Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chitani Khama pa Kuŵerenga
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
    • Chitani Khama pa Kuŵerenga

      NYAMA sizingachite zimene inuyo mukuchita tsopano lino. Kaŵirikaŵiri chifukwa chosoŵa mwayi wopita kusukulu, munthu mmodzi mwa anthu sikisi alionse sanaphunzire kuŵerenga—ndipo amene anaphunzira, saŵerenga kaŵirikaŵiri. Komabe, luso lanu la kuŵerenga mawu olembedwa limakupatsani mwayi woyenda kumadera ena, kukumana ndi anthu amene miyoyo yawo ingakupindulitseni, ndi kudziŵa zinthu zimene zingakuthandizeni kuthana ndi nkhaŵa za moyo.

      Mapindu amene mwana wasukulu angapeze kusukulu amadalira luso lake la kuŵerenga. Pokafuna ntchito, luso lake la kuŵerenga lidzakhudza mtundu wa ntchito imene angapeze ndi kuchuluka kwa maola amene ayenera kugwira ntchito yoti im’thandize pamoyo. Akazi apanyumba amene amaŵerenga bwino amatha kusamalira bwino mabanja awo pankhani ya zakudya zoyenerera, ukhondo, ndi kuwateteza ku matenda. Anakubala amene amatha kuŵerenga bwino angathandizenso ana awo kukula m’nzeru.

      Komabe, phindu lalikulu koposa la kuŵerenga n’lakuti kumathandiza “kum’dziŵadi Mulungu.” (Miy. 2:5) Njira zambiri zimene timatumikira nazo Mulungu zimafuna luso la kuŵerenga. Pamisonkhano yampingo pamakhala kuŵerenga Malemba ndi mabuku ozikidwa pa Baibulo. Kuti ulaliki wanu m’munda ukhale wogwira mtima zimadalira kwambiri kaŵerengedwe kanu. Ndipo kukonzekera mbali zimenezi kumafuna kuŵerenga. Pachifukwa chimenechi, kukula kwanu mwauzimu kumadalira kwambiri chizoloŵezi chanu cha kuŵerenga.

      Gwiritsani Ntchito Bwino Mwayiwo

      Ena amene amaphunzira njira za Mulungu sanaphunzire kwambiri sukulu. Iwo angafunikire kuphunzitsidwa kuŵerenga kuti apite patsogolo mwauzimu. Kapena angafunikire kuwathandiza kuti akulitse luso lawo la kuŵerenga. Ngati pali chosoŵa chimenechi, mipingo imayesetsa kulinganiza makalasi ophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba mwa kugwiritsa ntchito buku lakuti Dziperekeni pa Kuŵerenga ndi Kulemba. Anthu zikwizikwi apindula kwambiri ndi makonzedwe ameneŵa. Chifukwa chakuti kuŵerenga bwino n’kofunika kwambiri, mipingo ina yakhazikitsa makalasi othandiza anthu kuŵerenga bwino. Makalasiwo amachitika panthaŵi ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Ngakhale kumene kulibe masukulu amenewa, munthu akhoza kupitabe patsogolo mwa kupatula nthaŵi tsiku lililonse ndi kumaŵerenga motulutsa mawu ndi kumafika pa sukulu ya utumiki nthaŵi zonse komanso kumatengamo mbali.

      Mwatsoka, kuchuluka kwa mabuku a zithunzi ndi mawailesi akanema, mwa zinthu zina, kwapangitsa anthu ambiri kusakondanso kuŵerenga. Kuonerera kwambiri wailesi yakanema ndi kusaŵerenga kungalepheretse munthu kupita patsogolo m’maluso a kuŵerenga ndi kuganiza bwino. Sakhalanso ndi luso la kulingalira ndi kulankhula bwino.

      “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndiye amapereka mabuku omwe amatithandiza kulimvetsa Baibulo. Mabukuwo amakhala ndi mfundo zothandiza pankhani zofunika zauzimu. (Mat. 24:45; 1 Akor. 2:12, 13) Amatifotokozeranso zochitika za m’dziko zofunika kuzidziŵa ndi tanthauzo lake, amatithandiza kudziŵanso zina ndi zina za chilengedwe, ndipo amatiphunzitsa mmene tingachitire ndi zinthu zimene zingatidetse nkhaŵa. Koposa zonse, amatiphunzitsa mmene tingatumikirire Mulungu moyenerera kuti atiyanje. Kuŵerenga kwabwino koteroko kudzatithandiza kukula mwauzimu.

      Komabe, luso la kuŵerenga palokha silipindula kanthu. Tiyenera kuligwiritsa ntchito m’njira yoyenerera. Mofanana ndi kudya, tiyenera kusankha bwino zoŵerenga. N’kudyeranji chakudya chosathandiza thupi kapena chimene chingakudwalitseni? Mofananamo, n’kuŵerengeranji, ngakhale mongofuna kutayirapo nthaŵi, nkhani zimene zingaipitse maganizo ndi mtima wanu? Mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo ziyenera kutithandiza kusankha nkhani zimene tingaŵerenge. Musanasankhe zimene mungaŵerenge, kumbukirani malemba monga Mlaliki 12:12, 13; Aefeso 4:22-24; 5:3, 4; Afilipi 4:8; Akolose 2:8; 1 Yohane 2:15-17; ndi 2 Yohane 10.

      Ŵerengani ndi Cholinga Chabwino

      Kupenda nkhani zolembedwa m’Mauthenga Abwino anayiwo kumaonetsa kuti kuŵerenga ndi cholinga chabwino n’kofunika kwambiri. Mwachitsanzo, mu Uthenga Wabwino wa Mateyu, timaona kuti Yesu asanapereke mayankho a m’Malemba kwa atsogoleri achipembedzo ophunzirawo, pamafunso awo amachenjero, choyamba anawafunsa kuti “Kodi simunaŵerenga?” ndi kuti “Simunaŵerenga kodi?” (Mat. 12:3, 5; 19:4; 21:16, 42; 22:31) Phunziro limene tikutolapo apa n’lakuti ngati tiŵerenga ndi cholinga cholakwika, tikhoza kutengapo maganizo olakwika kapena kuphonyeratu mfundo yonse. Afarisi anali kuŵerenga Malemba chifukwa anali kuganiza kuti mwa kutero, akapeza moyo wosatha. Malinga ndi kunena kwa Yesu, mphatso imeneyo siipatsidwa kwa anthu amene sakonda Mulungu amenenso salandira njira Yake ya chipulumutso. (Yoh. 5:39-43) Zolinga za Afarisi zinali zadyera; choncho, zinthu zambiri anali kuzimva molakwika.

      Cholinga chabwino koposa choŵerengera Mawu a Mulungu ndicho chikondi chathu pa Yehova. Chikondi chotero chimatilimbikitsa kuphunzira chifuniro cha Mulungu, pakuti chikondi “chikondwera ndi choonadi.” (1 Akor. 13:6) Ngakhale kuti m’mbuyomu sitinali kukonda kuŵerenga, kukonda Yehova ndi ‘nzeru zathu zonse’ kudzalimbikitsa maganizo athu kuti tiphunzire za Mulungu. (Mat. 22:37) Chikondi chimadzutsa chidwi, ndipo chidwi chimalimbikitsa kuphunzira.

      Ganizirani Liŵiro la Kaŵerengedwe

      Kuŵerenga kumayendera pamodzi ndi kuzindikira. Ngakhale mmene mukuŵerengeramu panopo, mukuzindikira mawu ndi kukumbukira matanthauzo ake. Mukhoza kuŵirikiza liŵiro la kaŵerengedwe kanu ngati mukulitsa luso lanu la kuzindikira. M’malo moona liwu limodzi ndi limodzi, yesani kuona mawu ambiri nthaŵi imodzi. Mmene luso limeneli likukula, mudzaona kuti mukumvetsa bwino kwambiri zimene mukuŵerenga.

      Komabe, pamene muŵerenga nkhani zozama, kuti mumvetse zambiri muyenera kugwiritsa ntchito njira ina. Yehova popatsa uphungu Yoswa za kuŵerenga Malemba anati: “Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo.” (Yos. 1:8) Liwu lachihebri limene linamasuliridwa kuti, ‘kulingiriramo’ limatanthauzanso kusinkhasinkha. (Sal. 63:6; 77:12; 143:5) Posinkhasinkha, munthu amalingalira mozama; safulumira ayi. Kulingalira poŵerenga kumachititsa Mawu a Mulungu kukhomerezeka m’maganizo ndi m’mtima. Baibulo lili ndi maulosi, uphungu, miyambo, ndakatulo, ziweruzo za Mulungu, mfundo zokhudza chifuniro cha Yehova, ndi zitsanzo zambiri za zochitika zenizeni m’moyo—zonsezo n’zopindulitsa kwa aja ofuna kuyenda m’njira za Yehova. Baibulo ndi lopindulitsa kwabasi ngati muliŵerenga m’njira imene ingakhomereze mawu ake mozama m’maganizo ndi m’mtima mwanu!

      Phunzirani Kuzika Maganizo Pankhani

      Pamene mukuŵerenga, dziloŵetseni m’chochitika chimene chikufotokozedwacho. Yesani kuona anthuwo m’maganizo mwanu, ndiponso khalani okhudzidwa ndi mmene iwo akumvera m’zochitikazo. Zimenezi n’zosavuta poŵerenga nkhani ngati ya Davide ndi Goliati, yolembedwa m’chaputala 17 cha 1 Samueli. Ndipo ngakhale zinthu zofokozedwa mu Eksodo ndi Levitiko zokhudza kumangidwa kwa chihema kapena kuikidwa kwa ansembe zingakhale zosangalatsa kwambiri. Zingakhale zochititsa chidwi pamene muona m’maganizo mwanu mmene anali kupimira zinthu ndi kuona zipangizo zomangira. Kapena pamene muyerekeza kumva kununkhira kwa fungo lokoma la nsembe za mbewu zokazinga ndi nyama zimene zinali kuwotchedwa. Taganizani mmene kunalili koopsa kutumikira monga wansembe! (Luka 1:8-10) Kuzika maganizo anu ndi kuikirapo mtima mwa njira imeneyi kudzakuthandizani kumvetsa tanthauzo la zimene mukuŵerenga ndipo kudzakuthandizani kumakumbukira zinthu.

      Komabe, ngati simusamala poŵerenga, maganizo anu angayambe kuthaŵathaŵa. Maso anu angamayang’ane patsambapo, koma maganizo anu angakhale atapita kwinakwake. Kodi pali nyimbo imene ikuimba? Kodi wailesi yakanema ndi yotsegula? Kodi ena m’nyumbamo akulankhula? Ngati n’kotheka, ndi bwino kuŵerengera m’malo abata. Komabe, zosokoneza zingachokere mwa inu mwini. Mwina munatanganidwa kwambiri tsikulo. Eya, n’zosavuta kumangokumbukira zimene mwachita tsikulo! Zoona, ndi chinthu chabwino kukumbukira zochitika za tsikulo—koma osati pamene mukuŵerenga. Mwina maganizo anu amakhala ozikika poyamba, mwinanso mumapereka pemphero musanayambe kuŵerenga. Komano pamene mukuŵerenga, maganizo anu angayambe kuthaŵathaŵa. Zikatero yesaninso kuzika maganizo anu. Dziumirizeni kuzika maganizo anu pankhani imene mukuŵerenga. Pang’ono ndi pang’ono, mudzaona kuti mukuyamba kuchita bwino.

      Kodi muyenera kuchitanji mukapeza mawu amene simukuwamvetsa? Mawu ena achilendo amawamasulira kapena kuwafotokoza m’nkhani momwemo. Kapena mutha kuzindikira tanthauzo lake kuchokera m’nkhanimo. Apo ayi, yang’anani mawuwo mu mtanthauzira mawu (dikishonale) ngati muli nayo, kapena lembani mzera kunsi kwa mawuwo kuti mukafunse tanthauzo lake kwa munthu wina. Zimenezi zidzakuthandizani kudziŵa mawu ambiri ndi kumvetsa bwino zimene mukuŵerenga.

      Kuŵerenga Pamaso pa Anthu

      Pamene mtumwi Paulo anauza Timoteo kuti apitirize kuchita khama pa kuŵerenga, makamaka amatanthauza kuŵerenga kopindulitsa ena. (1 Tim. 4:13) Kuŵerenga pamaso pa anthu kogwira mtima kumafuna luso, osati kungotchula chisawawa mawu olembedwa. Woŵerengayo ayenera kudziŵa tanthauzo la mawuwo ndi kuzindikira zimene akunena. Pokhapokha akatero, m’pamene mfundo ndi malingaliro amene akuŵerenga angamveke molondola. Koma zimenezi zimafuna kukonzekera ndi kuyeseza bwinobwino. N’chifukwa chake Paulo analimbikitsa kuti: ‘Usamalire kuŵerenga.’ Luso limeneli mudzaliphunzira m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.

      Patulani Nthaŵi Yoŵerenga

      “Zolinganiza za wakhama zimapinduladi, koma waphuma mapeto ake amakhala wosoŵa.” (Miy. 21:5, NW) Zimenezi n’zoona ponena za chilakolako chathu cha kuŵerenga! Kuti ‘tipindule,’ tiyenera kulinganiza zinthu mwakhama kuti zochita zina zisatisoŵetse nthaŵi yoŵerenga.

      Kodi inuyo mumaŵerenga nthaŵi yanji? Kodi mumapindula mwa kuŵerenga m’mamaŵa? Kapena maganizo anu amagwira bwino zinthu masana? Ngati mungapatule mphindi 15 kapena 20 za kuŵerenga tsiku lililonse, mungadabwe mmene mungapindulire. Chinsinsi chake ndi kuŵerenga tsiku ndi tsiku mosalekeza.

      Kodi Yehova anafuniranji kuti zifuniro zake zazikulu zilembedwe m’buku? Kuti anthu akathe kufufuza m’Mawu ake olembedwa. Zimenezi zimawatheketsa kusinkhasinkha ntchito zodabwitsa za Yehova, kuzifotokozera ana awo, ndi kusunga m’maganizo mwawo zochita za Mulungu. (Sal. 78:5-7) Timaonetsa kuyamikira mphatso ya Yehova imeneyi mwa kuchita khama pa kuŵerenga Mawu ake opatsa moyo.

  • Kuphunzira Kumapindulitsa
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
    • Kuphunzira Kumapindulitsa

      KODI munaonapo anthu akusankhula zipatso? Ambiri amayang’ana maonekedwe ndi ukulu wa zipatsozo pofuna kudziŵa ngati n’zakupsa. Ena amanunkhiza zipatsozo. Enanso amazigwira, ngakhale kuzisinika kapena kuti kuzidiniza. Ndiponso ena amayesa kulemera kwake kwa zipatsozo, atagwira china uku china uku pofuna kumva chimene chili ndi madzi ambiri. Kodi anthuwo amakhala akuganizira chiyani? Amakhala akupenda mbali zosiyanasiyana, kuona kusiyana kwa zipatsozo, kukumbukira zimene anasankhapo m’mbuyomo, ndi kuyerekeza zimene tsopano akuona ndi zimene akuzidziŵa. Pamapeto pake amapeza phindu la kusankha zipatso zokoma chifukwa chosankha mosamala kwambiri.

      Koma mapindu a kuphunzira Mawu a Mulungu amaposa pamenepo. Pamene kuphunzira koteroko kukhala mbali yofunika kwambiri m’miyoyo yathu, chikhulupiriro chathu chimalimba, chikondi chathu chimazamirapo, ulaliki wathu umabala zipatso zambiri, ndipo zosankha zimene timapanga zimapereka umboni wokulirapo wakuti timagwiritsa ntchito luntha ndi nzeru yaumulungu. Ponena za mapindu oterowo, Miyambo 3:15 imati: ‘Zonse zokondweretsa sizilingana nawo.’ Kodi mumapeza mapindu oterowo? Zimadalira njira imene mumaphunzirira.—Akol. 1:9, 10.

      Kodi kuphunzira ndi chiyani? Kuphunzira kumasiyana ndi kuŵerenga wamba. Kumaphatikizapo kugwiritsa ntchito luso la kuganiza popenda nkhani mosamala. Kumaphatikizaponso kupenda zimene mukuŵerenga, poziyerekeza ndi zimene mukudziŵa kale, komanso kuzindikira zifukwa zoperekedwa pa mfundo zotchulidwazo. Pamene mukuphunzira, lingalirani mozama mfundo zimene zingakhale zatsopano kwa inu. Lingaliraninso mmene inuyo mungagwiritsire ntchito mokwanira uphungu wa m’Malemba. Monga Mboni ya Yehova, muyeneranso kulingalira za mipata imene mungagwiritse ntchito mfundozo kuthandiza ena. Mwachidziŵikire, kuphunzira kumaphatikizaponso kusinkhasinkha.

      Kukhala Wokonzekera M’maganizo

      Pokonzekera kuti muyambe kuphunzira, mumaikiratu pafupi zinthu ngati Baibulo, zofalitsa zilizonse zimene mukufuna kugwiritsa ntchito, pensulo kapena bolopeni, mwinanso ndi notibuku. Koma kodi mumakonzekeretsanso mtima wanu? Baibulo limatiuza kuti Ezara “adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita, ndi kuphunzitsa m’Israyeli malemba ndi maweruzo.” (Ezara 7:10) Kodi kukonzekeretsa mtima koteroko kumachitika motani?

      Pemphero limatithandiza kuyamba phunziro la Mawu a Mulungu ndi maganizo oyenera. Timafuna kuti mtima wathu, umunthu wathu wam’katikati, ukhale wolabadira malangizo amene Yehova akutipatsa. Poyamba phunziro lililonse, pemphani Yehova kuti akugaŵireni mzimu woyera. (Luka 11:13) M’pempheni kuti akuthandizeni kumvetsa tanthauzo la zimene muti muphunzire, mmene zimakhudzira chifuniro chake, mmene zingakuthandizireni kusiyanitsa chabwino ndi choipa, mmene muyenera kugwiritsira ntchito malangizo ake pamoyo wanu, ndi mmene nkhaniyo ikukhudzira ubwenzi wanu ndi iye. (Miy. 9:10) Pamene mukuphunzira panokha, pitirizani ‘kupempha nzeru kwa Mulungu.’ (Yak. 1:5) Dzifufuzeni moona mtima malinga ndi zimene mukuphunzira, ndipo pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuchotsa malingaliro olakwika ndi maganizo achiwembu. Nthaŵi zonse “yamikani Yehova” kaamba ka zinthu zimene amavumbula. (Sal. 147:7) Kuphunzira kophatikiza pemphero kumeneku kumatiyandikiza kwa Yehova, chifukwa kumatithandiza kumulabadira pamene atilankhula kudzera m’Mawu ake.—Sal. 145:18.

      Kulabadira koteroko kumasiyanitsa anthu a Yehova ndi anthu ena amene amaphunzira. Anthu osadzipereka kwa Mulungu amakhala ndi chizoloŵezi chokonda kukayikira ndi kutsutsa zinthu zolembedwa. Koma ife sitikhala ndi maganizo amenewo. Yehova timam’khulupirira ndi mtima wonse. (Miy. 3:5-7) Tikalephera kumvetsa penapake, sitimangodzigamulira kuti basi pamenepo panalakwika. Pamene tikufufuza ndi kufunafuna mayankho, timayembekezerabe kwa Yehova. (Mika 7:7) Monga Ezara, timakhala ndi cholinga cha kuchita ndi kuphunzitsa zimene timaphunzira. Pokhala ndi mtima umenewu, tidzatuta madalitso aakulu kuchokera pakuphunzira kwathu.

      Kaphunziridwe Koyenera

      M’malo mongoyamba pa ndime yoyamba kupitiriza mpaka kumapeto, pendani kaye nkhani yonseyo. Yambani mwa kupenda mawu a mutu wa nkhani. Umenewo ndiwo mutu wa zimene muphunzire. Kenako onetsetsani mmene mitu yaing’ono ikugwirizanira ndi mutu waukuluwo. Pendani zithunzi zonse, matchati, kapena mabokosi obwereza a nkhaniyo. Dzifunseni kuti: ‘Malinga ndi kupenda kumeneku, kodi ndikuyembekezera kuphunzira chiyani? Kodi zimene ndiphunzirezo zindipindulitsa motani?’ Njira imeneyi imakhala kalambulabwalo wa phunziro lanu.

      Tsopano pezani mfundo zake. Nkhani zophunzira za mu Nsanja ya Olonda ndi mabuku ena zimakhala ndi mafunso. Pamene muŵerenga ndime iliyonse, kumakhala kothandiza kulemba mzera kunsi kwa mayankho. Ngakhale kuti palibe mafunso, mukhoza kulembabe mzera kunsi kwa mfundo zofunikira kuzikumbukira. Ngati mwapeza mfundo yatsopano kwa inu, imani pamenepo kanthaŵi kuti muimvetse bwinobwino. Funafunani zitsanzo kapena mfundo zimene zingakuthandizeni mu ulaliki kapena zimene mungaphatikize m’nkhani imene mudzakambe m’tsogolo. Ganizirani anthu ena amene mungawalimbikitse chikhulupiriro mwa kuwauza zimene mukuphunzira. Lembani mzera kunsi kwa mfundo zimene mukufuna kukazigwiritsa ntchito, ndipo zipendeninso pamene mwatsiriza phunziro lanu.

      Pamene muŵerenga nkhaniyo, tsegulani malemba osagwidwa mawu. Pendani mmene lemba lililonse likukhudzira mfundo yaikulu ya ndimeyo.

      Mwina mungapeze mfundo zimene simuzimvetsa bwino kapena zimene mungafune kuzifufuza mozamirapo. M’malo mododometsedwa nazo, lembani mzera kunsi kwa mfundozo kuti muziyang’ane pambuyo pake. Nthaŵi zambiri mfundo zoterozo zimamveketsedwa bwino pamene mupitiriza kuŵerenga nkhaniyo. Ngati sizinamveketsedwe, mukhoza kuzifufuza mozamirapo. Kodi ndi zinthu zotani zimene zingafune khama ngati limenelo? Mwina mungapeze lemba logwidwa mawu limene simukulimvetsa bwino. Kapena mungakhale musakuona mmene likugwirizanira ndi nkhani imene ikufotokozedwa. Mwinanso mungaone kuti mfundo inayake mukuimva m’nkhaniyo koma osati kwenikweni moti n’kuifotokozera munthu wina bwinobwino. M’malo mongozidutsa mfundo zoterozo, n’chanzeru kuzifufuza mutamaliza kuphunzira zimene mwaziyamba kale.

      Pamene mtumwi Paulo analemba kalata yake yokhala ndi mfundo zambiri kwa Akristu achihebri, cham’katikati mwa kalatayo anaima kaye ndi kunena kuti: “Mutu wa izi tanenazi ndi uwu.” (Aheb. 8:1) Kodi inunso mumadzikumbutsa motero nthaŵi ndi nthaŵi? Taonani chifukwa chimene Paulo anachitira zimenezo. M’machaputala oyambirira a kalata yake, anali atasonyeza kale kuti Kristu monga Mkulu wa Ansembe wa Mulungu anali ataloŵa kale kumwamba kwenikweniko. (Aheb. 4:14–5:10; 6:20) Komabe, mwa kumveketsa ndi kugogomeza mfundo yaikulu imeneyo kumayambiriro kwa chaputala 8, Paulo anakonzekeretsa maganizo a aŵerengi a nkhani yake kuti akalingalire mozama za mmene mfundoyo imakhudzira miyoyo yawo. Anafotokoza kuti Kristu anakaonekera pamaso pa Mulungu m’malo mwa iwo ndi kuti anawatsegulira njira yokaloŵera ku “malo opatulika” kumwamba. (Aheb. 9:24; 10:19-22) Kutsimikizika kwa chiyembekezo chawo kunawathandiza kugwiritsa ntchito uphungu wa m’kalata yake wonena za chikhulupiriro, chipiriro, ndi khalidwe lachikristu. Mofananamo, pamene tikuphunzira, kuzika maganizo pa mfundo zazikulu kudzatithandiza kuona mmene nkhaniyo akuifotokozera ndipo kudzakhomereza m’maganizo mwathu zifukwa zomveka zochitira zinthu mogwirizana ndi nkhaniyo.

      Kodi kuphunzira kwanu panokha kudzakulimbikitsani kuchitapo kanthu? Funso limeneli n’lofunika kwambiri. Mukaphunzira mfundo inayake, dzifunseni kuti: ‘Kodi mfundoyi iyenera kukhudza motani maganizo anga ndi zolinga zanga m’moyo? Kodi mfundo imeneyi ndingaigwiritse ntchito motani pothetsa mavuto, popanga chosankha, kapena pokwaniritsa cholinga changa? Kodi ndingaigwiritse ntchito motani m’banja langa, mu ulaliki, mumpingo?’ Ganizirani mafunso ameneŵa mwa pemphero, ndi kulingalira mikhalidwe yeniyeni imene mungagwiritsepo ntchito zimene mwaphunzirazo.

      Mukamaliza mutu kapena nkhani, tengani nthaŵi yobwereza m’maganizo mwachidule. Onani ngati mungakumbukire mfundo zazikulu ndi zifukwa zake. Njira imeneyi idzakuthandizani kukumbukira mfundozo zikadzafunika m’tsogolo.

      Zimene Muyenera Kuphunzira

      Monga anthu a Yehova, tili ndi zambiri zoti tiphunzire. Koma kodi tiyenera kuyambira pati? Tsiku ndi tsiku, tiyenera kuphunzira lemba la tsiku ndi ndemanga zake m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku. Mlungu ndi mlungu, timafika pamisonkhano yampingo, ndipo kuphunzira kumene timachita pokonzekera misonkhano imeneyi kudzatithandiza kupindula zambiri. Kuwonjezera apo, ena agwiritsa ntchito nthaŵi mwanzeru mwa kuphunzira mabuku athu achikristu amene analembedwa m’mbuyomo iwo asanaphunzire choonadi. Ena amasankhula mavesi ena a kuŵerenga Baibulo kwawo kwa mlungu ndi mlungu ndi kuwaphunzira mozamirapo.

      Koma bwanji ngati mikhalidwe yanu sikukulolani kuphunzira mosamala nkhani zonse zokaphunzira pamisonkhano yampingo ya mlungu ndi mlungu? Pewani chizolowezi choipa chongoŵerenga nkhanizo kungoti muzimalize, kapenanso osaziphunzira n’komwe ati chifukwa simungazimalize. M’malo mwake, onani kuti mungaphunzire kufika pati, ndipo phunzirani zomwezo bwino lomwe. Teroni mlungu ndi mlungu. M’kupita kwa nthaŵi, yesetsani kulowetsapo misonkhano inanso.

      ‘Manga Nyumba Yako’

      Yehova amafuna kuti mitu ya mabanja izigwira ntchito zolimba kuti izipeza zofunika za mabanja awo okondekawo. “Longosola ntchito yako panjapo,” imatero Miyambo 24:27, “nuikonzeretu kumunda.” Komabe, simuyenera kunyalanyaza zosowa zauzimu za banja lanu. N’chifukwa chake vesilo likupitiriza kuti: “Pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.” Kodi mitu ya mabanja ingachite motani zimenezi? Miyambo 24:3 imati: ‘Luntha likhazikitsa [nyumba].’

      Kodi luntha lingapindulitse motani banja lanu? Luntha ndilo luso la maganizo lozindikira zinthu zobisika. Tinganene kuti phunziro la banja logwira mtima limayamba ndi kuliphunzira banja lanu lenilenilo. Kodi a m’banja lanu akupita patsogolo motani mwauzimu? Mvetserani pamene mukukambirana nawo. Kodi pakuoneka mzimu wodandaula kapena woipidwa ndi zinthu? Kodi amakondetsa chuma? Pamene muli muulaliki limodzi ndi ana anu, kodi amachita manyazi poonekera kwa anzawo kuti ndi Mboni za Yehova? Kodi amasangalala ndi pulogalamu yoŵerenga ndi kuphunzira Baibulo monga banja? Kodi akutengadi njira ya Yehova kukhala njira ya moyo wawo? Popenda mosamala mudzazindikira zimene muyenera kuchita monga mutu wa banja, kuti mukhazikitse ndi kukulitsa makhalidwe auzimu mwa aliyense wa m’banja lanu.

      Yang’anani mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kuti mupeze nkhani zokhudza zosowa zakutizakuti. Ndiyeno dziŵitsirantuni banja lanu zimene mudzaphunzire kotero kuti aganizirepo za nkhaniyo. Onetsetsani kuti paphunziropo pakukhala mkhalidwe wachikondi. Popanda kulanga aliyense kapena kuchititsa wina manyazi, unikani phindu la nkhaniyo, ndipo igwirizanitseni ndi zosowa za banja lanu. Onetsetsani kuti aliyense akutengapo mbali. Thandizani aliyense kuona mmene Mawu a Yehova alili “angwiro” popereka thandizo pa chosowa chilichonse pamoyo.—Sal. 19:7.

      Kupeza Mapindu Ambiri

      Anthu ozindikira koma opanda luntha lauzimu amatha kufufuza chilengedwe, zochitika zapadziko, ngakhalenso kudzifufuza iwo eniwo, koma amalephera kuzindikira tanthauzo lenileni la zimene amaona. Koma, mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, anthu amene amaphunzira Mawu a Mulungu nthaŵi zonse amatha kuona mu zinthu zimenezi, dzanja la Mulungu, kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo, ndi kukwaniritsidwa kwa chifuniro cha Mulungu chodalitsa anthu omvera.—Marko 13:4-29; Aroma 1:20; Chiv. 12:12.

      Komabe, luntha lodabwitsa limenelo lisatipangitse kukhala anthu onyada. M’malo mwake, kupenda Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku kuyenera kutithandiza kukhalabe odzichepetsa. (Deut. 17:18-20) Timatetezekanso ku “chenjerero la uchimo” chifukwa Mawu a Mulungu akakhala m’mitima mwathu, chikoka cha uchimo sichitha kugonjetsa mtima wathu potsutsana nacho. (Aheb. 2:1; 3:13; Akol. 3:5-10) Tikamatero, ‘tidzayenda koyenera Ambuye pom’kondweretsa monsemo, pamene tikubala zipatso m’ntchito yonse yabwino.’ (Akol. 1:10) Kuchita zimenezo ndiko cholinga chathu pophunzira Mawu a Mulungu, ndipo kuchikwaniritsa ndiko mphoto yopambana.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena