-
Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?Nsanja ya Olonda—2015 | August 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ANTHU AMENE ANAMWALIRA ADZAKHALANSO NDI MOYO?
Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?
“Ndinkaganiza kuti pali malo atatu amene anthu amapitako akamwalira. Malowa ndi kumwamba, kuhelo kapena kupuligatoliyo.a Ndinkadziwa kuti sindinali woyenera kupita kumwamba chifukwa sindinkachita zabwino kwambiri ndipo sindinali woipitsitsa moti n’kupita kuhelo. Sindinkadziwanso bwinobwino kuti kupuligatoliyo kumapita anthu otani. Ziphunzitso zonsezi ndinkangozimva kwa anthu koma ndinali ndisanaziwerengepo m’Baibulo.”—Lionel.
“Ndinaphunzitsidwa kuti anthu onse amapita kumwamba akamwalira, koma ndinkakayikira ngati zimenezi zinalidi zoona. Ndinkaganiza kuti munthu akamwalira ndiye kuti zake zathera pamenepo.”—Fernando.
Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti: ‘N’chiyani kwenikweni chimachitika munthu akamwalira? Kodi munthu akamwalira, amakazunzika kwinakwake? Kodi anthu amene anamwalira tidzawaonanso? Nanga tingatsimikize bwanji kuti tidzawaonanso?’ Kuti tipeze mayankho a mafunsowa, tiyeni tione zimene Baibulo limaphunzitsa. Choyamba, tiyeni tione zimene Baibulo limanena pa nkhani ya imfa. Kenako tiona zimene Baibulo linalonjeza kuti zidzachitikira anthu amene anamwalira.
Kodi akufa amadziwa chilichonse?
YANKHO LA M’BAIBULO: “Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse. Iwo salandiranso malipiro alionse, chifukwa zonse zimene anthu akanawakumbukira nazo zaiwalika. Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse, pakuti kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Manda kumene ukupitako.”b—Mlaliki 9:5, 10.
Manda ndi kumalo kumene anthu amakaikidwa akamwalira. Ndipo anthu amene amaikidwa kumeneko sadziwa kapena kuchita chilichonse. Kodi Yobu, yemwe anali munthu wokhulupirika, ankaona kuti manda ndi malo ozunzirako anthu akufa? Katundu komanso ana onse a Yobu anatha tsiku limodzi lokha. Kenako iyeyo anatuluka zilonda zowawa thupi lonse. Ndiyeno anapempha Mulungu kuti: “Zikanakhala bwino mukanandibisa m’Manda [“mu helo,” Catholic Douay Version], mukanandibisa mpaka mkwiyo wanu utachoka.” (Yobu 1:13-19; 2:7; 14:13) Popeza kuti pa nthawiyi Yobu anali akuzunzika, sakanapempha Mulungu kuti amupititse kumalo kumene akanazunzika kwambiri ndi moto. Choncho Yobu ankaona kuti kumanda ndi kumalo kumene angakapume.
Palinso nkhani zina zimene zingatithandize kudziwa zimene zimachitika munthu akamwalira. Tingawerenge zomwe zinalembedwa m’Baibulo zokhudza anthu 8 omwe anaukitsidwa.—Onani bokosi lakuti “Anthu 8 Otchulidwa M’Baibulo Amene Anaukitsidwa.”
Anthuwa ataukitsidwa, palibe ngakhale mmodzi amene anafotokoza kuti anali kumalo achisangalalo kapena ozunzirako anthu akufa. Akanakhala kuti anali kumalo oterewa, n’zosachita kufunsa kuti akanafotokozera anthu za malowa. Komanso zimenezi zikanalembedwa m’Baibulo kuti aliyense adziwe. Komatu palibe lemba lililonse la m’Baibulo lomwe limanena zoterezi. Uwu ndi umboni wakuti anthu 8 omwe anaukitsidwawo analibe choti anganene chifukwa sankadziwa kanthu ndipo zinali ngati anagona tulo tofa nato. Ndipotu nthawi zina Baibulo limayerekezera imfa ndi tulo. Mwachitsanzo, limati Davide ndi Sitefano omwe anali anthu okhulupirika “anagona tulo ta imfa.”—Machitidwe 7:60; 13:36.
N’chiyani chidzachitikire anthu amene anamwalira? Kodi angadzakhalenso ndi moyo?
a Mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, mawu akuti “Manda” amagwiritsidwa ntchito ponena za mawu achiheberi akuti “Sheol” ndiponso achigiriki akuti “Hades.” Mabaibulo ena amagwiritsa ntchito mawu akuti “helo,” komaMalemba sanena kuti malowa ndi kumene kumapita anthu akufa kuti azikazunzika ndi moto.
-
-
Kodi Akufa Angadzakhalenso ndi Moyo?Nsanja ya Olonda—2015 | August 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ANTHU AMENE ANAMWALIRA ADZAKHALANSO NDI MOYO?
N’chiyani Chidzachitikire Anthu Amene Anamwalira?
Kodi akufa angadzakhalenso ndi moyo?
YANKHO LA M’BAIBULO: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake [a Yesu] ndipo adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29.
Pa lembali, Yesu ankalonjeza kuti akadzayamba kulamulira monga Mfumu padzikoli, adzaukitsa anthu amene anamwalira. Fernando amene watchulidwa m’nkhani yapitayi anati: “Nditawerenga koyamba lemba la Yohane 5:28, 29, ndinasangalala kwambiri. Lembali linandithandiza kukhala ndi chikhulupiriro chakuti akufa adzakhalanso ndi moyo ndipo ndinayamba kuganizira kwambiri mmene moyo udzakhalire wosangalatsa mtsogolo.”
Yobu ankakhulupirira kuti akamwalira, Mulungu adzamuukitsa. Iye anafunsa kuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?” Yobu anayankha yekha funsoli ndipo anati: “Ndidzadikira masiku onse a ntchito yanga yokakamiza [nthawi yomwe ndili m’Manda], mpaka mpumulo wanga utafika. Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha.”—Yobu 14:14, 15.
Nkhani ya kuukitsidwa kwa Lazaro, imatitsimikizira kuti akufa adzakhalanso ndi moyo
Marita, yemwe anali mchemwali wake wa Lazaro, ankadziwa kuti akufa adzakhalanso ndi moyo. Mwachitsanzo, mchimwene wake Lazaro atamwalira Yesu anamuuza kuti: “Mlongo wako adzauka.” Marita anayankha kuti: “Ndikudziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lomaliza.” Kenako Yesu anamuuza kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo. Aliyense wokhulupirira mwa ine, ngakhale amwalire, adzakhalanso ndi moyo.” (Yohane 11:23-25) Yesu atangomaliza kunena zimenezi, anaukitsa Lazaro. Nkhani yosangalatsayi ikutithandiza kudziwa kuti mtsogolomu anthu ambiri adzaukitsidwa. Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kudziwa kuti anthu akuukitsidwa padziko lonse lapansi.
Kodi ena adzapita kumwamba?
YANKHO LA M’BAIBULO: Mawu a Mulungu amasonyeza kuti kuuka kwa Yesu n’kosiyana kwambiri ndi kwa anthu 8 omwe anatchulidwa m’Baibulo. Zili choncho chifukwa chakuti anthu 8 aja ataukitsidwa, anakhalanso padzikoli. Koma ponena za kuukitsidwa kwa Yesu, Baibulo limati: “Yesu Khristu . . . ali kudzanja lamanja la Mulungu, pakuti anapita kumwamba.” (1 Petulo 3:21, 22) Kodi ndi Yesu yekha amene anali woyenera kupita kumwamba? Yesu asanamwalire, anauza otsatira ake kuti: “Ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengerani kwathu, kuti kumene kuli ineko inunso mukakhale kumeneko.”—Yohane 14:3.
Yesu anapita kumwamba ndipo anakakonzera malo ophunzira ake ena. Anthu omwe amaukitsidwa n’kupita kumwamba, onse pamodzi adzakwana 144,000. (Chivumbulutso 14:1, 3) Kodi anthu amenewa azikatani kumwambako?
Anthuwa akakhala ndi ntchito yaikulu. Baibulo limanena kuti: “Wodala ndi woyera ndiye aliyense wouka nawo pa kuuka koyamba. Pa iwo, imfa yachiwiri ilibe ulamuliro. Koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.” (Chivumbulutso 20:6) Choncho anthu amene adzapite kumwamba adzakhala ansembe ndi mafumu ndipo azidzalamulira dzikoli limodzi ndi Yesu Khristu.
Kodi palinso ena amene adzaukitsidwe?
YANKHO LA M’BAIBULO: Baibulo limafotokoza mawu amene mtumwi Paulo ananena kuti: “Ndipo ine ndili ndi chiyembekezo mwa Mulungu, chimenenso anthu awa ali nacho, kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Machitidwe 24:15.
Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti anthu ambiri omwe anamwalira adzakhalanso ndi moyo
Kodi ndi anthu otani omwe ali m’gulu la “olungama” amene Paulo ananena kuti adzaukitsidwa? Taganizirani zimene zinachitikira Danieli yemwenso anali munthu wokhulupirika. Iye atatsala pang’ono kumwalira Yehova anamuuza kuti: “Udzapuma. Koma udzauka kuti ulandire gawo lako pa mapeto a masikuwo.” (Danieli 12:13) Kodi Danieli akadzauka akakhala kuti? Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Salimo 37:29) Yesu ananenanso kuti: “Odala ndi anthu amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5) Danieli ndi anthu ena okhulupirika adzaukitsidwa kuti adzakhalenso ndi moyo padziko lapansi mwinanso kwamuyaya.
Nanga ndi anthu otani amene ali m’gulu la “osalungama”? Ndi anthu ambirimbiri amene anakhalapo ndi moyo n’kumwalira koma analibe mwayi wophunzira Baibulo ndi kugwiritsa ntchito zimene Malemba amanena. Anthu amenewa akadzaukitsidwa, adzakhala ndi mwayi wodziwa Yehovaa ndi Yesu. (Yohane 17:3) Amene adzasankhe kutumikira Mulungu adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wopanda malire padziko lapansi, mofanana ndi Yehova.
Amene adzasankhe kutumikira Mulungu adzasangalala ndi moyo wopanda malire komanso wathanzi
Kodi zinthu zidzakhala bwanji padzikoli?
YANKHO LA M’BAIBULO: Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” (Chivumbulutso 21:4) “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.”—Yesaya 65:21.
Ganizirani mmene mudzasangalalire kukhala moyo woterewu limodzi ndi achibale anu amene adzaukitsidwe. Koma kodi tingatsimikize bwanji kuti akufa adzakhalanso ndi moyo?
a Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.
-
-
Tingatsimikize Bwanji Kuti Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo?Nsanja ya Olonda—2015 | August 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ANTHU AMENE ANAMWALIRA ADZAKHALANSO NDI MOYO?
Tingatsimikize Bwanji Kuti Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo?
Kodi kukhulupirira kuti akufa adzakhalanso ndi moyo ndi kungolimbikira mtunda wopanda madzi? Tiyeni tione zimene Paulo ankakhulupirira pa nkhaniyi. Iye analemba kuti: “Ngati tayembekezera Khristu m’moyo uno wokha, ndiye kuti ndife omvetsa chisoni kuposa anthu ena onse. Komabe, Khristu anaukitsidwa kwa akufa, n’kukhala chipatso choyambirira cha amene akugona mu imfa.” (1 Akorinto 15:19, 20) Uwu ndi umboni wakuti Paulo ankaona kuti nkhani yakuti akufa adzakhalanso ndi moyo si nkhambakamwa chabe. Ndipotu kuukitsidwa kwa Yesu n’kumene kunamuthandiza kuti asamakayikire zakuti anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo.a (Machitidwe 17:31) N’chifukwa chake Paulo ananena kuti Yesu ndi “chipatso choyambirira,” kutanthauza kuti anali munthu woyamba kupatsidwa moyo wosatha pambuyo poukitsidwa. Choncho ngati Yesu anali woyamba ndiye kuti anthu enanso anayenera kudzalandira moyo woterewu.
Yobu anauza Mulungu kuti: “Mudzalakalaka ntchito ya manja anu.”—Yobu 14:14, 15
Tiyeni tione umboni wina wosonyeza kuti anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo. Baibulo limasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu amene amanena zoona ndipo limati: “Mulungu . . . sanganame.” (Tito 1:2) Yehova sanayambe wanamapo ndipo sanganame ngakhale zitavuta bwanji. Iye sangangolonjeza kuti akufa adzakhalanso ndi moyo koma akudziwa kuti akunama. Zimenezi sizingachitike ngakhale pang’ono.
Chikondi n’chimene chinachititsa kuti Yehova akonze zoti anthu amene anamwalira adzakhalenso ndi moyo. Yobu anafunsa kuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo? . . . Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha. Mudzalakalaka ntchito ya manja anu.” (Yobu 14:14, 15) Yobu sankakayikira kuti ngakhale atamwalira, Atate wake wachikondi adzalakalaka kumuukitsa. Kodi Mulungu anasintha? Iye anati: “Ine ndine Yehova, sindinasinthe.” (Malaki 3:6) Mulungu amalakalakabe kuti adzaukitse anthu amene anamwalira n’cholinga choti adzasangalale ndi moyo wathanzi. Izi ndi zimene kholo lachikondi limene mwana wake wamwalira limalakalaka. Koma kholo lingasiyane ndi Mulungu chifukwa iye ali ndi mphamvu zochitira chilichonse chimene akufuna.—Salimo 135:6.
Ngakhale kuti imfa ndi yowawa, Mulungu adzaithetsa
Yehova adzapatsa Mwana wake mphamvu zoukitsa anthu amene anamwalira ndipo zimenezi zidzachititsa kuti achibale awo adzakhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya. Kodi Yesu amamva bwanji akamaganizira kuti adzaukitsa anthu omwe anamwalira? Asanaukitse Lazaro, Yesu anakhudzidwa ndi chisoni chimene achemwali ake a Lazaro ndi anzake anali nacho ndipo nayenso “anagwetsa misozi.” (Yohane 11:35) Nthawi inanso Yesu anakumana ndi mayi amasiye a ku Naini amene mwana wawo anamwalira. Mayiwa anali ndi mwana mmodzi yekha ndipo Yesu “anawamvera chifundo, choncho anawauza kuti: ‘Tontholani mayi.’” Nthawi yomweyo anaukitsa mwanayo. (Luka 7:13) Uwu ndi umboni wakuti Yesu samasangalala ndi imfa ndipo amakhudzidwa kwambiri akamaona kuti anthu ali ndi chisoni. Choncho adzasangalala kwambiri akamadzaukitsa anthu amene anamwalira n’kuona abale awo akusangalala.
Kodi muli ndi chisoni chifukwa cha imfa ya achibale anu? Mwina mumaganiza kuti achibale anuwo simudzawaonanso. Komatu mudzawaonanso chifukwa Yehova adzagwiritsa ntchito Mwana wake kuukitsa anthu amene anamwalira. Yehova akufuna kuti mudzadzionere nokha mmene zimenezi zidzachitikire. Iye akufuna kuti mudzalandire achibale anu pa nthawi imene azidzaukitsidwa. Imeneyitu idzakhala nthawi yosangalatsa chifukwa tidzachitira zinthu limodzi ndi achibale athu mpaka kalekale popanda kuganizira kuti tsiku linalake wina akhoza kumwalira.
Lionel, yemwe watchulidwa m’nkhani yoyambirira uja anati: “Kenako ndinaphunzira kuti akufa adzakhalanso ndi moyo. Poyamba zinali zovuta kukhulupirira ndipo ndinkaona ngati munthu amene ankandiuzayo ankandinamiza. Koma nditawerenga m’Baibulo ndinaona kuti n’zoona. Ndikuona kuchedwa kuti nthawiyi idzafike kuti ndidzaonanenso ndi agogo anga.”
Kodi mukufuna kudziwa zambiri? A Mboni za Yehova angasangalale kukusonyezani m’Baibulo lanu umboni wosonyeza kuti anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo.b
a Kuti mupeze umboni woti Yesu anaukitsidwadi, werengani buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? tsamba 78-86, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
b Ngati mukufuna kudziwa zambiri, werengani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? mutu 7. Bukuli ndi lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova ndipo
-