Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Mulungu Analenga Dziko Lapansili Chifukwa Chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
    • MUTU 3

      Kodi Mulungu Analenga Dziko Lapansili Chifukwa Chiyani?

      • N’chifukwa chiyani Mulungu analenga anthu?

      • Kodi Satana anatsutsa bwanji ulamuliro wa Mulungu?

      • Kodi moyo padzikoli udzakhala wotani m’tsogolo?

      1. Kodi Mulungu analenga dziko lapansili chifukwa chiyani?

      PAMENE Mulungu ankalenga dzikoli anali ndi cholinga chabwino kwambiri. Yehova ankafuna kuti padziko lapansili pazikhala anthu athanzi komanso osangalala. Baibulo limanena kuti “Yehova Mulungu . . . anakonza munda ku Edeni” ndipo “anameretsa . . . mtengo wamtundu uliwonse wooneka bwino ndi wa zipatso zabwino kudya.” Ndiyeno Mulungu atalenga mwamuna ndi mkazi oyambirira, Adamu ndi Hava, anawaika m’munda wokongola kwambiri umenewu kuti azikhalamo ndipo anawauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire.” (Genesis 1:28; 2:8, 9, 15) Choncho Mulungu ankafuna kuti anthu azibereka ana, akulitse munda wa Edeni mpaka ufike dziko lonse lapansi, ndiponso kuti azisamalira nyama.

      2. (a) Kodi timadziwa bwanji kuti zimene Mulungu ankafuna polenga dziko lapansi zidzachitikadi? (b) Malinga ndi zimene Baibulo limanena, kodi ndi anthu otani amene adzakhale ndi moyo wosatha?

      2 Kodi inuyo mumaona kuti zimene Yehova Mulungu ankafunazi, zoti anthu azikhala m’paradaiso, zidzachitikadi? Mulungu ananena kuti: “Ineyo ndalankhula . . . ndipo ndidzazichitadi.” (Yesaya 46:9-11; 55:11) Izi zikusonyeza kuti chilichonse chimene Mulungu wafuna kuchita sichilephereka. Iye ananena kuti dziko lapansi “sanalilenge popanda cholinga, [koma] analiumba kuti anthu akhalemo.” (Yesaya 45:18) Koma kodi Mulungu ankafuna kuti padzikoli pazikhala anthu otani? Nanga ankafuna kuti anthuwo azikhalapo kwa nthawi yaitali bwanji? Baibulo limayankha kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29; Chivumbulutso 21:3, 4.

      3. Kodi padziko lapansi pali mavuto otani, nanga zimenezi zimachititsa anthu kukhala ndi mafunso ati?

      3 N’zachidziwikire kuti zimenezi sizinachitikebe. Panopa anthu amamwalira chifukwa cha matenda komanso amamenyana n’kuphana. Chinachake chiyenera kuti chinalakwika chifukwa zimene zikuchitika masiku ano si zimene Mulungu ankafuna. Kodi n’chiyani chinachitika? N’chifukwa chiyani zimene Mulungu ankafuna sizinachitikebe? Palibe buku la mbiri yakale limene lingatiuze chimene chinachitika chifukwa nkhaniyi inayambira kumwamba.

      ZIMENE MNGELO WINA ANACHITA KUTI AKHALE MDANI WA MULUNGU

      4, 5. (a) Kodi ndani ankalankhula ndi Hava pogwiritsa ntchito njoka? (b) Kodi n’chiyani chingachititse munthu wakhalidwe labwino kusintha n’kukhala wakuba?

      4 Buku loyamba la m’Baibulo limatiuza za winawake amene anatsutsa Mulungu m’munda wa Edeni. Iye amatchedwa “njoka” koma sikuti anali njoka yeniyeni. Buku lomalizira la m’Baibulo limamutchula kuti “Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi.” Amatchedwanso “njoka yakale.” (Genesis 3:1; Chivumbulutso 12:9) Mngelo ameneyu, kapena kuti mzimu wamphamvu wosaoneka, anagwiritsa ntchito njoka polankhula ndi Hava. Zimene anachitazi n’zofanana ndi zimene munthu waluso amachita kuti mawu ake azimveka ngati chikulankhula ndi chidole. Sitikukayikira kuti mngelo ameneyu analipo pamene Mulungu ankalenga dziko lapansili kuti anthu akhalemo.—Yobu 38:4, 7.

      5 Koma kodi ndani analenga “Mdyerekezi,” kapena kuti “Satana” popeza Yehova analenga zinthu zabwino zokhazokha? Mwachidule tingati mwana mmodzi mwa ana auzimu amphamvu a Mulungu anadzipanga yekha kukhala Mdyerekezi. Koma kodi zimenezi zinatheka bwanji? Pajatu munthu amene poyamba anali wakhalidwe labwino komanso wokhulupirika amatha kusintha n’kukhala wakuba. Kodi n’chiyani chimam’pangitsa kuti asinthe? Munthuyo angayambe kulakalaka zinthu zinazake zolakwika. Ngati atamangoganizirabe zinthuzo, maganizo olakwikawo akhoza kukula. Ndiyeno atapeza mpata akhoza kuchita zinthu zimene wakhala akuganizazo.—Werengani Yakobo 1:13-15.

      6. Kodi mngelo wa Mulungu anakhala bwanji Satana Mdyerekezi?

      6 Izi ndi zimene zinachitika ndi Satana Mdyerekezi. Iye anamva Mulungu akuuza Adamu ndi Hava kuti abereke ana ndi kudzaza dziko lapansi. (Genesis 1:27, 28) Satana ayenera kuti anayamba kuganiza kuti, ‘Zingakhale bwinotu anthu onsewo atati azilambira ineyo osati Mulungu.’ Apa maganizo olakwika anayamba kukula mumtima mwake. Patapita nthawi anamuuza Hava zinthu zabodza zokhudza Mulungu n’cholinga chakuti zimene ankalakalakazo zitheke. (Werengani Genesis 3:1-5.) Zimene anachitazi zinam’pangitsa kuti akhale “Mdyerekezi,” kutanthauza “Woneneza.” Ndiponso anakhala “Satana,” kutanthauza “Wotsutsa.”

      7. (a) N’chifukwa chiyani Adamu ndi Hava anafa? (b) N’chifukwa chiyani ana onse a Adamu amakalamba ndi kufa?

      7 Zinthu zabodza zimene Satana Mdyerekezi ananena zinachititsa kuti Adamu ndi Hava asamvere Mulungu. (Genesis 2:17; 3:6) Kusamvera kwa Adamu ndi Hava kunachititsa kuti m’kupita kwa nthawi amwalire chifukwa ndi zimene Mulungu ananeneratu kuti zidzachitika ngati sadzamvera. (Genesis 3:17-19) Popeza Adamu atachimwa sanakhalenso wangwiro, ana ake onse anatengera uchimo wakewo. (Werengani Aroma 5:12.) Zimene zinachitikazi tingaziyerekeze ndi zimene zimachitika poumba njerwa. Ngati chikombole chili chopindika, ndiye kuti njerwa iliyonse imakhala yopindika. N’chimodzimodzinso ndi munthu aliyense. Tonse tinatengera uchimo kuchokera kwa Adamu. N’chifukwa chake anthu onse amakalamba ndi kufa.—Aroma 3:23.

      8, 9. (a) Kodi Satana ankaona kuti Yehova ndi wolamulira wotani? (b) N’chifukwa chiyani Mulungu sanaphe oukirawo nthawi yomweyo?

      8 Pamene Satana anachititsa Adamu ndi Hava kuti achimwire Mulungu, anayambitsa kagulu koukira ulamuliro wa Mulungu. Iye ankafuna kuti anthu aziona ngati Yehova salamulira bwino. Iye ankaona kuti Mulungu si wolamulira wabwino, amauza anthu zinthu zabodza komanso amawamana zabwino. Ankaonanso kuti anthu sakufunikira kulamuliridwa ndi Mulungu chifukwa paokha akhoza kudziwa kuti ichi ndi chabwino kapena choipa. Satana ankaonanso kuti anthu zingamawayendere bwino ngati atamalamuliridwa ndi iyeyo. Kodi Mulungu akanachita chiyani ndi kunyoza kotereku? Ena amaona kuti chidule chinali kungowapha onse oukirawo. Koma kodi kuchita zimenezi kukanasonyeza kuti Satana ankanena zabodza? Kodi zikanapangitsa anthu kutsimikizira kuti Mulungu ndi wolamulira wabwino?

      9 Popeza Yehova amaweruza mwachilungamo kwambiri, sanafune kuwononga anthu oukirawo nthawi yomweyo. Anaona kuti ndi bwino kudikira kaye kuti pakhale mpata wokwanira wotsimikizira kuti zimene Satana ananena zinali zabodza. Choncho Mulungu anapereka mwayi kwa anthu woti adzilamulire okha kwa kanthawi motsogoleredwa ndi Satana. Koma kodi Yehova anachita zimenezi chifukwa chiyani, nanga n’chifukwa chiyani walola kuti padutse nthawi yaitali chonchi asanathetse nkhaniyi? Tidzakambirana mfundo zimenezi m’Mutu 11. Koma panopo tingachite bwino kuganizira mfundo yakuti: Kodi Adamu ndi Hava anachita bwino kukhulupirira zonena za Satana yemwe anali asanawachitirepo chilichonse chabwino? Kodi zinali zomveka kukhulupirira kuti Yehova, yemwe anali atawapatsa chilichonse chomwe anali nacho, anali wankhanza komanso wabodza? Kodi mukanakhala inuyo mukanatani?

      10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili kumbali ya Yehova pamene akuyankha zimene Satana ananena?

      10 Tikufunikira kuganizira mafunso amenewa mofatsa chifukwa nafenso tiyenera kusankha kukhulupirira Mulungu kapena Satana. Nanunso muli ndi mwayi wokhala kumbali ya Yehova pamene akuyankha zimene Satana ananena. Zochita zanu zingasonyeze kuti mumasangalala kulamuliridwa ndi Yehova ndipo zimenezi zingasonyeze kuti Satana ndi wabodza. (Salimo 73:28; werengani Miyambo 27:11.) N’zomvetsa chisoni kuti pa anthu ambirimbiri omwe ali m’dzikoli, ndi anthu ochepa okha amene amasankha kukhala kumbali ya Yehova. Zimenezi zikusonyeza kuti Satana ndi amene akulamulira dzikoli. Koma kodi zimenezi ndi zomwe Baibulo limaphunzitsa?

      KODI AKULAMULIRA DZIKOLI NDI NDANI?

      Dzanja la Satana, akusonyeza Yesu maufumu a dziko lapansi

      Kodi Satana akananena bwanji kuti am’patsa Yesu maufumu adziko lapansi zikanakhala kuti maufumuwo si ake?

      11, 12. (a) Kodi kuyesedwa kwa Yesu kumasonyeza bwanji kuti Satana ndi amene akulamulira dzikoli? (b) Kodi pali umboni winanso uti wosonyeza kuti akulamulira dzikoli ndi Satana?

      11 Yesu ankadziwa kuti Satana ndi amene akulamulira dzikoli. Pa nthawi ina Satana anaonetsa Yesu “maufumu onse a padziko ndi ulemerero wawo.” Ndiyeno anamulonjeza kuti: “Ndikupatsani zinthu zonsezi ngati mutangogwada pansi n’kundiweramira kamodzi kokha.” (Mateyu 4:8, 9; Luka 4:5, 6) Kodi pamenepa tinganene kuti Yesu anayesedwa zikanakhala kuti si Satana amene akulamulira maufumu onsewa? Yesu sanatsutse zoti maboma a dziko lapansili ndi a Satana. Iye akanatha kutsutsa zikanakhala kuti Satana mabomawa si ake.

      12 N’zoona kuti Yehova ndi Mulungu Wamphamvuyonse ndipo ndi amene analenga chilengedwe chonse chochititsa chidwichi. (Chivumbulutso 4:11) Koma Yesu anafotokoza momveka bwino kuti Satana ndi “wolamulira wa dzikoli.” (Yohane 12:31; 14:30; 16:11) Baibulo limanenanso kuti Satana Mdyerekezi ndi “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akorinto 4:3, 4) Ponena za wotsutsa ameneyu, kapena kuti Satana, mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.

      MMENE DZIKO LA SATANA LIDZACHOTSEDWERE

      13. N’chifukwa chiyani tikufunikira dziko latsopano?

      13 Dzikoli likuwonjezeka kuipa tsiku ndi tsiku. Ladzaza ndi nkhondo, atsogoleri andale osakhulupirika, atsogoleri achipembedzo achinyengo ndi zigawenga zoopsa. Panopa dzikoli lafika poti silingakonzedwenso. Baibulo limatiuza kuti posachedwapa Mulungu achotsa dziko la Satanali pa nkhondo ya Aramagedo. Dziko loipali lidzalowedwa m’malo ndi dziko latsopano lolungama.—Chivumbulutso 16:14-16.

      14. Kodi Mulungu anasankha ndani kuti akhale Wolamulira wa Ufumu wake, nanga Baibulo linaneneratu chiyani zokhudza wolamulira ameneyu?

      14 Yehova Mulungu anasankha Yesu Khristu kuti akhale Wolamulira wa Ufumu wakumwamba kapena kuti boma lake. Zimenezi ndi zimene Baibulo linaneneratu kalekale kuti: “Kwa ife kwabadwa mwana. Ife tapatsidwa mwana wamwamuna, ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro. Iye adzapatsidwa dzina lakuti . . . Kalonga Wamtendere. Ulamuliro wake wangati wa kalonga udzafika kutali ndipo mtendere sudzatha.” (Yesaya 9:6, 7) Ponena za boma limeneli, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Monga mmene tionere m’mitu yakutsogoloku, posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzachotsa ndi kulowa m’malo maboma onse a dzikoli. (Werengani Danieli 2:44.) Kenako Ufumuwu udzabweretsa paradaiso padziko lapansi.

      DZIKO LATSOPANO LAYANDIKIRA

      Anthu akusangalala ndipo akuimba nyimbo m’dziko latsopano

      15. Kodi “dziko latsopano” n’chiyani?

      15 Baibulo limatitsimikizira kuti: “Pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.” (2 Petulo 3:13; Yesaya 65:17) Nthawi zina Baibulo likamanena kuti “dziko,” limatanthauza anthu amene akukhala padzikoli. (Genesis 11:1) Choncho “dziko latsopano” lolungama likutanthauza anthu amene Mulungu amasangalala nawo.

      16. Kodi ndi mphatso yotani imene Mulungu adzapereke kwa anthu, nanga tiyenera kuchita chiyani kuti tidzalandire mphatso imeneyi?

      16 Yesu analonjeza kuti m’dziko latsopano limene likubweralo, anthu amene amachita zimene Mulungu amasangalala nazo adzalandira mphatso ya “moyo wosatha.” (Maliko 10:30) Tatsegulani Baibulo lanu pa Yohane 3:16 ndi pa Yohane 17:3, muone zimene Yesu ananena kuti tiyenera kuchita kuti tidzapeze moyo wosatha. Tsopano tiyeni tione madalitso otchulidwa m’Baibulo omwe anthu amene Mulungu adzawapatse moyo wosatha adzasangalale nawo m’paradaiso akubwerayo.

      17, 18. N’chifukwa chiyani sitikayikira zoti padziko lonse padzakhala mtendere ndi chitetezo?

      17 Nkhondo, kusamvera malamulo, chiwawa ndi zinthu zonse zoipa zidzatha. “Woipa sadzakhalakonso. . . . Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi.” (Salimo 37:10, 11) Padzikoli padzakhala mtendere chifukwa Mulungu ‘adzaletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.’ (Salimo 46:9; Yesaya 2:4) Ndiyeno “wolungama adzaphuka, ndipo padzakhala mtendere wochuluka kwa nthawi yonse pamene mwezi udzakhalepo.” Zimenezi zikutanthauza kuti mtenderewo udzakhalapo mpaka kalekale.—Salimo 72:7.

      18 Anthu olambira Yehova adzakhala motetezeka. Kale Aisiraeli akamvera Mulungu ankakhala mwamtendere. (Levitiko 25:18, 19) Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kukhala ndi mtendere ngati umenewo m’Paradaiso.—Werengani Yesaya 32:18; Mika 4:4.

      19. Kodi tikudziwa bwanji kuti m’dziko latsopano mudzakhala chakudya chochuluka?

      19 Sikudzakhala njala. Wamasalimo anaimba kuti: “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.” (Salimo 72:16) Yehova Mulungu adzadalitsa anthu ake olungama ndipo “dziko lapansi lidzapereka zipatso zake.”—Salimo 67:6.

      20. Kodi n’chiyani chingatithandize kutsimikiza kuti dziko lonse lidzakhala paradaiso?

      20 Dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso. Malo amene anawonongedwa ndi anthu oipa adzakonzedwa ndipo mudzamangidwa nyumba zabwino zatsopano komanso mudzakhala minda yokongola. (Werengani Yesaya 65:21-24; Chivumbulutso 11:18) M’kupita kwa nthawi, malo okhala anthu adzawonjezeka mpaka dziko lonse lidzakhala lokongola komanso mudzakhala zinthu zambiri ngati mmene unalili munda wa Edeni. Mulungu sadzalephera ‘kutambasula dzanja lake ndi kukhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.’—Salimo 145:16.

      21. N’chiyani chikusonyeza kuti anthu adzakhala mwamtendere ndi zinyama?

      21 Anthu azidzakhala mwamtendere ndi zinyama. Nyama zakutchire ndi zoweta zidzadyera pamodzi. Ngakhale mwana wamng’ono sadzaopa nyama zimene panopa ndi zoopsa.—Werengani Yesaya 11:6-9; 65:25.

      22. Kodi matenda adzapitirirabe mpaka kalekale?

      22 Matenda adzatha. Yesu monga Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu, adzachiritsa anthu ambiri kuposa amene anawachiritsa ali padziko lapansi pano. (Mateyu 9:35; Maliko 1:40-42; Yohane 5:5-9) Pa nthawi imeneyo “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24; 35:5, 6.

      23. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kuuka kwa anthu idzakhala nkhani yosangalatsa kwambiri?

      23 Achibale komanso anzathu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo. Anthu onse amene anamwalira omwe Mulungu adzasankhe kuwakumbukira, adzaukitsidwa. Ndipotu Baibulo limanena kuti “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Machitidwe 24:15; werengani Yohane 5:28, 29.

      24. Kodi mumamva bwanji mukaganiza zodzakhala m’Paradaiso padziko lapansi?

      24 Zimene takambiranazi zikusonyeza kuti anthu amene amasankha kuphunzira za Mlengi wathu wamkulu, Yehova Mulungu, ndiponso kumutumikira adzasangalala ndi madalitso ambiri. Yesu ankanena za dziko lapansi la Paradaiso pamene ankauza chigawenga chimene chinapachikidwa pambali pake kuti: “Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Kuphunzira za Yesu Khristu n’kofunika kwambiri chifukwa madalitso onsewa adzatheka kudzera mwa iyeyo.

      ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA

      • Zimene Mulungu ankafuna zoti dziko lonse lidzakhale paradaiso zidzachitikadi.—Yesaya 45:18; 55:11.

      • Satana ndi amene akulamulira dzikoli panopa.—Yohane 12:31; 1 Yohane 5:19.

      • Pali madalitso ambiri amene Mulungu adzapereke kwa anthu m’dziko latsopano.—Salimo 37:10, 11, 29.

  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
    • MUTU 8

      Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

      • Kodi Baibulo limatiuza chiyani za Ufumu wa Mulungu?

      • Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zotani?

      • Kodi Ufumuwo udzakwaniritsa liti chifuniro cha Mulungu padziko lapansi?

      1. Kodi tikambirana zokhudza pemphero liti?

      ANTHU ambiri padziko lonse amalidziwa bwino pemphero limene ambiri amati ndi Pemphero la Atate Wathu, kapena Pemphero la Ambuye. Mayina onsewa amanena za pemphero lodziwika kwambiri limene Yesu Khristu anauza ophunzira ake ngati chitsanzo. Pempheroli lili ndi mfundo zofunika kwambiri ndipo tiyeni tikambirane mfundo zitatu zoyambirira. Kukambirana mfundo zotchulidwa mu pempheroli kungakuthandizeni kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa.

      2. Kodi Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti azipempherera zinthu zitatu ziti?

      2 Poyamba pemphero lachitsanzoli, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Muzipemphera motere: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.’” (Mateyu 6:9-13) Kodi mfundo zitatu za m’pempheroli n’zofunika bwanji?

      3. Kodi tiyenera kudziwa chiyani za Ufumu wa Mulungu?

      3 Tinaphunzira kale zambiri zokhudza dzina la Mulungu lakuti Yehova. Tinakambirananso zina ndi zina zokhudza cholinga cha Mulungu. Mwachitsanzo, tinakambirana zimene wachitira anthu komanso zimene adzawachitire m’tsogolo. Koma kodi Yesu ankanena za Ufumu uti pamene ankati tizipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere”? Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani? Kodi ukadzabwera udzayeretsa bwanji dzina la Mulungu? Komanso kodi kubwera kwa Ufumuwo kukugwirizana bwanji ndi kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Mulungu?

      KODI UFUMU WA MULUNGU N’CHIYANI?

      4. Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani, nanga Mfumu yake ndi ndani?

      4 Ufumu wa Mulungu ndi boma lokhazikitsidwa ndi Yehova Mulungu ndipo Mfumu yake ndi yosankhidwa ndi Mulunguyo. Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndi ndani? Ndi Yesu Khristu. Yesu monga Mfumu, ndi wamphamvu kuposa mafumu onse a padziko lapansi ndipo amatchedwa “Mfumu ya olamulira monga mafumu ndi Mbuye wa olamulira monga ambuye.” (1 Timoteyo 6:15) Iye ali ndi mphamvu zoti angathe kutichitira zinthu zonse zimene timafunikira zomwe wolamulira aliyense sangakwanitse.

      5. Kodi likulu la Ufumu wa Mulungu lili kuti, nanga Ufumuwo udzalamulira chiyani?

      5 Kodi likulu la Ufumu wa Mulungu lili kuti? Lili kumene kuli Yesu. Muyenera mukukumbukira zimene munaphunzira zoti Yesu ataphedwa, anaukitsidwa ndipo pasanapite nthawi anabwerera kumwamba. (Machitidwe 2:33) Choncho likulu la Ufumu wa Mulungu lili kumwamba, n’chifukwa chake Baibulo limautchula kuti ndi “Ufumu . . . wakumwamba.” (2 Timoteyo 4:18) Ngakhale kuti Ufumu wa Mulungu uli kumwamba, udzalamulira dziko lapansi.—Werengani Chivumbulutso 11:15.

      6, 7. Kodi Yesu akusiyana bwanji ndi mafumu ena?

      6 Kodi Yesu akusiyana bwanji ndi mafumu ena? Chifukwa chimodzi n’choti Yesu sadzafa. Poyerekezera Yesu ndi mafumu a padziko lapansi, Baibulo limam’tchula kuti “iye yekha ndiye amene ali ndi moyo wosakhoza kufa, amene amakhala m’kuwala kosafikirika.” (1 Timoteyo 6:16) Zimenezi zikutanthauza kuti Yesu apitiriza kuchitira anthu zabwino mpaka kalekale. Ndipotu m’tsogolomu adzachita zinthu zabwino zambiri zothandiza anthu ake.

      7 Taganizirani ulosi uwu wa m’Baibulo wonena za Yesu: “Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye, mzimu wanzeru, womvetsa zinthu, wolangiza, wamphamvu, wodziwa zinthu ndi woopa Yehova. Iye adzasangalala ndi kuopa Yehova. Sadzaweruza potengera zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengera zimene wangomva ndi makutu ake. Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa a padziko lapansi.” (Yesaya 11:2-4) Mawu amenewa akusonyeza kuti Yesu adzakhala Mfumu yachilungamo komanso yachifundo. Kodi simungasangalale kukhala ndi wolamulira ngati ameneyu?

      8. Kodi ndi ndani omwe adzalamulire limodzi ndi Yesu?

      8 Pali mfundo inanso yochititsa chidwi yokhudza Ufumu wa Mulungu. Mfundo yake ndi yoti Yesu sadzalamulira yekha. Iye adzakhala ndi ena amene adzamuthandize kulamulira. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti: “Tikapitiriza kupirira, tidzalamuliranso limodzi ndi iye monga mafumu.” (2 Timoteyo 2:12) Choncho Paulo, Timoteyo ndi anthu ena okhulupirika amene Mulungu wawasankha adzalamulira limodzi ndi Yesu mu Ufumu wakumwamba. Kodi ndi anthu angati amene anapatsidwa mwayi umenewu?

      9. Kodi ndi anthu angati amene adzalamulire limodzi ndi Yesu, nanga Mulungu anayamba liti kusankha anthu amenewa?

      9 Monga mmene tinaonera m’mutu 7, mtumwi Yohane anaona masomphenya a “Mwanawankhosa ataimirira paphiri la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000 olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate wake pamphumi pawo.” Kodi anthu 144,000 amenewa ndi ndani? Yohane anafotokoza kuti: “Amenewa ndiwo amatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita. Iwowa anagulidwa kuchokera mwa anthu, monga zipatso zoyambirira zoperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 14:1, 4) Anthu amenewa amatsatiradi Yesu Khristu mokhulupirika ndipo anasankhidwa kuti adzalamulire naye kumwamba. Iwo akadzaukitsidwa n’kupita kumwamba, “adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.” (Chivumbulutso 5:10) Kuchokera m’nthawi ya atumwi, Mulungu wakhala akusankha Akhristu okhulupirika kuti akwanitse chiwerengero cha 144,000.

      10. N’chifukwa chiyani tingati Mulungu anasonyeza chikondi pokonza zoti Yesu ndi a 144,000 adzalamulire anthu?

      10 Zimene Mulungu anakonza zoti Yesu ndi a 144,000 adzalamulire anthu zimasonyeza kuti Mulungu amakonda kwambiri anthu. Yesu ndi wolamulira wabwino chifukwa amadziwa mmene anthu amaganizira komanso mavuto amene timakumana nawo. Ponena za Yesu, Paulo anati: “Mkulu wa ansembe amene tili naye si mkulu wa ansembe amene sangatimvere chisoni pa zofooka zathu. Koma tili ndi mkulu wa ansembe amene anayesedwa m’zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda uchimo.” (Aheberi 4:15; 5:8) A 144,000 amene adzalamulire naye limodzi nawonso anakumanapo ndi mavuto ali padziko lapansi pano ndipo anapirira. Komanso anakhalapo opanda ungwiro ndipo ankadwala. Choncho akudziwa bwino mavuto amene anthu amakumana nawo.

      KODI UFUMU WA MULUNGU UDZACHITA ZOTANI?

      11. N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti ophunzira ake ayenera kumapemphera kuti chifuniro cha Mulungu chichitike kumwamba?

      11 Pamene Yesu anauza ophunzira ake kuti azipemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere, anawauzanso kuti azipemphera kuti chifuniro cha Mulungu chichitike, “monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano.” Mulungu ali kumwamba ndipo angelo ake omwe ali kumwambako akhala akuchita chifuniro chake nthawi zonse. Koma m’Mutu 3 tinaphunzira kuti mngelo wina woipa anasiya kuchita chifuniro cha Mulungu ndipo anachititsa kuti Adamu ndi Hava achimwe. M’Mutu 10 tidzaphunzira zinthu zina zimene Baibulo limanena zokhudza mngelo woipa ameneyu, yemwe amadziwika ndi dzina lakuti Satana Mdyerekezi. Satana limodzi ndi angelo ena omwe anayamba kumutsatira, amene amatchulidwa kuti ziwanda, analoledwa kukhalabe kumwambako kwa kanthawi. Choncho tingati pa nthawi imeneyi kumwambako kunali angelo ena omwe sankachita chifuniro cha Mulungu. Koma zimenezi zinali zoti zidzatha Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira. Zinali zoti Yesu Khristu akadzangokhazikitsidwa monga Mfumu, adzamenya nkhondo yolimbana ndi Satana.—Werengani Chivumbulutso 12:7-9.

      12. Kodi lemba la Chivumbulutso 12:10 likufotokoza zinthu ziwiri zapadera ziti?

      12 Mawu a ulosi otsatirawa akufotokoza zambiri za nkhondoyi: “Ndinamva mawu ofuula kumwamba, akuti: ‘Tsopano chipulumutso, mphamvu, ufumu wa Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake zafika, chifukwa woneneza abale athu [Satana] waponyedwa pansi. Iyeyo anali kuwaneneza usana ndi usiku pamaso pa Mulungu wathu.’” (Chivumbulutso 12:10) Kodi mwaona m’vesili zinthu ziwiri zapadera zimene zikuchitika? Choyamba, Yesu Khristu wayamba kulamulira mu Ufumu wa Mulungu. Chachiwiri, Satana waponyedwa padziko lapansi kuchokera kumwamba.

      13. Kodi n’chiyani chinachitika Satana atachotsedwa kumwamba?

      13 Kodi zotsatira za zinthu ziwiri zinachitikazi zinali zotani? Baibulo limafotokoza zomwe zinachitika kumwamba kuti: “Kondwerani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko!” (Chivumbulutso 12:12) Angelo okhulupirika anasangalala chifukwa Satana ndi ziwanda zake atachotsedwa kumwamba, aliyense kumwambako anali wokhulupirika kwa Yehova Mulungu. Panopa chifuniro cha Mulungu chikuchitika kumwamba chifukwa kuli mtendere komanso onse amachita zinthu mogwirizana.

      Zithunzi zosonyeza mavuto, nkhondo, uchigawenga, ndi kuwononga mpweya

      Kuchotsedwa kwa Satana ndi ziwanda zake kumwamba kunabweretsa mavuto ambiri padziko lapansi. Mavuto amenewa atha posachedwapa

      14. Kodi chinachitika n’chiyani Satana ataponyedwa padziko lapansi?

      14 Nanga n’chiyani chinachitika padziko lapansi? Baibulo limati: “Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chivumbulutso 12:12) Satana ndi wokwiya kwambiri chifukwa anachotsedwa kumwamba komanso chifukwa choti watsala ndi kanthawi kochepa kuti awonongedwe. Choncho akuchititsa mavuto kapena kuti “tsoka” padziko lapansi. Tidzaphunzira zambiri za “tsoka” limeneli m’mutu wotsatira. Poganizira mavuto amenewa, mwina tingakhale ndi funso lakuti, kodi zingatheke kuti Ufumu wa Mulungu uchititse chifuniro cha Mulungu kuchitika padziko lapansili?

      15. Kodi Mulungu ali nalo cholinga chotani dziko lapansili?

      15 Kumbukirani zimene Mulungu ankafuna pamene ankalenga dziko lapansi. Tinaphunzira m’mutu 3 kuti zimene Mulungu anachita m’munda wa Edeni, zinasonyeza kuti ankafuna kuti dziko lonse lapansi likhale paradaiso ndipo mukhale anthu olungama mpaka kalekale. Satana anachititsa kuti Adamu ndi Hava achimwe ndipo zimenezi zinasokoneza cholinga cha Mulungu ngakhale kuti cholingacho sichinasinthe. Yehova amafunabe kuti ‘olungama adzalandire dziko lapansi, ndipo adzakhale mmenemo kwamuyaya.’ (Salimo 37:29) Ufumu wa Mulungu ndi umene udzakwaniritse cholinga chimenechi. Koma kodi udzachikwaniritsa bwanji?

      16, 17. Kodi lemba la Danieli 2:44 limatiuza chiyani za Ufumu wa Mulungu?

      16 Taganizirani ulosi umene uli pa Danieli 2:44. Palembali timawerenga kuti: “M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.” Kodi lemba limeneli likutiuza chiyani za Ufumu wa Mulungu?

      17 Choyamba, likutiuza kuti Ufumu wa Mulungu udzakhazikitsidwa “m’masiku a mafumu amenewo,” kapena kuti mafumu ena akulamulirabe. Chachiwiri, likutiuza kuti Ufumu umenewu udzakhalapo mpaka kalekale. Sudzagonjetsedwa n’kulowedwa m’malo ndi ufumu wina. Chachitatu, tikuona kuti padzakhala nkhondo pakati pa Ufumu wa Mulungu ndi maufumu a padziko lapansi. Ufumu wa Mulungu udzapambana pa nkhondoyi moti udzatsalapo wokha ndipo uzidzalamulira anthu onse a padziko lapansi. Pa nthawiyi anthu azidzasangalala chifukwa cholamuliridwa ndi Ufumu wabwino kwambiri umenewu.

      18. Kodi nkhondo yomalizira imene idzakhale pakati pa Ufumu wa Mulungu ndi maboma a dzikoli imatchedwa chiyani?

      18 Baibulo limafotokoza zambiri zokhudza nkhondo imeneyi ya pakati pa Ufumu wa Mulungu ndi maufumu a padziko lapansi. Mwachitsanzo, limafotokoza kuti mapeto akamayandikira, mizimu yoipa izidzafalitsa nkhani zabodza n’cholinga choti isocheretse “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” Mizimuyi idzachita zimenezi kuti ‘iwasonkhanitsire pamodzi kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’ Mafumu a padziko lonse lapansi adzasonkhanitsidwa “kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Haramagedo,” kapena kuti Aramagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Chifukwa cha zimene zafotokozedwa m’mavesi awiriwa, nkhondo ya pakati pa maufumu a padziko lapansi ndi Ufumu wa Mulungu imatchedwa nkhondo ya Aramagedo.

      19, 20. Kodi n’chiyani chikulepheretsa kuti panopo chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansili?

      19 Kodi cholinga chomenyera nkhondo ya Aramagedo n’chiyani? Kumbukiraninso cholinga chimene Mulungu anali nacho polenga dziko lapansi. Yehova Mulungu ankafuna kuti dziko lonse lapansi likhale Paradaiso ndipo lidzaze ndi anthu olungama oti azimutumikira mpaka kalekale. Koma panopa zinthu sizili choncho chifukwa ndife ochimwa ndipo timadwala komanso kufa. Koma monga tinaphunzirira m’Mutu 5, Yesu anatifera n’cholinga choti tikhale ndi mwayi wodzapeza moyo wosatha. Tikukhulupirira kuti mukukumbukira mawu a m’buku la Yohane akuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yohane 3:16.

      20 Vuto lina limene likuchititsa kuti panopa zinthu zisakhale mmene Mulungu ankafunira ndi loti anthu ambiri amachita zinthu zoipa. Amanama, amachita zachinyengo ndiponso amachita zachiwerewere. Safuna kuchita chifuniro cha Mulungu. Anthu amene amachita zinthu zoipa zimenezi adzawonongedwa pa nkhondo ya Mulungu ya Aramagedo. (Werengani Salimo 37:10.) Vuto linanso ndi loti maboma samalimbikitsa anthu kuti azichita zimene Mulungu amafuna. Maboma ambiri alibe mphamvu, ndi ankhanza, ndiponso akatangale. Baibulo limanena zoona likamati: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.”—Mlaliki 8:9.

      21. Kodi Ufumu wa Mulungu udzapangitsa bwanji kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi?

      21 Pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo, anthu onse azidzalamuliridwa ndi boma limodzi, lomwe ndi Ufumu wa Mulungu. Ufumu umenewu uzidzachita chifuniro cha Mulungu ndipo udzabweretsa madalitso ambiri kwa anthu. Mwachitsanzo, udzachotsa Satana ndi ziwanda zake. (Chivumbulutso 20:1-3) Chifukwa cha nsembe ya Yesu, anthu omwe azidzalamuliridwa ndi Ufumuwu sazidzadwala kapena kufa. Adzakhala ndi mwayi wosangalala ndi moyo mpaka kalekale. (Werengani Chivumbulutso 22:1-3.) Pa nthawi imeneyo dziko lonse lapansi lidzakonzedwa n’kukhala paradaiso. Choncho Ufumu wa Mulungu udzachititsa kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi ndiponso kuti dzina lake liyeretsedwe. Zimenezi zikusonyeza kuti m’kupita kwa nthawi anthu onse mu Ufumuwo azidzalemekeza dzina la Yehova Mulungu.

      KODI UFUMU WA MULUNGU UDZATHETSA LITI MABOMA A PADZIKO LAPANSI?

      22. Kodi tikudziwa bwanji kuti Ufumu wa Mulungu sunabwere pa nthawi imene Yesu anali padziko lapansi kapena atangoukitsidwa kumene?

      22 Pamene Yesu ankauza ophunzira ake kuti azipemphera kuti, “Ufumu wanu ubwere” ankasonyeza kuti pa nthawi imeneyo Ufumuwo unali usanabwere. Kodi unabwera iye atangobwerera kumwamba? Ayi, chifukwa Petulo ndi Paulo ananena kuti ulosi wa pa Salimo 110:1 unakwaniritsidwa Yesu ataukitsidwa. Ulosiwu umati: “Yehova wauza Ambuye wanga kuti: ‘Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.’” (Salimo 110:1; Machitidwe 2:32-35; Aheberi 10:12, 13) Izi zikusonyeza kuti Yesu anayenera kudikira kaye.

      Mu Ufumu wa Mulungu, chifuniro cha Mulungu chidzachitika padziko lapansi ngati mmene chikuchitikira kumwamba

      23. (a) Kodi Ufumu wa Mulungu unayamba liti kulamulira? (b) Kodi mutu wotsatira udzafotokoza chiyani?

      23 Kodi anayenera kudikira kwa nthawi yaitali bwanji? M’zaka za m’ma 1800 ndi 1900, ophunzira Baibulo okhulupirika anayamba kuzindikira kuti nthawi yodikirayi idzatha mu 1914. (Kuti mumve zambiri za chaka chimenechi, onani Zakumapeto, tsamba 215-218.) Zinthu zosiyanasiyana zimene zinachitika padziko lonse lapansi kuyambira mu 1914, zimatsimikizira kuti zimene ophunzira Baibulowa ankakhulupirira zinali zoona. Kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo kumasonyeza kuti mu 1914, Khristu anakhala Mfumu ndipo Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira. Choncho tingati panopa tikukhala mu “kanthawi kochepa” kamene katsala kuti Satana awonongedwe. (Chivumbulutso 12:12; Salimo 110:2) Tinganenenso motsimikiza kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu uchititsa kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi. Kodi mukuona kuti nkhani imeneyi ndi yosangalatsa? Kodi mukukhulupirira kuti zimenezi zidzachitikadi? Mutu wotsatira udzakuthandizani kudziwa kuti zimenezi zidzachitikadi.

      ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA

      • Ufumu wa Mulungu ndi boma la kumwamba ndipo Mfumu yake ndi Yesu Khristu. Palinso anthu okwana 144,000 ochokera padziko lapansi omwe akalamulire naye limodzi.—Chivumbulutso 14:1, 4.

      • Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira mu 1914 ndipo utangokhazikitsidwa, Satana anaponyedwa padziko lapansi.—Chivumbulutso 12:9.

      • Posachedwapa Ufumu wa Mulungu uwononga maboma a padziko lapansi ndipo dziko lapansi lidzakhala paradaiso.—Chivumbulutso 16:14, 16.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena