-
N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuphunzira Baibulo?Nsanja ya Olonda—2015 | April 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGAKONDE KUPHUNZIRA BAIBULO?
N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuphunzira Baibulo?
Kodi Mulungu anatilengeranji?
N’chifukwa chiyani timavutika komanso kufa?
Kodi m’tsogolomu mudzachitika zotani?
Kodi Mulungu amadera nkhawa za ine?
Kodi inunso nthawi zina mumakhala ndi mafunso amenewa? Ngati ndi choncho, dziwani kuti si inu nokha. Anthu ambiri amafuna atadziwa mayankho a mafunso amenewa ndi enanso ambiri. Koma kodi n’zotheka kupeza mayankho a mafunsowa?
Anthu ambiri angayankhe kuti inde n’zotheka, chifukwa anthuwa anapeza mayankho a m’Baibulo a mafunsowa. Ngati nanunso mukufuna kudziwa mayankho a mafunso amenewa, tikukulimbikitsani kuti muyambe kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova kwaulere.a
Komabe ambiri amaona kuti sangapeze nthawi yophunzira Baibulo. Enanso amaona kuti kuphunzira Baibulo n’kovuta kwambiri. Pomwe ena amaopa kupangana ndi wa Mboni kuti aziwaphunzitsa Baibulo chifukwa amaona kuti zimenezi ziziwapanikiza. Koma ena salola kuti zimenezi ziwalepheretse kuphunzira Baibulo. Taonani zitsanzo zotsatirazi:
Mayi ena a ku England, dzina lawo a Gill, anati: “Ndili ku yunivesite ndinkaphunzira zokhudza Mulungu. Komanso ndinapempherapo m’chipembedzo chachisiki, chachibuda komanso m’matchalitchi osiyanasiyana. Koma sindinapeze mayankho a mafunso anga. Ndiyeno tsiku lina, wa Mboni za Yehova wina anabwera kunyumba kwathu. Wamboniyo anayankha mafunso anga onse pogwiritsa ntchito Baibulo. Chifukwa cha zimenezi ndinavomera kuti azindiphunzitsa Baibulo.”
Bambo ena a ku Benin, dzina lawo a Koffi, anati: “Ndinali ndi mafunso ambirimbiri, koma zimene abusa a kutchalitchi kwathu ankandiyankha, sizinkandigwira mtima. Koma wa Mboni wina anayankha mafunso anga onse pogwiritsa ntchito Baibulo. Atandifunsa ngati ndingakonde kuphunzira Baibulo kuti ndidziwe zambiri, ndinavomera.”
A José, a ku Brazil, anati: “Ndinkafuna nditadziwa zimene zimachitika munthu akamwalira. Ndinkakhulupirira kuti akufa angathe kuchitira anthu amoyo zinthu zoipa, komabe ndinkafuna nditadziwa zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. Choncho, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi mnzanga wina yemwe anali wa Mboni.”
Mayi ena a ku Mexico, dzina lawo a Dennize, anati: “Ndinkawerenga Baibulo koma sindinkalimvetsa. Kenako a Mboni za Yehova anabwera kwathu ndipo anandifotokozera momveka bwino maulosi angapo a m’Baibulo. Ndinkafuna kudziwa zambiri, choncho ndinavomera kuti azindiphunzitsa Baibulo.”
A Anju, a ku Nepal, anati: “Ndinkafuna kudziwa ngati Mulungu amandiganizira kapena ayi. Choncho, ndinaganiza zopemphera kwa Mulungu yemwe amatchulidwa m’Baibulo. Tsiku lotsatira, kunyumba kwathu kunabwera a Mboni ndipo atandipempha kuti ndiziphunzira nawo Baibulo, ndinavomera.”
Zimene anthuwa ananenazi zikutikumbutsa mawu a Yesu akuti: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyu 5:3) Mwachibadwa, anthufe timafuna kudziwa Mulungu ndipo Mulungu watipatsa Mawu ake, Baibulo. Choncho tiyenera kuphunzira Baibulo kuti timudziwe bwino Mulungu.
Koma kodi phunziro la Baibulo limachitika bwanji? Nanga kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni bwanji? Mafunso amenewa ayankhidwa m’nkhani yotsatira.
a Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.
-
-
Mwayi Woti Aliyense Aphunzire BaibuloNsanja ya Olonda—2015 | April 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGAKONDE KUPHUNZIRA BAIBULO?
Mwayi Woti Aliyense Aphunzire Baibulo
A Mboni za Yehovafe timadziwika ndi ntchito yathu yolalikira. Koma kodi mukudziwa kuti timaphunziranso Baibulo ndi anthu padziko lonse?
M’chaka cha 2014, a Mboni za Yehova pafupifupi 8,000,000 omwe akupezeka m’mayiko 240 ankaphunzira Baibulo ndi anthu pafupifupi 9,500,000 mwezi uliwonse.a Chiwerengero chimenechi ndi chachikulu kuposa chiwerengero cha anthu a m’mayiko 140.
Kuti tithe kugwira ntchitoyi, timasindikiza Mabaibulo, mabuku, magazini ndi zinthu zina zothandiza kuphunzira Baibulo zokwana 500 miliyoni m’zinenero pafupifupi 700. Zimenezi zimathandiza kuti anthu athe kuphunzira Baibulo m’chinenero chomwe amachidziwa bwino.
MAYANKHO A MAFUNSO AMENE ANTHU AMAKONDA KUFUNSA, OKHUDZA PHUNZIRO LA BAIBULO
Kodi phunziro la Baibulo limachitika bwanji?
Timasankha mutu ndipo kenako timakambirana mavesi osiyanasiyana a m’Baibulo ogwirizana ndi mutuwo. Mwachitsanzo, pophunzira Baibulo, tingathe kupeza mayankho a mafunso monga akuti: Kodi Mulungu ndi ndani, nanga ndi wotani? Kodi Mulungu ali ndi dzina? Nanga amakhala kuti? Kodi n’zotheka kukhala naye pa ubwenzi? Koma mwina mungadabwe kuti, kodi timadziwa bwanji mavesi a m’Baibulo omwe akunena za nkhaniyo?
Pophunzira Baibulo ndi anthu, timagwiritsa ntchito buku la masamba 224 lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?b Bukuli limatithandiza kudziwa mavesi amene akugwirizana ndi nkhani imene tikukambirana. Buku limeneli linapangidwa n’cholinga choti lithandize anthu kumvetsa mfundo zosavuta zimene Baibulo limaphunzitsa. M’bukuli muli mutu womwe umanena kuti akufa adzaukitsidwa. Mulinso mutu wonena za Mulungu, wonena za Yesu Khristu, za pemphero, chifukwa chake anthufe timavutika ndi ina yambiri.
Kodi phunziroli limachitikira kuti ndipo limachitika nthawi yanji?
Phunziroli limachitika pa nthawi ndi malo amene mungakonde.
Nanga limatenga nthawi yaitali bwanji?
Anthu ambiri amaphunzira Baibulo kwa ola limodzi mlungu uliwonse. Komabe, kutalika kwa nthawi ya phunziroli kumasiyanasiyana potengera zimene munthu angakonde. Ifeyo timatha kusintha kuti tigwirizane ndi zimene inuyo mukufuna. Ena amaphunzira kwa maminitsi 10 kapena 15 basi pa mlungu.
Kodi munthu amalipira ndalama zingati kuti aziphunzira Baibulo?
Phunziroli ndi laulere, ndipo mabuku amene timagwiritsa ntchito pophunzira sitilipiritsa. Zimenezi n’zogwirizana ndi zimene Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.”—Mateyu 10:8.
Pamatenga nthawi yaitali bwanji kuti munthu adzamalize kuphunzira?
Mukhoza kuphunzira Baibulo kwa nthawi imene inuyo mukufuna. Buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lili ndi mitu 19. Mukhoza kusankha mitu imene mukufuna kuphunzira kapena mukhoza kusankha kuphunzira mitu yonseyo. Zili kwa inunso kusankha kuti muziphunzira nthawi yaitali bwanji pa tsiku.
Ndikavomera kuti ndiziphunzira Baibulo, kodi ndiye kuti ndiyenera kukhala wa Mboni za Yehova?
Ayi. Timadziwa kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wosankha chipembedzo chimene akufuna. Komabe timadziwanso kuti munthu akaphunzira Baibulo angathe kusankha bwino pa nkhani ya chipembedzo.
Kodi ndingatani ngati ndikufuna kudziwa zambiri?
Pitani pa webusaiti yathu ya jw.org/ny. Webusaitiyi ingakuthandizeni kudziwa zambiri zokhudza a Mboni za Yehova.
Kodi ndingatani ngati ndikufuna kuphunzira Baibulo?
Mungalembe pa webusaiti yathu ya jw.org/ny kuti mupemphe munthu woti aziphunzira nanu Baibulo.
Mukhozanso kutilembera kalata pogwiritsa ntchito adiresi yoyenera pa maadiresi omwe ali patsamba 2.
Mungathenso kufunsa a Mboni za Yehova a kudera lanulo.
-