Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 1/1 tsamba 25-29
  • Kupirira Kwachimwemwe mu Middle East

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupirira Kwachimwemwe mu Middle East
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • “Mbali Yabwino”
  • “Dzina la Yehova Linapulumutsa Moyo Wanga”
  • “Chisamaliro cha Yehova Chinatizinga”
  • Chithandizo Cha m’Nthaŵi Yatsoka Chiri Pantchito!
  • “Kodi Ndinu Anthu Amtundu Wotani?”
Nsanja ya Olonda—1991
w91 1/1 tsamba 25-29

Kupirira Kwachimwemwe mu Middle East

Lipoti lochititsa chidwili likuchokera kwa Mboni za Yehova mu Lebanon

CHAKA chathu chautumiki cha 1990 chinayamba ndi zochitika zachiwawa zakuphulitsa mabomba m’Beirut. Ndiyeno panakhala bata kuchokera kumapeto kwa September 1989 mpaka January 1990.

Mkati mwa miyezi imeneyo chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 2,659 chinachitiridwa lipoti (mu November), kuyerekezera ndi 2,467 m’chaka chautumiki cha 1989. Anthu makumi anayi mphambu anayi anabatizidwa, ndipo mwezi uliwonse avareji ya anthu 65 anakhala ndi phande muutumiki wa upainiya wothandiza. Kwanthaŵi yoyamba, maphunziro Abaibulo oposa 2,000 anachitiridwa lipoti, ndipo tinayamba kuyembekezera zomwe zikakwaniritsidwa mtsogolo.

Koma nkhondo inaulikanso Kum’mawa kwa Beirut, kumene kuli mipingo yambiri, ndipo abale athu ambirimbiri anathaŵira kumbali zina za dzikoli. Kwa masiku ambiri sitinagwirizane nayo mipingo yokhala mmalo okanthidwawo, ndipo malipoti autumiki wakumunda anali osakwanira. Komabe, abale omwe anabalalikanawo anakagwirizana ndi mipingo yokhala m’malo omwe anathaŵirako, ndipo ntchito ya kunyumba ndi nyumba inapitirizabe ndi zotulukapo zabwino m’dziko lonseli. Panthaŵiyi, nyumba zambiri za abale athu zinatenthedwa kapena kuwonongedwa ndi mabomba ophulitsidwawo. Mlongo mmodzi anaphedwa.

Tinayang’ana kwa Yehova mwachidaliro kaamba ka thandizo ndi chitsogozo. Apainiya olimba mtima anadzipereka kupititsa zofunika zauzimu, limodzi ndi zakudya ndi madzi, kwa abale athu okhala m’madera olaliridwawo. Atasonkhezeredwa ndi kukonda kwawo Yehova ndi abalewo, iwo anaikadi moyo wawo pachiswe mwakudutsa misewu imene inadzalidwa mabomba. Umboni wabwino unaperekedwa pamene anthu anawona mabanja a abale athu akulandira thandizo. Iwo anawona zimene chikondi chenicheni chingachite pamene onse ali ogwirizana m’kulambiridwa kwa Mulungu mmodzi wowona, Yehova.​—Yohane 13:34, 35; 15:13.

Mkati mwa chaka chautumikicho, abalewo sanaphonye nlimodzi lomwe la makope amagazini athu. Monga momwe zinaliri kale ndi Nsanja ya Olonda, magazini a Galamukani! anayamba kufalitsidwa Mchiluya panthaŵi imodzi ndi Achingelezi, kuyambira ndi kope la January 8, 1990. Mboni ndi anthu okondwerera anasangalala kwambiri. Kunali kokondweretsanso kuwona zotulutsidwa zatsopano Mchiluya, monga ngati brosha ya Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu? ndi mabuku a The Bible​—God’s Word or Man’s? ndi Bukhu Langa La Nkhani za Baibulo.

Mphatso zauzimu zimenezi zinaperekedwa mosasamala kanthu za kutsekedwa kwa mafakitale ambiri ndi malo ena antchito m’Beirut. Mkhalidwe wachuma wadziko lonselo ngwoipa. Malo ambiri alibe magetsi, madzi, matelefoni. Tsopano, talolani kuti ena a abale athu asimbe mmene apezera chimwemwe ngakhale mkati mwakulimbana ndi mavuto ankhondo imene yakhala ikupitirizabe kwa zaka 15.

“Mbali Yabwino”

Mbale wina m’Beirut akulemba kuti: “Choyamba, ndikupereka chithokozo chochokera mumtima kwa Yehova chifukwa chakuti watisunga otetezereka mkati mwa gulu lake la kulambira kowona mosasamala kanthu za mikhalidwe yovuta yonse imene takhala tikuyang’anizana nayo. Mkati mwa zochitika zaposachedwapa, ndidali ndi zokumana nazo zimene zinandipatsa chimwemwe, ndipo ndimazilingalira kukhala mbali yabwino ya nkhondoyo.

“Mkati mwakuphulitsa mabomba kwamphamvu, tinakhala pansi pamakwerero a nyumba limodzi ndi anthu omwe tinalumikizana nawo nyumba, popeza kuti ndiwo malo otetezereka koposa mkati mwakuphulitsa mabomba. Tinalankhula nawo mosalekeza ponena za Ufumu wa Mulungu kukhala yankho lokha ku mavuto a anthu, ndipo tinapemphera mobwerezabwereza kwa Mulungu wathu, Yehova. Izi zinadziŵika kwa onse.

“Nthaŵi zina kuphulitsa mabombako kunatenga masiku angapo, ndipo sitinkapita kumisonkhano. Chotero ndinabwera ndi magazini a Nsanja ya Olonda ndikuwaphunzira tiri khale pamakwereropo. Zimenezi zinadzutsa chikondwerero cha anansi athu. Ena a iwo sankalankhula nafe chifukwa chakuti ndife Mboni za Yehova. Koma pamene nyumba yathu inakanthidwa ndi bomba, iwo anazizwa ndi chikondi chimene abale athu anachisonyeza. Tsopano iwo anafuna kulankhula nafe. Ichi chinatikhozetsa kuwagaŵira masabusikripishoni a Galamukani!

“Zokumana nazo zimenezi zinandipangitsa kutsimikiza maganizo kupitirizabe kulankhula ponena za chowonadi. Yehova ngwoyenerera kulambira kwathu konse ndi ulemu wathu wonse ndi ulemerero wonse.”

“Dzina la Yehova Linapulumutsa Moyo Wanga”

Mbale wa ku Mpingo wa Ras Beirut akusimba kuti: “Mkazi wanga, anyamata athu aang’ono aŵiri, ndi ine tinayamba tsiku lathu ndi uminisitala wa kunyumba ndi nyumba m’dera lakumadzulo kwa Beirut. Masana, tinali ndi msonkhano wa m’Chingelezi panyumba panga. Pofika 6:30 p.m. kunali kutada. Anthu okha omwe anapezeka m’makwalala anali amuna okhala ndi zida. Mabomba ankalakatika ngati mvula. Athu ambiri okhala m’nyumba yathu anathaŵa. Munalibe kaya madzi kapena magetsi. Kenaka tinamva kugogoda pakhomo.

“Poganizira kuti angakhale mmodzi wa anansi athu akufuna madzi kapena mkate, mkazi wanga anatsegula chitseko. Anangowona amuna anayi okhala ndi zida ali chiriri. Iwo analozetsa mfuti zawo kwa mkazi wanga ndikufunsa za ine monditchula dzina. Mlungu umenewo amuna asanu ndi anayi anatengedwa m’nyumba zawo mwanjira imeneyi naphedwa mwamsanga. Pamene amuna okhala ndi zidawo anandiwona, analozetsa mfuti zawo za otomatiki kumutu wanga nandilamulira kunka nawo. Ndinawauza kuti: ‘Ndidzanka nanu. Koma tandilolani ndithange ndavala.’ Ndinapemphera kwa Yehova ndi mtima wanga wonse, ndikupempha thandizo lake. Pamene ndinatha kupemphera, ndinadzimva womasuka kwambiri ndikuyamba kuwona amuna okhala ndi zida ndi owopsa ameneŵa ngati anthu wamba. Ndinkalankhula nawo mopanda mantha.

“Ndinawafunsa kuti: ‘Kodi mukufuna chiyani kwa ine? Tiyeni tilankhulire m’nyumba pang’ono tisanapite.’ Pamene tinali m’chipinda chochezera, mkulu wawo anandifunsa kuti: ‘Kodi ndikuyenerera kwanji kumene ulinako kumaloŵa m’nyumba za anthu ndikumawalalikira?’ Ndinayankha kuti: ‘Inu mumanyamula mfuti kukwaniritsa chifuno chanu, ndipo palibe amene amakudodometsani. Ine ndimanyamula mbiri yabwino ya mtendere imene Yesu anatilamulira kuilalikira.’ Ndiyeno ndinafotokoza zikhulupiriro ndi ntchito ya Mboni za Yehova. Pamene ndinangotchula dzina lakuti Yehova, iwo anati: ‘Tidzakhutiritsidwa kukufunsira mom’muno. Palibe chifuno chokutengera kupita nafe.’ Mwachiwonekere, mmodzi wa iwo ankadziŵa mbale wina. Iye anati: ‘Uyu alingati Jarjoura.’

“Tinachitira umboni kwa amuna okhala ndi mfuti amenewo ndikuyankha mafunso awo kwa ola limodzi ndi theka. Ndiyeno, mmalo monditenga m’buti la galimoto lawo monga momwe anachitira ndi ena, anapepesa, nandipsompsona, nandilonjeza thandizo lawo nthaŵi iriyonse pamene ndikalifunikira, ndipo anachoka. Nthaŵi yonseyo, ndinkachimva chitetezo cha Yehova. Kukhala ndi phande m’ntchito yakunyumba ndi nyumba mmawa umenewo ndikupezeka kumsonkhano masana kunandilimbitsa kuchirimika. Zowonadi, dzina la Yehova linapulumutsa moyo wanga.”​—Miyambo 18:10.

“Chisamaliro cha Yehova Chinatizinga”

Mbale wina wa ku Beirut akulemba kuti: “Linali Lachitatu, January 31, 1990. Pamene ndinkagwira ntchito ndi mchimwene wanga panyumba ya mlongo, kumenyanako kunayambanso. Mabomba anaphulika konsekonse. Chifukwa cha nkhondo yowopsayo, sitinathe kubwerera kunyumba. Mlongoyo anali wochereza kwambiri chinkana kuti anali ndi zidutswa zochepa zokha zamkate.

“Ndinada nkhaŵa kwambiri ponena za mkazi wanga chifukwa chakuti ndi Mfilipino ndipo wosazoloŵerana ndi chiwawa cha nkhondo. Komabe, patsiku lachiŵiri, ndinakhoza kubwerera kunyumba kwanga. Miyulu ya mipando inatseka makwalala, koma ndithokoza Yehova, banja langa linali losungika. Pambuyo pa bata lakanthaŵi kochepa, kuphulitsa mabomba kwamphamvu kunayambanso. Tinabisala m’nyumba ya mbale yapafupi ndi yathu. Tinalimo asanu​—mkazi wanga, mwana wanga wamwamuna wazaka ziŵiri zakubadwa, ineyo, mchimwene wanga, ndi mkazi wake. Mabomba, makombola, ndi maroketi zinalakatika m’malo onse otizinga, koma chisamaliro cha Yehova chinatizinga. Masiku aŵiri akuphulitsa mabomba kwamphamvu anapita, pamene tinapitirizabe kugona pansi ndi utsi wa mabomba uli bi m’mphuno zathu.

“Pamene tinkamvetsera kukuphulikako, tinakumbukira mawu a Davide pa Salmo 18:1-9, 16-22, 29, 30. M’mphindi zovuta zimenezo, ndipo mosasamala kanthu za zonse zomwe zinachitika, tinali achimwemwe ndipo tinkamwetulirabe. Tinapemphera kwa Yehova kuti ngati nkufa, tife mwakachetechete, popanda kuvutika. Chiyembekezo chathu chachiukiriro chinali cholimba.

“Tsiku lotsatira linali lozizwitsa. Pafupifupi mabomba 25 anagwera pafupi ndi nyumba imene tinabisalamo, koma panalibe ndimmodzi yemwe wa ife amene anavulala. Kodi mungayerekezere malingaliro athu pamene tinkachimva chitetezo cha Yehova? Mmawa wotsatira, mwamsanga tinalingalira zoti tithaŵe. Galimoto langa linali lokha limene silinatenthedwe pakhwalalapo. Ndinayendetsa pakati pa makombola ndi mabomba, ndipo ndiyamikira Yehova kuti, tinatha kuthaŵira kumalo komwe kunali bata pang’ono kuposa kwathu. Kumeneko, abale athu mwachikondi anatipatsa zovala, zakudya, ndi ndalama.

“Mosasamala kanthu za mavuto onsewo, tinali achimwemwe chifukwa chakuti Yehova anali nafe. Zinali kwenikweni ngati kuti iye adatumiza angelo ake kudzachinjiriza mabomba kuti asatigwere. (Salmo 34:7) Inde, chimwemwe chathu chinali chachikuludi. Koma chimwemwe chathu chidzakulirapo pambuyo populumuka Armagedo.”

Chithandizo Cha m’Nthaŵi Yatsoka Chiri Pantchito!

Madera ena a Beirut anawoneka ngati kuti anakanthidwa ndi chivomezi. Nyumba zambiri za abale athu zinapasulidwa kapena kuwonongedwa. Pamene vuto laposachedwapa linabuka, Komiti Yanthambi inalinganiza komiti ya chithandizo cha m’nthaŵi yatsoka kusamalira zosoŵa za abale. Inayamba kugwira ntchito pa February 16, 1990, pafupifupi ndi nthaŵi imene tinali okhoza kuloŵa m’madera okanthidwawo. Chifuno cha komiti imeneyi chinali cha mbali zitatu izi: kupereka chilimbikitso chauzimu kwa abale; kusamalira zosoŵa zawo za ndalama, chakudya, ndi madzi; ndikuwathandiza kukonza kapena kumanganso nyumba zawo.

Panalibe kufunikira kwakuitanira antchito aufulu. Tsiku lirilonse ambiri analaŵira mmamawa kudzathandiza. Tamverani ndemanga zina za amene anathandizidwa:

Mlongo wina, pamene nyumba yake inkayeretsedwa ndikukonzedwanso, anati: “Ndidamvapo mbiri yonena za thandizo loperekedwa ndi abale patagwa tsoka. Tsopano ndikuliwona ndikulimva.” Ngakhale mnansi wake, mkazi Wachisilamu, anauza mlongo ameneyu kuti: “Mumakondanadi. Chipembedzo chanu ndicho chowona. Tsopano ndidzathamangira kumudzi kwathu ndikukauza aliyense zimene inu mukuchita kunoko.” Mnansi ameneyu anabweretsa chakudya kwa antchito aufuluwo.

Mlongo wokalamba anapereka ndemanga yakuti: “Ndinayembekezera kuti mudzabwera kudzandichezera, koma sindinayembekezere kuti Sosaite ingatume munthu wina kundibweretsera madzi.” Iye ankalira pamene anapsompsona mbale yemwe anabwera kudzamthandiza.

Banja la anthu atatu​—mwamuna ndi mkazi omwe anali ofalitsa osabatizidwa ndi mnyamata wawo wamng’ono​—anachezeredwa ndikupatsidwa bokosi lalikulu la mkaka, mkate, madzi akumwa, ndi ndalama. Pamene iwo anauzidwa kuti Mboni za Yehova ndizo zinapanga makonzedwewo, mwamunayo anati: “Ndinakhala m’Tchalitchi cha Evangelical kwa zaka 11 ndipo ndinali wokangalika kwambiri. Koma kwa zaka 15 zankhondo zimenezi m’Lebanon, iwo sanalingalirepo kuchitira ziŵalo zawo chinthu chonga chimenechi.” Iye anapitiriza kuti: “Ili ndilodi gulu lokha la Mulungu.” Mwamunayo ndi mkazi wake anabatizidwa pamsonkhano wochitidwa mu May 1990.

Mkulu wina anapereka ndemanga yakuti: “Ndiribe mawu ofotokoza chiyamikiro chathu cha ntchito zachikondi zimene munachitira abale ovutikawo. Ndinasangalatsidwa kwambiri kwakuti ndinagwetsa misozi pamene ndinawona gulu la abale achichepere, antchito aufulu, akumanganso nyumba ya makolo anga. Ngakhale anansi athu omwe si Mboni anasonyeza chiyamikiro chawo. Tikumthokozadi Yehova ndi gulu lake kaamba ka chirikizo lothandiza limene laperekedwa. Ngowona chotani nanga mawu a wamasalmo pa Salmo 144:15 akuti: ‘Achimwemwe ali anthu amene Mulungu wawo ndiye Yehova.’”

“Kodi Ndinu Anthu Amtundu Wotani?”

Mlongo wina wokhala ndi banja analemba kuti: “Ndikufuna kulongosola chiyamikiro changa chachikulu kaamba ka chikondi cha Yehova ndi gulu lake. Nyumba yanga inakanthidwa ndi mabomba ambiri ndikutenthedwa. Ambiri anatiuza kuti siikakonzeka. Komabe, siiyi nanga, yoima nji ndiyokonzedwa mokwanira ngati kuti palibe chimene chinaichitikira, yozingidwa ndi nyumba mazana ambiri pakhwalala lathu zotenthedwa ndikuwonongedwa.

“Ngakhale anansi athu, omwe si Mboni za Yehova, amafunsa kuti: ‘Kodi chikondi chimenechi chimachokera kuti? Kodi ndinu anthu amtundu wotani? Kodi ndayani anthu awa amene akugwira ntchito mwachangu chotero ndi amene ali abata chotero ndiodzisungira bwino? Atamandiketu Mulunguyo amene wakupatsani chikondi chimenechi ndi mzimu wodzimana.’ Ngoyenerera chotani nanga mawu a Salmo 84:11, 12 akuti: ‘Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuŵa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; Sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro. Yehova wa makamu, wodala munthu wakukhulupirira Inu.’”

Mwamuna yemwe mkazi wake ndi ana ake ndi Mboni za Yehova analemba kuti: “Ndikufuna kukuyamikirani kaamba ka thandizo lanu la kukonza nyumba yathu. Ntchito yanu inasonyeza chikondi chowona mtima Chachikristu chimene nchosoŵa kwenikweni masiku ano. Mulungu adalitsetu zoyesayesa zanu.”

Pamene nyumba ya mkulu wina inakonzedwanso, iye anati: “Tikulephera kulankhula zimene ziri m’mitima yathu. Sititha kupeza mawu okuuzirani chiyamikiro chathu kaamba ka Yehova ndi gulu lake. Tinakumva kuyandikana thithithi ndi Yehova m’tsoka lathu. Chikondi chanu chalimbikitsa ziŵalo zonse za banja langa kukhala ndi phande m’kuthandiza ena osoŵa.”

Mu April, anthu 194 m’Lebanon anasangalala ndi ntchito yaupainiya wothandiza. Usiku wa Chikumbutso udali wabata kuposa usiku wa masiku ena onse, ndipo Chikumbutso chinachitidwa ndi opezekapo 5,034. Misonkhano yonse imene inakonzekeredwa inachitidwa, ndipo chiwonkhetso cha anthu obatizidwa m’chakacho chinali 121, mosasamala kanthu za mavuto omwe ali m’dzikolo. Mabanja ambiri m’mipingo anachokeratu m’dzikoli. Koma okondwerera atsopano akupita patsogolo kulinga kuubatizo, ndipo olengeza Ufumu okwanira 2,726 amenewo akupitirizabe kuwonjezeka m’chiŵerengero. Mkati mwa chaka chautumiki cha 1990, anthu onse a Yehova m’Lebanon anakumana ndi kukhulupirika kwa Yehova pamene anatisamalira bwino kwambiri ndikutitsogoza kupyola m’nthaŵi yachipwirikiti.​—Salmo 33:4, 5; 34:1-5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena