upo wanzeru, popeza kuti akuyang’anizana ndi nkhani zovuta kuposa ndi kale lonse. Ayenera kuzindikira kuti makolo awo okhulupirira ali aphungu okhoza bwino chifukwa chakuti adziŵa zambiri m’moyo ndipo asonyeza nkhaŵa yawo yachikondi kwa zaka zambiri. Chifukwa chake, panthaŵi imeneyi ya moyo, achinyamata anzeru samanyalanyaza makolo awo.

      6. Kodi makolo anzeru ndi achikondi adzakhala ndi maganizo otani polankhulana ndi achinyamata awo?

      6 Kulankhulana komasuka kumatanthauza kuti kholo lidzayesayesa kupatula nthaŵi pamene wachinyamata akufuna kukambitsirana nawo. Ngati muli kholo, tsimikizirani kuti kulankhulana kumakhala komasuka makamaka kumbali yanu. Zimenezi zingakhale zovuta. Baibulo limati pali “mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula.” (Mlaliki 3:7) Pamene wachinyamata wanu aona kuti ndi mphindi yakulankhula, mwina ingakhale mphindi yanu yakutonthola. Mwinamwake mumapatula nthaŵi imeneyi kaamba ka phunziro laumwini, kupumula, kapena kugwira ntchito zapanyumba. Chikhalirechobe, ngati wachinyamata wanu akufuna kukambitsirana nanu, yesani kusintha makonzedwe anu ndi kumvetsera. Ngati simutero, mwina sangayesenso. Kumbukirani chitsanzo cha Yesu. Panthaŵi ina, anali atapatula nthaŵi yakupumula. Koma pamene anthu anafika namzinga kuti amve kwa iye, analeka kupumulako nayamba kuwaphunzitsa. (Marko 6:30-34) Achinyamata ambiri amazindikira kuti makolo awo ali otanganitsidwa kwambiri, koma amafuna chitsimikizo chakuti makolo awo ali okonzeka kuwathandiza pamene awafuna. Chifukwa chake, patulani nthaŵi kaamba ka iwo ndipo khalani womvetsetsa.

      7. Kodi makolo ayenera kupeŵanji?

      7 Yesani kukumbukira mmene zinalili pamene munali wachinyamata, ndipo musataye mzimu wanu wakuseka! Makolo ayenera kusangalala kukhala pamodzi ndi ana awo. Pamene makolo apeza nthaŵi yomasuka, kodi amaigwiritsira ntchito motani? Ngati nthaŵi zonse amafuna kugwiritsira ntchito nthaŵi yawo yomasuka pa zinthu zosaphatikizapo banja lawo, achinyamata awo adzaona zimenezo mwamsanga. Ngati achichepere omasinkhuka aganiza kuti mabwenzi awo akusukulu amawalingalira kuposa mmene makolo awo amachitira, adzakhala ndi mavuto.

      ZIMENE MUYENERA KULANKHULANA NAWO

      8. Kodi ana angaphunzitsidwe motani kufunika kwa kuona mtima, kugwira ntchito zolimba, ndi mayendedwe abwino?

      8 Ngati makolo sanaphunzitsebe ana awo kufunika kwa kuona mtima ndi kugwira ntchito zolimba, iwo ayenera kuyesetsa kuchita zimenezo m’zaka zaunyamata. (1 Atesalonika 4:11; 2 Atesalonika 3:10) Kulinso kofunika kwa iwo kutsimikizira kuti ana awo akukhulupirira ndi mtima wonse za kufunika kwa kukhala ndi moyo wa makhalidwe abwino ndi woyera. (Miyambo 20:11) Kholo limaphunzitsa zambiri za zimenezi mwa kukhala chitsanzo. Monga momwe amuna osakhulupirira ‘angakodwere popanda mawu mwa mayendedwe a akazi’ awo, achinyamata nawonso angaphunzire mapulinsipulo oyenera mwa mayendedwe a makolo awo. (1 Petro 3:1) Chikhalirechobe, chitsanzo mwa icho chokha sichokwanira, pakuti ana amaonanso zitsanzo zina zambiri zoipa ndi zokopa zina zonyengerera za kunja kwa banja. Chotero, makolo osamala amafunikira kudziŵa malingaliro a achinyamata awo pa zimene amaona ndi kumva, ndipo zimenezi zimafuna kukambitsirana kophulapo kanthu.—Miyambo 20:5.

      9, 10. Kodi nchifukwa ninji makolo ayenera kuphunzitsa ana awo ponena za nkhani zakugonana, ndipo angachite motani zimenezi?

      9 Zimenezi nzoona makamaka ponena za nkhani zakugonana. Makolo, kodi mumachita manyazi kukambitsirana zakugonana ndi ana anu? Ngakhale ngati mumachita manyazi, yesetsani kuchita zimenezo, pakuti ngati simutero ana anuwo adzaphunzirabe zimenezo kwa munthu wina. Ngati saphunzira kwa inu, mudziŵa bwanji mwina angaphunzitsidwe zosayenera? M’Baibulo, Yehova samachita manyazi kutchula nkhani zakugonana, ndipo makolonso sayenera kutero.—Miyambo 4:1-4; 5:1-21.

      10 Ubwinonso ngwakuti, Baibulo lili ndi malangizo omveka bwino lomwe pazakugonana, ndipo Watchtower Society yafalitsa chidziŵitso chothandiza chochuluka chosonyeza kuti malangizo ameneŵa akugwirabe ntchito m’dziko lamakonoli. Bwanji osagwiritsira ntchito thandizo limeneli? Mwachitsanzo, bwanji osakambitsirana ndi mwana wanu wamwamuna kapena wamkazi mitu imene ingamuthandize m’buku loyamba ndi lachiwiri lakuti Mayankho a zimene achinyamata amafunsa? Mungakondwe ndi kudabwa ndi zotulukapo zake.

      11. Kodi njira yogwira mtima koposa ndi yotani imene makolo angaphunzitsire ana awo kutumikira Yehova?

      11 Kodi nkhani yofunika koposa imene makolo ndi ana angakambitsirane ndi yotani? Mtumwi Paulo ananena za iyo pamene analemba kuti: “Muwalere [ana anu] m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Ana ayenera kupitiriza kuphunzira za Yehova. Kwenikweni, afunikira kuphunzira kumkonda iye, ndipo ayenera kufuna kumtumikira. Chifukwa chake, chitsanzo chingaphunzitse zambiri. Ngati achichepere omasinkhuka aona kuti makolo awo amakonda Mulungu ‘ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse ndi maganizo awo onse’ ndi kuti zimenezi zikubala zipatso zabwino m’moyo wa makolo awo, angasonkhezereke kuchita chimodzimodzi. (Mateyu 22:37) Mofananamo, ngati achichepere aona kuti makolo awo ali ndi kaonedwe kabwino ka zinthu zakuthupi, akumaika Ufumu wa Mulungu patsogolo, adzathandizidwa kukulitsa mkhalidwe wa maganizo umodzimodzi.—Mlaliki 7:12; Mateyu 6:31-33.

      Chithunzi patsamba 69

      Phunziro la Baibulo lokhazikika nlofunika kwambiri pa banja

      12, 13. Kodi ndi mfundo ziti zimene tiyenera kukumbukira kuti phunziro labanja likhale lachipambano?

      12 Phunziro la Baibulo labanja la mlungu ndi mlungu limathandiza kwambiri kulankhulana ndi achichepere za makhalidwe abwino auzimu. (Salmo 119:33, 34; Miyambo 4:20-23) Kukhala ndi phunziro lokhazikika lotero nkofunika kwambiri. (Salmo 1:1-3) Makolo ndi ana awo ayenera kuzindikira kuti zinthu zina ziyenera kubwera m’mbuyo mwa phunziro labanja, osati mwa njira inayo. Ndiponso, maganizo oyenera ali ofunikira ngati phunziro labanja liti likhale logwira mtima. Tate wina anati: “Chinsinsi nchakuti wotsogoza achititse mkhalidwe wa phunziro labanja kukhala womasuka ndi waulemu—wosangulutsa koma osati wamaseŵera. Mkhalidwe wosapambanitsa nthaŵi zina ungakhale wovuta kupeza, ndipo kaŵirikaŵiri mudzafunikira kuwongolera maganizo a achichepere. Ngati zinthu sizikuyenda bwino kamodzi kapena kaŵiri, limbikirani ndipo yang’anani kutsogolo kunthaŵi yotsatira.” Tate mmodzimodziyu anati m’pemphero lake lotsegulira phunziro, nthaŵi zonse ankapempha mwachindunji thandizo la Yehova kuti onse okhalapo akhale ndi kaonedwe ka zinthu koyenera.—Salmo 119:66.

      13 Kuchititsa phunziro labanja kuli thayo la makolo okhulupirira. Zoona, makolo ena angakhale asali ndi mphatso yakuphunzitsa mwaluso, ndipo kungakhale kovuta kwa iwo kupeza njira zochititsira phunziro labanja kukhala lokondweretsa. Komabe, ngati mumakonda achinyamata anu ‘m’kuchita ndi m’choonadi,’ mudzakhala wofunitsitsa kuwathandiza mwa njira yodzichepetsa ndi yoona mtima kuti apite patsogolo mwauzimu. (1 Yohane 3:18) Angadandaule nthaŵi zina, koma mwachionekere adzaona chikhumbo chanu chachikulu chofuna kuwathandiza.

      14. Kodi Deuteronomo 11:18, 19 angagwiritsiridwe ntchito motani polankhulana zinthu zauzimu ndi achinyamata?

      14 Phunziro labanja sindiyo nthaŵi yokha pamene muyenera kukambitsirana nkhani zofunika zauzimu. Kodi mukukumbukira lamulo la Yehova kwa makolo? Iye anati: “Muzisunga mawu anga awa mumtima mwanu ndi m’moyo mwanu; ndi kuwamanga ngati chizindikiro pamanja panu; ndipo zikhale zapamphumi pakati pa maso anu. Ndipo muziwaphunzitsa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala inu pansi m’nyumba mwanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pakuuka inu pomwe.” (Deuteronomo 11:18, 19; onaninso Deuteronomo 6:6, 7.) Zimenezi sizikutanthauza kuti makolo ayenera nthaŵi zonse kumalalikira kwa ana awo. Koma mutu wa banja wachikondi ayenera nthaŵi zonse kukhala watcheru kuona mipata yokulitsira malingaliro abwino a banja lake pazinthu zauzimu.

      CHILANGO NDI ULEMU

      15, 16. (a) Kodi chilango nchiyani? (b) Kodi ndani ali ndi thayo lakupereka chilango, ndipo ndani ali ndi thayo la kutsimikiza kuti adzachilabadira?

      15 Chilango ndi chiphunzitso chimene chimawongolera, ndipo chimaphatikizapo kulankhulana. Lingaliro lalikulu la liwu la chilango ndilo kuwongolera kuposa kukhaulitsa—ngakhale kuti kukhaulitsa kungakhalepo. Ana anu anafunikira chilango pamene anali aang’ono, ndipo ngakhale kuti tsopano ndi achinyamata, amafunikirabe mtundu winawake wa chilango, mwinamwake chokulirapo. Achinyamata anzeru amadziŵa kuti zimenezi nzoona.

      16 Baibulo limati: “Chitsiru chipeputsa mwambo wa atate wake; koma wosamalira chidzudzulo amachenjera.” (Miyambo 15:5) Tikuphunzira zambiri pa lemba limeneli. Limasonyeza kuti chilango chiyenera kuperekedwa. Wachinyamata ‘sangasamalire chidzudzulo,’ ngati sichiperekedwa. Yehova amapatsa thayo la kupereka chilango kwa makolo, makamaka tate. Komabe, thayo la kumvetsera chilango chimenecho lili kwa wachinyamatayo. Iye adzaphunzira zambiri ndipo adzachita zolakwa zochepekera ngati alabadira chilango chanzeru cha atate wake ndi amake. (Miyambo 1:8) Baibulo limati: “Wokana mwambo adzasauka nanyozedwa; koma wolabadira chidzudzulo adzalemekezedwa.”—Miyambo 13:18.

      17. Kodi ndi kusapambanitsa kotani kumene makolo ayenera kuchita popereka chilango kwa ana awo?

      17 Polanga achinyamata, makolo sayenera kuchita mopambanitsa. Ayenera kupeŵa kukhala oumitsa zinthu kwambiri moti nkuputa ana awo, mwinamwake ngakhale kuchititsa ana awo kuleka kudzidalira. (Akolose 3:21) Komanso makolo sayenera kukhala olekerera moti nkulephera kupatsa ana awo chiphunzitso chofunikira. Kulekerera mwana kwa choncho nkwangozi. Miyambo 29:17 (NW), imati: “Langa mwana wako ndipo adzakupumitsa nadzasangalatsa kwambiri moyo wako.” Komabe, vesi 21 limati: “Ngati munthu alekerera kapolo wake kuyambira paubwana, atakula adzakhala wosayamikira.” Ngakhale kuti vesili likulankhula za kapolo, limagwiranso ntchito kwa wachinyamata aliyense m’banja.

      18. Kodi chilango chili umboni wa chiyani, ndipo kodi nchiyani chimene chimapeŵedwa pamene makolo salephera kupereka chilango choyenerera?

      18 Kwenikweni, chilango choyenera chili umboni wa chikondi cha makolo kwa mwana wawo. (Ahebri 12:6, 11) Ngati ndinu kholo, mumadziŵa kuti nkovuta kupereka chilango choyenerera ndi chanzeru nthaŵi zonse. Pofuna kusungitsa mtendere, kungakhale kosavuta kulola wachinyamata wosamvera kuchita zimene afuna. Komabe, m’kupita kwanthaŵi, kholo limene limatsatira njira imeneyi lidzatuta banja losalamulirika.—Miyambo 29:15; Agalatiya 6:9.

      NTCHITO NDI KUSEŴERA

      19, 20. Kodi ndi motani mmene makolo angachitire mwanzeru ndi nkhani ya zosangulutsa za ana awo achinyamata?

      19 M’nthaŵi zakale ana nthaŵi zonse anafunikira kuthandiza ntchito zapanyumba kapena m’munda. Lerolino achinyamata ambiri amakhala ndi nthaŵi yochuluka yomasuka. Kuti liwapatse zochita m’nthaŵiyo, dziko la malonda limapereka zinthu zochuluka zakuti achite m’nthaŵi yomasuka. Ndipo pokhala kuti dziko silimachirikiza kwambiri miyezo ya Baibulo ya makhalidwe, ngozi ilipo yaikulu.

      20 Chifukwa chake, makolo osamala amasungabe ulamuliro wawo wopanga zosankha ponena za zosangulutsa. Komabe, musaiŵale kuti wachinyamatayo akukula. Chaka chilichonse, mwachionekere adzafuna kuchitiridwa monga wachikulire. Chotero, nkwanzeru kwa kholo kupereka ufulu wowonjezereka wa kudzisankhira zosangulutsa pamene wachinyamata akukula—malinga ngati zosankhazo zikusonyeza kukula msinkhu mwauzimu. Nthaŵi zina, wachinyamata angasankhe nyimbo zosayenera, mabwenzi, ndi zina zotero. Zikachitika zimenezi, muyenera kukambitsirana ndi wachinyamatayo kuti mtsogolo akapange zosankha zabwino.

      21. Kodi kusakhala oumitsa zinthu ponena za nthaŵi ya kusanguluka kungatetezere motani wachinyamata?

      21 Kodi zosangulutsa ziyenera kupatsidwa nthaŵi yaikulu motani? M’maiko ena achinyamata amachititsidwa kukhulupirira kuti angaseŵere mulimonse mmene angafunire. Chotero, wachichepere womasinkhuka angalinganize zochita zake mwanjira yakuti ‘azingosanguluka’ nthaŵi zonse. Makolo ndiwo ayenera kuphunzitsa kuti nthaŵi iyenera kutayiridwanso pa zinthu zina, monga banja, phunziro laumwini, mayanjano ndi anthu okhwima mwauzimu, misonkhano yachikristu, ndi ntchito zapanyumba. Izi zidzaletsa “zokondweretsa za moyo” kutsamwitsa Mawu a Mulungu.—Luka 8:11-15.

      22. Kodi kusanguluka kuyenera kulinganizidwa ndi chiyani m’moyo wa wachinyamata?

      22 Mfumu Solomo anati: “Ndidziŵa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.” (Mlaliki 3:12, 13) Inde, kukondwera kuli mbali ya moyo woyenera. Chimodzimodzi ndi kugwira ntchito zolimba. Achinyamata ambiri lerolino samadziŵa za chikhutiro chimene chimadza ndi kugwira ntchito zolimba kapena ulemu waumwini umene umadza ndi kulimbana ndi vuto ndi kuligonjetsa. Ena samakhala ndi mwaŵi wakuphunzira maluso kapena ntchito imene angachirikizire moyo wawo akakula. Apa mpamene pali ntchito yaikulu kwa kholo. Kodi mudzatsimikizira kuti mwana wanu wapeza mwaŵi umenewu? Ngati mungakhoze kuphunzitsa wachinyamata wanu kuona phindu la kugwira ntchito zolimba ndi kusangalala nayo, iye adzakhala ndi kaonedwe ka zinthu kabwino kamene kadzadzetsa mapindu m’moyo wake wonse.

      KUCHOKERA PAUNYAMATA KUKHALA WACHIKULIRE

      Chithunzi patsamba 70

      Express love and appreciation for your children

      23. Kodi makolo angalimbikitse motani achinyamata awo?

      23 Ngakhale pamene muli ndi mavuto ndi wachinyamata wanu, zimene malemba amanena zimagwirabe ntchito: “Chikondi sichitha nthaŵi zonse.” (1 Akorinto 13:8) Musaleke kusonyeza chikondi chimene mosakayikira muli nacho. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimathokoza mwana aliyense pachipambano chake cha kuthetsa mavuto kapena kugonjetsa zopinga? Kodi ndimagwiritsira ntchito mipata yosonyezera chikondi changa ndi chiyamikiro kwa ana anga, mipatayo isanapite?’ Ngakhale kuti nthaŵi zina pangakhale kumvana molakwa, ngati achinyamata aona kuti mumawakondadi, mwachionekere iwonso adzakukondani.

      24. Kodi ndi pulinsipulo la Malemba lotani limene lili loona limene limagwira ntchito nthaŵi zambiri pankhani ya kulera ana, koma kodi tiyenera kukumbukiranji?

      24 Ndithudi, pamene ana akusinkhukira ku uchikulire, potsirizira pake adzayamba kupanga okha zosankha zazikulu kwambiri. Nthaŵi zina makolo sangakondwere nazo zosankhazo. Bwanji ngati mwana wawo asankha kuleka kutumikira Yehova Mulungu? Zimenezi zingachitikedi. Ngakhale ena a ana auzimu a Yehova anakana uphungu wake ndi kupanduka. (Genesis 6:2; Yuda 6) Ana sali makompyuta, amene angalinganizidwe kungochita zimene tikufuna. Iwo ali zolengedwa zokhala ndi ufulu wakudzisankhira, okhala ndi thayo kwa Yehova pazosankha zimene apanga. Chikhalirechobe, Miyambo 22:6 imagwirabe ntchito nthaŵi zambiri: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.”

      25. Kodi njira yabwino koposa ndi yotani imene makolo angasonyezere chiyamikiro kwa Yehova pa mwaŵi wawo wakukhala makolo?

      25 Motero, sonyezani ana anu chikondi chachikulu. Chitani zonse zomwe mungakhoze kuti mutsatire mapulinsipulo a Baibulo powalera iwo. Perekani chitsanzo chabwino cha makhalidwe aumulungu. Mukatero mudzapatsa ana anu mwaŵi wabwino koposa wakukula ndi kukhala achikulire anzeru, ndi owopa Mulungu. Iyi ndiyo njira yabwino koposa imene makolo angasonyezere chiyamikiro kwa Yehova pa mwaŵi wawo wa kukhala makolo.

      KODI MAPULINSIPULO A BAIBULO AŴA ANGATHANDIZE MOTANI . . . MAKOLO KULERA ACHINYAMATA AWO?

      Kulankhulana nkofunika.—Miyambo 15:22.

      Tiyenera kupenda Mawu a Mulungu nthaŵi zonse.—Salmo 1:1, 2.

      Munthu wochenjera amamvetsera chilango.—Miyambo 15:5.

      Zonse ziŵiri ntchito ndi kuseŵera zili ndi malo ake.—Mlaliki 3:12, 13.

      a Wachinyamata amene tikunena m’nkhani ino ndi mnyamata kapena mtsikana wazaka pafupifupi 13 mpaka 19. Ndizo zaka zaunyamata zimene tikutanthauza.

  • Kodi Muli ndi Wopanduka m’Nyumba?
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
    • Mutu 7

      Kodi Muli ndi Wopanduka m’Nyumba?

      Chithunzi patsamba 76

      1, 2. (a) Kodi Yesu anapereka fanizo lotani kuti agogomezere kupanda chikhulupiriro kwa atsogoleri achipembedzo achiyuda? (b) Kodi ndi mfundo yotani yonena za achinyamata omasinkhuka imene tingaphunzire m’fanizo la Yesu?

      MASIKU oŵerengeka imfa yake isanachitike, Yesu anafunsa gulu la atsogoleri achipembedzo achiyuda funso lodzutsa maganizo. Iye anati: “Nanga mutani? Munthu anali nawo ana aŵiri; nadza iye kwa woyamba, nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito ku munda wampesa. Koma iye anakana, nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pake analapa mtima napita. Ndipo anadza kwa winayo, natero momwemo. Ndipo iye anavomera, nati, Ndipita mbuye; koma sanapita. Ndani wa aŵiriwo anachita chifuniro cha atate wake?” Atsogoleri achiyudawo anayankha kuti: “Woyambayo.”—Mateyu 21:28-31.

      2 Yesu pano anali kugogomezera kusakhulupirika kwa atsogoleri achiyuda. Iwo anali ngati mwana wachiŵiri uja, akumalonjeza kuchita chifuniro cha Mulungu koma nalephera kusunga pangano lawo. Koma makolo ambiri adzazindikira kuti fanizo la Yesu linazikidwa pa kudziŵa bwino kwake za moyo wa banja. Monga momwe anasonyezera bwino lomwe, kaŵirikaŵiri kumakhala kovuta kudziŵa zimene achichepere amalingalira kapena kudziŵiratu zimene adzachita. Wachichepere angachititse mavuto ochuluka m’zaka zake zakusinkhuka komabe nkukula ndi kukhala wachikulire wanzeru ndi wolemekezeka. Izi nzimene tiyenera kukumbukira pamene tikambitsirana vuto la kupanduka kwa achinyamata.

      KODI WOPANDUKA NDI WOTANI?

      3. Kodi nchifukwa ninji makolo sayenera kufulumira kutcha mwana wawo wopanduka?

      3 Nthaŵi ndi nthaŵi, mwina mwamva za achinyamata amene amapandukira makolo awo kotheratu. Mwinamwake mukudziŵa banja limene lili ndi wachinyamata wooneka kukhala wosatheka kulamulira. Komabe, nthaŵi zina nkovuta kudziŵa kaya ngati mwana ali wopanduka weniweni. Ndiponso, kungakhale kovuta kudziŵa chifukwa chake ana ena amapanduka pamene ena—ngakhale m’banja limodzimodzi—samatero. Ngati makolo aona kuti mwina mmodzi wa ana awo akufuna kukhala wopanduka weniweni, kodi ayenera kuchitanji? Kuti tiyankhe, choyamba tiyenera kulongosola amene ali wopanduka.

      4-6. (a) Kodi wopanduka ndi wotani? (b) Kodi makolo ayenera kukumbukiranji ngati mwana wawo wachinyamata samamvera nthaŵi ndi nthaŵi?

      4 Mwachidule, wopanduka ndi munthu amene amapitiriza kusamvera mwadala kapena amene amatsutsa ndi kunyalanyaza ulamuliro. Ndithudi, ‘utsiru umangika mumtima mwa mwana.’ (Miyambo 22:15) Chotero ana onse panthaŵi ina amatsutsa ulamuliro wa makolo ndi wina uliwonse. Zimenezi zimachitika makamaka m’nthaŵi ya kukula kuthupi ndi m’maganizo kotchedwa zaka zakusinkhuka. Kusintha m’moyo wa munthu aliyense kumachititsa kupsinjika maganizo, ndipo zaka zakusinkhuka zili zamasinthidwe okhaokha. Mtsikana kapena mnyamata wanu womasinkhuka ali panjira yochoka ku ubwana kupita ku uchikulire. Pachifukwa chimenechi, mkati mwa zaka zakusinkhuka, makolo ena ndi ana awo akhala asakumvana. Kaŵirikaŵiri, makolo mwachibadwa amayesa kugwira kusinthako kuti kuyende pang’onopang’ono, pamene achinyamata amafuna kukufulumiza.

      5 Wachinyamata amene ali wopanduka amafulatira malango a makolo ake. Komabe, kumbukirani kuti machitidwe oŵerengeka a kusamvera samapanga mwana kukhala wopanduka. Ndipo ponena za nkhani zauzimu, ana ena poyamba angasonyeze chidwi chochepa m’choonadi cha Baibulo ndipo mwina sangachisonyeze konse, koma angakhale osapanduka. Monga kholo, musafulumire kugamula ponena za mwana wanu.

      6 Kodi achichepere onse amapandukira ulamuliro wa makolo awo m’zaka zawo zakusinkhuka? Ayi, osati onse. Ndithudi, umboni umasonyeza kuti ndi achinyamata oŵerengeka chabe amene amasonyeza kupanduka kwakukulu m’zaka zawo zakusinkhuka. Komabe, bwanji za mwana amene amapanduka mouma khosi ndi mopitirizabe? Kodi nchiyani chimene chingayambitse kupanduka koteroko?

      ZOCHITITSA KUPANDUKA

      7. Kodi ndi motani mmene mkhalidwe wausatana ungasonkhezerere mwana kupanduka?

      7 Chochititsa kupanduka chachikulu ndicho mkhalidwe wausatana wa dzikoli. “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Dziko lokhala m’mphamvu ya Satana lapanga makhalidwe owononga amene Akristu ayenera kulimbana nawo. (Yohane 17:15) Ochuluka a makhalidwewo ali oluluzika, angozi, ndi odzala ndi zisonkhezero zoipa lerolino kuposa kale. (2 Timoteo 3:1-5, 13) Ngati makolo samaphunzitsa ana awo, kuwachenjeza, ndi kuwatetezera, anawo angatengeke mosavuta ndi “mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera.” (Aefeso 2:2) Chogwirizana ndi zimenezi ndicho chisonkhezero cha mabwenzi. Baibulo limati: “Mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Mofananamo, iye amene ayanjana ndi aja omwerekera ndi mzimu wa dzikoli mwachionekere adzasonkhezeredwa ndi mzimu umenewo. Achichepere amafunikira chithandizo cha nthaŵi zonse kuti azindikire kuti kumvera mapulinsipulo aumulungu ndiko maziko a njira yabwino koposa ya moyo.—Yesaya 48:17, 18.

      8. Kodi ndi zinthu zotani zimene zingachititse mwana kupanduka?

      8 China chochititsa kupanduka chingakhale mkhalidwe wa panyumba. Mwachitsanzo, ngati kholo limodzi ndi chidakwa, ngati limagwiritsira ntchito anamgoneka, kapena ngati ndi lachiwawa kwa kholo linalo, kaonedwe ka moyo ka wachinyamata kangapotoke. Ngakhale m’nyumba zimene ziliko pamtendere, mwana angapanduke pamene aona kuti makolo ake samamsamalira. Komabe, si nthaŵi zonse pamene achinyamata amapanduka chifukwa cha zisonkhezero zakunja. Ana ena amafulatira malango a makolo awo mosasamala kanthu za kukhala ndi makolo amene amagwiritsira ntchito mapulinsipulo aumulungu ndi amene amawatetezera, makamaka ku dziko lowazinga. Chifukwa ninji? Mwinamwake chifukwa cha chinthu chinanso chochititsa mavuto athu—kupanda ungwiro kwa anthu. Paulo anati: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Adamu anali wopanduka wadyera, ndipo anasiyira ana ake onse choloŵa cha tsoka. Achichepere ena amangodzifunira kupanduka, monga momwe linachitira kholo lawo lakalero.

      ELI WOLEKERERA NDI REHABIAMU WOUMITSA ZINTHU

      9. Kodi ndi kupambanitsa kotani polera mwana kumene kungamsonkhezere kupanduka?

      9 Chinthu chinanso chimene chimachititsa achinyamata kupanduka ndicho lingaliro losayenera la makolo la kaleredwe ka ana. (Akolose 3:21) Makolo ena odera nkhaŵa amaumitsira zinthu kwambiri ana awo ndi kuwalanga mopambanitsa. Ena ali olekerera, osapereka zitsogozo zofunikira zimene zingatetezere achinyamata awo anthete. Nthaŵi zina kumakhala kovuta kupeza malo apakati pa mbali ziŵirizo zopambanitsa. Ndipo ana osiyanasiyana amakhala ndi zosoŵa zosiyanasiyana. Wina angafunikire chiyang’aniro chokulira kuposa wina. Komabe, zitsanzo ziŵiri za m’Baibulo zidzathandiza kusonyeza ngozi zake za kuchita mopambanitsa pakuumitsa zinthu kapena pakulekerera.

      10. Ngakhale kuti mwachionekere Eli anali mkulu wa ansembe wokhulupirira, kodi nchifukwa ninji anali kholo losachita bwino?

      10 Eli, mkulu wa ansembe wa Israyeli wakale anali tate. Anatumikira kwa zaka 40, mosakayikira anali ndi chidziŵitso chachikulu cha Chilamulo cha Mulungu. Mwachionekere, Eli anachita ntchito zake zaunsembe mokhulupirika ndithu ndipo ayenera kuti anaphunzitsa bwino lomwe Chilamulo cha Mulungu kwa ana ake, Hofeni ndi Pinehasi. Komabe, Eli anali wokondera kwambiri kwa ana ake. Hofeni ndi Pinehasi anali ansembe otumikira pazochitika, koma anali amuna “oipa,” okonda chabe kukhutiritsa zokhumba zawo ndi zilakolako zawo zachisembwere. Komabe, pamene anachita zauchisi m’malo opatulika, Eli analephera kulimbika mtima kuti awachotse paudindo wawo. Anangowadzudzula mofeŵa. Mwa kulekerera kwake, Eli analemekeza ana ake kuposa Mulungu. Chotulukapo, ana ake anapanduka pakulambira Yehova koyera ndipo nyumba yonse ya Eli inagwera m’tsoka.—1 Samueli 2:12-17, 22-25, 29; 3:13, 14; 4:11-22.

      11. Kodi makolo angatengepo phunziro lanji pa chitsanzo choipa cha Eli?

      11 Ana a Eli anali kale achikulire pamene izi zinachitika, koma mbiri yakale imeneyi imasonyeza ngozi ya kulephera kupereka chilango. (Yerekezerani ndi Miyambo 29:21.) Makolo ena angaone monga kulekerera ndiko chikondi, akumalephera kupereka malamulo omvekera bwino, osasintha, ndi anzeru ndi kuona kuti akutsatiridwa. Amanyalanyaza kupereka chilango chachikondi, ngakhale pamene mapulinsipulo aumulungu aswedwa. Chifukwa cha kulekerera kotero, ana awo angaleke kuwopa ulamuliro wa makolo kapena wina uliwonse.—Yerekezerani ndi Mlaliki 8:11.

      12. Kodi ndi cholakwa chotani chimene Rehabiamu anachita posonyeza mphamvu yake?

      12 Rehabiamu ali chitsanzo cha njira ina yakuchita mopambanitsa ndi ulamuliro. Iye anali mfumu yomaliza ya ufumu wogwirizana wa Israyeli, koma sanali mfumu yabwino. Rehabiamu analoŵa ufumu m’dziko limene anthu ake anali osakhutira chifukwa cha mtolo woikidwa pa iwo ndi atate wake, Solomo. Kodi Rehabiamu anasonyeza chifundo? Ayi. Pamene nthumwi zinampempha kuchepetsako malamulo ena otsendereza, analephera kulabadira uphungu wanzeru wochokera kwa aphungu ake achikulire nalamula kuti goli la anthu lilemetsedwe koposerapo. Kuuma khosi kwake kunabutsa chipanduko cha mafuko khumi akumpoto, ndipo ufumuwo unagaŵanika paŵiri.—1 Mafumu 12:1-21; 2 Mbiri 10:19.

      13. Kodi makolo angapeŵe motani kuchita cholakwa cha Rehabiamu?

      13 Makolo angatengepo maphunziro ofunika pa nkhani ya m’Baibulo ya Rehabiamu. Amafunikira ‘kufuna Yehova’ m’pemphero ndi kupenda njira zawo zolerera ana mogwirizana ndi mapulinsipulo a Baibulo. (Salmo 105:4) “Nsautso iyalutsa wanzeru,” amatero Mlaliki 7:7. Malire olingaliridwa bwino amapatsa achinyamata omasinkhuka mpata wakukula pamene akuwatetezera ku ngozi. Koma ana sayenera kukhala mumkhalidwe wokhwimitsa kwambiri ndi wopanikiza kwakuti alephera kukulitsa mlingo woyenera wa kudziimira paokha ndi kudzidalira. Pamene makolo ayesa kukhala achikatikati, osapereka ufulu wopambanitsa kapena ziletso zokhwimitsa, achinyamata ambiri sadzakhala ndi chikhoterero cha kupanduka.

      KUKWANIRITSA ZOFUNIKA ZAZIKULU KUNGALETSE KUPANDUKA

      Chithunzi patsamba 83

      Mwachionekere, ana amakula kukhala okhazikika bwino ngati makolo awathandiza kulimbana ndi mavuto apaunyamata

      14, 15. Kodi makolo ayenera kuona motani kakulidwe ka mwana wawo?

      14 Ngakhale kuti makolo amakondwera kuona mwana wawo akukula mwakuthupi akumakhala wachikulire, iwo angade nkhaŵa pamene mwana wawo womasinkhukayo ayamba kudziimira payekha akumaleka kuwadalira kwambiri. Mkati mwa nyengo yakusintha imeneyi, musadabwe ngati mwana wanu wachinyamata nthaŵi zina akhala wouma khosi kapena wosagwirizana nanu. Kumbukirani kuti cholinga cha makolo achikristu chiyenera kukhala kulera mwana kuti akule ndi kukhala Mkristu wokhwima, wokhazikika, ndi wanzeru.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 13:11; Aefeso 4:13, 14.

      15 Ngakhale kuti zingakhale zovuta, makolo amafunikira kuleka chizoloŵezi cha kuyankha mwaukali ku pempho lililonse la mwana womasinkhuka lofuna ufulu wokulirapo. Mwana afunikira kukula mwa njira yabwino monga munthu payekha. Ndithudi, pausinkhu wocheperapo, achinyamata ena amayamba kukhala ndi maganizo achikulire. Mwachitsanzo, Baibulo limanena za Mfumu yachichepere Yosiya kuti: “Akali mnyamata [pafupifupi zaka 15], anayamba kufuna Mulungu wa Davide.” Mwachionekere, wachinyamata wachitsanzo chabwino ameneyu anali ndi nzeru zauchikulire.—2 Mbiri 34:1-3.

      16. Pamene ana apatsidwa thayo lowonjezereka, kodi ayenera kudziŵa chiyani?

      16 Komabe, ufulu umadza ndi thayo. Chifukwa chake, lolani mwana wanu yemwe akukhwimayo kuyang’anizana ndi zotulukapo za zosankha zake ndi machitidwe ake. Lamulo lakuti, “chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta,” limagwira ntchito kwa achinyamata ndi achikulire omwe. (Agalatiya 6:7) Ana simungawatetezere kosatha. Koma bwanji ngati mwana wanu afuna kuchita chinthu china chosaloleka konse? Monga kholo losamala, muyenera kunena kuti, “Ayi.” Ndipo, pamene kuli kwakuti mungalongosole zifukwa zake, palibe chimene chiyenera kusintha ayi wanu kukhala inde. (Yerekezerani ndi Mateyu 5:37.) Komabe, yesani kunena “Ayi” wanu mwanjira yofatsa ndi yoyenerera, pakuti “mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo.”—Miyambo 15:1.

      17. Kodi ndi zosoŵa zina ziti za wachinyamata zimene kholo liyenera kukwaniritsa?

      17 Achichepere amafunikira chitetezero cha chilango cha nthaŵi zonse ngakhale kuti nthaŵi zina samakonda kwenikweni kutsatira ziletso ndi malamulo. Kumakhala kokwiyitsa ngati malamulo amasinthidwa kaŵirikaŵiri, malinga ndi mmene kholo likulingalirira panthaŵiyo. Ndiponso, ngati achinyamata alandira chilimbikitso ndi chithandizo chofunikira, chakuti alimbane ndi manyazi, kapena kupanda chidaliro chaumwini, mwachionekere adzakula ali okhazikika. Achinyamata amayamikiranso pamene makolo awo awadalira.—Yerekezerani ndi Yesaya 35:3, 4; Luka 16:10; 19:17.

      18. Kodi pali mfundo zoona zotani zolimbikitsa ponena za achinyamata?

      18 Makolo angatonthozedwe podziŵa kuti pamene mtendere, bata, ndi chikondi zilimo m’banja, nthaŵi zonse ana amakula bwino. (Aefeso 4:31, 32; Yakobo 3:17, 18) Inde, achichepere ambiri akula bwino ngakhale kuti analeredwa m’mikhalidwe yoipa, m’mabanja auchidakwa, achiwawa, kapena a zisonkhezero zina zoipa, ndipo akula kukhala achikulire abwino. Chifukwa chake, ngati muchititsa mkhalidwe wapanyumba kukhala wabwino moti ana anu achinyamata akumva kukhala otetezereka ndipo akudziŵa kuti mumawakonda ndi kuwasamalira—ngakhale ngati chichirikizo chimenecho chingatsagane ndi ziletso zoyenerera ndi chilango chogwirizana ndi mapulinsipulo a Malemba—nkothekera kwambiri kuti adzakula ndi kukhala achikulire amene mudzawanyadira.—Yerekezerani ndi Miyambo 27:11.

      PAMENE ANA AGWERA M’VUTO

      19. Pamene kuli kwakuti makolo ayenera kuphunzitsa mwana njira imene ayenera kuyendamo, kodi ndi thayo lotani limene limakhala pa mwanayo?

      19 Kulera ana kwabwino kumathandiza kwambiri. Miyambo 22:6 imati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” Komabe, bwanji nanga za ana amene amakhala ndi mavuto aakulu mosasamala kanthu kuti ali ndi makolo abwino? Kodi zimenezi nzotheka? Inde. Mawu a mwambo umenewu ayenera kutengedwa pamodzi ndi mavesi ena amene amagogomezera thayo la mwana la ‘kumvera’ makolo ndi kuwalabadira. (Miyambo 1:8) Makolo onse aŵiri limodzi ndi mwanayo ayenera kugwirizana pakugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Malemba kuti pakhale chigwirizano cha banja. Ngati makolo ndi ana samagwirizana, padzakhala zovuta.

      20. Pamene ana alakwa chifukwa cha kusalingalira bwino, kodi ndi kachitidwe kotani kamene kangakhale koyenera kwa makolo?

      20 Kodi makolo ayenera kuchita motani pamene mwana wawo wachinyamata alakwa ndi kugwera m’vuto? Pamenepo, makamaka wachichepereyo afunikira chithandizo. Ngati makolo akumbukira kuti akuchita ndi wachibwana, kudzakhala kosavuta kwambiri kukaniza chikhoterero cha kuchita mopambanitsa. Paulo anapatsa chilangizo anthu okhwima mumpingo kuti: “Ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso.” (Agalatiya 6:1) Makolo angatsatire njira imodzimodziyo pamene achita ndi wachichepere amene alakwa chifukwa cha kusalingalira bwino. Pamene akufotokoza momveka bwino chifukwa chake kachitidwe kake kanali kolakwa ndi mmene angapeŵere kubwerezanso cholakwacho, makolo ayenera kumveketsa bwino kuti chimene anachita ndicho choipa, osati wachichepereyo.—Yerekezerani ndi Yuda 22, 23.

      21. Mwa kutsatira chitsanzo cha mpingo wachikristu, kodi makolo ayenera kuchita motani ngati ana awo achita tchimo lalikulu?

      21 Bwanji ngati cholakwa cha wachichepereyo nchachikulu kwambiri? Pamenepo mwanayo amafunikira chithandizo chapadera ndi chilangizo chaluso. Pamene munthu amene ali chiŵalo cha mpingo achita tchimo lalikulu, amalimbikitsidwa kulapa ndi kufikira akulu kaamba ka chithandizo. (Yakobo 5:14-16) Pamene alapa, akulu amathandizana naye kuti abwezeretse mkhalidwe wake wauzimu. M’banja, thayo lakuthandiza wachinyamata wolakwa lili la makolo, ngakhale kuti angafunikire kukambitsirana nkhaniyo ndi akulu. Ndithudi, iwo sayenera kuyesa kubisa bungwe la akulu machimo aakulu alionse ochitidwa ndi mmodzi wa ana awo.

      22. Mwa kutsanzira Yehova, kodi makolo adzayesa kukhala ndi maganizo otani ngati mwana wawo achita cholakwa chachikulu?

      22 Vuto lalikulu loloŵetsamo ana a munthuwe limakhala lopereka chiyeso kwambiri. Pokhala ovutitsidwa maganizo, makolo angafune kuwopseza mwaukali mwana wawo wopandukayo, koma zimenezi angangoipidwa nazo. Kumbukirani kuti mtsogolo mwa wachichepereyo mungadalire panjira imene mumachitira naye panthaŵi yovuta imeneyi. Kumbukiraninso kuti Yehova anali wokonzekera kukhululukira pamene anthu ake anapambuka pachabwino—ngati akanalapa. Tamverani mawu ake achikondi: “Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.” (Yesaya 1:18) Nchitsanzo chabwino chotani nanga kwa makolo!

      23. Ngati mmodzi wa ana awo wachita tchimo lalikulu, kodi makolo ayenera kuchita motani, ndipo ayenera kupeŵanji?

      23 Chotero, yesani kulimbikitsa mwana wopandukayo kusintha njira yake. Funani uphungu wanzeru kwa makolo achidziŵitso ndi akulu a mpingo. (Miyambo 11:14) Yesani kusachita mwasontho ndi kunena kapena kuchita zinthu zimene zidzakuchititsa kukhala kovuta kwa mwana wanu kubwerera kwa inu. Peŵani mkwiyo ndi kuipidwa kosalamulirika. (Akolose 3:8) Musataye mtima ndi kuleka mofulumira. (1 Akorinto 13:4, 7) Pamene kuli kwakuti mumadana nacho choipa, peŵani kukhala wouma mtima ndi kuipidwa ndi mwana wanu. Chofunika koposa, makolo ayenera kuyesayesa kupereka chitsanzo chabwino ndi kusunga chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu.

      KUCHITA NDI WOPANDUKA WENIWENI

      24. Kodi ndi mkhalidwe womvetsa chisoni wotani umene nthaŵi zina umakhalapo m’banja lachikristu, ndipo kholo liyenera kuchita motani?

      24 Nthaŵi zina kumakhala koonekeratu kuti wachichepere watsimikiza mtima kupanduka ndi kukaniratu makhalidwe achikristu. Pamenepo muyenera kutembenuzira chisamaliro chanu pa kusunga kapena kumangirira moyo wa banja wa otsalawo. Samalani kuti musapereke maganizo anu onse kwa wopandukayo, ndi kunyalanyaza ana enawo. M’malo mwakuyesa kubisa vutolo kwa ena m’banja, kambitsiranani nawo nkhaniyo pamlingo woyenera ndi mwanjira yolimbikitsa.—Yerekezerani ndi Miyambo 20:18.

      25. (a) Mwa kutsatira chitsanzo cha mpingo wachikristu, kodi makolo ayenera kuchitanji ngati mwana akhala wopanduka weniweni? (b) Kodi makolo ayenera kukumbukiranji ngati mmodzi wa ana awo apanduka?

      25 Mtumwi Yohane anati ponena za munthu amene akhala wopanduka wosabwezeka mumpingo: “Musamlandire iye kunyumba, ndipo musamlankhule.” (2 Yohane 10) Makolo angakuone kukhala kofunikira kuchita zimenezo kwa mwana wawowawo ngati ali wamkulu ndipo ali wopandukiratu. Ngakhale kuti kachitidweko kangakhale kovuta ndi kosautsa maganizo, nthaŵi zina kali kofunika kuti enawo m’banja atetezereke. Muyenera kutetezera ndi kuyang’anira banja lanu nthaŵi zonse. Chifukwa chake, pitirizani kusunga malire a makhalidwe omvekera bwino ndi otsimikizika, komabe oyenerera. Lankhulanani ndi ana enawo. Khalani ndi chidwi cha kufuna kudziŵa mmene akuchitira kusukulu ndi mumpingo. Ndiponso, achititseni kudziŵa kuti ngakhale kuti simukuvomereza machitidwe a mwana wopandukayo, simukumuda iye. Danani ndi mchitidwe woipa osati mwanayo. Pamene ana aŵiri a Yakobo anadzetsa temberero pabanja chifukwa cha mchitidwe wawo wankhalwe, Yakobo anatemberera mkwiyo wawo wachiwawa, osati ana enieniwo.—Genesis 34:1-31; 49:5-7.

      26. Kodi makolo oona mtima angapeze kuti chitonthozo ngati mmodzi wa ana awo apanduka?

      26 Mungamve kukhala wamlandu pa zimene zachitika pabanja. Koma ngati mwapemphero mwachita zonse zomwe mukanakhoza, mwa kutsatira uphungu wa Yehova bwino lomwe, simufunikira kudziimba mlandu mopambanitsa. Pezani chitonthozo mwa kudziŵa kuti palibe aliyense amene angakhale kholo langwiro, koma inuyo munayesetsa moona mtima kukhala kholo labwino. (Yerekezerani ndi Machitidwe 20:26.) Kukhala ndi wopanduka weniweni m’banja nkopweteka mtima kwambiri, koma ngati zichitika kwa inu, khalani wotsimikiza kuti Mulungu amamvetsetsa ndipo sadzasiya konse atumiki ake okhulupirika. (Salmo 27:10) Chotero yesetsani kuchititsa nyumba yanu kukhala malo achitetezo chauzimu kwa ana alionse otsalawo.

      27. Pokumbukira fanizo la mwana woloŵerera, kodi makolo a mwana wopanduka ayenera kukhala ndi chiyembekezo cha chiyani nthaŵi zonse?

      27 Ndiponso, simuyenera konse kutaya chiyembekezo. Zoyesayesa zanu zoyambirira zakuphunzitsa koyenera m’kupita kwa nthaŵi zingakhudze mtima wa mwana woloŵererayo ndi kumchititsa kulingaliranso bwino. (Mlaliki 11:6) Mabanja achikristu ambiri akhala ndi chokumana nacho monga chanu, ndipo ena aona ana awo opanduka akubwerera, mofanana kwambiri ndi tate uja wa m’fanizo la Yesu la mwana woloŵerera. (Luka 15:11-32) Zimenezi zingachitikenso kwa inu.

      KODI MAPULINSIPULO A BAIBULO AŴA ANGATHANDIZE MOTANI . . . KHOLO KULETSA CHIPANDUKO CHACHIKULU M’BANJA?

      Popanda chithandizo, mwana angawonongedwe ndi mzimu wa dziko.—Miyambo 13:20; Aefeso 2:2.

      Makolo amafunikira kukhala osapambanitsa pakuika ziletso kapena pakulekerera.—Mlaliki 7:7; 8:11.

      Mchitidwe wolakwa uyenera kusamaliridwa, koma mwa mzimu wa chifatso.—Agalatiya 6:1.

      Awo amene amachita machimo aakulu ‘angachiritsidwe’ ngati alapa ndi kulandira chithandizo.—Yakobo 5:14-16.

      ULULANI ZAKUKHOSI

      Achinyamata omasinkhuka amakhala ndi zikayikiro ndi nkhaŵa zimene zimadza ndi ufulu wowonjezereka. Angakayikire za kukhoza kwawo kuima paokha m’dziko lino. Zili monga kuti anali kuyesa kuyenda pamsewu woterera. Inu achichepere, ululirani makolo anu zimene mumaopa ndi nkhaŵa zanu zimene muli nazo. (Miyambo 23:22) Kapena ngati mulingalira kuti makolo anu akukupanikizani kwambiri, lankhulani nawo za kufunika kwanu kupatsidwa ufulu wokulirapo. Linganizani kulankhula nawo panthaŵi imene muli womasuka bwino ndipo iwo sali otanganitsidwa. (Miyambo 15:23) Tcherani khutu bwinobwino kwa wina ndi mnzake.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena