Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 222-tsamba 229
  • Kuvutika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuvutika
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ngati Wina Anena Kuti—
  • Chilimbikitso kwa Anthu Amene Akuvutika
    Nsanja ya Olonda—2003
  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola kuti Anthu Azivutika?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Amavutika?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kupirira Mavuto Kuli Ndi Ubwino Wake
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 222-tsamba 229

Kuvutika

Tanthauzo: Chokumana nacho chimene munthu amakhala nacho pamene akupirira zopweteka kapena nsautso. Kuvutikako kungakhale kwakuthupi, kwamaganizo, kapena kwamalingaliro. Zinthu zambiri zingachititse kuvutika; mwachitsanzo, chivulazo chochitidwa ndi nkhondo ndi umbombo wa zamalonda, mikhalidwe yoipa yobadwa nayo, matenda, ngozi, “masoka achilengedwe,” zinthu zankhalwe zonenedwa kapena kuchitidwa ndi ena, zipsinjo za ziŵanda, kuzindikira kuyandikira kwa tsoka, kapena kupusa kwa munthu mwiniyo. Kuvutika kumeneku kumachititsidwa ndi zovutitsa zosiyanasiyana zimenezi kudzalingaliridwa panopa. Komabe, munthu angavutike chifukwa cha kuzindikira kwake mikhalidwe ya anthu ena kapena nkhaŵa yake yaikulu pakuwona mkhalidwe wopanda umulungu.

Kodi nchifukwa ninji Mulungu amalola kuvutika?

Kodi ndani amene kwenikweni amakuchititsa?

Anthu ndiwo amachititsa ambiri a mavutowo. Amamenya nkhondo, amachita upandu, amaipitsa malo, kaŵirikaŵiri amachita mabizinesi mu mkhalidwe wosonkhezeredwa ndi umbombo mmalo mwa kudera nkhaŵa ndi anthu anzawo, ndipo nthaŵi zina amadziloŵetsa m’zizoloŵezi zimene iwo amadziŵa kuti zingakhale zovulaza thanzi lawo. Pamene achita zinthu zimenezi, amavulaza anzawo ndi iwo eni. Kodi kuyenera kuyembekezeredwa kuti anthu akakhala osayambukiridwa ndi zotulukapo za zimene iwo amachita? (Agal. 6:7; Miy. 1:30-33) Kodi kuli kwanzeru kuimba Mulungu mlandu wa zinthu izi zimene anthu iwo eni amachita?

Satana ndi ziŵanda zake alinso ndi liwongo. Baibulo limavumbula kuti mavuto ochuluka ngochititsidwa ndi chisonkhezero cha mizimu yoipa. Kuvutika kochuluka kumene anthu ambiri amaimba nako mlandu Mulungu sikumachokera kwa iye konse.—Chiv. 12:12; Mac. 10:38; wonaninso tsamba 354, 355, pamutu wakuti “Satana Mdyerekezi.”

Kodi kuvutika kunayamba motani? Kupendedwa kwa zoyambitsa kumasumikizitsa maganizo pamakolo anthu oyamba aumunthu, Adamu ndi Hava. Yehova adawalenga ali angwiro naŵaika m’mikhalidwe ya paradaiso. Ngati iwo akadamvera Mulungu, sakadadwala konse kapena kufa. Akanasangalala ndi moyo wangwiro kosatha. Kuvutika sikunali mbali ya chifuno cha Yehova kwa anthu. Koma Yehova anawuza Adamu momvekera bwino kuti kupitirizabe kwake kukhala ndi zimene Iye adawapatsa kunadalira pa kumvera. Mwachiwonekere, iwo anafunikira kupuma, kudya, kumwa, ndi kugona kuti apitirizebe kukhala ndi moyo. Ndipo iwo anafunikira kusunga malamulo amakhalidwe abwino a Mulungu kuti akasangalale ndi moyo mokwanira ndi kukhala ndi moyo umenewo kosatha. Koma iwo anasankha kulondola njira ya iwo eni, kuika miyezo ya iwo eni ya chabwino ndi choipa, ndipo motero anapatuka kwa Mulungu Mpatsi wa Moyo. (Gen. 2:16, 17; 3:1-6) Tchimo linatsogolera ku imfa. Adamu ndi Hava anabala ana atachimwa, ndipo iwo sakanapitirizira kwa ana awowo chimene iwo panthaŵiyo analibe. Onse anabadwira mu uchimo, okhala ndi zikhoterero za kuchita cholakwa, zofooka zimene zikatsogolera kumatenda, choloŵa cha uchimo chimene potsirizira pake chikachititsa imfa. Chifukwa chakuti munthu aliyense padziko lapansi lerolino anabadwira mu uchimo, tonsefe timavutika m’njira zosiyanasiyana.—Gen. 8:21; Aroma 5:12.

Mlaliki 9:11 amanena kuti ‘nthaŵi ndi zochitika zosawonedweratu’ zirinso ndi chiyambukiro pa zimene zimatichitikira. Tingavulale, osati chifukwa chakuti Mdyerekezi amakuchititsa mwachindunji kapena chifukwa chakuti munthu wina aliyense watero, koma chifukwa chakuti mwangozi tiri pamalowo panthaŵi yolakwika.

Kodi nchifukwa ninji Mulungu samachitapo kanthu kudzetsa mpumulo kwa anthu? Kodi nchifukwa ninji ife tonse tiyenera kuvutika kaamba ka chinthu chimene Adamu anachita?

M’Baibulo, Mulungu amatiuza mmene tingapeŵere kuvutika kochuluka. Iye wapereka uphungu wabwino koposa ponena za kukhala ndi moyo. Pamene ugwiritsiridwa ntchito, umadzaza miyoyo yathu ndi tanthauzo, ukumachititsa moyo wa banja wachimwemwe, nutiloŵetsa m’mayanjano athithithi ndi anthu amene amakondanadi, ndipo umatitetezera ku zizoloŵezi zimene zingadzetse kuvutika kochuluka kosafunikira kwakuthupi. Ngati tinyalanyaza chithandizo chimenecho, kodi ndikolungama kuimba mlandu Mulungu kaamba ka vuto limene timadzidzetsera ife eni ndi ena?—2 Tim. 3:16, 17; Sal. 119:97-105.

Yehova wapanga makonzedwe a kuthetsa kuvutika konse. Iye analenga anthu aŵiri oyamba ali angwiro, ndipo mwachikondi anapanga makonzedwe alionse kuchitira kuti moyo ukakhale wokondweretsa kwa iwo. Pamene iwo anafulatira Mulungu dala, kodi Mulungu anali ndi thayo la kuloŵeramo kotero kuti atetezere ana awo kuziyambukiro zimene makolo awo adachita? (Deut. 32:4, 5; Yobu 14:4) Monga momwe timadziŵira bwino lomwe, anthu okwatirana angakhale ndi zisangalalo za kubala ana, koma iwo alinso ndi mathayo. Makhalidwe ndi zochita za makolo zimayambukira ana awo. Komabe, Yehova, anatumiza Mwana wake wokondedwa kwambiri kudziko lapansi, monga chisonyezero cha kukoma mtima kwachifundo kodabwitsa kudzapereka moyo wake monga dipo, kupereka mpumulo kwa ana a Adamu amene moyamikira akasonyeza chikhulupiriro m’kakonzedwe kameneka. (Yoh. 3:16) Monga chotulukapo, mwaŵi ngwotseguka kwa anthu okhala ndi moyo lerolino kupeza chimene Adamu anataya—moyo waumunthu wangwiro, wopanda mavuto, m’paradaiso pa dziko lapansi. Ndikakonzedwe kooloŵa manja chotani nanga mmene kameneko kaliri!

Wonani tsamba 122-124, pamutu wakuti “Dipo.”

Koma kodi nchifukwa ninji Mulungu wa chikondi angalole kuvutika kupitirizabe kwa nthaŵi yaitali motere?

Kodi tapindula chifukwa chakuti wakulola kufikira tsopano? “Ambuye sazengereza nalo lonjezano monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Pet. 3:9) Ngati Mulungu akanapha msanga Adamu ndi Hava, pambuyo pa uchimo wawo, palibe aliyense wa ife akanakhalako lerolino. Ndithudi ife sitikafuna zimenezo. Ndiponso, ngati Mulungu panthaŵi ina yapambuyo pake akanawononga onse amene anali ochimwa, ife sitikanabadwa. Chenicheni chakuti Mulungu walola dziko lauchimoli kukhalako kufikira lerolino, chatipatsa mwaŵi wa kukhala ndi moyo ndi kuphunzira njira zake, kupanga masinthidwe ofunikawo m’miyoyo yathu, ndi kudzichititsa ife eni kupindula ndi makonzedwe ake achikondi a moyo wamuyaya. Kutipatsa kwa Yehova mwaŵi kuli umboni wachikondi chake chachikulu. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu ali ndi nthaŵi yoikika yakuwononga dongosolo loipa iri ndipo adzatero mwamsanga.—Hab. 2:3; Zef. 1:14.

Mulungu angathe ndipo adzathetsa chivulazo chonse chimene chingadze pa atumiki ake m’dongosolo lino la zinthu. Mulungu sindiye amene amachititsa kuvutika. Koma kupyolera mwa Yesu Kristu, Mulungu adzaukitsa akufa, kuchiritsa nthenda zonse za anthu omvera, kufafaniza chizindikiro chirichonse cha uchimo, ndipo ngakhale kuchititsadi chisoni choyambacho kuzimiririka m’maganizo mwathu.—Yoh. 5:28, 29; Chiv. 21:4; Yes. 65:17.

Nthaŵi imene yapita yakhala yofunika kuthetsa nkhani zimene zinadzutsidwa m’Edene. Kaamba ka maumboni, wonani tsamba 354, 355, ndiponso 184-187.

Kwakukulukulu tikulakalaka kupeza mpumulo. Koma pamene Mulungu achitapo kanthu, kuyenera kukhala mmalo mwa onse okonda chilungamo, osati ochepekera okha. Mulungu alibe tsankhu.—Mac. 10:34.

Zitsanzo: Kodi sizowona kuti kholo la chikondi lingalole mwana kuchitidwa opareshoni yopweteka chifukwa cha zotulukapo zopindulitsa zimene zingatulukemo? Ndiponso, kodi sizowona kuti “zothetsera zamwamsanga” za matenda opweteka kaŵirikaŵiri zimakhala kokha zachiphamaso? Kaŵirikaŵiri nthaŵi yowonjezereka ikufunika kuthetseratu chochititsacho.

Kodi nchifukwa ninji Mulungu sanakhululukire Adamu ndipo mwakutero kutetezera kuvutika kowopsa kumene anthu akumana nako?

Kodi zimenezo zikanatetezeradi mavuto, kapena mmalo mwake, kodi zimenezo zikadapangitsa Mulungu kukhala ndi liwongo lake? Kodi nchiyani chimene chimachitika pamene atate amanyalanyaza dala zolakwa za ana ake mmalo mwakuchitapo kanthu mwamphamvu kupereka chilango? Kaŵirikaŵiri ana amaloŵetsedwa mumpangidwe umodzi wa cholakwa ndiyeno wina, ndipo mbali yaikulu ya liwongolo iri ndi atate.

Mofananamo, ngati Yehova akanakhululukira tchimo ladala la Adamu, kukanapangitsadi Mulungu kukhala ndi mbali m’cholakwacho. Zimenezo sizikanawongolera konse mikhalidwe padziko lapansi. (Yerekezerani ndi Mlaliki 8:11.) Ndiponso, kukanachititsa mtonzo kwa ana ake aungelo, ndipo kukanatanthauza kuti panalibe maziko enieni akuyembekezerera ubwino uli wonse. Koma mkhalidwe wotero sukanachitika konse, chifukwa chakuti chilungamo ndicho maziko osasunthika a Ulamuliro wa Yehova.—Sal. 89:14.

Kodi nchifukwa ninji Mulungu amalola ana kubadwa ndi nthenda zowopsa ndi kupunduka maganizo?

Mulungu samachititsa kupunduka kotero. Iye analenga anthu aŵiri oyamba ali angwiro, ndi mphamvu ya kubala ana angwiro m’chifanizo cha iwo eni.—Gen. 1:27, 28.

Talandira choloŵa cha uchimo kuchokera kwa Adamu. Choloŵa chimenecho chiri ndi kuthekera kwa kuchititsa kupunduka kwa kuthupi ndi kwa maganizo. (Aroma 5:12; kaamba ka maumboni owonjezereka wonani tsamba 223.) Choloŵa cha uchimo chimenechi chiri nafe kuyambira panthaŵi ya kukhaliridwa pakati m’mimba. Ndicho chifukwa chake Mfumu Davide analemba kuti: “Mayi wanga anandilandira m’zoipa.” (Sal. 51:5) Adamu akadapanda kuchimwa, pakanakhala zikhoterero zabwino zokha zakuzipereka. (Kaamba ka ndemanga pa Yoh. 9:1, 2, wonani tsamba 176.)

Makolo angavulaze ana awo osabadwa—mwachitsanzo, mwakumwa mankhwala oledzeretsa kapena mwa kusuta fodya m’nthaŵi ya kukhala ndi pakati. Ndithudi, sizowona kuti m’chochitika chirichonse amayi kapena atate amachititsa mwana kubadwa wopunduka kapena wodwala.

Yehova mwachikondi amapitirizira kwa ana mapindu a nsembe ya dipo ya Kristu. Mwakusonyeza kukoma mtima kwa makolo amene mokhulupirika amatumikira Mulungu, iye amawona ana awo achichepere kukhala oyera. (1 Akor. 7:14) Zimenezi zimasonkhezera makolo owopa Mulungu kukhala osamala ponena za mkhalidwe wa kwa Mulungu, chifukwa cha kudera nkhaŵa ndi ana awo. Kwa achichepere amene ali osinkhuka mokwanira kusonyeza chikhulupiriro ndi kusonyeza kumvera malamulo a Mulungu, Yehova amawapatsa mwaŵi wakukhala ndi mkhalidwe wovomerezeka monga atumiki ake. (Sal. 119:9; 148:12, 13; Mac. 16:1-3) Nkokondweretsa kuzindikira kuti Yesu, amene anali chisonyezero changwiro cha Atate ŵake, anasonyeza chikondwerero chapadera mu ubwino wa achichepere ngakhale kuukitsa mwana kwa akufa. Ndithudi iye adzapitirizabe kuchita zimenezo monga Mfumu Yaumesiya.—Mat. 19:13-15; Luka 8:41, 42, 49-56.

Kodi nchifukwa ninji Mulungu amalola “masoka achilengedwe,” amene amachititsa kuwonongeka kwakukulu kwa chuma ndi moyo?

Mulungu sakuchititsa zivomezi, mikuntho, maliyambwe, zirala, ndi kuphulika kwa volokano zimene kaŵirikaŵiri zimatulutsidwa m’nyuzi lerolino. Iye samagwiritsira ntchito zimenezi kupereka chilango pa anthu ena. Kwakukulukulu, zimenezi zimachititsidwa ndi mphamvu zachilengedwe zimene zakhala zikugwira ntchito chiyambire kulengedwa kwa dziko lapansi. Baibulo lidaneneratu zivomezi zazikulu ndi kupereŵera kwa zakudya kaamba ka tsiku lathu, koma zimenezo sizitanthauza kuti Mulungu kapena Yesu ndiwo amene amazichititsa, monga momwedi ziriri kuti katswiri wodziŵa nyengo sindiye amene amachititsa kuchitika kwa nyengo imene iye amaneneratu. Chifukwa chakuti zimenezo zikuchitika limodzi ndi zinthu zina zonse zonenedweratu m’chizindikiro chachiungwe cha mapeto a dongosolo iri la zinthu, ndizo mbali ya umboni wakuti madalitso a Ufumu wa Mulungu ayandikira.—Luka 21:11, 31.

Kaŵirikaŵiri anthu ali ndi liwongo lalikulu la chivulazo chochitidwa. Mwanjira yotani? Ngakhale pamene apatsidwa chenjezo lokwanira, anthu ambiri amakana kuchoka m’chigawo changozi kapena kulephera kulabadira kofunikako.—Miy. 22:3; yerekezerani ndi Mateyu 24:37-39.

Mulungu angathe kulamulira mphamvu zachilengedwe zotero. Iye anapatsa Yesu Kristu mphamvu ya kutontholetsa namondwe pa Nyanja ya Galileya, monga chitsanzo cha zimene Iye adzachitira anthu mu Ufumu Wake Waumesiya. (Marko 4:37-41) Mwakufulatira Mulungu, Adamu anakana kuloŵerera kotero kwa Mulungu mmalo mwake ndi ana ake. Opatsidwa moyo mkati mwa Kulamulira Kwaumesiya kwa Kristu adzapatsidwa chisamaliro chotero chachikondi, chisamaliro chimene boma lokha lopatsidwa ulamuliro ndi Mulungu lingapereke.—Yes. 11:9.

Kodi anthu amene akuvutika ndi nsautso akulangidwa ndi Mulungu chifukwa cha zoipa?

Awo amene amaswa miyezo ya Mulungu ya kukhala ndi moyo amavutika ndi zotulukapo zoipa. (Agal. 6:7) Nthaŵi zina amatuta mwamsanga zotulukapo zoŵaŵa kwambiri. M’zochitika zina, iwo angawonekere kwa nthaŵi yaitali kukhala akulemerera. Mosiyana, Yesu Kristu, amene sanachite cholakwa konse, anachitiridwa nkhalwe moipitsitsa ndi kuphedwa. Chotero, m’dongosolo lino la zinthu kulemelera sikuyenera kuwonedwa kukhala umboni wa dalitso la Mulungu, ndiponso nsautso siyenera kulingaliridwa kukhala umboni wa mkwiyo wake.

Pamene Yobu anatayikiridwa chuma chake nakanthidwa ndi nthenda yonyansa, zimenezo sizinali chifukwa cha mkwiyo wa Mulungu. Baibulo limanena momvekera bwino kuti wochititsa anali Satana. (Yobu 2:3, 7, 8) Koma mabwenzi amene anadza kudzazonda Yobu anasonyeza kuti mkhalidwe wa Yobu uyenera kutsimikizira kuti anali atachita kanthu kena kolakwa. (Yobu. 4:7-9, 15:6, 20-24) Yehova anawadzudzula, akumati: “Mkwiyo wanga wakuyakirani . . . kuti simunandinenera choyenera monga ananena mtumiki wanga Yobu.”—Yobu 42:7.

Ndithudi, anthu oipa, angalemelere kwakanthaŵi. Asafu analemba kuti: “Ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuwona mtendere wa oipa. Savutika monga anthu ena. Achita zaphwete nalankhula moipa za kusautsa: alankhula modzitama. Tapenyani, woipa ndi awa; ndipo pokhazikika chikhazikikire awonjezerapo pachuma chawo.” Sal. 73:3, 5, 8, 12.

Tsiku la kuimbidwa mlandu ndi Mulungu lidzadza. Panthaŵiyo iye adzalanga oipa, kuwawononga kosatha. Miyambo 2:21, 22 imati: “Pakuti owongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzadzulidwamo.” Pamenepo owongoka mtima, ambiri amene akumana ndi nsautso, adzasangalala ndi thanzi langwiro ndi kukhala ndi gawo lokwanira la zinthu zochuluka za dziko lapansi.

Ngati Wina Anena Kuti—

‘Kodi nchifukwa ninji Mulungu amalola kuvutika konseku?’

Mungayankhe kuti: ‘Imeneyo iri nkhani yodetsa nkhaŵa kwambiri kwa tonsefe. Taimani ndikufunseni, Kodi nchiyani chimene chikupangitsani kuifunsa lerolino?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘(Gwiritsirani ntchito mfundo za pa tsamba 222-225.)’ (2) ‘(Tchulani malemba ena amene akusonyeza mpumulo kuchokera ku mkhalidwe weniweni umene wadzetsa mavuto kwa anthu alionse paokha.)’

Kapena munganene kuti: (ngati nkhaŵa yawo iri chifukwa cha zisalungamo za dziko): ‘Baibulo limasonyeza chifukwa chake pali mikhalidweyi lerolino. (Mlal. 4:1; 8:9) Kodi mukudziŵa kuti limasonyezanso chimene Mulungu adzachita kutibweretsera mpumulo? (Sal. 72:12, 14; Dan. 2:44)’

Kuthekera kwina: ‘Mwachiwonekere inu mumakhulupirira Mulungu. Kodi mumakhulupirira kuti Mulungu ndiye chikondi? . . . Kodi mumakhulupirira kuti iye ngwanzeru ndi kuti ngwamphamvu yonse? . . . Pamenepa ayenera kukhala ndi zifukwa zabwino zololera kuvutika. Baibulo limasonyeza chimene zifukwa zimenezo ziri. (Wonani tsamba 222-225.)’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena