Kodi Mulungu Wakuitanani mu Mtendere?
“Koma ngati wosakhulupirirayo achoka, achoke; m’milandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo kapena mlongoyo, koma Mulungu watiitana ife mu mtendere.”—1 AKORINTO 7:15.
1. Mwamalemba, ndimotani mmene ukwati uyenera kuwonedwera?
YEHOVA sanafune nkomwe kuti ukwati utsogolere ku kulekana kapena chisudzulo chowawitsa mtima. Ukwati unayenera kukhala chomangira ‘cha thuupi limodzi’ chosatha, chotulukapo m’chisangalalo, mpumulo, ndi mtendere. (Genesis 2:24; Rute 1:9) Mwachisawawa, Malemba amalangiza anthu okwatirana kukhala limodzi, ngakhale ngati mmodzi wa mu ukwati ali Mkristu ndipo winayo ali wosakhulupirira. (1 Akorinto 7:12-16) M’kuwonjezerapo, kuchita mwachinyengo komwe kumatulukapo m’kuthetsa zomangira za ukwati kumapangitsa mmodzi kukhala woŵerengera mwa makhalidwe abwino kwa Mulungu, yemwe ‘adana nako kulekana.’—Malaki 2:13-16.
2. Ndimotani mmene Akristu amawonera kulekana ndi chisudzulo?
2 Kupanda ungwiro kwa umunthu ndi nsonga zina nthaŵi zina zatsogolera ku kulekana kapena kusudzulana ngakhale pakati pa atumiki obatizidwa a Mulungu. Chifukwa cha kawonedwe ka pamwamba kamene Akristu ali nako kaamba ka ukwati, ngakhale kuli tero, kaŵirikaŵiri masitepi amenewa amatengedwa kokha pambuyo pa kuyesetsa kopitiriza ku kugwiririra maukwati pamodzi. M’mbali imeneyi, Mulungu iyemwini anaika chitsanzo chapamwamba. Monga “mwamuna” wa Israyeli wakale, iye anapirira zaka mazana angapo za kuwuma mutu, kuwukira, ndi chigololo chauzimu ku mbali ya anthu ake. (Yesaya 54:1-5; Yeremiya 3:14-17; Hoseya 1:10, 11; 3:1-5) Kokha pambuyo pa kupyola malire a kuwasunga ndi pamene Yehova anachotsa iwo monga mtundu.—Mateyu 23:37, 38.
3. (a) Ndi kaamba ka zifukwa zovomerezeka mwa Malemba ziti zimene Mkristu angadzilekanitsire kwa mnzake wa mu ukwati? (b) Kusudzulana kwa m’Malemba kuli kothekera pansi pa mikhalidwe yotani?
3 Nthaŵi zina, akulu a mu mpingo amafikiridwa ndi akhulupiriri anzawo omafuna thandizo ndi mavuto a m’banja okulira. Akulu alibe lamulo la kuwuza aliyense kuchoka kapena kusudzula mnzake wa mu ukwati, koma iwo angaloze ku chimene Mawu a Mulungu amanena pa nkhani zimenezi. Monga mmene zasonyezedwera m’nkhani yapitayo, kulekana kuli kovomerezedwa m’Baibulo m’nkhani ya kusachirikiza kodzdifunira, kuipsya kwa kuthupi konkitsa, kapena kuika uzimu m’ngozi kotheratu. Chawonedwanso kuti kusudzula kwa m’Malemba ndi kuthekera kwa kukwatiranso kwa mtsogolo kwa munthu wina kuli kothekera ngati mnzanu wa mu ukwatiyo wachita “dama,” lomwe limakupatira mitundu yosiyanasiyana ya maunansi a kugonana a chisembwere. (Mateyu 19:9) Mwachibadwa, kulekana kapena chisudzulo siziyenera kukhala mapeto ofikiridwa ndi kuiwalidwa, popeza kuti chingakhale chothekera kubwezeretsa mtendere wa mu ukwati, ndipo ngakhale chigololo kapena mitundu ina ya dama chingakhululukidwe ndi mnzanu wa mu ukwati wopanda liwongoyo.—Mateyu 5:31, 32; yerekezani ndi Hoseya 3:1-3.
4. (a) Mwachidule fupikitsani chimene Paulo anawuza Akristu okwatira pa 1 Akorinto 7:10-16. (b) Ndi liti pamene chinganenedwe kuti: “Mulungu wakuitanani mu mtendere”?
4 Monga mmene tawonera m’nkhani yapitayo, mtumwi Paulo anafulumiza Akristu okwatira kusasiya anzawo a mu ukwati. (1 Akorinto 7:10-16) M’chiyang’aniro cha mawu a Paulo, ngati mnzake wa mu ukwati wosakhulupirira asankha kukhala ndi mnzake wa mu ukwati Wachikristu, wokhulupirirayo ayenera kuyesa kumuthandiza iye mwauzimu. (1 Petro 3:1-4) Kutembenuka kwake kudzachita zambiri kupanga nyumba malo a mpumulo ndi mtendere. Komabe, ngati wosakhulupirirayo atsutsa chikhulupiriro cha mnzake wa mu ukwati wokhulupirira mwamphamvu kotero kuti asankha kulekana, nchiyani chimene Mkristuyo angachite? Ngati wokhulupirirayo ayesera kumkakamiza kukhala, wosakhulupirirayo angapange mkhalidwewo kukhala wosagwirizanitsika kotero kuti Mkristuyo angachotseredwe mtendere kotheratu. Chotero m’zikondwerero za mtendere, wokhulupirirayo angalole wosakhulupirirayo kuchoka. (Mateyu 5:9) Kokha pamene mnzanu wa mu ukwati wosakhulupirirayo achoka ndi pamene chinganenedwe kuti: “Mulungu wakuitanani mu mtendere.” Mawu amenewa sangagwiritsiridwe ntchito moyenerera kulungamitsa kulekana kwa okwatirana aŵiri achikristu pa maziko osakhala a m’malemba kapena a bodza.
5. Ndi mafunso otani tsopano amene afunikira kulingalira kwathu?
5 Kulekana kulikonse kapena chisudzulo kuli ndi nsonga zake zaumwini, ndipo palibe “dongosolo lokhazikika” lomwe limakwaniritsa nkhani iriyonse. Koma kodi ndi mavuto otani amene Mkristu wolekedwa kapena wosudzulidwa angakumanizane nawo? Nchiyani chimene chingachitidwe ponena za iwo? Ndipo ndimotani mmene ena angakhalire a thandizo?
Zosowa za Malingaliro kapena za Kugonana
6. Ponena za mavuto, nchiyani chimene chinganenedwe ponena za kulekana kapena kusudzulana?
6 Kulekana kapena kusudzulana kovomerezedwa mwa Malemba kudzathetsa mavuto ena. Koma kachitidwe koteroko m’chenicheni kamatulukapo m’kusinthanitsa mpambo umodzi wa mavuto a wina kaamba ka ena. Mwachitsanzo, Mkristu mmodzi wosudzulidwa ananena kuti: “Sindingathe kulephera kuyamikira Yehova kuti tsopano ndiri ndi mtendere.” Koma iye anavomereza kuti: “Sichiri chopepuka kulera ana monga kholo limodzi. Ndipo nthaŵi zina wina angakhale wosungulumwa ndi wopsyinjika koposa. Ngakhale mwa kugonana sichiri chopepuka. Wina ayenera kusinthira ku mtundu wa moyo wosiyana kotheratu.”a
7. Nchifukwa ninji Mkristu ayenera kulingalira mosamalitsa ponena za zotulukapo za kulekana kapena kusudzulana?
7 Ngati Mkristu ali ndi chosankha, chotero, iye ayenera kulingalira mosamalitsa ponena za zotulukapo zothekera za kulekana kapena kusudzulana. Mwachitsanzo, lingalirani zosowa za malingaliro, mwinamwake chikhumbo cha mkazi kaamba ka woyanjana naye wa mwamuna. (Yerekezani ndi Genesis 3:16.) Mkazi wosudzulidwa angakhale ndi ziyembekezo zamphamvu za kukwatiwanso. Ena amakhumba kumasulidwa kuchokera ku ukwati woyesa, koma kodi iwo ali okonzekera kulandira kuthekera kwakuti sipangakhale mwaŵi wa kukwatiwanso?
8. (a) M’chiyang’aniro cha 1 Akorinto 7:11, nkuchiyani kumene okwatirana Achikristu olekana angapereke lingaliro la pemphero? (b) Ndi zosowa zotani zimene sizifunikira kuchepetsedwa pamene tikulingalira kulekana kapena kusudzulana?
8 Paulo analemba kuti: “Ngati mkaziyo achoka, akhale wosakwatiwa kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo.” (1 akorinto 7:11) Ndi kuyesayesa kwinawake, chingakhale chothekera kwa mkazi ‘kuyanjanitsidwanso’ ndi mwamuna wake kapena ‘kukhala wogwirizananso’ kwa iye. Ngati okwatirana achikristu alekana, chotero, iwo ayenera kupatsa kugwirizanansoko lingaliro losamalitsa, la pemphero. M’kuwonjezerapo, iwo sayenera kunyalanyaza chenicheni chakuti zisonkhezero za kugonana zingadzetse ngozi. Ndimotani mmene Mulungu mothekera akawonera iwo ngati kulephera kwawo kwa kugwirizana kukatulukapo kugwera mu chisembwere? Chochitira chitsanzo tsoka limeneli chiri chokumana nacho cha mkazi wina wobatizidwa. Pambuyo pa kusudzulana, iye anayamba kupita kocheza ndi mwamuna wa kudziko, mwamsanga anakhala ndi pakati, ndipo anachotsedwa. Ngakhale kuti iye pambuyo pake anabwezeretsedwanso, chokumana nacho chake chimagogomezera kufunika kwa kukhala ochenjera ndipo mwa pemphero kudalira pa Yehova kotero kuti tipewe ‘kuchimwira Mulungu.’ (Genesis 39:7-12) Chirinso chachidziŵikire kuti zosowa za malingaliro ndi za kugonana siziyenera kuchepetsedwa pamene kulekana kapena kusudzulana kulingaliridwa pachiyambi penipeni.
Kusungulumwa Kungachepetsedwe
9. Ndimotani mmene tingathandizire Akristu olekanitsidwa kapena osudzulidwa kuthetsa kusungulumwa?
9 Ngati kulekana kapena chisudzulo chiri chosapeweka, mavuto otulukapo akayenera kuyang’anizidwa. Mwachitsanzo, kusungulumwa kuli vuto lokulira kaamba ka Akristu ena olekanitsidwa kapena osudzulidwa. Nchiyani chimene ena angachite ponena za ichi? Chabwino, akulu a mu mpingo ndi ena angasonyeze chikondwerero chauzimu mwa anthu oterowo, kufunafuna kuwalimbikitsa iwo. (Yerekezani ndi 1 Atesalonika 5:14.) Pakati pa zinthu zina, tiyenera mwa kamodzikamodzi kuwaitana anthu amenewa ndi ana awo kunyumba zathu kaamba ka chakudya chabwino ndi kukambitsirana komangirira ndi banja lathu. Sichiri choyenerera kukhala ndi phwando lalikulu, popeza kuti “kudya masamba pali chikondano kuposa ng’ombe zonenepa pali udani.” (Miyambo 15:17) Madzulowo angaphatikizepo kusimba zokumana nazo zosangalalidwa mu utumiki kapena phunziro la gulu m’kukonzekera kaamba ka msonkhano Wachikristu.
10, 11. (a) Ndi mwanjira ina yotani mmene Mkristu wolekedwa kapena wosudzulidwa angathandizidwire? (b) Nchifukwa chotani chimene chiripo kaamba ka kukhalira wochenjera?
10 Kukhala ndi kholo losudzulidwa kapena lolekedwa ndi ana ake atagwirizana ndi banja lanu mu utumiki wa m’munda kungathandizenso iwo kuchita ndi kusungulumwa. Ndithudi, ena sangatenge malo a kholo losowalo, koma mkazi Wachikristu mmodzi wosudzulidwa ananena kuti: “Mavuto a kulera ana anga popanda mwamuna m’nyumba achepetsedwa mokulira ndi thandizo la akulu ndi atumiki mu mpingo omwe ayesera kulowa m’malo m’njira zokhoza kugwira ntchito.”
11 Komabe, pali chifukwa cha kukhalira ochenjera. Mlongo mmodzi anavomereza kuti: “Popeza kuti mwana wanga wamwamuna ali wopanda atate, mbale mwachifundo anatenga chikondwerero mwa iye. . . . Ndinayamba kuwona mmene iye analiri wachifundo ndi woolowa manja kwa mwana wanga wamwamuna, ndipo zikhumbo zolakwa zinayamba kukula mkati mwanga. Chinali monga kukulitsa kwa Davide chikhumbo cholakwa kaamba ka china chake chomwe sichinali chake.” (2 Samueli 11:1-4) Ngakhale kuti mkhalidwe woipa wa chisembwere cha kugonana sunachitike, mkazi ameneyu anachititsidwa manyazi ndi malingaliro ake ndi kachitidwe kake kotyasira, anafunafuna chikhululukiro cha Yehova, ndipo anathetsa kuyanjana ndi mbaleyo. Ichi chikuchitira chitsanzo bwino chotani nanga chifuno cha kukana malingaliro oipa ndi “kupewa kuwonjezereka kwa choipa”!—1 Atesalonika 5:22, The New American Bible; Agalatiya 5:24.
12. Munthu angachepetse kusungulumwa kwake mwa kutenga kachitidwe kotsimikizirika kotani?
12 Kusungulumwa kungachepetsedwe mwa kuchita zinthu kaamba ka ena. “Ngati muli wotanganitsidwa kufikira ndi kuthandiza ena, palibe malo kaamba ka kudzimverera chisoni ndi kusungulumwa,” anatero mlongo wina amene zomangira zake za ukwati zinawonongedwa. “Kufikira” koteroko ndi munthu wolekedwa kapena wosudzulidwa kungaphatikizepo kuitana banja kunyumba ya wina kaamba ka kuyanjana kwa madzulo komangirira mwauzimu. Ngati ichi mochepera sichiri chothekera kaamba ka zifukwa za chuma kapena zina zake, mungachezere ndi kulimbikitsa odwala kapena ena. Mungakhalenso okhoza kuthandiza achikulire ndi kugula kapena ntchito zosiyanasiyana. Dziperekeni inu eni m’njira zoterozo, ndipo mudzakhala ndi umboni wowonjezereka wakuti “muli chimwemwe chambiri m’kupatsa koposa m’kulandira.”—Machitidwe 20:35, NW.
13. Ndi liti lomwe liri thandizo lina la kulakira kusungulumwa?
13 Thandizo lina m’kulaka kusungulumwa liri kutenga chiyambi mokhazikika kugwirizana ndi akhulupiriri anzanu m’ntchito ya kulalikira Ufumu. “Nthaŵi zina, ndimadzimva wosungulumwa kaamba ka mwamuna,” anavomereza tero mlongo wina, “koma ndi kuwonjezereka kwa ntchito yanga ya utumiki wa m’munda ndi ufulu watsopano wa kuyanjana ndi abale ndi alongo, nyengo zimenezi ziri zosabwerezabwereza ndipo za kanthaŵi kochepa.” Kuchitira umboni kokhazikika kwa kunyumba ndi nyumba kungatsogolere ku maulendo obwereza ndi maphunziro a Baibulo a panyumba ndi anthu okondwerera, ena a amene angakhale anthu odzipereka a Yehova. Ndithudi, kulaka kusungulumwa sikuli chifukwa chathu cha kudzilowetsa mu utumiki, koma chimenecho chingakhale chotulukapo chimodzi cha ntchito yosangalatsa ndi yodalitsika imeneyi.—Miyambo 10:22.
14. Ndi machitachita otani amene ayenera kukhala ndi chiyambukiro chabwino pa Akristu olekedwa kapena osudzulidwa?
14 Anthu onse a Yehova angapindule mwauzimu kuchokera m’kugawana mu utumiki, kutenga mbali mu misonkhanno Yachikristu, ndi ‘kufuna choyamba Ufumu.’ (Mateyu 6:33) Popeza kuti machitachita omangirira amenewa ali ndi chotulukapo chabwino pa atumiki a Yehova mwachisawawa, zolondola zoterozo zingamangirirenso Akristu olekedwa kapena osudzulidwa. Ayi, machitachita amenewa sadzathetsa mavuto awo onse, koma ayenera kuwongolera kawonedwe kawo.
Pemphero Limachita Mbali Yokulira
15. Pemphero lingachite mbali yotani m’miyoyo ya awo omwe ayenera kusinthira ku umbeta kachiŵirinso?
15 Mlongo wina Wachikristu amene anafunikira kusinthira ku umbeta kachiŵirinso anathandizidwa mwa “kukhala wotanganitsidwa mu utumiki wa m’munda . . . ndi kuchezera odwala, okalamba, ndi osakangalika.” Koma iye anawonjezera kuti: “Pa nthaŵi iriyonse pamene ndimadzimva wosungulumwa, ndimapanga ulendo ndi kupemphera kaamba ka mphamvu, ndikumadziŵa kuti Satana ali wotanganitsidwa kwambiri.” Inde, pemphero la mtima wonse liri lofunikira ngati umphumphu kwa Mulungu uyenera kusungiriridwa. Mapemphero a Akristu olekedwa kapena osudzulidwa angaphatikizepo kupempha kaamba ka mzimu wa Yehova ndi chipatso chake cha kudiletsa kotero kuti alamulire zisonkhezero za kugonana. (Luka 11:13; Agalatiya 5:22, 23; Akolose 3:5, 6) M’kuwonjezerapo, popeza kuti kupanga zosankha komwe kunkapangidwa ndi mwamuna kungapangitse mavuto kaamba ka akazi olekedwa kapena osudzulidwa, iwo angafunikirenso kupemphera kaamba ka thandizo la Mulungu m’kulingalira nkhanizi mwanzeru ndi kuchita ndi ziyeso zosiyanasiyana.—Yakobo 1:2-8.
16. M’chigwirizano ndi kulekana kapena kusudzulana, nchiyani chimene chinganenedwe ponena za malingaliro a kudzimva wa liwongo?
16 Malingaliro a kudzimva wa liwongo angatsimikizire kukhala oyesa. Mkristu wina anavomereza kuti: “Liwongo lomwe mumalimva mkati mwa chisudzulo, ngakhale ngati simuli munthu wa liwongoyo, lingakhale lowawa.” Ndithudi, malingaliro a kudzimva wa liwongo ali omvetsetseka ngati chilekano kapena chisudzulo chichitika chifukwa chakuti mmodzi mosalungamitsika anakana kukwaniritsa mathayo aukwati. (1 Akorinto 7:3-5) Koma ngati kulekana kapena chisudzulo chichitika kaamba ka chifukwa cha m’Malemba pambuyo pa kulingalira kwa pemphero, chikakhala choyenera kupemphera kaamba ka thandizo la Yehova kulaka malingaliro a liwongo osayenera. Chingawonjezeredwe kuti akulu mu mpingo ayenera kukhala osamalira kupereka uphungu wozikidwa pa Baibulo ndi kusalemeretsa uphungu wawo m’njira imene Mkristuyo angapangidwe kudzimva wa liwongo ponena za kupeza kapena kulola kulekana kapena chisudzulo chovomerezeka ndi Baibulo.
Kuchinjirizidwa ndi “Mtendere wa Mulungu”
17. Nchiyani chomwe chingathandize Akristu onse kukhala achimwemwe ndi okhazikika m’dziko lovutitsidwali?
17 Akristu olekanitsidwa kapena osudzulidwa kaŵirikaŵiri ali ndi mavuto apadera. Komabe, ku ukulu wina, “zowawa zomwezo ziri nkukwaniridwa pa abale [athu] ali m’dziko.” (1 Petro 5:6-11) Mwachitsanzo, chizunzo chimayambukira onse amene amatumikira Yehova, ndipo Akristu ambiri amayang’anizana ndi mavuto a za chuma kapena za umoyo, kukhumudwitsidwa, ziyeso, ndi zina zotero. Mofanana ndi mboni zina za Yehova, chotero, Mkristu wolekedwayo kapena wosudzulidwa ayenera kusungirira kukwaniritsa zosowa zauzimu mwa phunziro la Baibulo, kupezeka pa misonkhano mokhazikika, utumiki wa m’munda wokangalika, moyo wabwino wa utumiki wopatulika, ndi pemphero lokhazikika kuti akhalebe moyandikira kwa Yehova. (Mateyu 5:3) Kulephera kuchita tero kukaika m’ngozi uzimu wa Mkristu aliyense, pamene kuli kwakuti ‘kufuna choyamba Ufumu’ kumapatsa mboni yokhulupirika iriyonse ya Yehova mlingo wodziŵika wa chimwemwe ndi kukhazikika m’dziko iri lovutitsidwa.
18. Ndi mafunso ndi masitepi otani amene afunikira kulingalira mosamalitsa ndi okwatirana Achikristu olekana?
18 Kukhazikika kwathu kwauzimu kumadalira pa kugwiritsira ntchito kwaumwini kwa Mawu a Mulungu. Chotero, ngati muli Mkristu wolekanitsidwa ndi mnzanu wa mu ukwati yemwe alinso wodzipereka kwa Mulungu, kodi mwatenga ku mtima uphungu wa Paulo pa 1 Akorinto 7:10-16? Makamaka ngati kulekana kwapitiriza kwa nthaŵi yaitali, mukachita bwino kukpanga kuyanjanitsidwanso kukhala nkhani ya pemphero lochokera ku mtima. Mungadzifunsenso inu mwini kuti: Nchiyani chimene Yehova akuyembekezera kwa ine monga munthu wokwatira? Kodi akristu okwatirana sayenera kugwirizanitsa miyoyo yawo ndi zifuno zaumulungu kaamba ka awo omwe akulowa mu ukwati? Kodi chingakhale chakuti sitikukumana ndi dalitso la Yehova chifukwa chakuti talephera kulemekeza malumbiro athu a ukwati? Tangolingalirani za ubwino womwe ungakwaniritsidwe ngati munakambitsirana nkhanizo modzichepetsa, kupemphera mowona mtima, ndi kugwirirapo ntchito mwakhama kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu m’moyo. Chikakhala chabwino chotani nanga ngati nonse aŵirinu mukathetsa mavuto anu a ukwati ndipo kachiŵirinso kusangalala ndi moyo pamodzi m’nyumba ya mpumulo ndi mtendere!
19. Mogwirizana ndi Afilipi 4:6, 7, ndi chinthu cha mtengo wapatali chotani chimene atumiki onse a Yehova angasangalale nacho?
19 Atumiki okhulupirika onse a Yehova afunikira ndipo angasangalale ndi chinachake cha mtengo wapatali—“mtendere wa Mulungu wa kupambana chidziŵitso chonse.” Monga Akristu, tingakhale ndi mtendere wa mtengo wapatali umenewu ngati tilabadira mawu a Paulo: “Musadere nkhaŵa konse, komatu m’zonse ndi pemphero ndi pembedzero pamodzi ndi chiyamiko zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu; ndipo mtendere wa Mulungu wa kupambana chidziŵitso chonse udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 4:6, 7.
20. (a) Nchiyani chimene chiri “mtendere wa Mulungu”? (b) Mosasamala kanthu za mkhalidwe wathu wa ukwati, nchiyani chimene tiyenera kuchita?
20 Mtendere umenewo uli kudekha mtima ndi bata zopatsidwa ndi Mulungu, ngakhale pakati pa mikhalidwe yoyesa kwambiri. Umachokera pa unansi wathithithi ndi Yehova ndi chidziŵitso chakuti tikuchita chomwe chiri chosangalatsa m’maso mwake. Awo okhala ndi “mtendere wa Mulungu” amalola mzimu wake kuwasonkhezera iwo, ndipo samagonjetsedwa ndi kudera nkhaŵa. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti amadziŵa kuti palibe chirichonse chomwe chingaloledwe kuchitika kwa iwo chomwe sichiri mwa chilolezo chaumulungu. (Aefeso 4:30; yerekezani ndi Machitidwe 11:26.) Chotero kaya tiri osakwatira kapena okwatira, olekedwa kapena osudzulidwa, lolani kuti tiwone kukhala wa mtengo wapatali “mtendere wa Mulungu.” Ndipo lolani kuti tikhale nacho chidaliro chofananacho chonga cha Davide, yemwe analengeza kuti: “Ndi mtendere ndidzagona pansi pomwepo ndidzagona tulo, chifukwa inu, Yehova, mundikhalitsa ine ndikhale bwino.”—Salmo 4:8.
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka kukambitsirana kwa mabanja a kholo limodzi, chonde onani Nsanja ya Olonda ya March 15, 1981, masamba 12-26.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Ndi pansi pa mikhalidwe yotani pamene chinganenedwe kuti: “Mulungu wakuitanani mu mtendere”?
◻ Ndimotani mmene kusungulumwa kungachepetsedwere?
◻ Ndi mbali yotani imene pemphero liyenera kuchita m’moyo wa Mkristu wolekedwa kapena wosudzulidwa?
◻ Ndimotani mmene mungalongosolere “mtendere wa Mulungu” umene umachinjiriza mitima ya atumiki a Yehova osakwatira, okwatira, olekedwa, kapena osudzulidwa?
[Chithunzi patsamba 29]
Pemphero lingabweretsere Akristu onse okhulupirika “mtendere wa Mulungu” umene udzachinjiriza mitima yawo ndi mphamvu za malingaliro