-
Samalani ndi Misampha ya MdyerekeziNsanja ya Olonda—2012 | August 15
-
-
Samalani ndi Misampha ya Mdyerekezi
‘Wonjokani mumsampha wa Mdyerekezi.’—2 TIM. 2:26.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
Ngati timafulumira kukayikira anthu ena, kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?
Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Pilato ndi Petulo pa nkhani ya kuopa anthu kapena kufuna kuwasangalatsa?
Kodi mungatani kuti musamadziimbe mlandu kwambiri?
1, 2. Kodi m’nkhani ino tikambirana misampha iti ya Mdyerekezi?
MDYEREKEZI amasaka atumiki a Yehova. Koma sikuti cholinga chake kwenikweni ndi kuwapha. Iye amafuna kuwagwira amoyo n’cholinga choti azichita zofuna zake.—Werengani 2 Timoteyo 2:24-26.
2 Mlenje amagwiritsa ntchito msampha kuti agwire nyama yamoyo. Amatha kukusa nyama kuti ifike pamalo amene angaikole ndi khwekhwe. Apo ayi, amatchera msampha pamalo obisika kuti nyama imene ikungodziyendera ikodwe. Ndi mmenenso Mdyerekezi amachitira pofuna kugwira atumiki a Mulungu. Kuti tisakodwe, tiyenera kukhala tcheru komanso kumvera machenjezo osonyeza kuti msampha wa Satana uli pafupi. M’nkhani ino, tikambirana mmene tingapewere misampha itatu ya Mdyerekezi imene yakola anthu ambiri. Misampha yake ndi (1) kusalankhula bwino, (2) kuopa anthu kapena kufuna kuwasangalatsa ndiponso (3) kudziimba mlandu kwambiri. M’nkhani yotsatira tidzakambirana misampha ina iwiri.
PEWANI KUSALANKHULA BWINO
3, 4. Kodi chingachitike n’chiyani ngati sitilamulira lilime lathu? Perekani chitsanzo.
3 Nthawi zina mlenje akafuna kugwira nyama, amayatsa tchire kuti zivumbuluke. Nayenso Mdyerekezi amafuna kuyatsa moto wophiphiritsa mu mpingo wachikhristu. Amatero n’cholinga choti anthu achoke mu mpingo kenako iyeyo awagwire. Koma mosazindikira, tikhoza kuchita zinthu zogwirizana ndi cholinga chakechi n’kugwidwa. Kodi zimenezi zingatheke bwanji?
4 Yakobo anayerekeza lilime ndi moto. (Werengani Yakobo 3:6-8.) Ngati sitilamulira lilime lathu, tikhoza kuyambitsa moto mu mpingo. Kodi zimenezi zingachitike bwanji? Tiyerekeze kuti pa misonkhano ya mpingo alengeza kuti mlongo wina wavomerezedwa kukhala mpainiya wokhazikika. Misonkhano itatha, ofalitsa awiri akukambirana za chilengezocho. Mmodzi akusangalala ndipo akumufunira zabwino mpainiyayo. Koma wina akukayikira zolinga za mpainiyayo n’kumanena kuti akungofuna kutchuka. Kodi inuyo mungafune kumacheza ndi wofalitsa uti? Mwina mwaona kale kuti zolankhula za wofalitsa wachiwiriyu zikhoza kuyatsa moto mu mpingo.
5. Kodi tingatani kuti tipewe kusalankhula bwino?
5 Kodi tingapewe bwanji kusalankhula bwino? Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.” (Mat. 12:34) Choncho, poyamba tiyenera kufufuza mtima wathu. Kodi timapewa maganizo amene angatichititse kulankhula zinthu zopweteka? Mwachitsanzo, kodi timatani ngati m’bale wina akuyesetsa kuchita zambiri mu mpingo? Kodi timaganiza kuti ali ndi zolinga zabwino kapena timafulumira kuganiza kuti zolinga zake n’zolakwika? Ngati timafulumira kukayikira ena, ndi bwino kukumbukira kuti Mdyerekezi anakayikiranso zolinga za Yobu, yemwe ankatumikira Mulungu mokhulupirika. (Yobu 1:9-11) M’malo mokayikira m’bale wathu, tiyenera kudzifunsa kuti, N’chifukwa chiyani ndikumukayikira? Kodi pali zifukwa zomveka? Kapena kodi ndikutengera mtima wosakonda anthu umene wafala m’masiku otsiriza ano?—2 Tim. 3:1-4.
6, 7. (a) Kodi tingakayikire anthu ena pa zifukwa ziti? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani anthu akatinena zachipongwe?
6 Tiyeni tione zifukwa zina zimene zingatichititse kukayikira ena. Chifukwa china chingakhale chakuti timafuna kuti titchuke ifeyo. Zili ngati tikukankhira ena pansi n’cholinga choti ifeyo tioneke aatali. Tikhoza kukayikiranso ena pofuna kudzikhululukira ngati tikulephera kuchita zinthu zina. Kaya timakayikira ena chifukwa cha kunyada, nsanje kapena kudziona kuti ndife olephera, zotsatira zake zimakhala zoipa.
7 Mwina timaona kuti tili ndi zifukwa zabwino zochititsa kuti tisalankhule bwino za munthu wina. N’kutheka kuti zolankhula za munthuyo zinatipsetsa mtima. Koma ngati zili choncho, si bwino kubwezera ndi mawu opwetekanso. Kuchita zimenezi kumangowonjezera mavuto ndipo kumagwirizana ndi zolinga za Mdyerekezi osati za Mulungu. (2 Tim. 2:26) Tiyenera kutsanzira Yesu pa nkhani imeneyi. Pamene anali kunenedwa zachipongwe, “sanabwezere zachipongwe.” M’malomwake, “anali kudzipereka kwa iye amene amaweruza molungama.” (1 Pet. 2:21-23) Yesu ankakhulupirira kuti Yehova akonza zinthu m’njira yoyenera ndiponso pa nthawi yake. Ifenso tiyenera kukhulupirira Mulungu. Tikamalankhula zinthu zolimbikitsa, timathandiza kuti mu mpingo mukhale mtendere, womwe umagwirizanitsa anthu.—Werengani Aefeso 4:1-3.
PEWANI MSAMPHA WOOPA ANTHU KOMANSO KUFUNA KUWASANGALATSA
8, 9. N’chifukwa chiyani Pilato anaweruza Yesu kuti aphedwe?
8 Nyama imene yakodwa imalephera kuyenda. Nayenso munthu amene wakodwa mumsampha woopa anthu kapena kufuna kuwasangalatsa amalephera kuchita zinthu zina. (Werengani Miyambo 29:25.) Tiyeni tikambirane zitsanzo za anthu awiri amene anali osiyana kwambiri. Iwo anakodwa mumsampha umenewu ndipo tiona zimene tingaphunzire pa zimene anachita.
9 Pilato, yemwe anali bwanamkubwa wachiroma, ankadziwa kuti Yesu sanalakwe chilichonse ndipo sankafunika kuphedwa. Pilato ananena kuti Yesu sanachite chilichonse “choyenera chilango cha imfa.” Nanga n’chifukwa chiyani anamuweruza kuti aphedwe? Chifukwa chakuti ankafuna kusangalatsa anthu. (Luka 23:15, 21-25) Pofuna kuti cholinga chawo chitheke, anthuwo anafuula kuti: “Mukamumasula ameneyu, ndiye kuti si inu bwenzi la Kaisara.” (Yoh. 19:12) Mwina Pilato ankaopa kuti akamasula Yesu, achotsedwa pa udindo kapena kuphedwa kumene. Choncho analolera kuchita zofuna za Mdyerekezi.
10. N’chifukwa chiyani Petulo anakana Khristu?
10 Chitsanzo china ndi mtumwi Petulo. Iye ankagwirizana kwambiri ndi Yesu. Sankaopanso kuuza anthu kuti Yesu ndi Mesiya. (Mat. 16:16) Petulo anakhalabe wokhulupirika kwa Yesu pa nthawi imene ophunzira ena anamusiya chifukwa chosamvetsa zimene ananena. (Yoh. 6:66-69) Adani atabwera kuti adzamange Yesu, Petulo anagwiritsa ntchito lupanga kuti amuteteze. (Yoh. 18:10, 11) Koma kenako anaopa anthu mpaka anakana zoti amadziwa Yesu Khristu. Kwa kanthawi, mtumwiyu anakodwa mumsampha woopa anthu ndipo izi zinamulepheretsa kuchita zinthu molimba mtima.—Mat. 26:74, 75.
11. Kodi anthu angatikakamize kuti tichite chiyani?
11 Akhristufe sitiyenera kulola anthu ena kutikakamiza kuti tichite zinthu zimene Mulungu amadana nazo. Abwana athu kapena anthu ena angatinyengerere kuti tichite chinyengo kapena chiwerewere. Akhristu apasukulu angakakamizidwe ndi anzawo kuti abere mayeso, aonere zolaula, asute, amwe mankhwala osokoneza bongo, aledzere kapena achite zachiwerewere. N’chiyani chingatithandize kuti tisachite zinthu zimene Yehova amadana nazo chifukwa choopa anthu kapena kufuna kuwasangalatsa?
12. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Pilato ndi Petulo anachita?
12 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Pilato ndi Petulo anachita? Pilato sankamudziwa bwino Khristu. Komabe iye ankadziwa kuti Yesu sanalakwe chilichonse komanso kuti sanali munthu wamba. Ngakhale zinali choncho, iye sanali wodzichepetsa ndipo sankakonda Mulungu woona. Choncho Mdyerekezi anamugwira wamoyo. Mosiyana ndi Pilato, Petulo ankadziwa choonadi ndipo ankakonda Mulungu. Koma nthawi zina, iye sankadzichepetsa, ankachita mantha ndiponso kugonja pa mayesero. Yesu atatsala pang’ono kumangidwa, Petulo anadzitama kuti: “Ngakhale ena onse atathawa kukusiyani, koma ine ndekha sindidzatero.” (Maliko 14:29) Ngati Petulo akanakhulupirira Mulungu mofanana ndi wamasalimo, akanakhala wokonzeka kukumana ndi mayesero. Tikutero chifukwa wamasalimoyu anaimba kuti: “Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa. Munthu wochokera kufumbi angandichite chiyani?” (Sal. 118:6) Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anatenga Petulo ndi atumwi ena awiri n’kupita m’munda wa Getsemane. Koma m’malo mokhala maso, Petulo ndi anzakewo anagona. Yesu anawadzutsa n’kuwauza kuti: “Amuna inu, khalani maso ndipo muzipemphera, kuti musalowe m’mayesero.” (Maliko 14:38) Koma Petulo anagonanso ndipo kenako anagonja poyesedwa chifukwa cha mantha.
13. Kodi tingatani kuti tisagonje poyesedwa?
13 Pali chinthu chinanso chimene tingaphunzire pa chitsanzo cha Pilato ndi Petulo. Kuti tisagonje tikamayesedwa, tiyenera kudziwa bwino choonadi, kukhala odzichepetsa, kukonda Mulungu ndiponso kumuopa osati kuopa anthu. Tikakhala ndi chikhulupiriro champhamvu chifukwa chodziwa bwino Mawu a Mulungu, tikhoza kuuza anthu ena molimba mtima zimene timakhulupirira. Zimenezi zingatithandize kuti tisagonje chifukwa choopa anthu. Koma sitiyenera kudzidalira kwambiri. M’malomwake, tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumazindikira kuti timafunika thandizo la Mulungu kuti tisagonje poyesedwa. Tiyenera kupempha Yehova kuti atipatse mzimu wake. Tikamakonda kwambiri Yehova, tidzatsatira malamulo ake ndiponso kulemekeza dzina lake. Tiyeneranso kukonzekera mayesero asanafike. Mwachitsanzo, kukonzekera ndiponso kupemphera limodzi ndi ana athu kungawathandize kuti asagonje anzawo akamawakopa kuti achite zoipa.—2 Akor. 13:7.a
PEWANI MSAMPHA WODZIIMBA MLANDU KWAMBIRI
14. Kodi Mdyerekezi amafuna kuti tizikhala ndi maganizo otani?
14 Nthawi zina mlenje amatchera diwa pamalo amene nyama zimakonda kudutsa. Nyama ikasuntha chingwe cha diwalo, mwala umagwa n’kuiphwanya. Munthu amene akudziimba mlandu kwambiri amakhala ngati wapsinjidwa ndi chimwala. Tikamaganizira kwambiri zinthu zimene tinalakwitsa kale tingamve ngati ‘taponderezeka kwambiri.’ (Werengani Salimo 38:3-5, 8.) Satana amafuna kuti tizidziona ngati ndife ochimwa kwambiri moti sitiyenera chifundo cha Yehova ndipo sitingathe kuchita zimene Mulungu amafuna.
15, 16. Kodi mungapewe bwanji msampha wodziimba mlandu kwambiri?
15 Kodi mungapewe bwanji msampha wodziimba mlandu kwambiri? Ngati mwachita tchimo lalikulu, yesetsani mwamsanga kukonza ubwenzi wanu ndi Yehova. Auzeni akulu kuti akuthandizeni. (Yak. 5:14-16) Chitani zonse zimene mungathe kuti mukonze cholakwacho. (2 Akor. 7:11) Mukalandira chilango, musakhumudwe. Umenewo ndi umboni woti Yehova amakukondani. (Aheb. 12:6) Yesetsani kuti musadzachitenso zinthu zimene zinayambitsa vutolo. Ngati mwalapa n’kutembenuka, khulupirirani kuti nsembe ya dipo ya Yesu Khristu ikhoza kuphimbiratu machimo anu.—1 Yoh. 4:9, 14.
16 Anthu ena amadziimbabe mlandu chifukwa cha machimo amene anakhululukidwa kale. Ngati mumatero, kumbukirani kuti Yehova anakhululukira Petulo ndi atumwi ena amene anasiya Mwana wake wokondedwa pa nthawi imene iye ankafunika kwambiri thandizo. Yehova anakhululukiranso munthu wa ku Korinto amene anachita chiwerewere ndi mkazi wa bambo ake, munthuyo atalapa. (1 Akor. 5:1-5; 2 Akor. 2:6-8) Mawu a Mulungu amanena za anthu ambiri amene anachita machimo akuluakulu omwe analapa n’kukhululukidwa ndi Mulungu.—2 Mbiri 33:2, 10-13; 1 Akor. 6:9-11.
17. Kodi dipo lingatithandize bwanji?
17 Yehova amakhululuka ndi kuiwala machimo ngati munthu walapa n’kulola kuti Mulungu amuchitire chifundo. Musamaganize kuti nsembe ya dipo ya Yesu singaphimbe machimo anu. Maganizo amenewa angachititse kuti mukodwe mumsampha wa Satana. Mdyerekezi amafuna kuti muziganiza kuti dipo silingaphimbe machimo anu. Koma Yehova amakhululukira anthu onse amene alapa. (Miy. 24:16) Kukhulupirira dipo kungakuthandizeni kuti musamadziimbe mlandu kwambiri. Zimenezi zingakupatseni mphamvu kuti muzitumikira Mulungu ndi mtima wanu wonse, maganizo anu onse ndiponso moyo wanu wonse.—Mat. 22:37.
TIKUDZIWA BWINO ZIWEMBU ZA SATANA
18. Kodi tingapewe bwanji misampha ya Mdyerekezi?
18 Satana amangofuna kutikola basi. Iye alibe nazo ntchito kuti msampha womwe ukole ndi uti. Koma ife tikhoza kupewa misampha ya Mdyerekezi chifukwa tikudziwa bwino ziwembu zake. (2 Akor. 2:10, 11) Kuti tipewe misamphayi, tiyenera kupempha Mulungu kuti atipatse nzeru zotithandiza kuthana ndi mayesero. Yakobo analemba kuti: “Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.” (Yak. 1:5) Tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene timapempha. Tiziphunzira Baibulo nthawi zonse ndiponso kutsatira zimene timaphunzira. Mabuku ofotokoza Baibulo ochokera kwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amatidziwitsa misampha ya Mdyerekezi ndiponso mmene tingaipewere.
19, 20. N’chifukwa chiyani tiyenera kudana ndi zoipa?
19 Kupemphera ndiponso kuphunzira Baibulo zimatithandiza kukonda zabwino. Koma tifunikanso kudana ndi zoipa. (Sal. 97:10) Kuganizira mavuto amene angabwere chifukwa chotsatira zilakolako zoipa kungatithandize kuzipewa. (Yak. 1:14, 15) Tikamakonda zabwino n’kumadana ndi zoipa, zinthu zimene Satana amagwiritsa ntchito kuti atikole, zimatinyansa kwambiri moti sitingakopeke nazo.
20 Timayamikira kwambiri kuti Mulungu amatithandiza kuti Satana asatichenjerere. Yehova amatilanditsa “kwa woipayo” pogwiritsa ntchito mzimu wake, Mawu ake ndiponso gulu lake. (Mat. 6:13) M’nkhani yotsatira tiona mmene tingapewere misampha ina iwiri imene Mdyerekezi akukola nayo atumiki a Mulungu ambiri.
-
-
Musasunthike Popewa Misampha ya SatanaNsanja ya Olonda—2012 | August 15
-
-
Musasunthike Popewa Misampha ya Satana
“Musasunthike polimbana ndi zochita zachinyengo za Mdyerekezi.”—AEF. 6:11.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
Kodi atumiki a Yehova angapewe bwanji msampha wa kukonda chuma?
Kodi Mkhristu wapabanja angapewe bwanji msampha wa chigololo?
Kodi kupewa msampha wa kukonda chuma ndiponso wa chiwerewere kuli ndi ubwino wotani?
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani Satana amadana ndi odzozedwa ndiponso a “nkhosa zina”? (b) Kodi tikambirana misampha iti ya Satana m’nkhani ino?
SATANA MDYEREKEZI sakonda anthu, makamaka atumiki a Yehova. Ndipo iye akumenya nkhondo yolimbana ndi odzozedwa amene ali padziko lapansi. (Chiv. 12:17) Akhristu olimba mtimawa akhala akutsogolera ntchito yolalikira ndiponso athandiza anthu kudziwa kuti Satana ndi amene akulamulira dzikoli. Mdyerekezi amadananso ndi a “nkhosa zina,” amene amathandiza odzozedwa ndiponso ali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. (Yoh. 10:16) Satana alibe chiyembekezochi. M’pake kuti ndi wokwiya kwambiri. Kaya tili ndi chiyembekezo chopita kumwamba kapena chokhala padziko lapansi, Satana satifunira zabwino. Cholinga chake ndi kutikola basi.—1 Pet. 5:8.
2 Kuti zimenezi zitheke, iye amatchera misampha yosiyanasiyana. Satana “wachititsa khungu maganizo” a anthu osakhulupirira moti iwo samvetsera uthenga wabwino ndipo saona misamphayi. Koma Mdyerekezi amakolanso anthu amene akudziwa za Ufumu. (2 Akor. 4:3, 4) M’nkhani yapita ija tinakambirana mmene tingapewere misampha itatu ya Satana. Misampha yake ndi (1) kusalankhula bwino, (2) kuopa anthu kapena kufuna kuwasangalatsa ndiponso (3) kudziimba mlandu kwambiri. Tiyeni tione mmene tingapewere misampha ina iwiri. Misampha yake ndi kukonda chuma ndiponso chigololo.
MSAMPHA WA KUKONDA CHUMA
3, 4. Kodi nkhawa za moyo wa nthawi ino zingachititse bwanji anthu kuyamba kukonda chuma?
3 M’fanizo lina, Yesu ananena za mbewu zimene zinafesedwa paminga. Iye anafotokoza kuti munthu akhoza kumva mawu “koma nkhawa za moyo wa m’nthawi ino ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma zimalepheretsa mawuwo kukula, ndipo iye amakhala wosabala zipatso.” (Mat. 13:22) Choncho kukonda chuma ndi msampha umene Satana amagwiritsa ntchito.
4 Pali zinthu ziwiri zimene zimagwira ntchito limodzi polepheretsa mawu kukula. Choyamba ndi “nkhawa za moyo wa m’nthawi ino.” ‘M’nthawi yovuta’ ino, pali zinthu zambiri zimene zingakudetseni nkhawa. (2 Tim. 3:1) Popeza zinthu zakwera mitengo komanso ntchito zikusowa, mukhoza kumavutika kuti mupeze zofunika pa moyo. Mukhozanso kumadera nkhawa zam’tsogolo mwina n’kumadzifunsa kuti, ‘Kodi zinthu zidzandiyendera bwanji ndikadzakalamba?’ Chifukwa cha zimenezi, anthu ena amayamba kufufuza chuma poganiza kuti akakhala ndi ndalama zambiri, sangadzavutike.
5. Kodi munthu angapusitsidwe bwanji ndi “chinyengo champhamvu cha chuma”?
5 Chinthu china chimene Yesu ananena ndi “chinyengo champhamvu cha chuma.” Chinyengochi limodzi ndi nkhawa zingalepheretse mawu kukula. Baibulo limanenadi kuti ‘ndalama zimateteza.’ (Mlal. 7:12) Koma kufufuza chuma n’kupanda nzeru. Ambiri azindikira kuti akamayesetsa kuti apeze chuma, amapezeka kuti akodwa mumsampha wokonda chumacho. Ena afika pokhala akapolo a chuma.—Mat. 6:24.
6, 7. (a) Kodi munthu wapantchito angakodwe bwanji mumsampha wokonda chuma? (b) Kodi Mkhristu amene wauzidwa kuti azigwira ovataimu ayenera kuganizira zinthu ziti?
6 Mtima wofuna chuma ukhoza kuyamba mosavuta. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti bwana wanu akukuuzani kuti: “Kampani yathu yapeza mwayi wa ntchito inayake. Tingofunika kugwira ovataimu kwa miyezi yochepa. Koma tidzakulipirani ndalama zambiri.” Kodi mungatani? N’zoona kuti mufunika kupezera banja lanu zinthu zofunika pa moyo koma kumbukirani kuti muli ndi udindo winanso. (1 Tim. 5:8) Pali zinthu zambiri zofunika kuziganizira. Kodi nthawi yowonjezerayo idzakhala yochuluka bwanji? Kodi sizidzakulepheretsani kutumikira bwino Mulungu, kusonkhana ndiponso kuchita Kulambira kwa Pabanja?
7 Posankha zochita, kodi mudzaganizira kwambiri za chiyani? Kodi mudzaganizira za ndalama zimene mungapeze kapena mudzaganizira mmene ntchitoyo ingakhudzire ubwenzi wanu ndi Yehova? Kodi mudzasiya kuika zinthu zokhudza Ufumu patsogolo n’cholinga choti mupeze ndalama zambiri? Apa n’zoonekeratu kuti kukonda chuma kungalepheretse munthu ndiponso banja lake kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ngati izi n’zimene zikukuchitikirani, kodi mungatani kuti muwonjoke mumsampha umenewu?—Werengani 1 Timoteyo 6:9, 10.
8. Kodi ndi nkhani za m’Baibulo ziti zimene zingatithandize kudzifufuza?
8 Kuti musakodwe mumsampha wokonda chuma, muyenera kudzifufuza nthawi ndi nthawi. Musakhale ngati Esau amene anachita zinthu zosonyeza kuti ankanyoza zinthu zauzimu. (Gen. 25:34; Aheb. 12:16) Musakhalenso ngati munthu wachuma amene Yesu anamuuza kuti: ‘Kagulitse katundu wako ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatero ubwere udzakhale wotsatira wanga.’ M’malo mochita zimenezi, iye “anachoka ali wachisoni, chifukwa anali ndi katundu wambiri.” (Mat. 19:21, 22) Chifukwa chokodwa mumsampha wokonda chuma, munthuyu anataya mwayi wotsatira munthu wofunika kwambiri kuposa wina aliyense. Samalani kuti inunso musataye mwayi wokhala wophunzira wa Yesu Khristu.
9, 10. Kodi Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziona bwanji zinthu zakuthupi?
9 Kuti tipewe msamphawu, tiyenera kutsatira malangizo a Yesu akuti: “Choncho musamade nkhawa n’kumanena kuti, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapena, ‘Tivala chiyani?’ Pakuti anthu a mitundu ina akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.”—Mat. 6:31, 32; Luka 21:34, 35.
10 M’malo mokopeka ndi chinyengo champhamvu cha chuma, yesetsani kukhala ndi maganizo a Aguri amene analemba kuti: “Musandipatse umphawi kapena chuma. Ndidye chakudya chimene ndikufunika kudya.” (Miy. 30:8) Aguri ankadziwa bwino kufunika kwa ndalama komanso kuopsa kwa chinyengo champhamvu cha chuma. Dziwani kuti nkhawa za moyo uno ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma zikhoza kuwononga ubwenzi wanu ndi Yehova. Kudera nkhawa kwambiri zinthu zakuthupi kukhoza kukuwonongerani nthawi ndi mphamvu moti simungafunenso kuika zinthu za Ufumu patsogolo. Choncho yesetsani kuti musakodwe mumsampha wa Satana wa kukonda chuma.—Werengani Aheberi 13:5.
CHIGOLOLO CHILI NGATI DZENJE LOBISIKA
11, 12. Kodi n’chiyani chingachititse Mkhristu kuchita chigololo ndi munthu wa kuntchito?
11 Alenje akafuna kugwira nyama yaikulu, amakumba dzenje pampita wake. Pamwamba pake amaphimbapo ndi timitengo ndi dothi. Msampha wina wa Satana, umene wakola anthu ambiri, umafanana ndi dzenje lotereli. Msampha wake ndi chiwerewere. (Miy. 22:14; 23:27) Akhristu ambiri achita zinthu zimene zawagwetsera mosavuta m’dzenje limeneli. Akhristu amene ali pa banja achita chigololo chifukwa chocheza mosayenera ndi anthu ena n’kuyamba kukondana.
12 Zimenezi zikhoza kuchitika kuntchito. Kafukufuku wina anasonyeza kuti hafu ya akazi amene anachita chigololo komanso pafupifupi amuna onse amene anachita chigololo, anachita ndi anthu a kuntchito kwawo. Kodi mumagwira ntchito ndi anthu amene si amuna kapena akazi anzanu? Ngati ndi choncho, kodi mumacheza nawo bwanji? Kodi mumaonetsetsa kuti simukucheza nawo mopitirira malire? Mwachitsanzo, mlongo amene amakonda kucheza ndi mwamuna wina kuntchito akhoza kuyamba kumuuza zakukhosi kwake mwinanso mavuto a m’banja lake. Apo ayi, m’bale amene amakonda kucheza ndi mkazi wina kuntchito akhoza kuyamba kuganiza kuti: “Mkazi ameneyu amalemekeza maganizo anga ndipo amamvetsera ndikamalankhula. Zikuoneka kuti amandidalira. Koma mkazi wanga satero.” Kodi Akhristu oterewa sangachite chigololo?
13. Kodi anthu mu mpingo angayambe bwanji kucheza mosayenera?
13 Mu mpingo, anthu akhozanso kuyamba kucheza mosayenera. Izi ndi zimene zinachitika ku mpingo wina. Daniel ndi mkazi wake Saraha anali apainiya okhazikika. Daniel anali mkulu yemwe sankakana ntchito iliyonse m’gulu la Yehova. Daniel ankaphunzira Baibulo ndi anyamata asanu ndipo atatu anabatizidwa. Abale atatuwa ankafunika thandizo. Daniel akatanganidwa ndi utumiki wina, Sarah ankathandiza abalewa. Iwo ankafuna munthu woti azimuuza zakukhosi kwawo ndipo ankachita zimenezi ndi Sarah. Nayenso Sarah ankafuna munthu wocheza naye ndipo ankangocheza ndi abalewo. Apa zinali ngati msampha watcheredwa. Daniel anati: “Chifukwa chothandiza anthuwa kwa nthawi yaitali, mkazi wanga anafooka moti ankafunika thandizo kuti ubwenzi wake ndi Yehova ulimbe ndiponso maganizo ake akhazikike. Vuto linanso linali loti ineyo ndinkangochita zinthu zina osaona zimenezi. Zotsatira zake zinali zomvetsa chisoni kwambiri. Mkazi wanga anachita chigololo ndi mmodzi mwa abalewo. Ndinkatanganidwa kwambiri ndi utumiki wosiyanasiyana moti sindinazindikire kuti mkazi wanga wayamba kufooka.” Kodi mungatani kuti zimenezi zisakuchitikireni?
14, 15. Kodi n’chiyani chingathandize Akhristu apabanja kupewa chigololo?
14 Kuti mupewe msampha wa chigololo, muyenera kuganizira kwambiri tanthauzo la kukhulupirika m’banja. Yesu anati: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mat. 19:6) Musamaganize kuti utumiki wanu ndi wofunika kwambiri kuposa mkazi kapena mwamuna wanu. Muyenera kukumbukiranso kuti munthu amene amakonda kusiya mkazi kapena mwamuna wake kuti akachite zinthu zina zosafunika kwenikweni, amayambitsa mavuto m’banja. Izi zingachititse kuti wina achite chigololo.
15 Koma bwanji ngati ndinu mkulu? Mtumwi Petulo analemba kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa. Osatinso chifukwa chofuna kupindulapo kenakake, koma ndi mtima wonse.” (1 Pet. 5:2) Choncho ngati ndinu mkulu, muyenera kusamalira abale ndi alongo mu mpingo. Komabe simuyenera kunyalanyaza mkazi wanu n’cholinga choti musamalire mpingo. Si nzeru kutanganidwa pothandiza mpingo pamene mkazi wanu akusowa thandizo kunyumba. Zimenezi zikhoza kuwononga banja lanu. Daniel ananena kuti, “Si bwino kumangotanganidwa ndi maudindo m’gulu la Yehova n’kumanyalanyaza banja lanu.”
16, 17. (a) Kodi Akhristu apantchito angasonyeze bwanji kuti safuna kuchita chibwenzi ndi munthu wina aliyense? (b) Tchulani magazini imene ili ndi malangizo othandiza Akhristu kupewa chigololo.
16 M’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! muli malangizo ambiri othandiza Akhristu apabanja kuti asagwere mumsampha wa chigololo. Mwachitsanzo mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 2006, muli malangizo akuti: “Kuntchito ndiponso kwina kulikonse, samalani ndi zinthu zimene zingachititse kuti muyambe kukondana ndi munthu winawake. Mwachitsanzo, kugwira ovataimu limodzi ndi munthu amene si mwamuna mnzanu kapena mkazi mnzanu kungathe kukulowetsani m’mayesero. Monga munthu wa pa banja, muyenera kusonyeza bwino mwa zolankhula zanu ndiponso khalidwe lanu kuti simufuna kuchita chibwenzi ndi munthu aliyense. Mosakayikira, monga munthu wodzipereka kwa Mulungu, simungachite mwadala zinthu zopatsa ena maganizo olakwika mwa kukopana ndi winawake kapena kuvala ndi kudzikongoletsa [mokopa ena]. . . . Kukhala ndi zithunzi za mwamuna kapena mkazi wanu ndiponso za ana anu kuntchito kwanu, kungathandize kuti inuyo ndiponso anthu ena azikumbukira kuti mumaona kuti banja lanu ndi lofunika. Onetsetsani kuti musalimbikitse, ngakhalenso kulekerera, zinthu zokukopani zimene wina akuchita.”
17 Nkhani yakuti “Kodi Kukhulupirika M’banja N’kutani?” mu Galamukani! ya April 2009, imanena kuti tiyenera kupewa kukhumbira ndiponso kuganizira zochita chiwerewere ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wathu. Nkhaniyi inanena kuti kuchita zimenezi kungachititse kuti muchitedi chigololo. (Yak. 1:14, 15) Ngati muli pa banja, mungachite bwino kukambirana ndi mkazi kapena mwamuna wanu nkhani ngati zimenezi nthawi ndi nthawi. Yehova ndi amene anayambitsa ukwati choncho ndi wopatulika. Mungasonyeze kuti mumayamikira zinthu zopatulika mukamakambirana ndi mkazi kapena mwamuna wanu nkhani zokhudza ukwati wanu.—Gen. 2:21-24.
18, 19. (a) Kodi zotsatira za chigololo n’zotani? (b) Kodi ubwino wa kukhala wokhulupirika m’banja ndi wotani?
18 Ngati mukuyesedwa kuti muyambe kukondana ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wanu, muyenera kuganizira mavuto amene amabwera chifukwa chochita dama kapena chigololo. (Miy. 7:22, 23; Agal. 6:7) Anthu amene achita chiwerewere amakhumudwitsa Yehova ndiponso mwamuna kapena mkazi wawo. Iwonso sasangalala. (Werengani Malaki 2:13, 14.) Muziganiziranso ubwino wokhala ndi makhalidwe oyera. Anthu amakhalidwe oyera amakhala ndi chikumbumtima choyera panopa komanso adzapeza moyo wosatha m’tsogolo.—Werengani Miyambo 3:1, 2.
19 Wamasalimo anaimba kuti: “Okonda chilamulo [cha Mulungu] amapeza mtendere wochuluka, ndipo palibe chowakhumudwitsa.” (Sal. 119:165) Choncho muzikonda kwambiri choonadi. Masiku ano ndi oipa ndiye “samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru.” (Aef. 5:15, 16) Masiku ano, Satana amagwiritsa ntchito misampha yambiri kuti akole atumiki a Mulungu. Koma Yehova watipatsa zinthu zonse zofunika kuti ‘tisasunthike’ poyesetsa ‘kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’—Aef. 6:11, 16.
-