-
Musalole Chilichonse Kusokoneza Ubwenzi Wanu ndi YehovaNsanja ya Olonda—2013 | January 15
-
-
Musalole Chilichonse Kusokoneza Ubwenzi Wanu ndi Yehova
“Sankhani lero amene mukufuna kum’tumikira.”—YOS. 24:15.
1-3. (a) N’chifukwa chiyani Yoswa ndi chitsanzo chabwino? (b) Kodi tiyenera kukumbukira chiyani tisanasankhe zochita?
ZINTHU zimene timasankha pa moyo wathu zikhoza kukhala ndi zotsatira zabwino kapena zoipa. Choncho kusankha zochita ndi udindo waukulu. Zimakhala ngati munthu amene akuyenda ndipo wafika pamphambano. Amafunika kusankha njira. Njira imodzi ikhoza kukamufikitsa kumene akupita koma ina ikhoza kumusocheretsa.
2 M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu amene anayenera kusankha zochita. Mwachitsanzo, Kaini anayenera kusankha kulamulidwa ndi mkwiyo kapena kuulamulira. (Gen. 4:6, 7) Yoswa anayenera kusankha kulambira Mulungu woona kapena milungu yonyenga. (Yos. 24:15) Yoswa ankafuna kukhalabe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova choncho anasankha zinthu zimene zikanamuthandiza kuchita zimenezo. Koma Kaini analibe cholinga chimenechi choncho anasankha zinthu zimene zinasokoneza ubwenzi wake ndi Yehova.
3 Nthawi zina, ifenso tiyenera kusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu. Zikatero, kumbukirani cholinga chanu chomwe ndi kulemekeza Yehova pa zonse zimene mumachita ndiponso kupewa chilichonse chimene chingasokoneze ubwenzi wanu ndi iye. (Werengani Aheberi 3:12.) M’nkhani ino ndiponso yotsatira tikambirana zinthu 7 zimene tiyenera kusankha mwanzeru kuti tisasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova.
NTCHITO
4. Kodi kugwira ntchito n’kofunika bwanji?
4 Akhristu amafunika kupeza zofunika pa moyo wawo komanso wa banja lawo. Baibulo limasonyeza kuti munthu amene safuna kusamalira banja lake amakhala woipa kuposa wosakhulupirira. (2 Ates. 3:10; 1 Tim. 5:8) Ntchito ndi yofunika kwambiri pa moyo wathu koma ngati sitisamala, ikhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Kodi ingasokoneze bwanji?
5. Kodi muyenera kuganizira mfundo ziti mukamasankha ntchito?
5 Tiyerekeze kuti mukufufuza ntchito. Ngati m’dera lanu ntchito zimasowa kwambiri, mukhoza kungovomera ntchito iliyonse imene mungaipeze. Koma bwanji ngati ntchitoyo ndi yosemphana ndi mfundo za m’Baibulo? Nanga bwanji ngati ntchitoyo ndi yopanikiza kapena muzifunika kuyendayenda moti izikulepheretsani kuchita zinthu zina ndi mpingo kapena banja lanu? Kodi mudzayambabe ntchitoyo poganiza kuti kugwira ntchito zoterezi n’kwabwino kusiyana ndi kukhala pa ulova? Kumbukirani kuti ngati mutasankha molakwika, mukhoza kusokoneza ubwenzi wanu ndi Yehova. (Aheb. 2:1) N’chiyani chingakuthandizeni kusankha mwanzeru pofufuza ntchito kapena poona ngati ntchito imene mukugwira ili yabwino?
6, 7. (a) Kodi anthu amakhala ndi zolinga zotani akamagwira ntchito? (b) Nanga ndi cholinga chiti chimene chingakuthandizeni kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova? Perekani chifukwa.
6 Monga tanenera poyamba paja, muyenera kukumbukira cholinga chanu. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikufuna kuti ntchitoyi indithandize kuchita chiyani?’ Ngati cholinga chanu ndi kupeza zofunika pa moyo wanu kapena wa banja lanu kuti muzitumikira bwino Yehova, iye adzakuthandizani. (Mat. 6:33) Iye amadziwa mmene angakuthandizireni ngakhale pamene ntchito yatha kapena ngati chuma cha dziko sichikuyenda bwino. (Yes. 59:1) Yehova “amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.”—2 Pet. 2:9.
7 Koma bwanji ngati cholinga chanu n’kungofuna kulemera basi? Mwina mukhoza kulemeradi. Koma kugwira ntchito n’cholinga chimenechi kungakugwetseni m’mavuto aakulu. (Werengani 1 Timoteyo 6:9, 10.) Kuika patsogolo ndalama kapena ntchito kungasokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova.
8, 9. Kodi makolo ayenera kuganizira zinthu ziti pa nkhani ya ntchito? Fotokozani.
8 Ngati ndinu kholo, muyenera kuganizira mmene zosankha zanu zingakhudzire ana anu. Kodi iwo amaona kuti mumaika patsogolo chiyani? Ntchito kapena ubwenzi wanu ndi Yehova? Ngati amaona kuti mumaika patsogolo chuma, kutchuka kapena moyo wapamwamba, nawonso akhoza kukutsatirani pa njira yoopsa imeneyi. Apo ayi akhoza kusiya kukulemekezani. Mlongo wina wachitsikana anati: “Kuyambira kalekale bambo anga amatanganidwa kwambiri ndi ntchito yawo. Poyamba tinkaganiza kuti akuchita zimenezi pofuna kupezera banja lathu zinthu zabwino kwambiri. Tinkaona kuti akungofuna kutisamalira bwino. Koma m’zaka zaposachedwapa, tikuona kuti zinthu zasintha. Iwo amangokhalira kugwira ntchito n’cholinga choti azitibweretsera zinthu zapamwamba osati zofunika pa moyo. Panopa anthu amangoona kuti banja lathu ndi lolemera osati lolimbikitsa ena kutumikira Yehova. Ndingakonde bambo anga atamatitsogolera potumikira Yehova osati kumangotipezera ndalama.”
9 Makolo, musalole kuti ntchito isokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova. Muzipereka chitsanzo chabwino kwa ana anu. Asonyezeni kuti kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ndi chuma chamtengo wapatali kwambiri kuposa ndalama kapena katundu.—Mat. 5:3.
10. Kodi wachinyamata amene akuganizira ntchito yoti adzagwire ayenera kukumbukira chiyani?
10 Ngati ndinu wachinyamata ndipo mukuganizira ntchito yoti mudzagwire, kodi mungatani kuti musankhe bwino? Monga tanenera kale, muyenera kukumbukira cholinga chanu pa moyo. Kodi kuphunzira ndiponso kugwira ntchito imene mukuiganizirayo kudzakuthandizani kuika patsogolo kutumikira Yehova? Kapena kodi kudzasokoneza ubwenzi wanu ndi iye? (2 Tim. 4:10) Kodi mudzalola kutengera anthu amene amasangalala pokhapokha ngati ali ndi ndalama? Kapena kodi mudzatsanzira Davide amene analemba kuti: “Ndinali mwana, ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha chakudya”? (Sal. 37:25) Kumbukirani kuti njira ina imakhala yosocheretsa pomwe ina imakuthandizani kukhala pa ubwenzi ndi Yehova n’kumasangalala. (Werengani Miyambo 10:22; Malaki 3:10.) Kodi inuyo mudzasankha njira iti?a
ZOSANGALATSA
11. Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya zosangalatsa? Koma kodi tiyenera kukumbukira chiyani?
11 Baibulo sililetsa kusangalala. Silinenanso kuti munthu akamachita zosangalatsa ndiye kuti akungotaya nthawi. Paja Paulo anauza Timoteyo kuti: “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.” (1 Tim. 4:8) Baibulo limanenanso kuti pali “nthawi yoseka” ndi “nthawi yodumphadumpha mosangalala.” Limatilimbikitsanso kupeza nthawi yopuma. (Mlal. 3:4; 4:6) Koma ngati sitisamala, zosangalatsa zikhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Pali njira ziwiri. Njira yoyamba ndi kusankha zosangalatsa zolakwika ndipo yachiwiri ndi kuthera nthawi yambiri mukuzichita.
Zosangalatsa zimakhala bwino ngati zili zoyenera ndiponso sizikukutherani nthawi yambiri
12. Kodi muyenera kuganizira zinthu ziti posankha zosangalatsa?
12 Choyamba tiyeni tikambirane mtundu wa zosangalatsa zimene timasankha. Zosangalatsa zabwino zilipo ndithu. Koma zosangalatsa zambiri zimalimbikitsa zinthu zimene Mulungu amadana nazo monga chiwawa, kukhulupirira mizimu ndiponso chiwerewere. Choncho ndi bwino kuganizira kwambiri mtundu wa zosangalatsa zimene mumakonda. Kodi zimakuchititsani kukhala munthu wotani? Kodi zimakuchititsani kukhala ndi mtima wachiwawa, wampikisano kapena wokondetsa dziko lanu? (Miy. 3:31) Kodi zimakuwonongerani ndalama zambiri? Kodi zingakhumudwitse anthu ena? (Aroma 14:21) Kodi zosangalatsa zanu zimachititsa kuti muzicheza ndi anthu otani? (Miy. 13:20) Kodi zimakulimbikitsani kuchita zinthu zoipa?—Yak. 1:14, 15.
13, 14. Kodi muyenera kukumbukira mfundo ziti mukamaganizira nthawi imene mungathere pochita zosangalatsa?
13 Tiyenera kuganiziranso za kuchuluka kwa nthawi imene timathera pochita zosangalatsa. Ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimatha nthawi yambiri ndikuchita zosangalatsa moti sindikhala ndi nthawi yokwanira yochitira zinthu monga kulalikira ndi kusonkhana?’ Kutha nthawi yaitali tikuchita zosangalatsa kumapangitsanso kuti tisasangalale nazo kwenikweni. Nthawi zambiri, anthu amene satha nthawi yaitali akuchita zosangalatsa ndi amene amasangalala nazo kwambiri. Tikutero chifukwa amakhala atachitiratu zinthu zonse “zofunika kwambiri.” Choncho ikafika nthawi yochita zosangalatsa sadziimba mlandu.—Werengani Afilipi 1:10, 11.
14 Ngakhale kuti kuchita zosangalatsa kwa nthawi yaitali kungaoneke kosangalatsa, kukhoza kutisokonezera ubwenzi wathu ndi Yehova. Umboni wake ndi zimene zinachitikira mlongo wina wa zaka 20 dzina lake Kim. Iye anati: “Ndinkakonda kupita kulikonse kumene anthu akunjoya. Kumapeto kwa mlungu uliwonse kunkachitika zinazake kuyambira Lachisanu mpaka Lamlungu. Koma panopa ndazindikira kuti pali zinthu zina zofunika kwambiri zimene ndingamachite. Panopa ndikuchita upainiya ndipo ndimadzuka 6 koloko m’mawa kuti ndipite mu utumiki choncho n’zosatheka kuti ndizikhala konjoya mpaka 1 koloko kapena 2 koloko usiku. Kucheza ndi anzathu kulibe vuto koma ngati sitisamala kukhoza kutisokoneza. Tiyenera kukhala ndi malire ngati mmene timachitira ndi zinthu zina.”
15. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti azisangalala ndi zinthu zabwino?
15 Makolo afunika kupezera banja lawo zinthu zofunika. Amafunikanso kuthandiza aliyense m’banja kuti azikhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, kukhala wosangalala ndiponso kudzimva kuti amakondedwa. Ngati ndinu kholo musakhale ndi mtima woona kuti kusangalala n’kulakwa. Koma muzisamalanso kuti banja lanu lisamasangalale ndi zinthu zoipa. (1 Akor. 5:6) Ngati mungasankhe mosamala, mukhoza kupeza zosangalatsa zabwino za banja lanu.b Kuchita zimenezi kungathandize kuti banja lanu lonse likhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.
ANTHU A M’BANJA LATHU
16, 17. Kodi makolo ambiri akumana ndi vuto liti? Nanga tikudziwa bwanji kuti Yehova amamvetsa mmene zikuwapwetekera?
16 Ubwenzi wa pakati pa makolo ndi ana umakhala wamphamvu kwambiri moti Yehova anauyerekezera ndi mmene amakondera anthu ake. (Yes. 49:15) Choncho m’pomveka kuti timamva chisoni kwambiri ngati munthu wina m’banja lathu wasiya Yehova. Mlongo wina amene mwana wake wamkazi anachotsedwa anati: “Zinandipweteka koopsa. Ndinkadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani wasiya Yehova?’ Ndinkadziimba mlandu kwambiri.”
17 Yehova amadziwa mmene zikukupwetekerani. Iyenso “zinam’pweteka kwambiri mumtima” pamene mwana wake woyamba padziko lapansi anamupandukira komanso pamene anthu ena ambiri anachita zimenezi Chigumula chisanafike. (Gen. 6:5, 6) Anthu amene sanakumanepo ndi zimenezi sangamvetse bwino mmene zimapwetekera. Komabe, si bwino kulola zochita za munthu amene wachotsedwa kuti zisokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Kodi mungatani ngati mukumva chisoni chifukwa choti munthu wina m’banja lanu wasiya Yehova?
18. N’chifukwa chiyani makolo sayenera kudziimba mlandu ngati mwana wawo wasiya Yehova?
18 Musamadziimbe mlandu pa zimene zinachitika. Yehova wapereka ufulu wosankha kwa anthu. Munthu aliyense m’banja, amene wadzipereka n’kubatizidwa, ali ndi udindo “wonyamula katundu wake.” (Agal. 6:5) Yehova amaona kuti wochimwa aliyense ayenera kudziyankhira pa zimene wasankha. Iye sangakuimbeni mlandu inuyo. (Ezek. 18:20) Si bwinonso kuimba mlandu anthu ena. Muziona kuti chilango chimene Yehova wapereka n’choyenera. Muzilimbana ndi Mdyerekezi osati akulu amene akuyesa kuteteza mpingo.—1 Pet. 5:8, 9.
Si kulakwa kuyembekezera kuti m’bale wanu amene anachotsedwa adzabwerera kwa Yehova
19, 20. (a) Kodi makolo a mwana amene wachotsedwa angatani kuti apirire chisoni chawo? (b) Kodi makolo oterewa ayenera kuyembekezera chiyani?
19 Koma ngati mungakwiyire Yehova, dziwani kuti ubwenzi wanu ndi iye usokonezeka. Munthu wa m’banja lanu yemwe wasiya Yehova akufunikira kuona kuti mumafunitsitsa kusangalatsa Yehova kuposa wina aliyense, ngakhale a m’banja lanu. Choncho kuti mukwanitse kupirira, yesetsani kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Musamadzipatule, koma muzicheza ndi abale ndi alongo okhulupirika. (Miy. 18:1) Muzimuuza Yehova nkhawa zanu zonse m’pemphero. (Sal. 62:7, 8) Musamafufuze zifukwa zochezera ndi wachibale wanu amene wachotsedwa, kulemberana naye makalata, kutumizirana mauthenga a pafoni kapena pa Intaneti. (1 Akor. 5:11) Muzitanganidwa ndi zinthu zimene zingalimbitse ubwenzi wanu ndi Mulungu. (1 Akor. 15:58) Mlongo amene tamutchula uja anati: “Ndikudziwa kuti ndiyenera kutumikira Yehova mwakhama ndiponso kulimbitsa ubwenzi wanga ndi iye n’cholinga choti mwana wanga akadzabwezeretsedwa, ndidzathe kumuthandiza.”
20 Baibulo limanena kuti chikondi “chimayembekezera zinthu zonse.” (1 Akor. 13:4, 7) Si kulakwa kuyembekezera kuti m’bale wanu amene anachotsedwa adzabwezeretsedwa. Chaka chilichonse anthu ochimwa ambiri amalapa n’kubwerera m’gulu la Yehova. Yehova sanyinyirika akaona kuti alapa. M’malomwake, amakhala “wokonzeka kukhululuka.”—Sal. 86:5.
SANKHANI MWANZERU
21, 22. Kodi mukufunitsitsa kusankha bwanji zinthu pa moyo wanu?
21 Yehova wapatsa anthu ufulu wosankha. (Werengani Deuteronomo 30:19, 20.) Koma ufulu umenewu umabwera limodzi ndi udindo waukulu. Mkhristu aliyense ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikuyenda panjira iti? Kodi ndalola zinthu monga ntchito, zosangalatsa kapena anthu a m’banja langa kusokoneza ubwenzi wanga ndi Yehova?’
22 Yehova sadzasiya kukonda anthu ake. Koma kusankha zolakwika n’kumene kumasokoneza ubwenzi wathu ndi iye. (Aroma 8:38, 39) Tisalole kuti zimenezi zitichitikire. Tsimikizani mumtima mwanu kuti china chilichonse chisasokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova. M’nkhani yotsatira tiona zinthu zina zinayi zimene tiyenera kusankha mwanzeru kuti tisasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova.
a Kuti mumve zambiri pa nkhani yosankha ntchito, onani mutu 38 m’buku lakuti, Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri.
b Mfundo zina zothandiza mungazipeze mu Galamukani! ya November 2011, patsamba 17 mpaka 19.
-
-
Pitirizani Kuyandikira YehovaNsanja ya Olonda—2013 | January 15
-
-
Pitirizani Kuyandikira Yehova
“Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—YAK. 4:8.
1, 2. (a) Kodi Satana amapusitsa bwanji anthu? (b) N’chiyani chingatithandize kuyandikira Mulungu?
YEHOVA MULUNGU analenga anthu ndi mtima woti azifuna kumuyandikira. Koma Satana amafuna kuti tikhale ndi maganizo ake akuti sitifunika kuyandikira Yehova. Limeneli ndi bodza limene Satana anapusitsa nalo Hava m’munda wa Edeni ndipo akupitirizabe mpaka pano. (Gen. 3:4-6) Kuyambira nthawi imeneyo, anthu ambiri akhala akuganiza kuti safunika kuyandikira Mulungu.
2 Koma tikhoza kupewa misampha ya Satana chifukwa “tikudziwa bwino ziwembu zake.” (2 Akor. 2:11) Satana amatilimbikitsa kusankha zinthu zolakwika n’cholinga choti tisokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Koma malinga ndi nkhani yapita ija, tikhoza kusankha bwino ntchito, zosangalatsa komanso zoyenera kuchita ndi anthu a m’banja lathu. M’nkhani ino, tiona zimene tiyenera kuchita kuti zipangizo zamakono, thanzi lathu, ndalama komanso kunyada zisatilepheretse ‘kuyandikira Mulungu.’—Yak. 4:8.
ZIPANGIZO ZAMAKONO
3. Kodi zipangizo zamakono zingakuthandizeni bwanji nanga zingakusokonezeni bwanji?
3 Masiku ano, zipangizo zamakono zili ponseponse. Ngati titazigwiritsa ntchito bwino, zikhoza kutithandiza. Koma kupanda kuzigwiritsa ntchito bwino, zikhoza kutisokonezera ubwenzi wathu ndi Atate wathu wakumwamba. Mwachitsanzo, tiyeni tikambirane za makompyuta. Magazini imene mukuwerengayi inalembedwa ndiponso kusindikizidwa pogwiritsa ntchito kompyuta. Pa kompyuta, munthu ukhoza kufufuza zinthu, kulankhulana ndi anthu komanso kupeza zinthu zosangalatsa zabwino. Koma n’zothekanso kutengeka kwambiri ndi makompyuta. Otsatsa malonda amayesetsa kuchititsa anthu kuganiza kuti afunika kupeza zipangizo zamakono zimene zangotuluka kumene. Mnyamata wina ankafunitsitsa kwambiri kakompyuta kenakake kam’manja moti anazemba n’kukagulitsa impso yake kuti agule kakompyutako. Kumenekutu n’kupusa kwambiri.
4. Kodi Mkhristu wina anathana bwanji ndi vuto lotengeka kwambiri ndi kompyuta?
4 Koma kulola kuti zipangizo zamakono zisokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova n’koopsa kwambiri. M’bale wina wa zaka 28, dzina lake Jon,a anati: “Ndimadziwa kuti Baibulo limati ‘tizigwiritsa ntchito bwino nthawi yathu’ n’cholinga choti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova. Koma pa nkhani ya makompyuta munthune ndili ndi vuto lalikulu kwabasi.” Jon ankakhala pa Intaneti mpaka pakati pa usiku. Iye anati: “Makamaka ndikatopa kwambiri m’pamene zinkandivuta kusiya kucheza ndi anthu pa Intaneti kapena kuonera mavidiyo, omwe nthawi zina sanali abwino.” Kuti athane ndi vutoli, anakonza zoti kompyuta yakeyo izizima yokha ikafika nthawi yoti akagone.—Werengani Aefeso 5:15, 16.
Makolo ayenera kuthandiza ana awo kugwiritsa ntchito mwanzeru zipangizo zamakono
5, 6. (a) Kodi makolo ali ndi udindo wotani kwa ana awo? (b) Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti azicheza ndi anthu oyenera?
5 Ngati ndinu kholo, sikuti mumafunika kuona chilichonse chimene ana anu akuchita. Komabe mumafunika kuona mmene akuchitira zinthu pa kompyuta. Musamangowalekerera akuonera zinthu zachiwerewere, zachiwawa, zamizimu kapena kucheza ndi anthu oipa. Imeneyi si njira yowatangwanitsira kapena yowachititsa kuti asakuvutitseni. Ngati mutawalekerera, akhoza kumaganiza kuti ndi zabwinobwino. Muli ndi udindo woteteza ana anu, ngakhale akuluakulu, kuti china chilichonse chisasokoneze ubwenzi wawo ndi Yehova. Pajatu ngakhale nyama zimateteza ana awo. Kodi mukuganiza kuti chimbalangondo chachikazi chingatani ngati munthu wina akufuna kupha tiana take?—Yerekezerani ndi Hoseya 13:8.
6 Muzithandiza ana anu kuti azicheza ndi Akhristu achitsanzo chabwino komanso amisinkhu yosiyanasiyana. Musaiwale kuti inuyo mumafunika kucheza mokwanira ndi ana anu. Muzipeza nthawi yochitira limodzi zinthu monga kuseka, kusewera, kugwira ntchito ndiponso ‘kuyandikira Mulungu.’b
THANZI
7. N’chifukwa chiyani tonse timafuna kukhala ndi thanzi labwino?
7 Nthawi zina timamva munthu akufunsa mnzake kuti, “Mukupeza bwanji?” M’pake kufunsa chonchi chifukwa chakuti kungoyambira pamene Adamu ndi Hava anamvera Satana n’kusokoneza ubwenzi wawo ndi Yehova, anthufe timadwala. Satana amasangalala akaona kuti tikudwala chifukwa zimakhala zovuta kutumikira Yehova. Ndipo ngati titafa ndiye kuti sitim’tumikiranso. (Sal. 115:17) N’chifukwa chake timayesetsa kusamalira moyo wathu.c Tiyeneranso kuganizira thanzi la abale ndi alongo athu.
8, 9. (a) Kodi tingapewe bwanji kuchita zinthu mopitirira malire pa nkhani ya thanzi lathu? (b) Kodi mtima wosangalala umathandiza bwanji?
8 Koma si bwino kuchita zinthu mopitirira malire. Anthu ena amangokhalira kukamba za kadyedwe koyenera, mankhwala oyenera kapena zinthu zina zothandiza kuti azioneka bwino. Amakamba kwambiri za zimenezi kusiyana ndi mmene amakambira za Ufumu wa Mulungu. Mwina amaganiza kuti akuthandiza anzawo. Komatu tikakhala pa misonkhano, si bwino kutsatsa malonda kapena kulimbikitsa anthu kugwiritsa ntchito mankhwala enaake kapena zinthu zina zodzikongoletsera. N’chifukwa chiyani tikutero?
9 Akhristufe timasonkhana kuti tikambirane za Yehova ndiponso kuti tizikhalabe achimwemwe chifukwa chotsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. (Agal. 5:22) Kaya wina watipempha kapena ayi, kupereka malangizo okhudza mankhwala kapena zinthu zina zodzikongoletsera si kwabwino pamene tili pa misonkhano. Kungasokoneze cholinga cha misonkhano ndiponso kungachititse ena kukhumudwa. (Aroma 14:17) Munthu aliyense ayenera kusankha yekha zochita pa nkhani ya mankhwala. Ndipotu palibe aliyense amene angapeze njira yothetsera matenda onse. Ngakhale madokotala apamwamba amadwala, kukalamba ndiponso kufa. Kudera nkhawa kwambiri za thanzi lathu sikungatalikitse moyo. (Luka 12:25) Koma “mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa.”—Miy. 17:22.
10. (a) Kodi Yehova amaona kuti ndi makhalidwe ati amene amakongoletsa munthu? (b) Kodi ndi liti pamene tidzakhale ndi thanzi langwiro?
10 M’pomveka kuganiziranso za maonekedwe athu. Koma si bwino kumangoganizira zimene tingachite kuti tifufute zizindikiro zonse za ukalamba. Zizindikiro zoterezo zikhoza kusonyeza kuti ndife anzeru, olemekezeka komanso kuti munthu wamkati ndi wokongola. Pajatu Baibulo limati: “Imvi ndizo chisoti chachifumu cha ulemerero zikapezeka m’njira yachilungamo.” (Miy. 16:31) Umu ndi mmene Yehova amationera ndipo ifenso tizidziona choncho. (Werengani 1 Petulo 3:3, 4.) Chotero kodi ndi bwino kuchititsa maopaleshoni oopsa kapena kuyamba kugwiritsa ntchito mankhwala oopsa n’cholinga choti tizingooneka okongola? “Chimwemwe chimene Yehova amapereka” n’chimene chimakongoletsa munthu ngakhale wokalamba kapena wodwala chifukwa chakuti chimachokera mumtima. (Neh. 8:10) M’dziko latsopano ndi mmene tidzakhala ndi thanzi langwiro ndiponso kuoneka okongola ngati kamwana. (Yobu 33:25; Yes. 33:24) Podikira nthawi imeneyo, tiyeni tizichita zinthu mwanzeru ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu. Kuchita zimenezi kungatithandize kuyandikirabe Yehova ndiponso kukhala ndi moyo wabwino ngakhale panopa.—1 Tim. 4:8.
NDALAMA
11. Kodi ndalama zingasokoneze bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova?
11 Ndalama pazokha zilibe vuto ndipo si kulakwa kuchita bizinezi mwachilungamo. (Mlal. 7:12; Luka 19:12, 13) Koma “kukonda ndalama” kumasokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. (1 Tim. 6:9, 10) “Nkhawa za moyo wa m’nthawi ino,” kapena kuti kudera nkhawa kwambiri mmene tingapezere zinthu zofunika pa moyo, kungasokonezenso ubwenzi wathu ndi Yehova. Ndi mmene zililinso ndi “chinyengo champhamvu cha chuma.” Munthu akhoza kumaganiza kuti ndalama zingam’pangitse kukhala wotetezeka ndiponso wosangalala mpaka kalekale. Koma zimenezi si zoona. (Mat. 13:22) Pa nkhaniyi, Yesu ananena momveka bwino kuti munthu “sangatumikire” Mulungu ndi chuma pa nthawi imodzi.—Mat. 6:24.
12. Kodi anthu amachita zotani kuti apeze ndalama zambiri pa nthawi yochepa? Kodi tingapewe bwanji zimenezi?
12 Kuona kuti ndalama n’zofunika kwambiri kungatipangitse kuchita zinthu zolakwika. (Miy. 28:20) Ena pofuna kupeza ndalama mwamsangamsanga, afika pogula matikiti otchovera juga kapena kuyamba mabizinezi oti alemere mwachangu. Ena afika mpaka ponyengerera anzawo mu mpingo kuti nawonso akhoza kupeza ndalama zambiri. Ena apusitsidwa pouzidwa kuti akongoze anthu ena ndalama ndipo adzawabwezera chiwongola dzanja chochuluka. Mtima wadyera ungachititse kuti tipusitsidwe n’kutaya ndalama zambiri. Choncho tiyenera kusamala kuti tisayambe mtima umenewu. Tiyeni tizichita zinthu mwanzeru. Tizizindikira kuti nthawi zambiri n’zosatheka kupeza ndalama zambirimbiri pa nthawi yochepa.
13. Kodi maganizo a Yehova amasiyana bwanji ndi a anthu a m’dzikoli pa nkhani ya ndalama?
13 Tikamaika ‘ufumu ndi chilungamo cha Mulungu’ pa malo oyamba, Yehova amatidalitsa pamene tikamagwira ntchito mwakhama kuti tipeze zofunika pa moyo. (Mat. 6:33; Aef. 4:28) Iye safuna kuti tiziwodzera pa misonkhano chifukwa chogwira ntchito kwambiri. Safunanso kuti tikakhala pa misonkhano tizidera nkhawa za ndalama. Koma anthu ambiri m’dzikoli amaganiza kuti afunika kudzipereka kwambiri kuti apeze ndalama zochuluka n’cholinga choti adzakhale ndi moyo wabwino m’tsogolo. Ndiye amalimbikitsa ana awo kukhala ndi moyo wokonda chuma umenewu. Yesu anasonyeza kuti maganizo amenewa ndi osathandiza. (Werengani Luka 12:15-21.) Nkhani imeneyi ikutikumbutsa za Gehazi. Iye ankaganiza kuti akhoza kumachita zinthu mwadyera uku akutumikira Yehova.—2 Maf. 5:20-27.
14, 15. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudalira ndalama? Perekani chitsanzo.
14 Pali nkhwazi zina zimene zimamira m’nyanja n’kufa chifukwa chosafuna kusiya nsomba zolemera kwambiri zimene zagwira. Zinthu ngati zimenezi zikhoza kuchitikiranso Mkhristu. M’bale wina yemwe ndi mkulu mu mpingo, dzina lake Alex, anati: “Ndimayesetsa kwambiri kuti ndisawononge ndalama. Ngakhale pa zinthu ngati mankhwala a tsitsi, ndimasamala. Ngati ndapungula ambiri, ndimabwezeretsa ena n’kungogwiritsa ntchito ochepa.” Koma m’bale yemweyu anayamba bizinezi ina yotentha kwambiri. Iye ankafuna kuti akapeza ndalama zambiri, asiye ntchito n’kuyamba upainiya. Ndiye anayamba kutanganidwa kwambiri ndi bizinezi yakeyo. Anafika mpaka potenga ndalama zake zonse ndiponso kubwereka zina poganiza kuti apeza phindu lalikulu. Tsoka ndi ilo analuza nazo kwambiri. Alex anati: “Ndinayesetsa kuti ndalama zanga zibwerere. Ndinkaganiza kuti ndikadikira pang’ono zinthu ziyamba kuyenda bwino.”
15 Kwa miyezo ingapo, Alex ankangoganiza za bizinezi yake basi. Ankalephera kuganiza za zinthu zimene zingalimbitse ubwenzi wake ndi Yehova ndiponso ankalephera kugona. Koma zinthu sizinayambebe kuyenda bwino ngati mmene ankaganizira. Ndalama zake zonse zinatha ndipo anagulitsa nyumba yake. Iye anati: “Ndinazunzitsa banja langa.” Koma zimene zinachitikazi zinam’pangitsa kuphunzira zinthu zina zofunika kwambiri. Anati: “Tsopano ndazindikira kuti aliyense wodalira dziko la Satanali, amagwiritsidwa fuwa lamoto.” (Miy. 11:28) Kudalira ndalama zimene tili nazo kapena luso lathu lopeza ndalama m’dzikoli kuli ngati kudalira Satana, yemwe ndi “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akor. 4:4; 1 Tim. 6:17) Alex anasintha zinthu pa moyo wake “chifukwa cha uthenga wabwino” ndipo tsopano akukhala moyo wosalira zambiri. Kuchita zimenezi kwathandiza iye ndi banja lake kukhala osangalala komanso kuyandikira Yehova.—Werengani Maliko 10:29, 30.
KUNYADA
16. Kodi ndi zinthu ngati ziti zimene tinganyadire? Kodi chingachitike n’chiyani ngati timadziona kuti ndife apamwamba kapena anzeru kwambiri?
16 Kunyadira zinthu zabwino kulibe vuto lililonse. Mwachitsanzo, tiyenera kunyadira kuti ndife Mboni za Yehova. (Yer. 9:24) Kusadzikayikira kumathandizanso munthu kusankha bwino zinthu ndiponso kutsatira mfundo zapamwamba za Mulungu. Koma kudziona ngati ndife apamwamba kapena anzeru kwambiri kukhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova.—Sal. 138:6; Aroma 12:3.
M’malo molakalaka udindo mu mpingo, muzisangalala ndi utumiki
17, 18. (a) Tchulani anthu a m’Baibulo amene anali odzichepetsa ndiponso amene anali onyada. (b) Kodi m’bale wina anachita chiyani n’cholinga choti kunyada kusasokoneze ubwenzi wake ndi Yehova?
17 M’Baibulo muli zitsanzo za anthu onyada komanso odzichepetsa. Davide anali wodzichepetsa ndipo ankadalira Yehova kuti amutsogolere. Choncho Yehova anamudalitsa. (Sal. 131:1-3) Koma Yehova analanga Mfumu Nebukadinezara ndi Belisazara chifukwa anali odzikuza. (Dan. 4:30-37; 5:22-30) Masiku anonso, zingativute nthawi zina kukhala odzichepetsa. Mtumiki wothandiza wina wa zaka 32, dzina lake Ryan, anasamukira ku mpingo wina. Iye anati: “Ndinkaganiza kuti posachedwa ndikhala mkulu koma chaka chathunthu chinadutsa.” Kodi Ryan anakwiya poganiza kuti akulu sakumulemekeza? Kodi anasiya kusonkhana n’kulola kuti kunyada kusokoneze ubwenzi wake ndi Yehova ndiponso anthu ake? Kodi mukanakhala inuyo mukanatani?
18 Ryan ananena kuti: “Ndinawerenga nkhani zonse zimene ndinapeza m’mabuku athu zokhudza kulephereka kwa zinthu zimene tikuyembekezera.” (Miy. 13:12) Ananenanso kuti: “Ndinazindikira kuti ndinafunika kukhala woleza mtima ndiponso wodzichepetsa. Ndinayenera kulola kuti Yehova andiphunzitse.” Ryan anasiya kudziganizira kwambiri n’kuyamba kuganizira ndiponso kuthandiza anthu ena mu mpingo komanso mu utumiki. Pasanapite nthawi, anali kuchititsa maphunziro a Baibulo ambiri. Iye anati: “Ndinaikidwa kukhala mkulu patapita chaka ndi hafu ndipo pa nthawiyi, ndinali ndisakuyembekeza n’komwe. Ndinali nditasiya kuganizira kwambiri zimenezi chifukwa ndinkasangalala kwambiri mu utumiki.”—Werengani Salimo 37:3, 4.
PITIRIZANI KUKHALA PAFUPI NDI YEHOVA
19, 20. (a) Kodi tingatani kuti zinthu zimene timachita tsiku lililonse zisasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova? (b) Perekani zitsanzo za anthu amene anakhalabe pafupi ndi Yehova.
19 Zinthu 7 zimene takambirana m’nkhani ino ndiponso yapita ija pazokha si zolakwika. Timanyadira kuti ndife Mboni za Yehova. Banja losangalala ndiponso thanzi labwino ndi mphatso zamtengo wapatali zochokera kwa Yehova. Timadziwa kuti ntchito ndiponso ndalama zimatithandiza kupeza zofunika pa moyo wathu. Timadziwanso kuti zosangalatsa zimatitsitsimula ndipo zipangizo zamakono zingatithandize. Koma tikamachita chilichonse pa nthawi yolakwika kapena m’njira yolakwika, tikhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova.
Musalole chilichonse kusokoneza ubwenzi wanu ndi Yehova
20 Satana angasangalale kwambiri ubwenzi wathu ndi Yehova utasokonezeka. Koma n’zotheka inuyo ndi banja lanu kupewa zimenezi. (Miy. 22:3) Muziyandikira Yehova n’kukhalabe naye pafupi. Tili ndi zitsanzo zambiri m’Baibulo zimene zingatithandize. Mwachitsanzo, Inoki ndi Nowa “anayenda ndi Mulungu woona.” (Gen. 5:22; 6:9) Nayenso Mose “anapitiriza kupirira moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.” (Aheb. 11:27) Mulungu ankathandiza Yesu chifukwa iyeyo ankachita zosangalatsa Atate wake wakumwamba nthawi zonse. (Yoh. 8:29) Yesetsani kutsanzira anthu ngati amenewa. “Muzikhala okondwera nthawi zonse. Muzipemphera mosalekeza. Muziyamika pa chilichonse.” (1 Ates. 5:16-18) Musalole chilichonse kusokoneza ubwenzi wanu ndi Yehova.
a Mayina asinthidwa.
b Onani Galamukani! ya October 2011 ya mutu wakuti, “Kodi Mungalere Bwanji Ana Anu Kuti Akule Bwino?”
c Onani Galamukani! ya March 2011 ya mutu wakuti, “Mfundo Zisanu Zokuthandizani Kukhala ndi Thanzi Labwino”
-