Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Mulungu Amaona Kuti Akazi Ndi Otsika?
    Nsanja ya Olonda—2012 | September 1
    • Kodi Mulungu Amaona Kuti Akazi Ndi Otsika?

      “Mkazi ndi amene anayambitsa uchimo n’chifukwa chake tonse timafa.”​—ECCLESIASTICUS (buku lowonjezera la m’Baibulo) LOLEMBEDWA M’MA 100 B.C.E.

      “Inu ndi amene mumatichimwitsa: Inu ndi amene munayambitsa kudya mtengo woletsedwa uja: Ndinu amene munayamba kuphwanya lamulo la Mulungu . . . Inutu ndi amene munachimwitsa Adamu, yemwe analengedwa m’chifanizo cha Mulungu.”​—ZIMENE TERTULLIAN ANANENA M’BUKU LAKE LOLEMBEDWA M’MA 100 C.E. PONENA ZA KAVALIDWE KA AKAZI.

      MAWU amenewa sapezeka m’Baibulo. Koma kwa zaka zambiri anthu akhala akuchitira nkhanza akazi chifukwa cha mawuwa. Masiku anonso, anthu ena ochita zinthu monyanyira, amachitira nkhanza akazi poganiza kuti mabuku achipembedzo amasonyeza kuti akaziwo ndi amene ayenera kuimbidwa mlandu pa mavuto onse amene anthu akukumana nawo. Kodi Mulungu amafuna kuti akazi azinyozedwa komanso kuchitiridwa nkhanza? Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi? Tiyeni tione.

      Kodi Mulungu anatemberera akazi?

      Ayi. Koma “njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi,” ndi imene Mulungu ‘anaitemberera.’ (Chivumbulutso 12:9; Genesis 3:14) Pamene Mulungu ananena kuti Adamu ‘adzalamulira’ mkazi wake, sankatanthauza kuti mwamuna ayenera kumuona mkazi wake ngati kapolo. (Genesis 3:16) Mulungu anangoneneratu za mavuto amene Adamu ndi Hava adzakumane nawo chifukwa cha uchimo.

      Choncho nkhanza zimene akazi amakumana nazo ndi zotsatira za uchimo wa anthu osati cholinga cha Mulungu. Baibulo siliphunzitsa kuti akazi ayenera kuponderezedwa ndi amuna chifukwa cha tchimo limene linachitika m’munda wa Edeni.​—Aroma 5:12.

      Kodi Mulungu analenga akazi kukhala otsika poyerekezera ndi amuna?

      Ayi. Lemba la Genesis 1:27 limati: “Mulungu analenga munthu m’chifaniziro chake, m’chifaniziro cha Mulungu anam’lenga iye. Anawalenga mwamuna ndi mkazi.” Choncho kuyambira pa chiyambi, Mulungu analenga anthu, mwamuna ndi mkazi yemwe, kuti azitha kusonyeza makhalidwe amene Mulungu ali nawo. Ngakhale kuti Adamu ndi Hava anali osiyana, iwo anapatsidwa malamulo ndiponso ufulu wofanana.​—Genesis 1:28-31.

      Mulungu asanalenge Hava, ananena kuti: “Ndimupangira womuthandiza [Adamu], monga mnzake womuyenerera.” (Genesis 2:18) Kodi mawu akuti “mnzake” akusonyeza kuti mkazi anali wotsika poyerekeza ndi mwamuna? Ayi. Taganizirani ntchito imene dokotala ndi nesi amagwira pa nthawi imene dokotalayo akuchita opaleshoni. Kodi dokotala kapena nesi angagwire ntchito yake popanda mnzakeyo? N’zosatheka. Ngakhale kuti dokotalayo ndi amene amachita opaleshoni sitinganene kuti iye ndi wofunika kwambiri kuposa nesiyo. Mofanana ndi zimenezi, Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi kuti azithandizana osati kuti azipikisana.​—Genesis 2:24.

      Kodi n’chiyani chimasonyeza kuti Mulungu saona kuti akazi ndi otsika?

      Mulungu anadziwiratu kuti amuna ena azidzapondereza akazi, choncho anapereka malamulo oteteza akazi. Ponena za Chilamulo cha Mose chimene chinakhazikitsidwa cha m’ma 1500 B.C.E., wolemba mabuku wina, (Laure Aynard) analemba kuti: “Malamulo ambiri amene anali m’Chilamulo anali oteteza akazi.”​—La Bible au féminin (Baibulo Lonena za Akazi).

      Mwachitsanzo, m’Chilamulo munali malamulo oti munthu azilemekeza abambo ndi amayi ake. (Ekisodo 20:12; 21:15, 17) Munalinso lamulo lokhudza amayi oyembekezera. (Ekisodo 21:22) Masiku ano, kutsatira mfundo za malamulo a Mulungu amenewa kungathandize kuti akazi azitetezedwa ngakhale kuti m’mayiko ambiri muli malamulo opondereza akazi. Koma pali zinanso zimene zimasonyeza kuti Mulungu saona kuti akazi ndi otsika.

      Chilamulo Chinasonyeza Mmene Mulungu Amaonera Akazi

      Chilamulo chimene Yehova Mulungu anapatsa Aisiraeli chinawathandiza kwambiri kukhala ndi thanzi labwino, kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kukhalabe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Aisiraeli akamamvera malamulo a Mulungu, ankakhala “pamwamba pa mitundu yonse ya padziko lapansi.” (Deuteronomo 28:1, 2) Kodi m’Chilamulo munali malamulo otani okhudza akazi? Taonani mfundo zotsatirazi.

      1. Ufulu umene akazi anali nawo. Akazi mu Isiraeli anali ndi ufulu wambiri mosiyana ndi akazi a mitundu ina. Ngakhale kuti mwamuna anapatsidwa udindo wokhala mutu wa banja, iye ankatha kulola mkazi wake ‘kuona munda, kuugula’ n’kulimamo “mpesa.” Ngati mkaziyo anali ndi luso lopota ulusi ndi kuluka nsalu, ankatha kuchita bizinezi yakeyake. (Miyambo 31:11, 16-19) M’Chilamulo cha Mose, akazi ankaonedwa kuti ndi anthu okhala ndi ufulu wawo.

      Akazi achiisiraeli analinso ndi mwayi wokhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Baibulo limafotokoza za Hana amene anapemphera kwa Mulungu za mavuto ake komanso kumulonjeza Mulungu zimene adzachite. (1 Samueli 1:11, 24-28) Panalinso mayi wina wa ku Sunemu amene ankakonda kupita kwa mneneri Elisa pa tsiku la Sabata. (2 Mafumu 4:22-25) Komanso panali akazi ena monga Debora ndi Hulida amene Mulungu ankawagwiritsira ntchito. N’zochititsa chidwi kuti ngakhale ansembe komanso amuna ena otchuka ankafunsira malangizo kwa akazi amenewa.​—Oweruza 4:4-8; 2 Mafumu 22:14-16, 20.

      2. Mwayi wamaphunziro. Popeza pangano la Chilamulo linkakhudzanso akazi, iwo ankakhalapo Chilamulo chikamawerengedwa ndipo anali ndi mwayi wophunzira zimene Chilamulocho chikunena. (Deuteronomo 31:12; Nehemiya 8:2, 8) Akazi ankaphunzitsidwanso kuchita zinthu zina zokhudza kulambira. Mwachitsanzo, ena anali “kutumikira mwadongosolo” pachihema chokumanako ndipo ena anali m’gulu loimba.​—Ekisodo 38:8; 1 Mbiri 25:5, 6.

      Akazi ambiri anali ndi luso lochita bizinezi. (Miyambo 31:24) Pa nthawi imeneyi, anthu a mitundu ina ankaona kuti udindo wophunzitsa ana aamuna ndi wa bambo yekha. Koma mu Isiraeli mayi ankaloledwanso kulangiza ana aamuna mpaka mwanayo atakula. (Miyambo 31:1) N’zodziwikiratu kuti akazi achiisiraeli sankakhala osaphunzira.

      3. Akazi ankalemekezedwa. Limodzi mwa Malamulo Khumi linanena momveka bwino kuti: “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.” (Ekisodo 20:12) Komanso mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Mwana wanga, tamvera malangizo a bambo ako, ndipo usasiye malamulo a mayi ako.”​—Miyambo 1:8.

      M’Chilamulo munalinso malamulo onena za mmene anthu osakwatira angasonyezere ulemu kwa akazi. (Levitiko 18:6, 9; Deuteronomo 22:25, 26) Mwamuna wabwino ankayenera kuganizira zimene mkazi wake angakwanitse ndi zimene sangakwanitse.​—Levitiko 18:19.

      4. Akazi ankatetezedwa. M’Mawu ake, Yehova amanena kuti iye ndi “Tate wa ana amasiye ndi woweruzira akazi amasiye milandu.” M’mawu ena tingati iye ankateteza ufulu wa ana ndi akazi amasiye. (Salimo 68:5; Deuteronomo 10:17, 18) Choncho, mkazi wina wamasiye, yemwe mwamuna wake anali mneneri, atachitiridwa zinthu mopanda chilungamo ndi munthu wina amene anali naye ngongole, Yehova analowererapo ndipo anathandiza mayiyo. Izi zinachititsa kuti mayiyu asachite manyazi.​—2 Mafumu 4:1-7.

      Aisiraeli asanalowe m’Dziko Lolonjezedwa, mwamuna wina dzina lake Tselofekadi anamwalira alibe mwana wamwamuna. Choncho ana ake aakazi asanu anapempha Mose kuti awapatse “cholowa” m’Dziko Lolonjezedwa. Koma Yehova analamula kuti iwo apatsidwenso zinthu zina kuwonjezera pa zimene anapemphazo. Iye anauza Mose kuti: “Uwapatsedi malo monga cholowa chawo, pakati pa abale a bambo awo. Cholowa cha bambo awocho chikhale chawo.” Kuyambira pa nthawi imeneyo, akazi achiisiraeli ankapatsidwa cholowa cha bambo awo komanso iwo akamwalira, ana awo ankapatsidwa cholowacho.​—Numeri 27:1-8.

      Anthu Anayamba Kupotoza Mmene Mulungu Amaonera Akazi

      M’Chilamulo cha Mose, akazi ankalemekezedwa ndipo sankapheredwa ufulu. Komabe kuyambira cha m’ma 300 B.C.E., Ayuda anayamba kutengera chikhalidwe cha Agiriki. Agiriki ankaona kuti akazi ndi otsika.​—Onani bokosi lakuti, “Zolemba Zina Zakale Zili ndi Mfundo Zolimbikitsa Kusala Akazi.”

      Mwachitsanzo, wolemba ndakatulo wina wachigiriki, amene anakhalako m’zaka za m’ma 700 B.C.E., ananena kuti mavuto onse amene ali padzikoli anachititsa ndi akazi. M’ndakatulo yakeyi, iye ananena kuti amuna amene amachitira limodzi zinthu ndi akazi amakumana ndi mavuto aakulu kwambiri. Maganizo amenewa anali ofala kwambiri m’chipembedzo chachiyuda m’zaka za m’ma 100 B.C.E. Buku lina lotchedwa Talmud lomwe linayamba kulembedwa m’ma 100 C.E. linachenjeza amuna kuti: “Musamacheze kwambiri ndi akazi chifukwa angakuchititseni kuti muchite chiwerewere.”

      Kwa zaka zambiri, Ayuda ambiri anakhala ndi maganizo olakwika amenewa ponena za akazi. Mwachitsanzo pa nthawi imene Yesu anabwera padziko lapansi, anapeza kuti akazi ankakhala kwaokha kukachisi. Amuna okha ndi amene ankaloledwa kuphunzitsidwa nkhani zokhudza chipembedzo ndipo akazi sankaloledwa kukhala ndi amuna m’sunagoge. Mu Talmud muli mawu a Rabi wina amene ananena kuti: “Bambo amene amaphunzitsa mwana wake wamkazi Tora [Chilamulo] ndiye kuti akumuphunzitsa zolaula.” Atsogoleri a chipembedzo achiyuda ankachititsa amuna ambiri kuti aziona akazi ngati anthu osafunikira. Iwo ankachita zimenezi pophunzitsa zabodza zokhudza mmene Mulungu amaonera akazi.

      Yesu ali padziko lapansi, anaona kuti Ayuda ankasala akazi ndipo zimenezi zinkaonekera kwambiri m’miyambo yawo. (Mateyu 15:6, 9; 26:7-11) Kodi miyambo imeneyi inachititsanso Yesu kuti aziona akazi ngati otsika? Kodi iye ankawaona bwanji akazi, ndipo tikuphunzirapo chiyani? Kodi zimene Yesu anaphunzitsa zingathandize kuti akazi asamasalidwe? Nkhani yotsatira iyankha mafunso amenewa.

      Zolemba Zina Zakale Zili ndi Mfundo Zolimbikitsa Kusala Akazi

      Kuyambira m’nthawi ya atumwi, olemba mabuku ena monga Philo wa ku Alexandria anayamba kugwiritsa ntchito maganizo a Agiriki pomasuliranso nkhani zimene zili m’buku la Genesis. Iye ankaona kuti Hava anachita chigololo, choncho anayenera “kulandidwa ufulu wake n’kuyamba kulamuliridwa ndi mwamuna.” Ayuda ambiri komanso mabuku amene Abambo a Tchalitchi analemba anatengera maganizo olakwikawa.

      M’buku lina lachiyuda lolembedwa m’ma 100 C.E., Rabi wina, yemwenso amagwirizana ndi mfundo yoti akazi ayenera kuphimba kumutu, anafotokoza chifukwa chake iwo ayenera kuchita zimenezi. Iye anati: “Kuphimba kumutu ndi kumene kumasonyeza kuti akazi ndi ochimwa ndipo amachita manyazi chifukwa cha zimene anachita.” Katswiri wina wamaphunziro azachipembedzo, amene anthu ambiri ankakhulupirira zolemba zake m’zaka za m’ma 100 C.E., ankanena kuti akazi ayenera kudzimvera chisoni kwambiri chifukwa cha zimene Hava anachita. Maganizo amenewa, omwe amaonedwa ngati ochokera m’Baibulo, achititsa kuti akazi azionedwa ngati otsika.

  • Mulungu Amafuna Kuti Akazi Azilemekezedwa
    Nsanja ya Olonda—2012 | September 1
    • Mulungu Amafuna Kuti Akazi Azilemekezedwa

      ALI padziko lapansi, Yesu anasonyeza bwino makhalidwe a Atate ake komanso mmene amachitira zinthu. Iye anati: “Sindichita kanthu mongoganiza ndekha. Koma ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira. . . . Ndimachita zinthu zomukondweretsa nthawi zonse.” (Yohane 8:28, 29; Akolose 1:15) Choncho, tingadziwe mmene Mulungu amaonera akazi tikaphunzira ndi kumvetsa bwino mmene Yesu ankachitira zinthu ndi akazi, komanso mmene ankawaonera.

      Kuchokera pa zimene zinalembedwa m’Mauthenga Abwino, akatswiri ambiri amaphunziro amavomereza kuti Yesu ankaona akazi mosiyana kwambiri ndi mmene anthu ena pa nthawiyo ankawaonera. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu ankalemekeza akazi? Kodi zimene Yesu ankaphunzitsa zimathandizanso masiku ano kuti akazi azilemekezedwa?

      Mmene Yesu Ankaonera Akazi

      Yesu sankaona kuti akazi analengedwa n’cholinga choti amuna azigona nawo basi. Atsogoleri ena achipembedzo achiyuda ankaona kuti kuchita zinthu ndi akazi kungapangitse kuti munthu achite chiwerewere. Chifukwa cha zimenezi akazi sankaloledwa kulankhula ndi amuna pagulu komanso sankaloledwa kuyenda osaphimba kumutu. Koma Yesu analangiza amuna kuti azilemekeza akazi ndipo asamawasale koma kuti amunawo azidziletsa.​—Mateyu 5:28.

      Yesu ananenanso kuti: “Aliyense wosiya mkazi wake ndi kukwatira wina, wachita chigololo molakwira mkaziyo.” (Maliko 10:11, 12) Choncho iye anatsutsa zimene Arabi ankaphunzitsa kuti amuna azisiya akazi awo “pa chifukwa chilichonse.” (Mateyu 19:3, 9) Mfundo yoti mwamuna akachita chigololo amalakwira mkazi wake inali yachilendo kwa Ayuda ambiri. Arabi ankawaphunzitsa kuti mwamuna akachita chigololo sanalakwire mkazi wake. Koma mkazi akachita chigololo ndi amene ankaonedwa kuti ndi wosakhulupirika. Katswiri wina wa Baibulo ananena kuti: “Pamene Yesu ananena kuti mwamuna akachita chigololo nayenso walakwira mkazi wake, anasonyeza kuti nawonso akazi ndi ofunika.”

      Mmene mfundoyi imathandizira masiku ano: Mumpingo wa Mboni za Yehova, akazi amakhala momasuka ndi amuna pamisonkhano. Komabe, iwo amaonetsetsa kuti pakati pawo sipakuchitika zinthu zosayenera kapena kuzolowerana mopambanitsa chifukwa amuna achikhristu amaona ‘akazi achikulire ngati amayi awo, akazi achitsikana ngati alongo awo ndipo sakhala ndi maganizo alionse oipa.’​—1 Timoteyo 5:2.

      Yesu ankaphunzitsanso akazi. Arabi ankaona kuti akazi ndi osayenera kuwaphunzitsa. Koma mosiyana ndi zimenezi, Yesu ankawaphunzitsa komanso ankawalimbikitsa kunena momasuka maganizo awo. Yesu sanalepheretse Mariya kukhala ndi mwayi womvetsera pamene iyeyo ankaphunzitsa, ndipo pamenepa anasonyeza kuti ntchito ya akazi si kuphika basi. (Luka 10:38-42) Malita, mchemwali wake wa Mariya, nayenso anapindula ndi zimene Yesu ankaphunzitsa, ndipo umboni wa zimenezi ndi zomwe iye anayankha Yesu, Lazaro atamwalira.​—Yohane 11:21-27.

      Yesu ankachitanso chidwi ndi zimene akazi amaganiza pa nkhani zosiyanasiyana. Pa nthawi imeneyo, akazi ambiri achiyuda ankakhulupirira kuti munthu amakhala wosangalala akakhala ndi mwana wamwamuna wotchuka, apo ayi mneneri. Pa nthawi ina mayi wina atafuula kuti: “Ndi wodala mayi amene mimba yake inanyamula inu,” Yesu anamuuza mfundo ina yosonyeza kuti maganizo amenewa ndi olakwika. (Luka 11:27, 28) Zimene Yesu anauza mayiyu zikusonyeza kuti kumvera Mulungu ndiye kofunika kwambiri kuposa kutchuka.​—Yohane 8:32.

      Mmene mfundoyi imathandizira masiku ano: Akulu mumpingo wachikhristu amalola kuti akazi aziyankha momasuka pamisonkhano. Iwo amayamikira akazi okonda zinthu zauzimu chifukwa chokhala “aphunzitsi a zinthu zabwino” pa zochita zawo zonse. (Tito 2:3) Akazi ndi odalirikanso kwambiri pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.​—Salimo 68:11; onani bokosi lakuti, “Kodi Mtumwi Paulo Analetsa Akazi Kulankhula?” patsamba 9.

      Yesu sankaona kuti akazi ndi otsika. Kale, ana aakazi ankaonedwa kuti ndi otsika poyerekeza ndi ana aamuna. Mu Talmud muli mawu awa osonyeza kuti anthu ambiri analidi ndi maganizo amenewa: “Wodala ndi munthu amene ali ndi ana aamuna, koma tsoka kwa iye amene ali ndi ana aakazi.” Makolo ena ankaona kuti kukhala ndi mwana wamkazi ndi chintchito chifukwa ankayenera kumupezera mwamuna, kumuperekera malowolo komanso ankaona kuti mwana wamkaziyo sadzawathandiza akadzakalamba.

      Yesu anasonyeza kuti palibe kusiyana pakati pa mwana wamkazi ndi wamwamuna. Iye anachita zimenezi poukitsa mwana wamkazi wa Yairo monganso anachitira poukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye wa ku Nayini. (Maliko 5:35, 41, 42; Luka 7:11-15) Yesu atachiritsa mayi wina “amene mzimu woipa unamudwalitsa zaka 18,” anamutchula kuti “mwana wa Abulahamu.” Zimene Yesu anachitazi, potchula mkaziyu kuti “mwana wa Abulahamu,” zinali zachilendo kwa Ayuda. (Luka 13:10-16) Pomutchula mayiyo ndi mawu olemekeza amenewa, Yesu anazindikira kuti mayiyu anali ndi chikhulupiriro cholimba ndipo sanali wotsika poyerekezera ndi amuna.​—Luka 19:9; Agalatiya 3:7.

      Mmene mfundoyi imathandizira masiku ano: Ku Asia kuli mwambi wakuti: “Kulera mwana wamkazi n’kopanda phindu chifukwa kuli ngati kuthirira dimba la munthu wina.” Koma makolo achikhristu sakhala ndi maganizo amenewa ndipo iwo amasamalira ana awo, aamuna ndi aakazi, mofanana. Iwo amaonetsetsa kuti ana awo onse akusamalidwa mofanana pa nkhani ya maphunziro ndi thandizo lachipatala.

      Yesu ankaona kuti akazi nawonso ndi odalirika. M’khoti la Ayuda, umboni wa mkazi unkaonedwa mofanana ndi wa kapolo. Wolemba mbiri wina wa m’nthawi ya atumwi, dzina lake Josephus, analangiza anthu kuti: “Musamagwiritse ntchito umboni wa akazi chifukwa ndi achibwanabwana.”

      Mosiyana ndi zimenezi, Yesu atangoukitsidwa anaonekera kwa akazi ndipo anawauza kuti akauze anthu za kuuka kwake. (Mateyu 28:1, 8-10) Ngakhale kuti akazi okhulupirika amenewa anali mboni zoona ndi maso kuphedwa ndiponso kuikidwa m’manda kwa Ambuye wawo, atumwi zinawavuta kukhulupirira kuti zimene akaziwa ankanena zinali zoona. (Mateyu 27:55, 56, 61; Luka 24:10, 11) Komabe poonekera choyamba kwa akazi, Khristu anasonyeza kuti akazi ndi ofunikanso pa nkhani yochitira umboni mofanana ndi amuna.​—Machitidwe 1:8, 14.

      Mmene mfundoyi imathandizira masiku ano: M’mipingo ya Mboni za Yehova, akulu amasonyeza kuti saona kuti akazi ndi otsika. Iwo amachita zimenezi pogwiritsa ntchito zimene akaziwo amanena. Komanso amuna achikhristu ‘amapatsa ulemu’ akazi awo mwa kumvetsera zimene akunena.​—1 Petulo 3:7; Genesis 21:12.

      Mfundo za M’Baibulo Zimathandiza Akazi Kukhala Osangalala

      Amuna akamatengera chitsanzo cha Khristu, amalemekeza akazi awo komanso kuwapatsa ufulu ngati mmene Mulungu anafunira poyamba. (Genesis 1:27, 28) M’malo motsatira maganizo oti amuna ndi apamwamba kuposa akazi, amuna achikhristu amatsatira mfundo za m’Baibulo. Zimenezi zimathandiza kuti akazi awo azikhala osangalala m’banja.​—Aefeso 5:28, 29.

      Pa nthawi imene mayi wina, dzina lake Yelena, ankayamba kuphunzira Baibulo n’kuti mwamuna wake akumuchitira nkhanza. Komanso iye anakulira m’dera limene amuna ankakonda kuba akazi kuti akakhale akazi awo ndiponso kuchitira nkhanza akazi kunali ponseponse. Yelena ananena kuti: “Zimene ndinaphunzira m’Baibulo zinandithandiza kwambiri. Ndinayamba kuona kuti Mulungu amandikonda kwambiri komanso amandiona kuti ndine wofunika. Ndinaonanso kuti ngati mwamuna wanga atayamba kuphunzira Baibulo angayambe kundikonda.” Patapita nthawi mwamuna wake anayambadi kuphunzira Baibulo ndipo kenako anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Yelena ananenanso kuti: “Mwamuna wanga anasiya kundichitira nkhanza ndipo tinaphunzira kukhululukirana.” Pomalizira pake Yelena anati: “Mfundo za m’Baibulo zandithandiza kwambiri kuti ndiziona kuti ndine wofunika komanso wotetezeka m’banja.”​—Akolose 3:13, 18, 19.

      Pali mabanja ambiri amene apindula chifukwa chophunzira Baibulo. Akazi ambirimbiri akusangalala m’banja chifukwa choti iwo ndi amuna awo akuyesetsa kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo m’banja mwawo. Akazi oterewa amalemekezedwa, kulimbikitsidwa komanso amakhala omasuka kucheza ndi Akhristu anzawo.​—Yohane 13:34, 35.

      Amuna ndi akazi achikhristu amazindikira kuti onse ndi ochimwa ndipo ndi opanda ungwiro. Iwo amadziwanso kuti ali mbali ya chilengedwe chimene “chinaperekedwa ku mkhalidwe wopanda pake.” Komabe amazindikiranso kuti kukhala pa ubwenzi ndi Atate wawo, Yehova Mulungu, kumawathandiza kukhala ndi chiyembekezo choti ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.’ Chimenechitu ndi chiyembekezo chosangalatsa kwambiri kwa amuna ndi akazi omwe, amene onse Mulungu amawakonda.​—Aroma 8:20, 21.

      Kodi Mtumwi Paulo Analetsa Akazi Kulankhula?

      Mtumwi Paulo analemba kuti: “Akazi akhale chete m’mipingo.” (1 Akorinto 14:34) Kodi iye ankatanthauza chiyani ponena mawu amenewa? Kodi ankawaderera akazi? Ayi, chifukwatu iye anena kuti akazi amaphunzitsa zinthu zothandiza. (2 Timoteyo 1:5; Tito 2:3-5) M’kalata yake yopita kwa Akorinto, Paulo sanangolangiza akazi okha koma analangizanso amuna, omwe anali ndi mphatso yolankhula malilime komanso yonenera, kuti ‘azikhala chete’ munthu wina akamalankhula.a (1 Akorinto 14:26-30, 33) Ziyenera kuti akazi ena ankasangalala kwambiri ndi zimene ankaphunzira mumpingo moti munthu wina akamalankhula ankamudula mawu n’kuyamba kumufunsa mafunso. Izi zinali zofala pa nthawiyo. Choncho kuti pasakhale chisokonezo, Paulo anawauza kuti ‘azikafunsa amuna awo kunyumba.’​—1 Akorinto 14:35.

      a Kuti mudziwe zambiri za ntchito imene akazi amagwira mumpingo, onani nkhani yakuti “Kodi Akazi a Mboni za Yehova Amaphunzitsa Mawu a Mulungu?” patsamba 23.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena