Nyimbo 84
“Ndikufuna”
Losindikizidwa
1. Anasonyeza chikondi
Pobweradi padzikoli.
Mwana wa Mulungu
Kukhala ndithu
Ndi anthu n’kuwaphunzitsa.
Anachiritsa odwala,
Akhungu ndi olumala.
Analitu wokhulupirika
Ananena: “Ndikufuna.”
2. Yehova watithandiza
Chifukwatu watipatsa
Mphatso ya Kapolo.
Tigwira ntchito
Nayetu mosangalala.
Ngati timakonda anthu
Iwo adzadziwiratu.
Choncho amasiye akapempha
Uwauze: “Ndikufuna.”
(Onaninso Yoh. 18:37; Aef. 3:19; Afil. 2:7.)