Ndinachirimika Paziyeso Zoopsa
YOSIMBIDWA NDI ÉVA JOSEFSSON
Kagulu kathu kochepa kanasonkhana m’boma la Újpest ku Budapest, Hungary, pamsonkhano waufupi wopitira mu utumiki wachikristu. Munali mu 1939, patakhala nthaŵi yochepa kuti Nkhondo Yadziko II iyambike, ndipo ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa ku Hungary. Amene anali kuphunzitsa za m’Baibulo poyera m’masikuwo nthaŵi zambiri anali kugwidwa.
POPEZA kuti inali nthaŵi yanga yoyamba kuchita nawo ntchitoyi, ndinada nkhaŵa. Mbale wina wachikristu wachikulire anandicheukira nandiuza kuti: “Éva, usachite mantha. Kutumikira Yehova ndiko mwayi waukulu koposa umene munthu angakhale nawo.” Mawu otonthoza ndi olimbikitsa amenewo anandithandiza kuchirimika paziyeso zambiri zoopsa.
Kubadwira Mumtundu Wachiyuda
Ndinali mwana wamkulu pa ena onse m’banja lathu lachiyuda la ana asanu. Amayi sanakhutiritsidwe ndi Chiyuda, ndipo anayamba kufufuza zipembedzo zina. Panthaŵiyi anakumana ndi Erzsébet Slézinger, mkazi wina wachiyuda amene anali kufunafunanso choonadi cha Baibulo. Erzsébet anatenga Amayi kuti akaonane ndi a Mboni za Yehova, ndipo chotsatirapo chake, inenso ndinakhala ndi chidwi chachikulu ndi ziphunzitso za m’Baibulo. Posapita nthaŵi ndinayamba kugaŵana ndi ena zimene ndinaphunzira.
Pamene ndinakwanitsa zaka 18 zakubadwa m’chilimwe cha mu 1941, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova Mulungu mwa ubatizo mu Mtsinje wa Danube. Amayi anabatizidwanso nthaŵi yomweyo, koma Atate sanali kutsatira chikhulupiriro chathu chachikristu chatsopanocho. Patangopita nthaŵi yochepa nditabatizidwa, ndinalingalira zoyamba kuchita upainiya, kutanthauza kuti kuchita utumiki wa nthaŵi zonse. Ndinafunikira kukhala ndi njinga, choncho ndinayamba kugwira ntchito m’chipinda china chofufuziramo zasayansi m’fakitale ina yaikulu yowomba nsalu.
Kuyambika kwa Ziyeso
Anazi analanda Hungary, ndipo fakitale imene ndinali kugwirako ntchitoyo inayamba kuyang’aniridwa ndi Ajeremani. Tsiku lina antchito onse anaitanidwa kuti akaonekere pamaso pa akuluakulu kuti akapereke lumbiro loti adzakhala okhulupirika kwa Anazi. Anatiuza kuti ngati sitichita zimenezo tidzapeza mavuto aakulu. Pamwambo wina pamene tinafunikira kutamanda Hitler, ndinaimirira mwaulemu koma sindinachite nawo zimenezo. Anandiitanira kuofesi tsiku lomwelo, kundipatsa malipiro anga, ndipo anandichotsa ntchito. Popeza kuti ntchito zinali zosoŵa, ndinakayikira zoti ndingakwanitse malingaliro anga ochita upainiya. Komabe, tsiku lotsatira ndinapeza ntchito yatsopano imene inali ndi malipiro ochulukirapo.
Tsopano ndinaona kuti cholinga changa chochita upainiya chinatheka. Ndinali ndi apainiya anzanga angapo, ndipo mpainiya mnzanga womaliza anali Juliska Asztalos. Tinali kugwiritsira ntchito Baibulo lathu lokha mu utumiki, ndipo tinalibe mabuku ogaŵira. Ngati tikumana ndi anthu okondwerera, tinali kupanga maulendo obwereza ndi kuwabwereka mabuku.
Nthaŵi zonse ine ndi Juliska tinali kusintha gawo loti tifole. Tinali kuchita zimenezi chifukwa chakuti wansembe atazindikira kuti tinali kufikira ‘nkhosa zake,’ anali kulengeza kutchalitchi kuti ngati a Mboni za Yehova awachezera ayenera kukamuuza kapena kukanena kupolisi. Anthu achikondi akatiuza za chilengezo chimenechi, tinali kupita kugawo lina.
Tsiku lina ine ndi Juliska tinafikira mnyamata wina wamng’ono amene anasonyeza chidwi. Tinagwirizana naye za ulendo wobwereza kuti tidzambwereke mabuku oti aziŵerenga. Koma pamene tinabwererako tinapezako apolisi, ndipo anatigwira ndi kutitengera kupolisi ya ku Dunavecse. Mnyamatayo anamgwiritsira ntchito monga nyambo yotikolera. Pamene tinafika kupolisiko, tinaona wansembe uja ali komweko ndipo tinadziŵa kuti iye anali nawo m’gulu la anthu amene anatigwirawo.
Chiyeso Changa Choopsa Koposa
Kupolisiko, anandimeta tsitsi langa lonse, ndipo anandiimiritsa wamaliseche pamaso pa apolisi ngati 12. Iwo anandifunsa mafunso, ncholinga choti adziŵe amene anali mtsogoleri wathu ku Hungary. Ndinafotokoza kuti tinalibe mtsogoleri winanso koma Yesu Kristu yekha. Kenaka anandimenya koopsa ndi ndodo zawo, koma sindinapereke abale anga achikristu.
Atatha zimenezo, anandimanga miyendo ndipo anaika manja anga pamutu panga ndi kuwamanganso. Kenaka, onsewo kupatulapo wapolisi mmodzi, anandigona molandizana. Anandimanga kwambiri moti zipsera za pamikono yanga zinakhalapobe mpaka zaka zitatu pambuyo pake. Anandivulaza kwambiri moti anandisunga m’chipinda chapansi kwa milungu iŵiri mpaka pamene zilonda zanga zambiri zinapola.
Nthaŵi ya Mpumulo
Kenaka ananditengera kundende ya ku Nagykanizsa, kumene kunali a Mboni za Yehova ambiri. Zaka ziŵiri zosangalatsa zinatsatirapo mosasamala kanthu zoti tinali m’ndende. Tinali kuchita misonkhano yathu yonse mobisa, ndipo tinali kuchita zonse monga mpingo. Tinalinso ndi mwayi waukulu wochita umboni wamwamwayi. Munali m’ndende imeneyi mmene ndinakumana ndi Olga Slézinger, mlongo wakuthupi wa Erzsébet Slézinger, mkazi amene anatiphunzitsa choonadi cha Baibulo ine ndi amayi anga.
Podzafika mu 1944 Anazi a ku Hungary anatsimikiza mtima zofafaniza Ayuda a ku Hungary, monga momwe anali kuwapheranso m’madera ena amene analanda. Tsiku lina anafika kwa ine ndi Olga. Anatilongedza m’sitima yapamtunda yonyamula ng’ombe, ndipo titayenda ulendo wovuta kwambiri kupyola Czechoslovakia, tinafika kumene anali kutitengerako chakummwera kwa Poland—msasa wopherako anthu wa Auschwitz.
Kupulumuka ku Auschwitz
Ndinali kukhala womasuka ndikakhala ndi Olga. Iye anali wanthabwala ngakhale paziyeso. Pamene tinafika ku Auschwitz, tinakaonekera pamaso pa munthu wankhanza kwambiri wotchedwa Dr. Mengele, amene ntchito yake inali yolekanitsa anthu obwera kumene amene anali oti sangathe kugwira ntchito ndi anthu amphamvu. Anthu osatha kugwira ntchitowo anali kuwatumiza kuzipinda zophera za mpweya wakupha. Pamene anafika pa ife, Mengele anafunsa Olga kuti, “Uli ndi zaka zingati?”
Motsimikiza, ndiponso ataphethira mwanthabwala, iye anayankha kuti, “20.” Koma zenizeni nzakuti anali ndi zaka zoŵirikiza kaŵiri zimene anatchulazo. Koma Mengele anaseka ndipo anamuuza kuti apite kudzanja lamanja ndipo anapulumuka.
Andende onse a ku Auschwitz anaikidwa zizindikiro pazovala zawo zakundende—Ayuda anawaika chizindikiro cha Nyenyezi ya Davide, ndipo a Mboni za Yehova anawaika chizindikiro chofiirira changodya zitatu. Pamene anafuna kusoka chizindikiro cha Nyenyezi ya Davide pazovala zathu, tinafotokoza kuti tinali a Mboni za Yehova ndipo tinafuna chizindikiro changodya zitatucho. Tinasankha zimenezi osati chifukwa chakuti tinachita manyazi kuti tinabadwira mumtundu wachiyuda ayi, koma chifukwa chakuti tsopano tinali a Mboni za Yehova. Anayesa kutikakamiza kuti tilole chizindikiro chachiyuda mwa kutiponda zidyali ndiponso kutimenya. Koma tinachirimikabe mpaka pamene anavomereza kuti ndife a Mboni za Yehova.
M’kupita kwa nthaŵi, ndinakumana ndi mng’ono wanga Elvira, amene anali wocheperako ndi zaka zitatu. Banja lathu lonse la anthu asanu ndi aŵiri analitengera ku Auschwitz. Ine ndekha ndi Elvira ndiye anativomereza kuti tingagwire ntchito. Atate, Amayi, ndi abale athu atatu anafera m’zipinda za mpweya wakupha. Panthaŵiyo Elvira sanali Mboni, ndipo sitinali kukhalira pamodzi mumsasamo. Iye anapulumuka, anasamukira ku United States, nakhala Mboni ku Pittsburgh, Pennsylvania, ndipo pambuyo pake anafera komweko mu 1973.
Kupulumuka m’Misasa Ina
M’nyengo yachisanu cha mu 1944/45, Ajeremani analingalira zosamutsa anthu onse okhala ku Auschwitz, popeza kuti Arasha anali kuyandikira. Choncho, anatisamutsira ku Bergen-Belsen kumpoto kwa Germany. Titangofika kumene, ine ndi Olga anatitumiza ku Braunschweig. Kumeneko anatiuza kuti tithandizire kuchotsa zidutswa za zinthu zimene zinasakazidwa ndi mabomba a asilikali a maiko Ogwirizana. Ine ndi Olga tinakambitsirana za nkhaniyo. Popeza kuti sitinali kudziŵa bwino kuti kaya ntchitoyo ingaswe uchete wathu, tonse aŵirife tinapangana zoti tisagwire nawo.
Chosankha chathucho chinautsa mapiri pachigwa. Tinamenyedwa ndi zikoti zachikopa ndipo kenaka anatitengera ku kagulu kowombera ndi mfuti. Anatipatsa mphindi imodzi yoti tilingalirenso bwino za nkhaniyo, ndipo anatiuza kuti ngati sitisintha malingaliro athu, iwo adzatiwombera. Tinawauza kuti sitikufunikira nthaŵi yoti tilingalire za nkhaniyo chifukwa chakuti tinali titatsimikiza kale mtima. Komabe, popeza kuti mkulu wa pamsasapo panalibe, ndiponso chifukwa chakuti iye yekhayo ndiye anali ndi ulamuliro wopereka lamulo lakupha, iwo analephera kutipha.
Titangochoka pamenepo anatikakamiza kuti tiimirire pabwalo la msasawo tsiku lonse lathunthu. Asilikali aŵiri otenga mfuti ndiwo anali kutilondera, ndipo anali kulandirana patapita maola aŵiri alionse. Sanali kutipatsa chakudya chilichonse, ndipo tinavutika kwambiri chifukwa cha kuzizira, popeza kuti unali mwezi wa February. Panapita mlungu umodzi akutizunza motero, koma mkulu uja sanatulukirebe. Choncho, anatikweza m’lole, ndipo tinadabwa kuti anatitengeranso ku Bergen-Belsen.
Panthaŵiyo thanzi la ine ndi Olga linafooka. Tsitsi langa lambiri linasosoka ndipo ndinali kudwala malungo. Ndinali kugwira ntchito kokha chifukwa cha kuyesetsa kwambiri. Msuzi wa kabichi ndi kachiphathi kamodzi ka buledi tsiku lililonse sizinali zokwanira. Koma tinafunikirabe kugwira ntchito chifukwa chakuti awo amene analephera kutero anali kuphedwa. Alongo achijeremani amene anali kugwira nane ntchito m’khichini anali kundithandiza kuti ndizipumako. Pamene alonda anali kuyendera, alongowo anali kundichenjeza, ndipo ine ndinali kuimirira pathebulo logwirirapo ntchito, kungokhala ngati ndikugwira ntchito mwakhama.
Tsiku lina Olga anali wotopa kwambiri kotero kuti sanathe kupita kumalo ake antchito, ndipo atatero sitinamuonenso. Bwenzi langa ndi mnzanga wolimba mtima anandisiya, munthu amene anandithandiza kwambiri m’miyezi yovuta imeneyo m’misasa. Monga wotsatira wodzozedwa wa Ambuye wathu Yesu Kristu, iye ayenera kuti analandira mphotho yake yakumwamba nthaŵi yomweyo.—Chivumbulutso 14:13.
Kumasulidwa ndi Moyo Wapambuyo Pake
Nkhondo itatha m’May 1945 ndiponso titamasulidwa, ndinali wofooka kwambiri moti sindinasangalale kuti goli la ozunza linathyoka; ndiponso sindinatsagane ndi magalimoto amene anali kutenga omasulidwa kupita nawo kumaiko amene anali ofunitsitsa kuwalandira. Ndinakhalira m’chipatala kwa miyezi itatu kuti ndipezenso nyonga. Pambuyo pake ananditengera ku Sweden, umene unakhala mudzi wanga watsopano. Nditangofika, ndinayamba kuyanjana ndi abale ndi alongo anga achikristu ndipo m’kupita kwa nthaŵi ndinayambanso kusamalira chuma changa chamtengo wapatali cha utumiki wakumunda.
Mu 1949, ndinakwatiwa ndi Lennart Josefsson, amene anatumikira kwa zaka zambiri monga woyang’anira woyendayenda wa Mboni za Yehova. Iyenso anaponyedwako m’ndende chifukwa cha kumamatirabe chikhulupiriro chake m’nthaŵi ya Nkhondo Yadziko II. Tinayamba moyo wathu wokhalira pamodzi monga apainiya pa September 1, 1949, ndipo anatitumiza kuti tikatumikire kutauni ya Borås. M’zaka zathu zoyambirira kumeneko, tinali kuchita mokhazikika maphunziro khumi a Baibulo mlungu uliwonse ndi anthu okondwerera. Tinali ndi chimwemwe choona mpingo wa ku Borås ukukula mpaka kukhala mipingo itatu pazaka zisanu ndi zinayi, ndipo tsopano kuli mipingo isanu.
Sindinathe kuchita upainiya kwa nthaŵi yaitali chifukwa chakuti mu 1950 tinakhala makolo a mwana wamkazi, ndipo zaka ziŵiri pambuyo pake, mwana wamwamuna. Choncho, ndinali ndi mwayi waukulu wophunzitsa ana athu choonadi chamtengo wapatali chimene mbale wokondedwa wa ku Hungary anandiphunzitsa pamene ndinali ndi zaka 16 zokha, ndipo choonadi chimenecho nchakuti: “Kutumikira Yehova ndiwo mwayi waukulu koposa umene munthu angakhale nawo.”
Ndikamakumbukira za moyo wanga wakumbuyoku, ndimazindikira kuona kwa zimene wophunzira Yakobo analemba pamene anatikumbutsa za chipiriro cha Yobu kuti: “Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Ngakhale kuti inenso ndinavutika ndi ziyeso zoopsa, ndadalitsidwa kwambiri ndi ana aŵiri, anzawo a muukwati, ndiponso adzukulu asanu ndi mmodzi—onsewo ali olambira Yehova. Kuwonjezera pamenepo, ndili ndi ana ndi zidzukulu zauzimu zambirimbiri, ndipo ena a iwo akutumikira monga apainiya ndi amishonale. Tsopano chiyembekezo changa chachikulu nchakuti ndidzaonane ndi okondedwa amene akugona muimfa ndi kuwakupatira pamene aukitsidwa kuchokera kumanda awo achikumbukiro.—Yohane 5:28, 29.
[Chithunzi patsamba 31]
Mu utumiki ku Sweden itatha Nkhondo Yadziko II
[Chithunzi patsamba 31]
Ine ndi mwamuna wanga