Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 2/15 tsamba 25-28
  • Kubweretsa Kuunika Kumalo Akutali a mu Bolivia

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubweretsa Kuunika Kumalo Akutali a mu Bolivia
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Umboni wa Chitsogozo cha Angelo
  • Kulalikira Mkati mwa Malo Otentha
  • Kuthedwa Nzeru pa Mitsinje Yakumalo Otentha
Nsanja ya Olonda—1991
w91 2/15 tsamba 25-28

Kubweretsa Kuunika Kumalo Akutali a mu Bolivia

KUMPOTO ndi kum’mawa kwa mapiri aatali a Bolivia kuli zigwa zotambalala zakumalo otentha, zokhala ndi zomera zogudira. Izo nzogawidwa ndi mitsinje yamadzi oyenda mwamphamvu yomwe imakhotakhota m’nkhalango ndi m’madambo. Kodi kulalikira mbiri yabwino Yaufumu kumachitika motani kumadera akutali oterowo?

Tangodzilingalirani muli m’bwato lalikulu loyendetsedwa ndi injini yokhala kumbuyo, losemedwa kuchokera ku tsinde lamtengo waukulu wamphako. Chimenechi chinali chokumana nacho cha aminisitala anthaŵi zonse asanu ndi mmodzi ochokera ku Trinidad, mzinda wokhala m’chigawo cha El Beni cha Bolivia. Iwo anakonzekera ulendowu kotero kuti angakachitire umboni kumidzi yakumtsinjewo yomwe sinafikiridwepo ndikale lonse ndi “mbiri yabwino ya ufumu.” (Mateyu 24:14, NW) Pambuyo podutsa gawo lotakata la madzi oti mbuu, ngalaŵa yawo inayamba kuyandama m’kamfuleni kulinga ku Mtsinje wa Mamoré.

Mmodzi wa anthu a m’gululo akusimba motere: “Tinatsala pang’ono kufika ku Mamoré pamene tinapeza kuti mbali yomalizira ya mfuleniwo inali youma. Tikumatuluka m’botimo, tinayamba kumira m’matope ofika mu ntchafu! Mkazi wanga anataya nsapato zake pamene ankayesera kuonjoka. Koma ndithandizo la anthu odutsa, tinakhoza kukoka bwato lolemeralo kutuluka m’matopemo kunka pamalo ouma. Pambuyo pa maola aŵiri otopetsa, tinafika ku Mamoré.

“Kenaka tinayenda bwinobwino kukwera ndi mtsinjewo, womwe unali wokometseredwa ndi magombe aatali okhala ndi zomera zakumalo otentha. Pamene kulira kwa injini kunamveka, nkhasi zazikulu zinalumpha kuchoka pa zipinjiri zoyandama, pamene madolphin okongola analumpha kutuluka m’madzi kwa nthaŵi ndi nthaŵi. Malo athu oimapo oyamba anasonyezedwa ndi utsi wochokera pamoto wapagombe woyatsidwira kuthamangitsa tizilombo. Pambuyo pokocheza bwato lathu pakati pa nthambi zolukanalukana, tinakambitsirana ndi anthu aubwenzi ponena za madalitso Aufumu akudzawo. Moyamikira anatipatsa zipatso ndi mazira.

“Pamene tsikulo linkapita, tinaimanso m’malo ena owonjezereka kufesa mbewu zowonjezereka za chowonadi. Pamene tinkafika ku San Antonio nkuti kutada kale. Anthu a m’mudzimo anali atagona. Komabe, pamene mbiri yoti padzawonetsedwa kanema inafalikira, nyali zinayamba kuyatsidwa. Kavalo ndi ngolo zinamangidwa kukatenga katundu wathu kuloŵa naye m’taunimo. Anthu ambiri anakhala ozoloŵerana ndi Mboni za Yehova ponse paŵiri pakanema ndi mwaumwini.

“Tsiku lotsatira tinapitiriza kuchezera malo atsopano. Pagombe lalitali, akazi ankachapa zovala zawo, ndipo ngakhale mwana, m’zikamba zazikulu za nkhasi. Iwo anali asanamvepo konse za uthenga wathu wa Baibulo. Pamalo ena matemba ankalumpha kwambiri kutuluka m’madzi pafupi ndi botilo, ndipo ambiri anagwera mkati. Chotero pamapeto posonyeza kanemayo, tinadya nsomba zokazinga tisanagone. Pamene tinamaliza ulendowo, mabuku ambiri anali atagaŵiridwa m’dera lakutali limeneli, ndipo tinali okhutira kuti tinathandiza ambiri kumva mbiri yabwino kwa nthaŵi yoyamba.”​—Yerekezerani ndi Aroma 15:20, 21.

Umboni wa Chitsogozo cha Angelo

Tangodzilingalirani tsopano kuti muli paulendo wokafuna munthu mmodzi m’tauni ya anthu 12,000, yomwe mukuichezera kwa nthaŵi yoyamba. Mukudziŵa zochepa za munthuyo koma dzina lake basi. Chimenecho ndicho chinali chitokoso choyang’anizana ndi aminisitala aŵiri a nthaŵi zonse omwe anafika pa Guayaramerín akumayembekezera kupeza munthu yemwe anaphunzirapo Baibulo ndikupezekapo pamisonkhano m’tauni ina koma anasamukira ku tauni imeneyi. Pambuyo pokhazikika, okwatirana achipainiyawo analingalira kuwongolako miyendo pakati pa tauni, pamene makamu a anthu anasonkhana kaya pamagome odyera kapena akungokambitsirana. Pafupifupi nthaŵi yomweyo mwamuna wina anafikira okwatiranawo nayamba kukambitsirana. Iwo anamfunsa ngati akumudziŵa mkazi yemwe ankamfunayo. “Ayi,” iye anatero, “koma apongozi anga aakazi ndi mmodzi wa Mboni za Yehova.” Popeza kuti m’taunimo simunkadziŵika kuti muli Mboni, iwo analingalira kuti anali wosokonezeka.

Komabe, tsiku lotsatira anachezera mkazi wokalamba ameneyu, yemwe anali wobindikiritsidwa pakama chifukwa cha mwendo wothyoka. “Ndine mmodzi wa Mboni za Yehova, koma sindinabatizidwebe,” iye anatero. Pamene anafunsidwa kuti ndani anamphunzitsa chowonadi, iye analoza ku chithunzi cha mdzukulu wake wamkazi chomwe chinali pakhoma nati: “Ndiye amene anandiphunzitsa.” Iwo sanakhulupirire zimene anawona! Anali mkazi wachichepere yemwe ankafunafuna! “Kodi nchifukwa ninji mpongozi wanu anakana kuti samudziŵa?” iwo anafunsa motero. “Oo, iye anakwatiwa tsopano, ndipo mpongozi wangayo amadziŵa dzina la mwamuna wake lokha,” iye anayankha motero. Mdzukulu wamkaziyo panthaŵiyo anali kwinakwake, koma phunziro Labaibulo linachititsidwa mwakulemberana makalata. Kodi panali chotulukapo chotani? Onse aŵiri iye ndi agogo ake anapita patsogolo kufikira anabatizidwa. Nyumba yawo inatumikira monga Nyumba Yaufumu ya mpingo womakulawo, ndipo monga minisitala wanthaŵi zonse, mkazi wachichepereyo watsogoza anthu ambiri ku gulu la Yehova.

Kulalikira Mkati mwa Malo Otentha

Kenaka, talingalirani kuti ndege yanu ikutera pansi pakamsewu kaudzu pa San Joaquín, mkati mwenimweni mwa malo otentha a Bolivia. Muli ndi malingaliro osakhazikika pamene mukulingalira za mliri wodabwitsa, umene zaka ziŵiri zapitazo, unasesa gawo limodzi mwa magawo asanu a anthu a m’tauni imeneyi.

Okwatirana achipainiya ofika kuchokera ku Trinidad pa ndegewo alawa kale kuchereza kwa anthuwa. Mwamunayo akufotokoza motere: “Kukambitsirana Baibulo kochitidwa pamene tinali kuuluka kunatsogoza ku chiitano chakukhala panyumba ya mwini wake, kwaulere. Ochereza athu anatipatsa zakudya zathu pamtengo wotsika, kutitheketsa kupereka nthaŵi yathu yonse ku ntchito yolalikira. Mwamsanga titangofika, tinauzidwa kuti tifunikira kukawonekera kumisasa ya asirikali panthaŵi yomweyo. Pamene mkuluyo anamva kuti ndife Mboni za Yehova osati ogalukira, anasonyeza chikondwerero chodabwitsa nagula Baibulo, limodzinso ndi mabuku a Baibulo ndi masabusikripishoni a magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pambuyo pake, pafupifupi munthu aliyense m’tauniyo anamvetsera mwatcheru ku lonjezo la Baibulo la umoyo wangwiro mtsogolo moyandikiramu.”​—Chibvumbulutso 21:4.

Aminisitala anayi anthaŵi zonse anafuna kuchoka ku San Joaquín kunka ku San Ramón, koma choyendera chokha chomwe chinalipo chinali ngolo yokokedwa ndi ng’ombe. Iwo anagwiritsira ntchito makatoni a mabuku monga mipando. Posakhalitsa makatoniwa anatiwama chifukwa cha mabampu ndi kunjiduka kwamphamvu kwa ngolo yokutidwayo, yokhala ndi magudumu aatali amitengo. Ngakhale nkhuku zomwe zinali mkati zinachita chizungulire ndi kuyendako.

Pambuyo pamaola khumi a kuyenda kupyola ziyangoyango, anafika pamalo pamene sipankaoneka ndi nkukuluzi womwe, ndipo kunkada. Woyendetsayo anachenjeza gululo mwakunena kuti, “Ndiganiza kuti tasokera!” Iwo anangoyamba kumene kuganiza kuti, ‘Kodi tingakhale motani m’ziyangoyango zimenezi zokhala ndi njoka ndi nyama zolusa zowopsa?’ pamene woyendetsayo anawonjezera kuti, “Koma musadandaule. Nyamazi zinabwerako kale kuno.” Zinalidi tero. Mkati mwa ola limodzi zinatuluka m’ziyangoyangomo nkutulukira pa San Ramón!

Kunonso, masiku ambiri anatheredwa akulengeza Paradaiso akudzayo kwa anthu omwe anali asanamvepo za iyo ndi kale lonse. Palibe Mboni zomwe zinkakhala kuno; komabe chinachake chinachitika chimene chinasintha zimenezo.

M’mishonale Wachikatolika ankatsatira Mbonizo pamene zinkapita kukhomo ndi khomo. Kenaka anasemphana ndipo zinampeza ali m’nyumba yotsatira yomwe izo zinaifikira. Podabwitsidwa ndi ubwenzi wake, anamsiyira bukhu lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Ngakhale kuti iye sanali wokondweretsedwa kwenikweni, anapatsa bukhulo kwa mlamu wake wamkazi, yemwe anaŵerenga zamkati mwake, naphunzira mowonjezereka, ndipo pambuyo pake anakhala Mboni yobatizidwa.

Kuthedwa Nzeru pa Mitsinje Yakumalo Otentha

Tsopano tadzilingalirani muli pachoyendetsera cha ngalaŵa yamumtsinje mukumayandama pamadzi owopsa, amphamvu osakhazikika. Matanthwe obisika, magombe amatope, ndi matsinde a mitengo, limodzi ndi kamvuluvulu wam’madzi wamwadzidzidzi, ndizo zowopsa zoŵerengeka zokha. Mapiranha, nyesi, ndi mastingray nzambiri m’madzi ameneŵa. Zimenezo ndizo zinali zitokoso zoyang’anizana ndi abale a ku Riberalta omwe anali ndi ntchito yochitira umboni kwa anthu okhala m’phepete mwa mtsinje m’deralo.

Kuti afikire malo akutali ameneŵa, iwo anasema ngalaŵa yotchedwa Luz de los Ríos (Kuunika kwa Mitsinje). Mkati mwa kuchezetsa kwa oyang’anira dera ndi chigawo, analingalira zoitenga ngalaŵayo kukaiyesa. Zonse zinayenda bwino kufikira pamene denga linakodwa ku nthambi yolenjekeka. Mafunde aakulu anakankha ngalaŵayo naigunditsa ku mtengo wakugwa. Mofanana ndi lupanga, nthambi yothyoka yosongoka inaboola m’mbali mwa botilo​—inatsala pang’ono kupha mkazi wa woyang’anira chigawo! Madzi analoŵa mkati, ndipo ngalaŵayo inaguduka, nitaira okweramowo m’madzi othamangawo. Ndipo woyang’anira chigawo ndi mkazi wake sankadziŵa kusambira! Mwathandizo la awo omwe anali okhoza kusambira, iwo anafika kumtunda mwachisungiko. Koma ngalaŵayo inasoŵeratu. Masiku ena pambuyo pake inapezeka pamtunda wa makilomita asanu kunsi kwa mfuleniwo. Katundu yense, kuphatikizapo makatoni 20 a mabuku, anataika.

Sitima Yankhondo ya Bolivia ndiyo inathandiza kuyandamitsanso ngalaŵayo, ndipo pambuyo pa milungu ingapo yoikonza, ngalaŵayo inakonzeka kumaliza ulendo wake woyamba. Ulendo wovutawo unayamba ndi mphepo yoipa ndi vuto la injini.

Pamalo oyamba pamene abalewo anakocheza, anakumana ndi gulu la Aevanjeliko, omwe anaseka nati: “Boti lanu laling’onoli silikhoza kuyenda pa mtsinje uno!” Kuyesayesa kusonyeza zithunzithunzi kunalephera chifukwa cha jenereta yowonongeka. Pamene zinabwerera pamtsinje, Mbonizo zinamva kuti kunabwera ngalaŵa zina zokhala ndi zokuzira mawu zikumachenjeza za kudza kwa “aneneri onyenga.” Mwachiwonekere, izi zinali ntchito za Aevanjelikowo. Komabe, zinangosonkhezera chikhumbo chofuna kudziŵa cha anthuwo.

Ngakhale kuti ulendowo unathetsa chinenezo chonyenga chochokera kwa aneneri onyenga enieni, abalewo anadzimva kukhala omangika, popeza kuti kutsogolo kwawo kunali kudakali ulendo wamasiku 21 kukafika ku Fortaleza.

Ali paulendowo, iwo anachitira umboni kwa mfumu ya fuko lakutali; iye anamvetsera mwatcheru. Kupyolera m’nkhani Yabaibulo yomwe inaperekedwa ndi mmodzi wa apainiyawo, gulu la okhuza maliro kumalo olambulidwa bwino akutali linatonthozedwa ndi chiyembekezo chowona kaamba ka akufa. Mwamuna wina wokalamba wandevu zazitali zaimvi analongosola chiyamikiro chake chamtima wonse, ndipo anafunsa mmene angalembetsere ku magazini athu kwa zaka khumi! Mu Fortaleza, anthu 120 anapindula ndi programu ya Sosaite ya zithunzithunzi.

Ha, apainiya ameneŵa anadzimva kukhala okhutiritsidwa motani nanga pokhala atabweretsa chowonadi kumalo akutali! Ndithudi, palibe njira ina yomwe njachisungiko ndi yokhutiritsa yogwiritsira ntchito moyo wa munthuwe kuposa kutumikira Mlengi wa moyo weniweniwo, Yehova Mulungu.​—Salmo 63:3, 4.

[Mapu/​Zithunzi patsamba 26]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

BOLIVIA

Guayaramerín

Riberalta

Fortaleza

San Joaquín

San Ramón

Trinidad

San Antonio

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena