Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 6/1 tsamba 29-30
  • Nkhondo ya Casiodoro de Reina Kaamba ka Baibulo la Chispanya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkhondo ya Casiodoro de Reina Kaamba ka Baibulo la Chispanya
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Dzina la Mulungu m’Matembenuzidwe a Chispanya
  • Nkhondo Yomwe Baibulo Lachispanya Linamenya Kuti Likhalepobe
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Mmene Mawu a Mulungu Anafikira ku Spain M’zaka za m’ma 500 Mpaka 1500 AD
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Baibulo Lakumana ndi Zambiri
    Galamukani!—2007
  • Dzina la Mulungu ndi Otembenuza Baibulo
    Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 6/1 tsamba 29-30

Nkhondo ya Casiodoro de Reina Kaamba ka Baibulo la Chispanya

SPAIN wa m’zaka za zana la 16 anali malo owopsa kuŵerengeramo Baibulo. Tchalitchi cha Katolika chinalamula bwalo la Inquisition kuthetsa kubuka kulikonse kwakung’ono kwa kutsutsa mwambo. Koma panali mnyamata wina kummwera kwa Spain amene sanangoŵerenga chabe Malemba komanso anaŵinda za kuwatembenuzira m’chinenero chakumaloko kotero kuti Mspanya aliyense athe kuwaŵerenga. Dzina lake anali Casiodoro de Reina.

Chidwi cha Reina pa Baibulo chinadzutsidwa mkati mwa zaka zimene anathera ali panyumba ya agulupa ku San Isidro del Campo, kunja kwa Seville, ku Spain. Mkati mwa ma 1550, unyinji wa amonke panyumba ya agulupa imeneyi yapadera unathera maola ambiri ukuŵerenga Malemba m’malo mogwira ntchito zawo zatchalitchi. Ndipo uthenga wa Baibulo unasintha maganizo awo. Anakana chiphunzitso chachikatolika chonena za kugwiritsira ntchito mafano ndi kukhulupirira purigatoriyo. Malingaliro awo anadziŵika m’deralo mosapeŵeka, ndipo powopa kugwidwa ndi bwalo la Spanish Inquisition, anasankha zothaŵira kumaiko akunja. Reina anali mmodzi wa anthu 12 amene anakhoza kuthaŵira ku Geneva, Switzerland.

Pambuyo pa mwaŵi wa kuthaŵa umenewo, iye anali kuyendayenda m’mizinda ya ku Ulaya, akumatha kuzemba omlondalonda. Mu 1562 omuimba mlandu ogwiritsidwa mwala anatentha chomuumba chake ku Seville, koma ngakhale chiwopsezo chankhalwe chimenecho sichinachititse Reina kusiya ntchito yake ya kutembenuza Malemba. Ngakhale kuti iwo analonjeza anthu mphotho ya kugwidwa kwake ndipo iye anawopa kugwidwa nthaŵi zonse, anagwira ntchito ya kutembenuza m’Chispanya kosalekeza. “Kusiyapo nthaŵi imene ndinali kudwala kapena kuyenda ulendo, . . . sindinaleke kugwira ntchito,” anafotokoza motero.

Mkati mwa zaka khumi Reina anamaliza ntchito yake. Mu 1569 Baibulo lake lonse lotembenuzidwa linafalitsidwa ku Basel, Switzerland. Buku limeneli linali la matembenuzidwe okwana achispanya kuchokera m’zinenero zoyambirira. Kwa zaka mazana ambiri kunali ma Baibulo achilatini, koma Chilatini chinali chinenero cha anthu apamwamba. Reina anakhulupirira kuti aliyense ayenera kudziŵa za m’Baibulo, ndipo anaika moyo wake pachiswe mochirikiza cholinga chimenecho.

M’mawu oyamba a matembenuzidwe ake, anafotokoza zifukwa zake. “Kuletsa kutembenuzidwa kwa Malemba Opatulika m’chinenero cha anthu onse mwachionekere kumadzetsa chitonzo choipitsitsa pa Mulungu ndi ngozi pa ubwino wa anthu. Imeneyi ndiyo ntchito yeniyeni ya Satana ndi amene amawalamulira. . . . Poona kuti Mulungu anapatsa Mawu ake kwa anthu, pofuna kuti awamvetse ndi kuti onse awagwiritsire ntchito, iye amene angawaletse m’chinenero chilichonse alibe cholinga chabwino.”

Mawu ameneŵa anali amphamvu, ofalitsidwa patapita zaka 18 Index ya Spanish Inquisition italetsa mwapadera Baibulo ‘m’Chikasitilia romance [Chispanya] kapena m’chinenero china chilichonse chakumaloko.’ Mwachionekere, Reina sanalole kuwopa munthu kuletsa kukonda kwake choonadi.

Kuwonjezera pa kukhala ndi chikhumbo chachikulu cha kupangitsa Baibulo kupezeka kwa anthu onse olankhula Chispanya, Reina anafunanso kutulutsa matembenuzidwe olondola koposa omwe akanatha. M’mawu ake oyamba, anafotokoza maubwino a kutembenuza mwachindunji kuchokera ku zinenero zoyambirira. Zophophonya zina zinaloŵetsedwa m’malembo Vulgate yachilatini, Reina anafotokoza motero. Chimodzi chodziŵika kwambiri cha zimenezi chinali kuchotsedwa kwa dzina la Mulungu.

Dzina la Mulungu m’Matembenuzidwe a Chispanya

Reina anazindikira kuti dzina la Mulungu, Yehova, liyenera kuonekera m’matembenuzidwe alionse okhulupirika a Baibulo, monga momwe linalili m’malembo oyambirira. Anakana kutsatira mwambo wa kuloŵetsa m’malo dzina la Mulungu ndi maina aulemu onga akuti “Mulungu” kapena “Ambuye.” M’mawu ake oyamba a matembenuzidwe ake, anafotokoza zifukwa zake molunjika kwenikweni.

“Tasunga dzinalo (Iehoua), ndi zifukwa zamphamvu kwambiri. Choyamba, chifukwa chakuti paliponse pamene lingapezeke m’matembenuzidwe athu, lingapezekenso m’malembo achihebri, ndipo ife taona kuti sitingathe kulichotsa kapena kulisintha popanda kusonyeza kusakhulupirika kapena kuswa lamulo la Mulungu, limene limalamula kuti tisachotse kapena kuwonjezera kanthu. . . . Mwambo [wa kuchotsa dzinalo], wosonkhezeredwa ndi Mdyerekezi, unachokera m’mwambo wa arabi amakono amene, ngakhale kuti amanena kuti amalilemekeza, kwenikweni abisa dzina Lake loyera, akumachititsa anthu a Mulungu kuliiŵala [dzinalo] limene iye anafuna kudzilekanitsa nalo ndi milungu . . . ina yonse.”

Chikhumbo choyamikirika cha Reina cha kulemekeza dzina la Mulungu chinakhala ndi zotulukapo zazikulu. Kufikira m’tsiku lathu lino, unyinji wa matembenuzidwe achispanya​—achikatolika ndi achiprotesitanti omwe​—atsatira chitsanzo chimenechi, akumagwiritsira ntchito dzina la Mulungu mokwanira. Makamaka chifukwa cha Reina, oŵerenga matembenuzidwe a Baibulo lachispanya angathe kuzindikira mosavuta kuti Mulungu ali ndi dzina lake limene limamsiyanitsa ndi milungu ina yonse.

Chokondweretsa nchakuti dzina la Yehova limaoneka bwinobwino patsamba la mutu wa Baibulo la Reina. Reina anapereka moyo wake pa chifuno chabwino cha kusunga Mawu a Mulungu, kuwapangitsa kupezeka m’chinenero chimene anthu mamiliyoni ambiri akanatha kuŵerenga.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena